A A A A A

Good Character: [Discipline]


2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.

AEFESO 6:4
Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi cilangizo ca Ambuye.

MIYAMBO 10:17
Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; Koma wosiya cidzudzulo asocera.

MIYAMBO 12:1
Wokonda mwambo akonda kudziwa; Koma wakuda cidzudzulo apulukira.

MIYAMBO 13:1
Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; Koma wonyoza samvera cidzudzulo.

MIYAMBO 13:24
Wolekereramwanace osammenya amuda; Koma womkonda amyambize kumlanga.

MIYAMBO 22:6
Phunzitsa mwana poyamba njira yace; Ndipo angakhale atakalamba sadzacokamo.

MIYAMBO 22:15
Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; Koma ntyole yomlangira idzauingitsira kutari.

MIYAMBO 29:15-17
[15] Ntyole ndi cidzudzulo zipatsa nzeru; Koma mwana womlekerera acititsa amace manyazi.[16] Pocuruka oipa zolakwa zicuruka; Koma olungama adzaona kugwa kwao.[17] Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; Nadzasangalatsa moyo wako.

CHIVUMBULUTSO 3:19
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero cita cangu, nutembenuke mtima.

TITO 1:8
komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

MIYAMBO 23:13-14
[13] Usamane mwana cilango; Pakuti ukammenya ndi ntyole safa ai.[14] Udzammenya ndi ntyole, Nudzapulumutsa moyo wace kunsi kwa manda.

AHEBRI 12:10-11
[10] Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa ciyero cace.[11] Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.

YOBU 5:17-18
[17] Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; Cifukwa cace usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.[18] Pakuti apweteka, namanganso mabala; Alasa, ndi manja ace omwe apoletsa.

MIYAMBO 3:11-12
[11] Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, Ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwace;[12] Pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; Monga atate mwana amene akondwera naye.

DEUTERONOMO 8:5-6
[5] Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.[6] Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kumuopa.

1 AKORINTO 9:25-27
[25] Koma yense wakuyesetsana adzikaniza zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakubvunda; 3 koma ife wosabvunda.[26] Cifukwa cace ine ndithamanga cotero, si nonga cosinkhasinkha. Ndilimbaaa cotero, si monga ngati kupanda nlengalenga;[27] koma 4 ndipumpuatha thupi langa, ndipo ndiliyesa capolo; kuti, kapena ngakhale rdalalikira kwa ena, 5 ndingakhale votayika ndekha.

2 AKORINTO 7:9-11
[9] Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.[10] Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.[11] Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.

MASALIMO 94:12-14
[12] Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; Ndi kumphunzitsa m'cilamulo canu;[13] Kuti mumpumitse masiku oipa; Kufikira atakumbira woipa mbuna.[14] Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace, Ndipo sadzataya colandira cace.

AHEBRI 12:5-9
[5] ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese copepuka kulanga kwa Ambuye, Kapena usakomoke podzudzulidwa ndilye;[6] Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, Nakwapula mwana ali yense amlandira.[7] Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu acitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wace wosamlanga?[8] Koma ngati mukhala opanda cilango, cimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.[9] Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

AEFESO 6:1-9
[1] Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ici ncabwino.[2] Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),[3] kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikuru padziko.[4] Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi cilangizo ca Ambuye.[5] Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukila kanthu kena, monga kwa Kristu;[6] si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima;[7] akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai;[8] podziwa kuti cinthu cokoma ciri conse yense acicita, adzambwezera comweci Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.[9] Ndipo, ambuye inu, muwacitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankhu kwa iye.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society