A A A A A

God: [Offerings]


1 MBIRI 29:9
Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi cimwemwe cacikuru.

2 AKORINTO 9:7
Yense acite monga anatsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

MACHITIDWE A ATUMWI 20:35
M'zinthu zonse ndinakupatsani citsanzo, cakuti pogwiritsa nchito, koteromuyenerakuthandiza ofoka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

DEUTERONOMO 16:17
apereke yense monga mwa mphatso ya m'dzanja lace, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

AHEBRI 13:15-16
[15] Potero mwa iye tipereke ciperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo cipatso ca milomo yobvomereza dzina lace.[16] Koma musaiwale kucitira cokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulunguakondweranazo.

LUKA 6:38
6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

LUKA 16:10
Iye amene akhulupirika m'cacing'onong'ono alinso wokhulupirika m'cacikuru; ndipo iye amene ali wosalungama m'cacing'onong'ono alinso wosalungama m'cacikuru.

MALAKI 3:10
Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

MATEYU 23:23
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la citowe, nimusiya zolemera za cilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kucitira cifundo, ndi cikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzicita, osasiya izi zomwe.

MIYAMBO 11:24
Alipo wogawira, nangolemerabe; Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.

MIYAMBO 28:27
Wogawira aumphawi sadzasowa; Koma wophimba maso ace adzatembereredwa kwambiri.

MASALIMO 4:5
Iphani nsembe za cilungamo, Ndipo mumkhulupirire Yehova.

AROMA 12:1
Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa, Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

MIYAMBO 3:9-10
[9] Lemekeza Yehova ndi cuma cako, Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;[10] Motero nkhokwe zako zidzangoti the, Mbiya zako zidzasefuka vinyo.

LUKA 12:33-34
[33] Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.[34] Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

MATEYU 6:19-21
[19] Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:[20] koma mudzikundikire nokha cuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba;[21] pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.

MATEYU 6:31-33
[31] Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani?[32] Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.[33] Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

MASALIMO 96:7-9
[7] Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, Mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu,[8] Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lace; Bwerani naco copereka, ndipo fikani ku mabwalo ace.[9] Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa: Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi.

MARKO 12:41-44
[41] Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni cuma ambiri anaponyamo zambiri.[42] Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tanng'ono tofa kakobiri kamodzi.[43] Ndipo anaitana ophunzira ace, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo:[44] pakuti anaponyamo onse mwa zocuruka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwace zonse anali nazo, inde moyo wace wonse.

LUKA 21:1-4
[1] Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni cuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.[2] Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri.[3] Ndipo iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse;[4] pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwace anaikamo za moyo wace, zonse anali nazo.

MALAKI 3:8-12
[8] Kodi munthu adzalanda za Mulungu? ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzi limodzi la magawo khumi, ndi zopereka.[9] Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.[10] Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.[11] Ndipo ndidzadzudzula zolusa cifukwa ca inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zace, zosaca m'munda, ati Yehova wa makamu.[12] Ndipo amitundu onse adzacha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society