A A A A A

God: [Miracles]


MACHITIDWE A ATUMWI ३:१६
Ndipo pa cikhulupiriro ca m'dzina lace dzina lacelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo cikhulupiriro ciri mwa iye cinampatsa kucira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.

DEUTERONOMO 10:21
Iye ndiye lemekezo lanu, Ive ndiye Mulungu wanu, amene anacita nanu zazikuru ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.

EKSODO 15:26
ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kucita zoona pamaso pace, ndi kuchera khutu pa malamulo ace, ndi kusunga malemba ace onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aaigupto sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuciritsa iwe.

YEREMIYA 32:27
Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu lonse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?

YOHANE 2:11
Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira iye.

LUKA १८:२७
Koma iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

MARKO 9:23
Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.

MATEYU १७:२०
Ndipo Iye ananena kwa iwo, Cifukwa cikhulupiriro canu ncacing'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala naco cikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosacitika. [

MATEYU 19:26
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, ici sicitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.

MATEYU 21:21
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala naco cikhulupiriro, osakayika-kayika, mudzacita si ici ca pa mkuyu cokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nvania, cidzacitidwa.

AROMA १५:१८-१९
[१८] Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,[१९] mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu;

MACHITIDWE A ATUMWI 19:11-12
[11] Ndipo Mulungu anacita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo;[12] kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsaru zopukutira ndi za panchito, zocokera pathupi pace, ndipo nthenda zinawacokera, ndi mizimu yoipa inaturuka.

YOBU ५:८-९
[८] Koma ine ndikadafuna Mulungu, Ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;[९] Amene acita zazikuru ndi zosalondoleka, Zinthu zodabwiza zosawerengeka.

AEFESO 3:20-21
[20] Ndipo kwa iye amene angathe kucita koposa-posatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kucita mwa ife,[21] kwa iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Kristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.

MACHITIDWE A ATUMWI ४:२९-३१
[२९] Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,[३०] m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.[३१] Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

MARKO 16:17-20
[17] Ndipo zizindikilo izi zidzawatsata iwo akukhulupirira; m'dzina langa adzaturutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;[18] adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzacira.[19] Pamenepo Ambuye Yesu, ata-tha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.[20] Ndipo iwowa anaturuka, nalalikira ponse ponse, ndipo Ambuye anacita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikilo zakutsatapo, Amen.

LUKA ९:१३-१७
[१३] Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tiribe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.[१४] Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma iye anati kwa ophunzira ace, Khalitsani iwo pansi magulu magulu, ngati makumi asanu asanu.[१५] Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo.[१६] Ndipo iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.[१७] Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, mitanga khumi ndi iwiri.

LUKA 8:43-48
[43] Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wace zonse, ndipo sanathe kuciritsidwa ndi mmodzi yense,[44] anadza pambuyo pace, nakhudza mphonje yacobvala cace; ndipo pomwepo nthenda yace inaleka.[45] Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.[46] Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti a ndazindikira Ine kuti mphamvu yaturuka mwa Ine.[47] Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pace, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cace ca kumkhudza iye, ndi kuti anaciritsidwa pomwepo.[48] Ndipo iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

YOHANE 4:46-54
[46] Cifukwa cace Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunalimkulu wina wa mfumu, mwana wace anadwala m'Kapernao.[47] Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wacokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa iye, nampempha kuti atsike kukaciritsa mwana wace; pakuti anali pafupi imfa.[48] Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikilo ndi zozizwa, simudzakhulupira.[49] Mkuluyo ananena kwa iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.[50] Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo, Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka.[51] Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ace anakomana, naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.[52] Cifukwa cace anawafunsa ora lace anayamba kuciralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lacisanu ndi ciwiri malungo anamsiya.[53] Cifukwa cace atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupira iye yekha ndi a pa banja lace onse.[54] Ici ndi cizindikilo caciwiri Yesu anacita, ataeokera ku Yudeya, ndi kulowa m'Galileya.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society