A A A A A

God: [God's Love]


1 AKORINTO 13:13
Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.

1 YOHANE 3:1
Taonani, cikondico Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere. Mwa ici dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira iye.

1 YOHANE 4:7-8
[7] Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu,[8] iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.

1 YOHANE 4:16-19
[16] Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.[17] M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.[18] Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.[19] Tikonda ife, cifukwa anayamba iye kutikonda.

AGALATIYA 2:20
Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.

YEREMIYA 29:11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

YEREMIYA 31:3
Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi cikondi cosatha; cifukwa cace ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

YOHANE 15:13
Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace.

MASALIMO 86:15
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wacisomo, Wosapsa mtima msanga, ndi wocurukira cifundo ndi coonadi.

MASALIMO 136:26
Yamikani Mulungu wa kumwamba, Pakuti cifundo cace ncosatha.

AROMA 5:8
Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.

DEUTERONOMO 7:9
Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.

ZEFANIYA 3:17
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi cimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'cikondi cace; adzasekerera nawe ndi kuyimbirapo.

AEFESO ๒:๔-๕
[๔] koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco,[๕] tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),

1 PETRO 5:6-7
[6] Potero dzicepetseni pansi pa dzanja la mphamvu lao Mulungu, kuti panthawi yace akakukwezeni;[7] ndi kutaya pa iye nkhawa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.

AROMA 8:37-39
[37] Koma 13 m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.[38] Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu,[39] ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society