A A A A A

Good Character: [Faith]


MATEYU 21:22
Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.

AROMA 10:17
Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.

AHEBRI 11:1-6
[1] Koma cikhulupiriro ndico cikhazikitso ca zinthu zoyembekezeka, ciyesero ca zinthu zosapenyeka.[2] Pakuti momwemo akulu anacitidwa umboru.[3] Ndi cikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zocokera mwa zoonekazo.[4] Ndi cikhulupiriro Abeli anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kami, mene anacitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nacitapo umboni Mulungu pa mitulo yace; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.[5] Ndi cikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anacitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;[6] koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.

MARKO 11:22-24
[22] Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu,[23] Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwace, koma adzakhulupirira kuti cimene acinena cicitidwa, adzakhala naco.[24] Cifukwa cace ndinena ndi inu, Zinthu ziri zonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.

YAKOBO 2:19
Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; ucita bwino; ziwanda zikhulupiranso, ndipo zinthunthumira.

AEFESO 2:8-9
[8] Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;[9] cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.

LUKA 1:37
Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

MIYAMBO 3:5-6
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;[6] Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

2 AKORINTO 5:7
(pakuti tiyendayenda mwa cikhulupiriro si mwa cionekedwe);

AEFESO 2:8
Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;

1 AKORINTO 2:5
kuti cikhulupiriro canu cisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

YAKOBO 1:5-8
[5] Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,[6] Koma apemphe ndi cikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.[7] Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;[8] munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zace zonse.

AFILIPI 4:13
Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.

YAKOBO 1:5-8
[5] Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,[6] Koma apemphe ndi cikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.[7] Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;[8] munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zace zonse.

AFILIPI 4:13
Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.

YAKOBO 2:24
Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi nchito yace, osati ndi cikhulupiriro cokha.

LUKA 17:5
Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere cikhulupiriro.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society