A A A A A

God: [Viruses / Diseases]


YESAYA 26:20
Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.

YEREMIYA 25:32-33
[32] Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.[33] Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.

2 MBIRI 7:13-14
[13] Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;[14] ndipo anthu anga ochedwa dzina langa akadzicepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira coipa cao, ndi kuciritsa dziko lao.

CHIVUMBULUTSO 6:3-8
[3] Ndipo pamene anamasula cizindikilo caciwiri, ndinamva camoyo caciwiri nicinena, Idza.[4] Ndipo anaturuka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakucotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikuru.[5] Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacitatu, ndinamva camoyo cacitatu nicinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lace.[6] Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.[7] Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacinai, ndinamva mau a camoyo cacinai nicinena, Idza.[8] Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.

1 SAMUELE 5:6
Koma Yehova anabvuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lace, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'miraga yace.

2 AKORINTO 4:7
Koma tiri naco cuma ici m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosacokera kwa ife;

EKSODO 20:3
Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.

YAKOBO 4:10
Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

MATEYU 6:24
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.

AFILIPI 4:6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

MASALIMO 103:2-3
[2] Lemekeza Yehova, moyo wanga, Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:[3] Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; Naciritsa nthenda zako zonse;

NUMERI 11:31-33
[31] Ndipo kudacokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zocokera kunyanja, nizitula kucigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa cigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.[32] Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wace wonse, ndi mawa lace lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa cigono.[33] Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukuru ndithu.

EKSODO 9:8-11
[8] Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.[9] Ndipo lidzakhala pfumbi losalala pa dziko lonse la Aigupto, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zironda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Aigupto.[10] Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zironda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.[11] Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose cifukwa ca zirondaw; popeza panali zironda pa alembi ndi pa Aaigupto onse.

YAKOBO 1:2-6
[2] Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundu mitundu;[3] pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.[4] Koma cipiriro cikhale nayo nchito yace yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda cirema, osasowa kanthu konse.[5] Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,[6] Koma apemphe ndi cikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

CHIVUMBULUTSO 9:15-19
[15] Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi caka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu.[16] Ndipo ciwerengero ca nkhondo za apakavalo ndico zikwi makumi awiri zocurukitsa zikwi khumi; ndinamva ciwerengero cao.[17] Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulfure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao muturuka moto ndi utsi ndi sulfure.[18] Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulfure, zoturuka m'kamwa mwao.[19] Pakuti mphamvu ya akavalo in m'kamwa mwao, ndi m'micira yao; pakuti micira yao ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo aipsa nayoyo.

MARKO 13:32-37
[32] Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yace sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.[33] Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yace.[34] Monga ngati munthu wa paulendo, adacoka kunyumba kwace, nawapatsa akapolo ace ulamuliro, kwa munthu ali yense nchito yace, nalamulira wapakhomo adikire.[35] Cifukwa cace dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yace yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;[36] kuti angabwere balamantha nakakupezani muli m'tulo.[37] Ndipo cimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.

MASALIMO 91:2-14
[2] Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira,[3] Pakuti adzakuonjola ku msampha wa msodzi, Ku mliri wosakaza.[4] Adzakufungatira ndi nthenga zace, Ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ace; Coonadi cace ndico cikopa cocinjiriza.[5] Sudzaopa coopsa ca usiku, Kapena mubvi wopita usana;[6] Kapena mliri woyenda mumdima, Kapena cionongeko cakuthera usana.[7] Pambali pako padzagwa cikwi, Ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako; Sicidzakuyandikiza iwe.[8] Koma udzapenya ndi maso ako, Nudzaona kubwezera cilango oipa.[9] Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga Udaika Wam'mwambamwamba cokhalamo cako;[10] Palibe coipa cidzakugwera, Ndipo colanga sicidzayandikiza hema wako.[11] Pakuti adzalamulira angelo ace za iwe, Akusunge m'njira zako zonse.[12] Adzakunyamula pa manja ao, Ungagunde phazi lako pamwala.[13] Udzaponda mkango ndi mphiri; Udzapondereza msona wa mkango ndi cinjoka:[14] Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; Ndidzamkweza m'mwamba, papeza adziwa dzina langa.

LUKA 21:5-38
[5] Ndipo pamene ena analikunena za Kacisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati iye,[6] Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzace, umene sudzagwetsedwa.[7] Ndipo iwo anamfunsa iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? ndipo cizindikilo ndi cianipamene izi ziti zicitike?[8] Ndipo iye anati, Yang'anirani musasoceretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.[9] Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kucitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.[10] Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina:[11] ndipo kudzakhala zibvomezi zazikuru, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsya ndi zizindikilo zazikuru zakumwamba.[12] Koma zisanacitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, cifukwa ca dzina langa.[13] Kudzakhala kwa inu ngati umboni.[14] Cifukwa cace tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire cimene mudzayankha.[15] Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.[16] Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a pfuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani,[17] Ndipo anthu onse adzadana ndi inu cifukwa ca dzina langa.[18] Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.[19] Mudzakhala nao moyo wanu m'cipiriro.[20] Koma pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti cipululutso cace cayandikira.[21] Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo aturuke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo.[22] Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.[23] Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! pakuti padzakhala cisauko cacikuru padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.[24] Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.[25] Ndipo kudzakhala zizindikilo pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wace wa nyanja ndi mafunde ace;[26] anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;[27] pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.[28] Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.[29] Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse:[30] pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.[31] Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.[32] Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitacitika.[33] Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.[34] Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;[35] pakuti Iidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.[36] Koma inu dikirani nyengo zonse ndi kupemphera, kutimukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzacitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.[37] Ndipo usana uli wonse iye analikuphunzitsa m'Kacisi; ndi usiku uli wonse anaturuka, nagona pa phiri lochedwa la Azitona.[38] Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa iye kuKacisi kudzamvera Iye.

MATEYU 24:1-35
[1] Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo.[2] Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.[3] Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?[4] Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.[5] Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.[6] Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.[7] Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m'malo akuti akuti.[8] Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.[9] Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, cifukwa ca dzina langa.[10] Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzace, nadzadana wina ndi mnzace.[11] Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsaanthuambiri.[12] Ndipo cifukwa ca kucuruka kwa kusayeruzika, cikondano ca anthu aunyinji cidzazirala.[13] Koma iye wakulimbika cilimbikire kufikira kucimariziro, yemweyo adzapulumuka.[14] Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu h mitundu yonse; ndipo pomwepo cidzafika cimariziro.[15] Cifukwa cace m'mene mukadzaona conyansa ca kupululutsa, cimene cidanenedwa ndi Danieli mneneri, citaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)[16] pomwepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri:[17] iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwace;[18] ndi iye wa m'munda asabwere kutenga copfunda cace.[19] Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo![20] Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yacisanu, kapena pa Sabata;[21] pakuti pomwepo padzakhala masauko akuru, monga sipadakhale otero kuyambira ciyambi ca dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.[22] Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense: koma cifukwa ca osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.[23] Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze;[24] cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.[25] Cifukwa cace akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'cipululu; musamukeko.[26] Onani, ali m'zipinda; musabvomereze.[27] Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwace kwa Mwana wa munthu.[28] Kumene kuli konse uli mtembo, miimba Idzasonkhanira konko.[29] Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace, ndi nyenyezi zidzagwa kucokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:[30] ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo cizindikiro ca Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pacifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.[31] Ndipo Iye adzatumiza angelo ace ndi kulira kwakukuru kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ace ku mphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ace ena.[32] Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene tsopano nthambi yace iri yanthete, nipuka masa-i mba ace, muzindikira kuti dzinja liyandikira;[33] comweconso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.[34] Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kucoka, kufikira zinthu zonsezi zidzacitidwa.[35] Thambo ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society