A A A A A

God: [Trinity]


1 AKORINTO 8:6
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zicokera kwa iye, ndi ire kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.

2 AKORINTO 3:17
Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

2 AKORINTO 13:14
Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mulungu, ndi ciyanjano ca Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.

AKOLOSE 2:9
pakuti mwa iye cikhalira cidzalo ca Umulungu m'thupi,

YESAYA 9:6
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

YESAYA 44:6
Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wace, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

YOHANE 1:14
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.

YOHANE 10:30
Ine ndi Atate ndife amodzi.

LUKA 1:35
Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.

MATEYU 1:23
Onani namwali adzaima, Nadzabala mwana wamwamuna, Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe.

MATEYU 28:19
Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

MATEYU 3:16-17
[16] Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;[17] ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.

AROMA 14:17-18
[17] Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala cakudya ndi cakumwa, koma cilungamo, ndi mtendere, ndi cimwemwe mwa Mzimu Woyera.[18] Pakuti iye amene atumikira Kristu mu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu.

LUKA 3:21-22
[21] Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo,[22] ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

GENESIS 1:1-2
[1] PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.[2] Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa madzi.

YOHANE 5:7-8
[7] Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndiribe wondibvika ine m'thamanda, pali ponse madzi abvundulidwa; koma m'mene ndirinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.[8] Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende,

1 PETRO 1:1-2
[1] PETRO, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala: alendo a cibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,[2] monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.

2 AKORINTO 1:21-22
[21] Koma iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Kristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;[22] amenenso anatisindikiza cizindikilo, natipatsa cikole ca Mzimu mu mitima yathu.

1 AKORINTO 12:4-6
[4] Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.[5] Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.[6] Ndipo pali macitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakucita zinthu zonse mwa onse.

AEFESO 4:4-6
[4] Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi ca maitanidwe anu;[5] Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi, ubatizo umodzi,[6] Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.

AKOLOSE 1:15-17
[15] amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse;[16] pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.[17] Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.

YOHANE 14:9-11
[9] Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?[10] Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.[11] Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe.

AFILIPI 2:5-8
[5] Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,[6] ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,[7] koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;[8] ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

YOHANE 10:30-36
[30] Ine ndi Atate ndife amodzi.[31] Ayuda anatolanso miyala kuti amponye iye.[32] Yesu anayankha iwo, ndakuonetsani inu nchito zabwino zambiri za kwa Atate; cifukwa ca nchito yiti ya izo mundiponya miyala?[33] Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,[34] Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'cilamulo canu, Ndinati Ine, Muli milungu?[35] Ngati anawacha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo colemba sicingathe kutyoka),[36] kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko lapansi, Ucita mwano; cifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society