A A A A A

God: [God's Timing]


1 TIMOTEO 3:15
kuti udziwe kuyenedwa kwace pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Eklesia wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mcirikizo wa coonadi.

YOHANE 6:54
11 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

YOHANE 8:32
ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

YESAYA 40:31
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga kuma osalema; adzayenda koma osalefuka.

HABAKUKU 2:3
Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama; akacedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

MLALIKI 3:1
Kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi cofuna ciri conse ca pansi pa thambo ciri ndi mphindi yace;

MASALIMO 27:14
Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; Inde, yembekeza Yehova.

MARKO 6:3
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

YOHANE 12:48
12 iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye; 13 mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomariza.

YOHANE 1:1
PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

AGALATIYA 6:9
Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

MASALIMO 31:15
Nyengo zanga ziri m'manja mwanu: Mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

AGALATIYA 1:19
Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

MALAKI 1:11
Pakuti kuyambira koturukira dzuwa kufikira kolowera kwace dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa cofukiza ndi copereka coona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

2 PETRO 3:8
Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.

MASALIMO 37:7
Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye: Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace, Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.

MLALIKI 3:11
Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.

MALIRO 3:25-26
[25] Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.[26] Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha cipulumutso ca Yehova.

MACHITIDWE A ATUMWI 1:7
Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha.

AGALATIYA 4:4
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wace, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,

AEFESO 5:16
akucita macawi, popeza masiku ali oipa,

YOHANE 3:3-5
[3] Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.[4] Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa?[5] Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

AHEBRI 12:14
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

GENESIS 1:1
PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

MALIRO 3:25
Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.

MASALIMO 145:15
Maso a onse ayembekeza Inu; Ndipo muwapatsa cakudya cao m'nyengo zao.

MLALIKI 8:6
pakuti kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi ciweruzo cace; popeza zoipa za munthu zimcurukira;

AROMA 8:28
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.

MIYAMBO 3:5-6
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;[6] Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

AEFESO 1:10
kuti pa tnakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.

YOHANE 16:13
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.

AGALATIYA 4:19
Tiana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Kristu aumbika mwa inu,

MATEYU 16:18
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo.

MATEYU 18:15-18
[15] Ndipo ngati mbale wako akucimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.[16] Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.[17] Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.[18] Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.

AEFESO 1:22-23
[22] ndipo 3 anakonza zonse pansi pa mapazi ace, nampatsa iye 4 akhale mutu pamtu pa zonse,[23] 5 kwa Eklesia amene ali thupi lace, 6 mdzazidwe wa iye amene adzazazonse m'zonse.

AEFESO 5:23
Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

MACHITIDWE A ATUMWI 4:32
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka cuma anali naco ndi kace ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

1 AKORINTO 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.

YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

YOHANE 14:6-28
[6] Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.[7] Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye.[8] Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira.[9] Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?[10] Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.[11] Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe.[12] Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate.[13] Ndipo cimene ciri conse mukafunse m'dzina langa, ndidzacicita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.[14] Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzacita.[15] Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.[16] Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,[17] ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.[18] Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.[19] Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.[20] Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.[21] Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.[22] Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?[23] Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.[24] Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.[25] Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.[26] Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.[27] 4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.[28] Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine.

MASALIMO 37:7-9
[7] Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye: Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace, Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.[8] Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: Usabvutike mtima ungacite coipa,[9] Pakuti ocita zoipa adzadulidwa: Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.

MASALIMO 49:1
Dzamveni kuno, anthu inu nonse; Cherani khutu, inu nonse amakono,

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society