A A A A A

Mpingo: [Atumiki]


1 TIMOTEO 3:1-13
[1] Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna nchito yabwino.[2] Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;[3] wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba cuma;[4] woweruza bwino nyumba yace ya iye yekha, wakukhala nao ana ace omvera iye ndi kulemekezeka konse.[5] Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?[6] Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.[7] Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumcitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.[8] Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a cisiriro conyansa;[9] okhala naco cinsinsi ca cikhulupiriro m'cikumbu mtima coona.[10] Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda cifukwa.[11] Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.[12] Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.[13] Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukuru m'cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.

AFILIPI 1:1
PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:

MACHITIDWE A ATUMWI 6:1-7
[1] Koma masiku awo, pakucurukitsa ophunzira, kunauka cidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa citumikiro ca tsiku ndi tsiku.[2] Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.[3] Cifukwa cace, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yahwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge nchito iyi.[4] Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.[5] Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi cikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolao, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:[6] amenewo anawaika pamasopa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.[7] Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo ciwerengero ca akuphunzira cidacurukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikuru la ansembe linamvera cikhulupiriroco.

AROMA 16:1
Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya;

TITO 1:7
Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;

MACHITIDWE A ATUMWI 6:3
Cifukwa cace, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yahwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge nchito iyi.

YOHANE 8:32
ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

AEFESO 4:11
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;

MACHITIDWE A ATUMWI 20:28
Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.

YOHANE 6:54
11 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

MARKO 6:3
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

1 AKORINTO 12:28
Ndipotu Mulunguanailea ena m'Eklesia, poyamba arumwi, aciwiri aneneri, acitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso zamaciritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundu mitundu.

AGALATIYA 1:19
Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

MALAKI 1:11
Pakuti kuyambira koturukira dzuwa kufikira kolowera kwace dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa cofukiza ndi copereka coona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

AHEBRI 13:17
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akacite ndi cimwemwe, osati mwacisoni: pakuti ici sicikupindulitsani inu.

YOHANE 3:3-5
[3] Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.[4] Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa?[5] Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

AHEBRI 12:14
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

MACHITIDWE A ATUMWI 6:4
Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.

1 TIMOTEO 3:1-7
[1] Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna nchito yabwino.[2] Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;[3] wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba cuma;[4] woweruza bwino nyumba yace ya iye yekha, wakukhala nao ana ace omvera iye ndi kulemekezeka konse.[5] Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?[6] Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.[7] Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumcitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

1 TIMOTEO 2:12
Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.

MACHITIDWE A ATUMWI 14:23
Ndipo pamene anawaikira akuru mosankha mu Mpingo Mpingo, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, anaikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.

1 TIMOTEO 5:17
Akuru akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akucititsa m'mau ndi m'ciphunzitso.

AHEBRI 13:7
Kumbukilani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira citsiriziro ca mayendedwe ao mutsanze cikhulupiriro cao.

TITO 1:8
komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

1 PETRO 5:2
Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwacangu;

TITO 1:6
ngati wina ali wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zace, kapena wosakana kumvera mau.

1 TIMOTEO 5:22
Usafulumira kuika manja pa munthu ali yense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.

TITO 1:5
Cifukwa ca ici ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akuru m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;

AGALATIYA 4:19
Tiana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Kristu aumbika mwa inu,

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society