A A A A A

God: [Free Will]


1 AKORINTO 10:13
Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

2 MBIRI 9:7
Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima ciimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu.

2 PETRO 3:9
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

AGALATIYA 5:13
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; cokhaco musacite nao ufulu wanu cothandizira thupi, komatu mwa cikondi citiranani ukapolo.

YOHANE 7:17
Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.

YOSWA 24:15
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

MARKO 8:34
Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ace, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wace, nanditsate Ine.

MIYAMBO 16:9
Mtima wa munthu ulingalira njira yace; Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.

CHIVUMBULUTSO 3:20
Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

AROMA 6:23
Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

AROMA 13:2
Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza coikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga

AROMA 10:9-10
[9] kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:[10] pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m'kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso

AGALATIYA 5:16-17
[16] Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.[17] Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.

GENESIS 2:16-17
[16] Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko;[17] koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.

YESAYA 55:6-7
[6] Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;[7] woipa asiye njira yace, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ace, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamcitira cifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.

YOHANE 1:12-13
[12] Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace;[13] amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi cifuniro ca thupi, kapena ndi cifuniro ca munthu, koma ca Mulungu.

DEUTERONOMO 30:19-20
[19] Ndicititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;[20] kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ace, ndi kummamatira iye, tr pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ocuruka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.

EZEKIELE 18:30-32
[30] Cifukwa cace ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israyeli, yense monga mwa njira zace, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.[31] Tayani, ndi kudzicotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israyeli?[32] Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; cifukwa cace bwererani, nimukhale ndi moyo.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society