A A A A A

God: [God's Grace]


AEFESO 2:8-9
[8] Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;[9] cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.

TITO 2:11
Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse,

AROMA 11:6
Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndinchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo.

MACHITIDWE A ATUMWI 15:11
Koma tikhulupira tidzapulumuka mwa cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, monga iwo omwe.

AHEBRI 4:16
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

MACHITIDWE A ATUMWI 20:32
Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a cisomo cace, cimene ciri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu colowa mwa onse oyeretsedwa.

YAKOBO 4:6
Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.

AEFESO 1:7
Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,

AROMA 5:1-2
[1] Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu;[2] amene ife tikhoza kulowa naye ndi cikhulupiriro m'cisomo ici m'mene tirikuunamo; ndipo tikondwera m'ciyembekezo ca ulemerero wa Mulungu.

TITO 3:7
kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha.

AROMA 3:20-24
[20] cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi Debito za lamulo; pakuti ucimo udziwika ndi lamulo.[21] Koma tsopano cilungamo ca Mulungu caoneka copanda lamulo, cilamulo ndi aneneri acitira ici umboni;[22] ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana;[23] pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;[24] ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;

YOHANE 1:17
Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu.

2 TIMOTEO 2:1
Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'cisomo ca m'Kristu Yesu.

2 TIMOTEO 1:9
amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa nchito zathu, komatu monga mwa citsimikizo mtima ca iye yekha, ndi cisomo, copatsika kwa ife mwa Kristu Yesu zisanayambe nthawi zoyamba,

2 AKORINTO 12:9
Ndipo ananena kwa ine, Cisomo canga cikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufoko. Cifukwa cace makamaka ndidzadzitamandira rriokondweratu m'maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.

AROMA 3:24
ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;

MACHITIDWE A ATUMWI 20:24
Komatu sindiuyesa kanthu moyo, wanga, kuti uli wa mtengo wace kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kucitira umboni Uthenga Wabwino wa cisomo ca Mulungu.

1 PETRO 5:10
Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

AEFESO 2:4-9
[4] koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco,[5] tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),[6] ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Kristu Yesu;[7] kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.[8] Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;[9] cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.

AROMA 2:8-10
[8] koma kwa iwo andeu, ndi osamvera coonadi, koma amvera cosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,[9] nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu ali yense wakucita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mhelene;[10] koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu ali yense wakucita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene;

1 AKORINTO 15:10
Koma ndi cisomo ca Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo cisomo cace ca kwa ine sicinakhala copanda pace, koma ndinagwirira nchito yocuruka ya iwo onse; koma si ine, komacisomo ca Mulungu cakukhala ndi ine.

AEFESO 2:5
tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),

TITO 2:11-12
[11] Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse,[12] ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

2 AKORINTO 12:8-9
[8] Za ici ndinapemphera Ambuye katatu kuti cicoke rkwafne.[9] Ndipo ananena kwa ine, Cisomo canga cikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufoko. Cifukwa cace makamaka ndidzadzitamandira rriokondweratu m'maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.

YOHANE 1:14
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.

AEFESO 4:7
Ndipo kwa yense wa ife capatsika cisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu.

2 PETRO 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere zicurukitsidwe m'cidziwitso ca Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.

AROMA 1:7
kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

AROMA 5:17
Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu.

YOHANE 1:16
Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo.

TITO 2:11-14
[11] Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse,[12] ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;[13] akulindira ciyembekezo eodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkuru ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu;[14] amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole Ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ace eni eni, acangu pa nchito zokoma.

AROMA 5:2
amene ife tikhoza kulowa naye ndi cikhulupiriro m'cisomo ici m'mene tirikuunamo; ndipo tikondwera m'ciyembekezo ca ulemerero wa Mulungu.

2 AKORINTO 6:1
Ndipo a ocita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire cisomo ca Mulungu kwacabe inu,

2 ATESALONIKA 1:12
kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa iye, monga mwa cisomo ca Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.

1 TIMOTEO 1:13-16
[13] ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wacipongwe; komatu anandicitira cifundo, popeza ndinazicita wosazindikira, wosakhulupirira;[14] koma cisomo ca Ambuye wathu cidacurukatu pamodzi ndi cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.[15] Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; wa iwowa ine ndine woposa;[16] komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.

AROMA 6:23
Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

AROMA 3:23
pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

2 AKORINTO 9:8
Ndipo Mulungu akhoza kucurukitsira cisomo conse kwa inu; kuti inu, pokhala naco cikwaniro conse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukacurukire ku nchito yonse yabwino;

YAKOBO 2:8
Koma ngati mucita cikwanirire lamulolo lacifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, mucita bwino:

1 YOHANE 5:3
Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa.

2 PETRO 3:9
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

AROMA 3:27
Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La nchito kodi? lai; koma ndi lamulo la cikhulupiriro.

YAKOBO 2:12
Lankhulani motero, ndipo citani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.

AROMA 7:12
Cotero cilamulo ciri coyera, ndi cilangizo cace ncoyera, ndi colunaama, ndi cabwino.

AROMA 1:16
Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society