A A A A A

God: [Plans]


MIYAMBO 19:21
Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

YEREMIYA 29:11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

MIYAMBO 15:22
Zolingalira zizimidwa popanda upo Koma pocuruka aphungu zikhazikika.

MASALIMO 33:11
Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire, Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.

MIYAMBO 16:3
Pereka zocita zako kwa Yehova, Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

MIYAMBO 21:5
Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu; Koma yense wansontho angopeza umphawi.

MASALIMO 20:4
Likupatse ca mtima wako, Ndipo likwaniritse upo wako wonse.

MASALIMO 33:10
Yehova aphwanya upo wa amitundu: Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.

LUKA 14:28
Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza?

MIYAMBO 16:9
Mtima wa munthu ulingalira njira yace; Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.

AROMA 8:28
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.

AFILIPI 1:6
pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;

YESAYA 14:26-27
[26] Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.[27] Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? ndi dzanja lace latambasulidwa, ndani adzalibweza?

YOHANE 6:44
Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

MASALIMO 143:8
Mundimvetse cifundo canu mamawa; Popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; Popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.

MIYAMBO 23:4
Usadzitopetse kuti ulemere; Leka nzeru yako yako.

MASALIMO 90:12
Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, Kuti tikhale nao mtima wanzeru.

MASALIMO 3:31-32
[31] Moyo wanganso wanthunthumira kwakukuru; Ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?[32] Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; Ndipulumutseni cifukwa ca kukoma mtima kwanu.

YESAYA 46:3-11
[3] Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israyeli, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani cibadwire;[4] ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.[5] Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?[6] Amene ataya golidi, namturutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golidi; iye napanga nazo mlungu; iwo agwada pansi, inde alambira.[7] Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwace, nukhala ciriri; pamalo pacepo sudzasunthika; inde, wina adzaupfuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zobvuta zace.[8] Kumbukirani ici, nimucirimike, mudzikumbutsenso, olakwa inu.[9] Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine;[10] ndilalikira za cimariziro kuyambira paciyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanacitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzacita zofuna zanga zonse;[11] ndiitana mbalame yolusa kucokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kucokera ku dziko lakutari; inde, ndanena, ndidzacionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzacicitanso.

YOHANE 1:12-13
[12] Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace;[13] amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi cifuniro ca thupi, kapena ndi cifuniro ca munthu, koma ca Mulungu.

CHIVUMBULUTSO 17:8
Cirombo cimene unaciona cinaliko, koma kulibe; ndipo cidzaturuka m'phompho, ndi kunka kucitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo ciyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona cirombo, kuti cinaliko, ndipo kulibe, ndipo cidzakhalako.

AMOSI 3:7
Pakuti Ambuye Yehova sadzacita kanthu osaulula cinsinsi cace kwa atumiki ace aneneri.

YAKOBO 4:1-17
[1] Zicokera kuti nkhondo, zicokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizicokera ku zikhumbitso zanu zocita nkhondo m'ziwalo zanu?[2] Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimucita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimucita nkhondo; mulibe kanthu, cifukwa simupempha.[3] Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukacimwaze pocita zikhumbitso zanu.[4] Akazi acigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uti udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.[5] Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena cabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kucita nsanje?[6] Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.[7] Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.[8] Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.[9] Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni.[10] Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.[11] Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.[12] Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?[13] Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakuti wakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, Ddi kupindula nao;[14] inu amene simudziwa cimene cidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.[15] Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzacita kakuti kakuti.[16] Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kuli konse kotero nkoipa.[17] Potero kwa iye amene adziwa kucita bwino, ndipo sacita, kwa iye kuli cimo.

MIYAMBO 3:5-6
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;[6] Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

2 PETRO 3:9
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

1 TIMOTEO 2:4
amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.

GENESIS 1:26
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

MATEYU 28:18-20
[18] Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.[19] Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:[20] ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

MIYAMBO 6:6-8
[6] Pita kunyerere, wolesi iwe, Penya njira zao nucenjere;[7] Ziribe mfumu, Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;[8] Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; Nizituta dzinthu zao m'masika.

YEREMIYA 1:5
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.

AEFESO 1:4
monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,

AHEBRI 4:3
Popeza ife amene takhulupira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyowanga, Ngati adzalowa mpumulo wanga: zingakhale nebitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.

AROMA 3:10-18
[10] monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;[11] Palibe mmodzi wakudziwitsa, Palibe mmodzi wakuloodola Mulungu;[12] Onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pace; Palibe mmodzi wakucita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.[13] M'mero mwao muli manda apululu; Ndi lilime lao amanyenga; Ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;[14] M'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;[15] Miyendo yao icita liwiro kukhetsa mwazi;[16] Kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao;[17] Ndipo njira ya mtendere sanaidziwa;[18] Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.

YESAYA 55:10-11
[10] Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kucokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzyala, ndi cakudya kwa wakudya;[11] momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.

YESAYA 9:6-7
[6] Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.[7] Za kuenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikirsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Cangu ca Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.

DEUTERONOMO 29:29
Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zobvumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti ticite mau onse a cilamulo ici.

AROMA 9:22-24
[22] Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuonetsa mkwiyo wace, ndi kudziwitsa mph amvu yace, analekerera ndi cilekerero cambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera cionongeko?[23] ndi kuti iye akadziwitse ulemerero wace waukuru pa zotengera zacifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero,[24] ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?

1 PETRO 2:9-10
[9] Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa;[10] inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira cifundo, koma tsopano mwalandira cifundo.

AROMA 8:18-25
[18] Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.[19] Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.[20] Pakuti colengedwaco cagonietsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca iye amene anacigonjetsa,[21] ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wa cibvundi, ndi kolowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu,[22] Pakuti tidziwa kuti colengedwa conse cibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.[23] Ndipo si cotero cokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo ciomboledwe ca thupi lathu.[24] Pakuti ife tinapolumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pa kuti ayembekezera ndani cimene acipenya?[25] Koma ngati tiyembekezera cimene: siticipenya, pomwepo ticilindirira ndi cipiriro.

EKSODO 20:1-17
[1] Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati:[2] INE ndine YEHOVA Mulungu wako, amene ndinaturutsa iwe ku dziko la Aigupto, ku nyumba ya akapolo.[3] Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.[4] Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;[5] usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;[6] ndi kuwacitira cifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.[7] Usaehule dzina la Yehova Mulungu wako pacabe; cifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosacimwa, amene achula pacabe dzina lacelo.[8] Uzikumbukila tsiku la Sabata, likhale lopatulika.[9] Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumariza nchito zako zonse;[10] koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire nchito iri yonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;[11] cifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamariza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula tsiku ladsanu ndi ciwiri; cifukwa cace Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.[12] Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti acuruke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.[13] Usaphe.[14] Usacite cigololo.[15] Usabe.[16] Usamnamizire mnzako.[17] Usasirire nyumba yace ya mnzako, usasirire mkazi wace wa mnzako, kapena wanchito wace wamwamuna, kapena wanchito wace wamkazi, kapena ng'ombe yace, kapena buru wace, kapena kanthu kali konse ka mnzako.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society