A A A A A

Mulungu: [Madalitso Azachuma]


1 SAMUELE 2:7
Yehova asaukitsa, nalemeza; Acepetsa, nakuzanso.

2 AKORINTO 8:9
Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera.

3 YOHANE 1:2
Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera,

MLALIKI 9:10
Ciri conse dzanja lako licipeza kucicita, ucicite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe nchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.

AGALATIYA 6:9
Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

GENESIS 13:2
Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golidi,

HOSEYA 4:6
Anthu anga aonongeka cifukwa ca kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala cilamulo ca Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

YAKOBO 5:12
Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kuchula mwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina liri lonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akha; le iai; kuti mungagwe m'ciweruziro.

YOHANE 6:12
Ndipo pamene adakhuta, Iyeananena kwa akuphunzira ace, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

LUKA 6:38
6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

LUKA 12:34
Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

MIYAMBO 10:22
Madalitso a Yehova alemeretsa, Saonjezerapo cisoni.

MIYAMBO 11:14
Popanda upo wanzeru anthu amagwa; Koma pocuruka aphungu pali cipulumutso.

MIYAMBO 19:17
Wocitira waumphawi cifundo abwereka Yehova; Adzambwezera cokoma caceco.

MIYAMBO 21:17
Wokonda zoseketsa adzasauka; Wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

MIYAMBO 22:9
Mwini diso lamataya adzadala; Pakuti apatsa osauka zakudya zace.

MIYAMBO 28:22-27
[22] Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera, Osadziwa kuti umphawi udzamfikira.[23] Adzamkomera mtima wodzudzula m'tsogolo mwace, Koposa wosyasyalika ndi lilime lace.[24] Wobera atate wace, pena amace, nati, Palibe kulakwa; Ndiye mnzace wa munthu wopasula.[25] Wodukidwa mtima aputa makangano; Koma wokhulupirira Yehova adzakula.[26] Wokhulupirira mtima wace wace ali wopusa; Koma woyenda mwanzeru adzapulumuka,[27] Wogawira aumphawi sadzasowa; Koma wophimba maso ace adzatembereredwa kwambiri.

MASALIMO 24:1
Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zace zomwe, Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.

MATEYU 6:33
Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

MATEYU 23:23
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la citowe, nimusiya zolemera za cilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kucitira cifundo, ndi cikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzicita, osasiya izi zomwe.

MATEYU 25:21
Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.

AROMA 13:8
Musakhale ndi mangawa kwa munthu ali yense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzace wakwanitsa lamulo.

MIYAMBO 3:9-10
[9] Lemekeza Yehova ndi cuma cako, Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;[10] Motero nkhokwe zako zidzangoti the, Mbiya zako zidzasefuka vinyo.

MASALIMO 121:1-2
[1] Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?[2] Thandizo langa lidzera kwa Yehova, Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

MARKO 11:22-23
[22] Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu,[23] Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwace, koma adzakhulupirira kuti cimene acinena cicitidwa, adzakhala naco.

GENESIS 1:26-27
[26] Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[27] Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

2 AKORINTO 9:6-8
[6] Koma nditi ici, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.[7] Yense acite monga anatsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.[8] Ndipo Mulungu akhoza kucurukitsira cisomo conse kwa inu; kuti inu, pokhala naco cikwaniro conse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukacurukire ku nchito yonse yabwino;

LUKA 14:28-30
[28] Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza?[29] Kuti kungacitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ace, osakhoza kuimariza, anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye,[30] ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza.

LUKA 6:34-36
[34] Ndipo 2 ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti inde anthu ocimwa amakongoletsa kwa ocimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.[35] Koma 3 takondanani nao adani anu, ndi kuwacitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikuru, ndipo 4 inu mudzakhala ana a Wamkurukuruyo; cifukwa iye acitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.[36] Khalani inu acifundo monga Atate wanu ali wacifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

YAKOBO 5:1-3
[1] Nanga tsono acuma inu, lirani ndi kucema cifukwa ca masautso anu akudza pa inu,[2] Cuma canu caola ndi zobvala zanu zajiwa ndi njenjete.[3] Golidi wanu ndi siliva wanu zacita dzimbiri, ndipo dzimbiri lace lidzacita mboni zoneneza Inu ndipo zidzadya nyama yanu ngat: moto. Mwadzikundikira cuma masiku otsiriza.

GENESIS 12:1-20
[1] Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Turuka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;[2] ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukuru, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;[3] ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi,[4] Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anaturuka m'Harana.[5] Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wace, ndi Loti mwana wa mphwace, ndi cuma cao cimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harana; naturuka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.[6] Ndipo Abramu anapitira m'dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.[7] Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.[8] Ndipo iye anacoka kumeneko kunka ku phiri la kum'mawa kwa Beteli, namanga hema wace; Beteli anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.[9] Ndipo Abramu anayenda ulendo wace, nayendayenda kunka kumwela.[10] Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramo ku Aigupto kukakhala kumeneko, cifukwa kuti njala inali yaikuru m'dziko m'menemo.[11] Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m'Aigupto, anati kwa Sarai mkazi wace, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;[12] ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aaigupto, adzati, Uyu ndi mkazi wace: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.[13] Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti cidzakhala cabwino ndi ine, cifukwa ca iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.[14] Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Aigupto, Aaigupto anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.[15] Ndipo akaronga ace a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwace kwa Farao.[16] Ndipo anamcitira Abramu bwino cifukwa ca iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi aburu akazi, ndi ngamila.[17] Koma Yehova anabvutitsa Farao ndi banja lace ndi nthenda zazikuru cifukwa ca Sarai mkazi wace wa Abramu,[18] Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nciani ici wandicitira ine? cifukwa canji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako?[19] Cifukwa canji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nucoke.[20] Ndipo Farao analamulira anthu ace za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wace ndi zonse anali nazo.

MATEYU 6:1-34
[1] Yang'anirani kuti musacite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.[2] Cifukwa cace pamene pali ponse upatsa mphatso zacifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amacita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.[3] Koma iwe popatsa mphatso zacifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe cimene licita dzanja lako lamanja;[4] kotero kuti mphatso zako zacifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.[5] Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.[6] Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.[7] Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao.[8] Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.[9] Cifukwa cace pempherani inu comweci: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.[10] Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano.[11] Mutipatse ife lero cakudya cathu calero.[12] Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.[13] Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.[14] Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.[15] Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.[16] Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.[17] Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako:[18] kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.[19] Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:[20] koma mudzikundikire nokha cuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba;[21] pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.[22] Diso ndilo nyali ya thupi; cifukwa cace ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa.[23] Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Cifukwa cace ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukuru ndithu![24] Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.[25] Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?[26] Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?[27] Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?[28] Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:[29] koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa.[30] Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?[31] Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani?[32] Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.[33] Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.[34] Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.

DEUTERONOMO 28:1-68
[1] Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwacangu, ndi kusamalira kucita malamulo ace onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;[2] ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.[3] Mudzakhala odala m'mudzi, ndi odala kubwalo.[4] Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.[5] Zidzakhala zodala mtanga wanu, ndi coumbiramo mkate wanu.[6] Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala poturuka inu.[7] Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.[8] Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse muturutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani,[9] Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace.[10] Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akuchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.[11] Ndipo Yehova adzakucurukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo,[12] Yehova adzakutsegulirani cuma cace cokoma, ndico thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yace, ndi kudalitsa nchito zonae za dzanja lanu; ndipo mudza kongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.[13] Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mcira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwacita;[14] osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu yina kuitumikira.[15] Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,[16] Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo.[17] Zidzakhala zotembereredwa mtanga wanu ndi coumbiramo mkate wanu.[18] Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.[19] Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa poturuka inu.[20] Yehova adzakutumizirani temberero, cisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukaturutsa dzanja lanu kucita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika rosanga, cifukwa ca zocita inu zoipa, zimene wandisiya nazo,[21] Yehova adzakumamatiritsani mliri kufikira akakuthani kukucotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.[22] Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya cifuwa, ndi malungo, ndi cibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, cinsikwi ndi cinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.[23] Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko liri pansi panu ngati citsulo.[24] Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale pfumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kucokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.[25] Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawaturukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.[26] Ndipo mitembo yanu idzakhalacakudya ca mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zirombo zonse za pa dziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.[27] Yehova adzakukanthani ndi zirombo za ku Aigupto, ndi nthenda yoturuka mudzi, ndi cipere, ndi mphere, osacira nazo.[28] Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima;[29] ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.[30] Mudzaparana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzanka munda wamphesa, osalawa zipatso zace.[31] Adzapha ng'ombe yanu pamaso panu, osadyako inu; adzalanda buru wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.[32] Adzapereka ana anu amuna ndi akazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.[33] Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi nchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;[34] nimudzakhala oyeruka cifukwa comwe muciona ndi maso anu,[35] Yehova adzakukanthani ndi cironda coipa cosacira naco kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu.[36] Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu yina ya mitengo ndi miyala.[37] Ndipo mudzakhala codabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.[38] Mudzaturuka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.[39] Mudzanka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wace, kapena kuchera mphesa zace, popeza citsenda cidzaidya.[40] Mudzakhala nayo mitengo yaazitona m'malire anu onset osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo yaazitona zidzapululuka.[41] Mudzabala ana amuna ndi akazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.[42] Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zao zao za dzombe.[43] Mlendo wokhala pakati panu adzakulira-kulira inu, koma inu mudzacepera-cepera.[44] Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mcira.[45] Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace ndi malemba ace amene anakulamulirani;[46] ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati cizindikilo ndi cozizwa, nthawi zonse.[47] Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi cimwemwe ndi mokondwera mtima, cifukwa ca kucuruka zinthu zonse;[48] cifukwa cace mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lacitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.[49] Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wocokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;[50] mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamcitira cifundo mwana;[51] ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.[52] Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.[53] Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.[54] Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu diso lace lidzaipira mbale wace, ndi mkazi wa pa mtima wace, ndi ana ace otsalira;[55] osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ace alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse.[56] Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lace popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lace lidzamuipira mwamuna wa pamtima pace, ndi mwana wace wamwamuna ndi wamkazi;[57] ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.[58] Mukapanda kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo YEHOVA MULUNGU ANU;[59] Yehova adzacita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwiza, miliri yaikuru ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.[60] Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Aigupto, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.[61] Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la cilamulo ici, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.[62] Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mukacuruka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu.[63] Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukucitirani zabwino, ndi kukucurukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.[64] Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu yina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.[65] Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.[66] Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzacita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.[67] M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! ndi madzulo mudzati, Mwenzi utafika m'mawa! cifukwa ca mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi cifukwa ca zopenya maso anu zimene mudzazipenya.[68] Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Aigupto ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogulainu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society