A A A A A

God: [Who God Is]


AKOLOSE 1:16
pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.

GENESIS 1:1
PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

AHEBRI 1:3
ameneyo, pokhala ali cinyezimiro ca ulemerero wace, ndi cizindikilo ceni ceni ca cikhalidwe cace, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yace, m'mene adacita ciyeretso ca zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,

AHEBRI 4:12
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

YESAYA 44:6
Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wace, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

YOHANE 1:1
PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

YOHANE 1:14
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

YOHANE 4:24
Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'coonadi.

1 YOHANE 1:5
Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima.

1 YOHANE 4:8
iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.

1 YOHANE 4:16
Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.

2 SAMUELE 7:22
Cifukwa cace wamkuru ndi Inu Yehova. Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.

YOHANE 17:3
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.

MASALIMO 34:8
Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

MASALIMO 86:5
Pakuti fnu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, Ndi wa cifundo cocurukira onse akuitana Inu.

CHIVUMBULUTSO 1:1
CIBVUMBULUTSO ca Yesu Kristu, cimene Mulungu anambvumbulutsira acionetsere akapolo ace, ndico ca izi ziyenera kucitika posacedwa: ndipo potuma mwa mngelo wace anazindikiritsa izi kwa kapolo wace Yohane;

CHIVUMBULUTSO 22:13
Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, ciyambi ndi citsiriziro.

AROMA 5:8
Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.

ZEFANIYA 3:17
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi cimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'cikondi cace; adzasekerera nawe ndi kuyimbirapo.

CHIVUMBULUTSO 1:17-18
[17] Ndipo pamene ndinamuona iye, ndinagwa pa mapazi ace ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lace lamanja pa ine, nati, Usaope, ine ndine woyamba ndi wotsiriza,[18] ndi Wamoyoyo; ndipo 1 ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade.

2 TIMOTEO 3:16-17
[16] Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:[17] kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kucita nchito iri yonse yabwino.

YOHANE 10:30-33
[30] Ine ndi Atate ndife amodzi.[31] Ayuda anatolanso miyala kuti amponye iye.[32] Yesu anayankha iwo, ndakuonetsani inu nchito zabwino zambiri za kwa Atate; cifukwa ca nchito yiti ya izo mundiponya miyala?[33] Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society