A A A A A

Mpingo: [Kupita ku Tchalitchi]


AHEBRI 10:24-25
[24] ndipo tiganizirane wina ndi mnzace kuti tifulumizane ku cikondano ndi nchito zabwino,[25] osaieka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amacita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lirikuyandika.

MATEYU 18:20
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndiri komweko pakati pao.

AKOLOSE 3:16
Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.

AEFESO 4:11-13
[11] Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;[12] kuti akonzere oyera mtima: ku nchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu;[13] kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa cikhulupiriro, ndi wa cizindikiritso ca Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa cidzaloca Kristu.

MACHITIDWE A ATUMWI 2:42
Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

AROMA 10:17
Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.

MATEYU 16:18
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo.

MACHITIDWE A ATUMWI 9:31-32
[31] Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.[32] Koma kunali, pakupita Petro ponse ponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhalaku Luda.

MATEYU 6:33
Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

YAKOBO 1:22
Khalani akucita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

2 TIMOTEO 4:2
lalikira mau; cita nao pa nthawi yace, popanda nthawi yace; tsutsa, dzudzula, cenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi ciphunzitso.

MATEYU 28:19-20
[19] Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:[20] ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society