A A A A A

God: [God's Will]


YEREMIYA 29:11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

1 TIMOTEO 2:3-4
[3] Pakuti ici ncokoma ndi colandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;[4] amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.

1 ATESALONIKA 5:18
M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

1 ATESALONIKA 4:3
Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;

AHEBRI 13:20-21
[20] Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye woturuka mwa akufa 1 Mbusa wamkuru wa nkhosa 2 ndi mwazi wa cipangano cosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,[21] 3 akuyeseni inu opanda cirema m'cinthu ciri conse cabwino, kuti mucite cifuniro cacej ndi kucita mwa ife comkondweretsa pamaso pace, mwa Yesu Kristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

LUKA 9:23
Ndipo iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wace tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.

MASALIMO 119:105
Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, Ndi kuunika kwa panjira panga,

YAKOBO 1:5
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,

MIYAMBO 3:5-6
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;[6] Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

1 PETRO 2:15
Pakuti cifuniro ca Mulungu citere, kuti ndi kucita zabwino mukatontholetse cipulukiro ca anthu opusa;

MATEYU 6:10
Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano.

AEFESO 5:15-20
[15] Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;[16] akucita macawi, popeza masiku ali oipa,[17] Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani.[18] Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu,[19] ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;[20] ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;

2 PETRO 3:9
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

1 YOHANE 1:9
Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.

1 TIMOTEO 2:4
amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.

MIKA 6:8
Iye anakuuza, munthuwe, comwe ciri cokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti ucite colungama, ndi kukonda cifundo ndi kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako?

MIYAMBO 16:4
Zonse Yehova anazipangaziri ndi zifukwa zao; Ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa,

AHEBRI 10:36
Pakuti cikusowani cipiriro, kuti 8 pamene mwacita cifuniro ca Mulungu, mukalandire lonjezano.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society