A A A A A

Mpingo: [Chizunzo cha Mpingo]


MACHITIDWE A ATUMWI 8:1
Ndipo Saulo analikubvomerezana nao pa imfa yace. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukuru pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi samariya, koma osati atumwi ai.

MATEYU 5:44
koma Ine ndinena kwa inu, 15 Kondanani nao adani anu, ndi 16 kupempherera iwo akuzunza inu;

2 TIMOTEO 3:12
Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.

YOHANE 15:20
Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.

CHIVUMBULUTSO 2:10
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena ainu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala naco cisautso masiku khumi. Khala wokholupirfka kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

AROMA 8:35
Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?

MATEYU 5:11
Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.

AROMA 12:14
Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere.

YOHANE 5:16
Ndipo cifukwa ca ici Ayuda analondalonda Yesu, popeza anacita izo dzuwa la Sabata.

MATEYU 5:10-12
[10] Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.[11] Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.[12] Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

2 AKORINTO 12:10
Cifukwa cace ndisangalala m'tnaufoko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, cifukwa ca Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wamphamvu.

MACHITIDWE A ATUMWI 13:50
Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, 12 nawautsira cizunzo Paulo ndi Bamaba, ndipo ana wapitikitsaiwom'malire ao.

MACHITIDWE A ATUMWI 7:52
23 ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudzakwace kwa Wolungamayo; wa iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;

MARKO 4:17
ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo cifukwa ca mau, pomwepo akhumudwa.

AGALATIYA 4:29
Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano,

MARKO 10:30
amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi irinkudza, moyo wosatha.

MATEYU 13:21
ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo.

MACHITIDWE A ATUMWI 22:4
ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.

MATEYU 5:10
Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

AGALATIYA 6:12
Onseamene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu.

LUKA 21:12
Koma zisanacitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, cifukwa ca dzina langa.

MARKO 10:29-30
[29] Yesu anati, Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca Ine, ndi cifukwa ca Uthenga Wabwinowo,[30] amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi irinkudza, moyo wosatha.

AROMA 8:35-37
[35] Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?[36] Monganso kwalembedwa, 12 Cifukwa ca Inu tirikuphedwa dzuwa lonse; Tinayesedwa monga nkhosa zakupha,[37] Koma 13 m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.

MACHITIDWE A ATUMWI 11:19-21
[19] Pamenepo iwotu, akubalalika cifukwa ca cisautsoco cidadza pa Stefano, anafikira ku Foinike, ndi Kupro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.[20] Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kupro, ndi Kurene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.[21] Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupira unatembenukira kwa Ambuye.

MACHITIDWE A ATUMWI 9:4-5
[4] ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?[5] Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;

AGALATIYA 5:11
Koma ine, abale, ngati ndilalikiransoindulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.

MATEYU 10:23
Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.

MATEYU 5:12
Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

1 TIMOTEO 1:13
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wacipongwe; komatu anandicitira cifundo, popeza ndinazicita wosazindikira, wosakhulupirira;

MATEYU 5:11-12
[11] Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.[12] Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

LUKA 11:49
Mwa icinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

1 ATESALONIKA 3:3-4
[3] kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife ticite izi.[4] Pakutinso, pamenetinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudacitika, monganso mudziwa.

AHEBRI 11:36-38
[36] kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi 18 kuwatsekera m'ndende;[37] 19 anaponyedwa miyala, anacekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda obvala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ocitidwa zoipa,[38] (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi 20 m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.

YOHANE 15:20-21
[20] Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.[21] Koma izi zonse adzakucitirani cifukwa ca dzina langa, cifukwa sadziwa wondituma Ine.

MATEYU 10:21-23
[21] Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuimfa, ndi atate mwana wace: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.[22] Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa; koma iye wakupirira kufikira cimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa.[23] Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.

MATEYU 24:8-10
[8] Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.[9] Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, cifukwa ca dzina langa.[10] Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzace, nadzadana wina ndi mnzace.

LUKA 21:12-19
[12] Koma zisanacitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, cifukwa ca dzina langa.[13] Kudzakhala kwa inu ngati umboni.[14] Cifukwa cace tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire cimene mudzayankha.[15] Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.[16] Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a pfuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani,[17] Ndipo anthu onse adzadana ndi inu cifukwa ca dzina langa.[18] Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.[19] Mudzakhala nao moyo wanu m'cipiriro.

1 AKORINTO 4:8-13
[8] M wadzala kale, mwalemerera kale, mwacita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi mucitadi ufumu, kuti ifenso tikacite ufumu pamodzi ndi inu.[9] Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife coonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.[10] Tiri opusa ife cifukwa ca Kristu, koma muli ocenjera inu mwa Kristu; tiri ife ofoka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.[11] Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tid amarisece, tikhomedwa, tiribe pokhazikika;[12] ndipo tigwiritsa nchito, ndi kucita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;[13] ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano,

AHEBRI 10:32-34
[32] Koma tadzikumbursani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa 4 mudapirira citsutsano cacikuru ca zowawa;[33] pena pocitidwa 5 cinthu cooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ocitidwa zotere.[34] Pakuti 6 munamva cifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa cuma canu, 7 pozindikira kuti muli naco nokha cuma coposa caeikhalire.

AHEBRI 11:33-38
[33] amene mwa cikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anacita cilungamo, analandira malonjezano, 11 anatseka pakamwa mikango,[34] 12 nazima mphamvu ya moto, 13 napulumuka lupanga lakuthwa, 14 analimbikitsidwa pokhala ofok a, anakula mphamvu kunkhondo, 15 anapitikitsa magulu a nkhondo yacilendo.[35] 16 Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo 17 ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,[36] kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi 18 kuwatsekera m'ndende;[37] 19 anaponyedwa miyala, anacekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda obvala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ocitidwa zoipa,[38] (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi 20 m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.

MACHITIDWE A ATUMWI 12:1-19
[1] Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Eklesia kuwacitira zoipa.[2] Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo a mbale wa Yohane.[3] Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda cotupitsa.[4] Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anai anai, amdikire iye; ndipo anafuna kumturutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.[5] Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Eklesia anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.[6] Ndipo pamene Herode anati amturutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikari awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhalapakhomoanadikira ndende.[7] Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga, Ndipo maunyolo anagwa kucoka m'manja mwace.[8] Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'cuuno, numange nsapato zako. Nacita cotero. Ndipo ananena naye, Pfunda cobvala cako, nunelitsate ine.[9] Ndipo anaturuka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti ncoona cocitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.[10] Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi paciwiri, anadza ku citseko cacitsulo cakuyang'ana kumudzi; cimene cidawatsegukira cokha; ndipo anaturuka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamcokera.[11] Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wace nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku cilingiriro conse ca anthu a Israyeli.[12] Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza ku nyumba ya Marlys amace wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera,[13] Ndipo m'mene anagogoda pa citseko ca pakhomo, linadza kudzabvomera buthu, dzina lace Roda.[14] Ndipo pozindikira mau ace a Petro, cifukwa ca kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.[15] Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wace.[16] Koma Petro anakhala cigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa.[17] Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale cete, anawafotokozera umo, adamturutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi, Ndipo anaturuka napita kwina.[18] Koma kutaca, panali phokoso lalikuru mwa asilikari, Petro wamuka kuti.[19] Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kaisareya, nakhalabe kumeneko.

MACHITIDWE A ATUMWI 9:1-14
[1] Koma Saulo, wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsya ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,[2] napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.[3] Ndipo poyenda ulendo wace, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kocokera kumwamba;[4] ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?[5] Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;[6] komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.[7] Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.[8] Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.[9] Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.[10] Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,[11] Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera[12] ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.[13] Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;[14] ndi kuti pane ali nao ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.

AGALATIYA 1:13
Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Ciyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,

CHIVUMBULUTSO 2:8-10
[8] Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smurna lemba; Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:[9] Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.[10] Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena ainu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala naco cisautso masiku khumi. Khala wokholupirfka kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

MACHITIDWE A ATUMWI 26:9-11
[9] Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.[10] Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.[11] Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.

1 AKORINTO 4:12
ndipo tigwiritsa nchito, ndi kucita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

MACHITIDWE A ATUMWI 12:1
Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Eklesia kuwacitira zoipa.

AFILIPI 3:6
monga mwa cangu, wolondalonda Eklesia; monga mwa cilungamo ca m'lamulo wokhala wosalakwa ine.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society