A A A A A

God: [Time]


2 AKORINTO 6:2
(pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, Ndipo m'tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza; Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la cipulumutso);

1 YOHANE 2:17
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.

MLALIKI 3:11
Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.

YEREMIYA 29:11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

YOHANE 9:4
Tiyenera kugwira nchito za iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira nchito,

MIYAMBO 16:9
Mtima wa munthu ulingalira njira yace; Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.

MIYAMBO 21:5
Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu; Koma yense wansontho angopeza umphawi.

MIYAMBO 27:1
Usanyadire zamawa, Popeza sudziwa tsiku lina lidzabala ciani?

MASALIMO 31:15
Nyengo zanga ziri m'manja mwanu: Mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

MASALIMO 90:12
Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, Kuti tikhale nao mtima wanzeru.

AROMA 13:11
Ndipo citani ici, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano cipulumutso cathu ciri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.

ESTERE 4:14
Pakuti ukakhala cete konse tsopano lino, cithandizo ndi cipulumutso zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu cifukwa ca nyengo yonga iyi.

MARKO 13:32-33
[32] Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yace sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.[33] Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yace.

2 PETRO 3:8-9
[8] Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.[9] Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

AKOLOSE 4:5-6
[5] Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kucita macawi nthawi ingatayike.[6] Mau anu akhale m'cisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akarani.

AEFESO 5:15-17
[15] Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;[16] akucita macawi, popeza masiku ali oipa,[17] Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani.

1 ATESALONIKA 5:1-3
[1] Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani,[2] Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku,[3] Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.

MIYAMBO 6:6-8
[6] Pita kunyerere, wolesi iwe, Penya njira zao nucenjere;[7] Ziribe mfumu, Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;[8] Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; Nizituta dzinthu zao m'masika.

YAKOBO 4:13-17
[13] Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakuti wakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, Ddi kupindula nao;[14] inu amene simudziwa cimene cidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.[15] Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzacita kakuti kakuti.[16] Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kuli konse kotero nkoipa.[17] Potero kwa iye amene adziwa kucita bwino, ndipo sacita, kwa iye kuli cimo.

MLALIKI 3:1-8
[1] Kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi cofuna ciri conse ca pansi pa thambo ciri ndi mphindi yace;[2] mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzyala ndi mphindi yakuzula zobzyalazo;[3] mphindi yakupha ndi mphindi yakuciza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;[4] mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakubvina;[5] mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;[6] mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;[7] mphindi yakung'amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;[8] mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society