A A A A A

God: [Names of God]


EKSODO 3:14-15
[14] Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.[15] Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Molungu wa makolo anu, Molungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Molungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili nw dzina langa nthawi yosatha, ici ndi cikumbukiro canga m'mibadwo mibadwo.

EKSODO 20:7
Usaehule dzina la Yehova Mulungu wako pacabe; cifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosacimwa, amene achula pacabe dzina lacelo.

EKSODO 34:14
pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lace ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

GENESIS 1:1
PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

GENESIS 17:1
Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.

YESAYA 7:14
Cifukwa cace Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu cizindikilo; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamucha dzina lace Imanueli.

YESAYA 42:8
Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

YESAYA 45:5
Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'cuuno, ngakhale sunandidziwa;

YESAYA 55:6
Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;

YEREMIYA 16:21
Cifukwa cace, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.

YOHANE 1:1
PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

OWERUZA 13:18
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza liri lodabwitsa?

LEVITIKO 19:12
Musamalumbira monama ndi kuchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

MATEYU 6:9
Cifukwa cace pempherani inu comweci: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.

MATEYU 28:19
Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

MACHITIDWE A ATUMWI 4:12
Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwanalo.

MIYAMBO 18:10
Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; Wolungama athamangiramo napulumuka.

MIYAMBO 30:4
Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'maraya ace? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lace ndani? dzina la mwanace ndani? kapena udziwa.

MASALIMO 61:8
Potero ndidzayimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse, Kuti ndicite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

CHIVUMBULUTSO 1:8
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

AROMA 8:15
Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,

MASALIMO 20:7-8
[7] Ena atama magareca, ndi ena akavalo: Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu.[8] Iwowa anagonieka, nagwa: Koma ife tauka, ndipo takhala ciriri.

AFILIPI 2:10-11
[10] kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,[11] ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

EKSODO 3:13-15
[13] Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lace ndani? ndikanena nao ciani?[14] Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.[15] Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Molungu wa makolo anu, Molungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Molungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili nw dzina langa nthawi yosatha, ici ndi cikumbukiro canga m'mibadwo mibadwo.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society