A A A A A

Good Character: [Compassion]


AKOLOSE 3:12
Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

EKSODO 33:19
Ndipo iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzachula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzacitira ufulu amene ndidzamcitira ufulu; ndi kucitira cifundo amene ndidzamcitira cifundo.

YESAYA 30:18
Cifukwa cace Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo cifukwa cace Iye adzakuzidwa, kuti akucitireni inu cifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa ciweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

YESAYA 49:10-13
[10] Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawacitira cifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.[11] Ndipo ndidzasandutsa mapiri anga onse akhale njira, ndipo makwalala anga adzakwezeka.[12] Taonani, awa adzacokera kutari; ndipo taonani, awa ocokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ocokera ku dziko la Sinimu.[13] Yimbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, yimbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, nadzacitira cifundo obvutidwa ace.

YESAYA 54:10
Pakuti mapiri adzacoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakucokera iwe, kapena kusunthika cipangano canga ca mtendere, ati Yehova amene wakucitira iwe cifundo.

YESAYA 63:7
Ndidzachula za cifundo cace ca Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wace waukuru kwa banja la Israyeli, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa cifundo cace, ndi monga mwa nchito zocuruka za cikondi cace.

YAKOBO 5:11
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za cipiriro ca Yobu, ndipo mwaona citsiriziro ca Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala cikondi, ndi wacifundo.

MALIRO 3:32
Angakhale aliritsa, koma adzacitira cisoni monga mwa kucuruka kwa zifundo zace.

MASALIMO 51:1
Mundicitire ine cifundo, Mulungu, Monga mwa kukoma mtima kwanu; Monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu Mufafanize macimo anga.

MASALIMO 103:13
Monga atate acitira ana ace cifundo, Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye.

MASALIMO 116:5
Yehova ngwa cifundo ndi wolungama; Ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.

MASALIMO 119:77
Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; Popeza cilamulo canu cindikondweretsa.

MASALIMO 119:156
Zacifundo zanu ndi zazikuru, Yehova; Mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.

MASALIMO 145:9
Yehova acitira cokoma onse; Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.

AROMA 9:15
Pakuti anati ndi Mose, Ndidzacitira cifundo amene ndimcitira cifundo, ndipo ndidzakhala ndi cisoni kwa iye amene ndikhala naye cisoni.

2 AKORINTO 1:3-4
[3] Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,[4] woo titonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iri yonse, mwa citonthozo cimene titonthozedwa naco tokha ndi Mulungu.

AFILIPI 2:1-3
[1] Ngati tsono muli citonthozo mwa Kristu, ngati cikhazikitso ca cikondi, ngati ciyanjano ca Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,[2] kwaniritsani cimwemwe canga, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala naco cikondi comwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;[3] musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;

MATEYU 9:35-38
[35] Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, naciritsa nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.[36] Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi cisoni cifukwa ca iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.[37] Pomwepo ananena kwa ophunzira ace, Zotuta zicurukadi koma anchito ali owerengeka.[38] Cifukwa cace pempherani Mwini zotuta kuti akokose anchito kukututakwace.

MASALIMO 103:1-5
[1] Lemekeza Yehova, moyo wanga; Ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lace loyera.[2] Lemekeza Yehova, moyo wanga, Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:[3] Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; Naciritsa nthenda zako zonse;[4] Amene aombola moyo wako ungaonongeke; Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma:[5] Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; Nabweza ubwana wako unge mphungu.

MATEYU 20:29-34
[29] Ndipo pamene iwo analikuturuka m'Yeriko, khamu lalikuru la anthu linamtsata Iye.[30] Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'rnphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anapfuula nati, Muticitire ife cifundo, Inu Mwana wa Davide.[31] Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, muticitire cifundo, Inu Mwana wa Davide.[32] Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikucitireni ciani?[33] Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye,[34] Ndipo Yesu anagwidwa ndi cifundo, nakhudza maso ao; ndipo pornwepo anapenyanso, namtsata Iye.

MATEYU 14:13-21
[13] Ndipo Yesu pakumva, anacokera kumeneko m'ngalawa, kunka ku malo acipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kucokera m'midzi.[14] Ndipo Iye anaturuka, naona khamu lalikuru la anthu, nacitira iwo cifundo, naciritsa akudwala ao.[15] Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ace anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga cipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite ku midzi kukadzigulira okha kamba.[16] Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe cifukwa ca kumukira, apatseni ndinu adye.[17] Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tiribe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.[18] Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine.[19] Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi pamaudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.[20] Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, mitanga khumi ndi iwiri yodzala.[21] Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

MATEYU 15:29-39
[29] Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.[30] Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ace: ndipo Iye anawaciritsa;[31] kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nacira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.[32] Ndipo Yesu anaitana ophunzira ace, nati, Mtima wanga ucitira cifundo khamu la anthuwa, pakuti ali cikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira,[33] Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'cipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu?[34] Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono.[35] Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse;[36] natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.[37] Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala malicero asanu ndi awiri odzala.[38] Ndipo anadyawo anali amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana.[39] Ndipo m'mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m'ngalawa, nafika m'malire Magadani.

MATEYU 6:30-44
[30] Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?[31] Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani?[32] Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.[33] Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.[34] Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.[35] Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.[36] Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.[37] Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?[38] Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli.[39] Wonyenga iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.[40] Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.[41] Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo cidzatsegulidwa kwa inu;[42] pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo citsegulldwa.[43] Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wace mkate, adzampatsa mwala?[44] Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi?

LUKA 15:11-32
[11] Ndipo iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri;[12] ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wace, Atate, ndigawirenitu zanga za pa cuma canu. Ndipo iye anawagawira za moyo wace.[13] Ndipo pakupita masiku owerengekamwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wace ku dziko lakutari; ndipo komweko anamwaza cuma cace ndi makhalidwe a citayiko.[14] Ndipo pamene anatha zace zonse, panakhala njala yaikuru m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.[15] Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwace kukaweta nkhumba.[16] Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yace ndi makoko amene nkhumba rimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.[17] Koma m'mene anakumbukila mumtima, anati, Anchito olipidwa ambiri a atate wanga ali naco cakudya cocuruka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?[18] Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena nave, Atate, ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu;[19] sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa anchito anu.[20] Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wace. Koma pakudza iye kutali, atate wace anamuona, nagwidwa cifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pace, nampsompsonetsa.[21] Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu.[22] Koma atateyo ananena kwaakapolo ace, Turutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni phete ku dzanja lace ndi nsapato ku apazi ace;[23] ndipo idzani naye mwana wa ng'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;[24] cifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.[25] Koma mwana wace wamkuru anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuyimba ndi kubvina.[26] Ndipo anaitana mmodzi wa anayamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?[27] Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwana wa ng'ombe wonenepa, cifukwa anamlandira iye wamoyo.[28] Koma anakwiya, ndipo sanafuna kulowamo, Ndipo atate wace anaturuka namdandaulira.[29] Koma anayankha nati kwa atate wace, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthawi iri yonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.[30] Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi aciwerewere, munamphera iye mwana wa ng'ombe wonenepa.[31] Koma iye ananena nave, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako.[32] Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: cifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society