A A A A A

Mpingo: [Kubadwa kwa Yesu]


MATEYU 1:18-23
[18] Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.[19] Koma Yosefe, mwamuna wace, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri,[20] Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.[21] Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao.[22] Ndipo zonsezi zinakhala kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,[23] Onani namwali adzaima, Nadzabala mwana wamwamuna, Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe.

LUKA 2:7-21
[7] Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.[8] Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.[9] Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru.[10] Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;[11] pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.[12] Ndipo ici ndi cizindikilo kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsaru atagonamodyera.[13] Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,[14] Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.[15] Ndipo panali, pamene angelo anacokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzace, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone cinthu ici cidacitika, cimene Ambuye anatidziwitsira ife.[16] Ndipo iwo anadza ndi cangu, napeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.[17] Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.[18] Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.[19] Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.[20] Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.[21] Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula iye, anamucha dzina lace Yesu, limene anachula mngeloyo asanalandiridwe iye m'mimba.

MATEYU 2:1-12
[1] Ndipo pa kubadwa kwace kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,[2] nati, Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? cifukwa tinaona nyenyezi yace kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.[3] Ndipo Herode mfumuyo pakumva ici anabvutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.[4] Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe akuru onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Kristuyo?[5] Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; cifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,[6] Ndipo iwe: Betelehemu, dziko la Yudeya, Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akuru a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzacokera mwaiwe, Amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.[7] Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yace idaoneka nyenyeziyo.[8] Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.[9] Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako.[10] Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukuru.[11] Ndipo pofika ku nyumba anaona kamwanako ndi Mariya amace, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula cuma cao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.[12] Ndipo iwo, pocenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anacoka kupita ku dziko lao pa njira yina.

AGALATIYA 4:4
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wace, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,

LUKA 2:1-4
[1] Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linaturuka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;[2] ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya.[3] Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu ali yense ku mudzi wace.[4] Ndipo Yosefe yemwe anakwera kucokera ku Galileya, ku mudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, ku mudzi wa Davine, dzina lace Betelehemu, cifukwa iye anali wa banja ndi pfuko lace la Davine;

CHIVUMBULUTSO 12:1-5
[1] Ndipo cizindikilo cacikuru cinaoneka m'mwamba; mkazi wobvekedwa dzuwa, ndi mwezi ku mapazi ace, ndi pamutu pace korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;[2] ndipo anali ndi pakati; ndipo apfuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.[3] Ndipo cinaoneka cizindikilo cina m'mwamba, taonani, cinjoka cofiira, cacikuru, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pace nduwira zacifumu zisanu ndi ziwiri.[4] Ndipo mcira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo cinjoka cinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, ico cikalikwire mwana wace.[5] Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wace amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wacifumu wace.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society