A A A A A

Mpingo: [Aphunzitsi Onyenga]


EZEKIELE 13:9
Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pace, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israyeli, kapena kulowa m'dziko la Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova,

YEREMIYA 23:16
Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zacabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.

LUKA 6:26
Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! pakuti makolo ao anawatero momwemo ananeri onama.

MATEYU 24:24
cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.

MATEYU 16:11-12
[11] Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani cotupitsa ca Afarisi ndi Asaduki.[12] Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauza kupewa cotupitsa ca mikate, koma ciphunzitso ca Afarisi ndi Asaduki.

2 TIMOTEO 4:3-4
[3] Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:[4] ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe.

2 TIMOTEO 4:3-4
[3] Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:[4] ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe.

MACHITIDWE A ATUMWI 20:28-30
[28] Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.[29] Ndidziwa ine kuti, nditacoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;[30] ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.

2 PETRO 3:14-18
[14] Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.[15] Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu cipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa cwa iye, anakulemberani;[16] monganso m'akalata ace onse pokanba momwemo za izi; m'menemo nuli zina zobvuta kuzizindikira, zinene anthu osaphunzira ndi osachazikika apotoza, monganso atero lao malembo ena, ndi kudziononga lao eni.[17] Inu, tsono, okondedwa, oozizindikiratu izi, cenjerani, kuti ootengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya cichazikiko canu.[18] Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi Yesu vistu; kwa iye kukhale uleme'ero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.

1 YOHANE 4:1-6
[1] Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati icokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anaturuka kulowa m'dziko lapansi.[2] M'menemo muzindikira Mzimu Wl Mulungu: mzimu uli wonse umen ubvomereza kuti Yesu Kristu ana dza m'thupi, ucokera mwa. Mulungu[3] ndipo mzimu uli wonse umen subvomereza Yesu sucokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzirm wa wokana Kristu umene mudamvi kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,[4] Inu ndinu ocokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti iye wakukhah mwa inu aposa iye wakukhala m'dzi ko lapansi. Iwo ndiwo ocoken m'dziko lapansi;[5] mwa ici alankhula monga ocokera m'dziko lapansi, ndipo dziko tapansi liwamve ra.[6] Ife ndife ocokera mwa Mu lungu; iye amene azindikira Mu lungu atimvera; iye wosacoken mwa Mulungu satimvera ife. Mo mwemo tizindikira mzimu wa coonadi, ndi mzimu wa cisokeretso.

MATEYU 7:15-20
[15] Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa.[16] Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?[17] Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa,[18] Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma.[19] Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto.[20] Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.

2 PETRO 1:12-21
[12] Mwa ici sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'coonadi ciri ndi inu.[13] Ndipo ndiciyesa cokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;[14] podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Kristu anandilangiza.[15] Koma ndidzacitanso cangu kosalekeza kuti nditacoka ine, mudzakhoza kukumbukila izi,[16] Pakuti sitinatsata miyambi yacabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m'maso ukulu wace.[17] Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;[18] ndipo mau awa ocokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi iye m'phiri lopatulika lija,[19] Ndipo tiri nao mau a cinenero okhazikika koposa; amene mucita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukaca, nikauka nthanda pa mtima yanu;[20] ndi kudziwa ici poyamba, kuti palibe cinenero ca lembo citanthauzidwa pa cokha,[21] pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

TITO 1:6-16
[6] ngati wina ali wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zace, kapena wosakana kumvera mau.[7] Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;[8] komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;[9] wogwira mau okhulupirika monga mwa ciphunzitso, kuti akakhoze kucenjeza m'ciphunzitso colamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.[10] Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pace, ndi onyenga, makamaka iwo a kumdulidwe,[11] amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera cifukwa ca cisiriro conyansa.[12] Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zirombo zoipa, aumbombo, aulesi.[13] Umboni uwu uli woona. Mwa ici uwadzudzule mokaripa, kuti akakhale olama m'cikhulupiriro,[14] osasamala nthanu zacabe za Ciyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana naco coonadi.[15] Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi cikumbu mtima cao.[16] Abvomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi Debito zao amkana iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa nchito zonse zabwino osatsimikizidwa.

2 PETRO 2:1-22
[1] Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha citayiko cakudza msanga.[2] Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; cifukwa ca iwo njira ya coonadi idzanenedwa zamwano.[3] Ndipo m'cisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene ciweruzo cao sicinacedwa ndi kale lomwe, ndipo citayiko cao siciodzera.[4] Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adacimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe;[5] ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa cilungamo, ndi anzace asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza cigumula;[6] ndipo pakuisandutsa makara midzi ya Sodoma ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika citsanzo ca kwa iwo akakhala osapembedza;[7] ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja[8] (Pakuti wolungamayo pokhala pakati pao, ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wace wolungama tsiku ndi tsiku ndi nchito zao zosayeruzika).[9] Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;[10] kama makamaka iwo akutsata zathupi, m'cilakolako ca zodetsa, napeputsa cilamuliro; osaopa kanthu, otsata cifuniro ca iwo eni, santhunthumira kucitira mwano akulu;[11] popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakucita mwano.[12] Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akucitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,[13] ocitidwa zoipa kulipira kwa cosalungama; anthu akuyesera cowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zirema, akudyerera m'madyerero acikondi ao, pamene akudya nanu;[14] okhala nao maso odzala ndi cigololo, osakhoza kuleka ucimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;[15] posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya cosalungama;[16] koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwace mwini; buru wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyarukakwa mneneriyo.[17] Iwo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene iadima wakuda bii uwasungikira,[18] Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pace, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo;[19] ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali aka polo a cibvundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wace.[20] Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa cizindikiritsoca, Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zorsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo,[21] Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya cilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.[22] Cidawayenera iwo ca nthanthi yoona, Garu wabwerera ku masanzi ace, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope.

MATEYU 23:1-29
[1] Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ace,[2] nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;[3] cifukwa cace zinthu ziri zonse zimene iwo akauza inu, citani nimusunge; koma musatsanza nchito zao; pakuti iwo amalankhula, komasamacita.[4] Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi cala cao.[5] Koma amacita nchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa citando cace ca njirisi zao, nakulitsa mphonje,[6] nakonda malo a ulemu pamapwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge,[7] ndi kulankhulidwa m'misika, ndi kuchedwa ndi anthu, Rabi.[8] Koma inu musachedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.[9] Ndipo inu musachule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.[10] Ndipo musachedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.[11] Koma wamkuru wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.[12] Ndipo amene ali yense akadzikuza yekha adzacepetsedwa; koma amene adzicepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.[13] Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, Ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. [[14] ][15] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.[16] Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene ali yense akalumbira kuchula Kacisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula golidi wa Kacisi, wadzimangirira.[17] Inu opusa, ndi akhungu: pakuti coposa nciti, golidi kodi, kapena Kacisi amene ayeretsa golidiyo?[18] Ndiponso, Amene ali yense akalumbira kuchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula mtulo wa pamwamba pace wadzimangirira.[19] Inu akhungu, pakuti coposa nciti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?[20] Cifukwa cace wakulumbira kuchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pace.[21] Ndipo wakulumbira kuchula Kacisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo.[22] Ndipo wakulumbira kuchula Kumwamba, alumbira cimpando ca Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.[23] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la citowe, nimusiya zolemera za cilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kucitira cifundo, ndi cikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzicita, osasiya izi zomwe.[24] Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma ngamila mummeza.[25] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsuka kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.[26] Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa cikho ndi mbale, kuti kunja kwace kukhalenso koyera.[27] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwace, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.[28] Comweco inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi cinyengo ndi kusayeruzika.[29] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society