A A A A A

Angelo ndi Ziwanda: [Belezebule]


MATEYU 12:24
Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samaturutsa ziwanda koma ndi mphamvu yace ya Beelzebule, mkuru wa ziwanda.

MARKO 3:22
Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Beelzibule, ndipo, Ndi mkuru wao wa ziwanda aturutsa ziwanda.

MATEYU 10:25
Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamucha mwini banja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ace?

MATEYU 12:27
Ndipo ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Beelzebule, ana anu amaziturutsa ndi mphamvu ya yani? cifukwa cace iwo adzakhala oweruza anu.

LUKA 11:15-19
[15] Koma ena mwa iwo anati, Ndi Beelzebule mkuru wa ziwanda amaturutsa ziwanda.[16] Koma ena anamuyesa, nafuna kwa iye cizindikilo cocokera Kumwamba.[17] Koma iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m'kati mwace upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwace igwa.[18] Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.[19] Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi Beelzebule, ana anu aziturutsa ndi yani? Mwa ici iwo adzakhala oweruza anu.

2 MAFUMU 1:1-3
[1] NDIPO atamwalira Ahabu, Moabu anapandukana ndi Israyeli.[2] Ndipo Ahaziya anagwa kubzola ku made wa cipinda cace cosanja cinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni ngati ndidzacira nthenda iyi.[3] Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti mukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni?

LUKA 11:18
Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.

MARKO 3:20-30
[20] Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.[21] Ndipo pamene abale ace anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaruka.[22] Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Beelzibule, ndipo, Ndi mkuru wao wa ziwanda aturutsa ziwanda.[23] Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kuturutsa Satana?[24] Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika.[25] Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, siikhoza kukhazikika nyumbayo,[26] Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika.[27] Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nvumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ace, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwace.[28] Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa macimo onse a ana a anthu, ndi zamwano ziri zonse adzacita mwano nazo;[29] koma ali yense adzacitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anaparamuladi cimo losatha;[30] pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

2 MAFUMU 1:16
Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli kufunsira mau ace? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

GENESIS 1:1
PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

MATEYU 9:34
Koma Afarisi analinkunena, Aturutsa ziwanda ndi mphamvu zace za mfumu ya ziwanda.

CHIVUMBULUTSO 21:20
acisanu, ndi sardoau; acisanu ndi cimodzi, ndi sardiyo; acisanu ndi ciwiri, ndi krusolito; acisanu ndi citatu, ndi berulo; acisanu ndi cinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndt cimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi ciwiri, ndi ametusto.

YOBU 2:11
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za coipa ici conse cidamgwera, anadza, yense kucokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

2 MAFUMU 1:6
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

YOHANE 1:1
PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

LUKA 11:19
Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi Beelzebule, ana anu aziturutsa ndi yani? Mwa ici iwo adzakhala oweruza anu.

EKSODO 6:23
Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wace wa Nasoni, akhale mkazi wace; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara.

LUKA 3:1
Ndipo pa caka cakhumi ndi cisanu ca ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode ciwanga ca Galileya, ndi Filipo mbale wace ciwanga ca dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo ciwanga ca Abilene;

GENESIS 10:10
Ndipo kuyamba kwace kwa ufumu wace kunali Babele, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.

GENESIS 14:1
Ndipo panali masiku a Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara, ndi Kedorelaomere mfumu ya Elami, ndi Tidala mfumu ya Goimu,

DEUTERONOMO 14:5
ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.

RUTE 1:2
Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wace ndiye Naomi, ndi maina a ana ace awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo a ku Efrata ku Betelelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Moabu, nakhala komweko.

NEHEMIYA 1:1
MAU a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, caka ca makumi awiri, pokhala ine ku Susani ku nyumba ya mfumu,

ESTERE 1:1
IZI zinacitika masiku a Ahaswero, ndiye Ahasweroyo anacita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.

1 MAFUMU 1:2
Pamenepo anyamata ace ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

CHIVUMBULUTSO 16:16
Ndipo anawasonkhanitsira ku malo ochedwa m'Cihebri Harmagedo.

YESAYA 34:14
Ndipo zirombo za m'cipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzace; inde mancici adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.

MATEYU 22:37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

MARKO 3:1-6
[1] Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lace lopuwala.[2] Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamciritsa dzuwa la Sabata; kuti ammange mlandu.[3] Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.[4] Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa dzuwa la Sabata kucita zabwino, kapena zoipa? kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala cete.[5] Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva cisoni cifukwa ca kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linacira dzanja lace.[6] Ndipo Afarisi anaturuka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.

MARKO 10:46-52
[46] Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikuturuka m'Yeriko, ndi ophunzira ace, ndi khamu lalikuru la anthu, mwana wa Timeyu, Bartimeyu, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira.[47] Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kupfuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundicitire ine cifundo.[48] Ndipo ambiri anamuyamula kuti atonthole: koma makamaka anapfuulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundicitire cifundo.[49] Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.[50] Ndipo iye anataya copfunda cace, nazunzuka, nadza kwa Yesu.[51] Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikucitire ciani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.[52] Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.

DANIELE 1:7
Ndi mkuru wa adindo anawapatsa maina ena; Danieli anamucha Belitsazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaeli, Mesaki; ndi Azariya, Abedinego.

OWERUZA 4:6
Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?

2 MAFUMU 19:37
Ndipokunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wace, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarihadoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

EZEKIELE 23:4
Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkuru, ndi Oholiba mng'ono wace; nakhala anga, nabala ana amuna ndi akazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.

YEREMIYA 1:1
MAU a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;

GENESIS 10:22
Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Ashuri, ndi Aripakasadi, ndi Ludi, ndi Aramu.

EZARA 4:7
Ndipo masiku a Aritasasta Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli, ndi anzao otsala, analembera kwa Aritasasta mfumu ya Perisiya; ndi cilembedwe cace ca kalatayo anamlemba m'Ciaramu, namsanduliza m'Ciaramu.

MATEYU 10:3
Filipo, ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;

MACHITIDWE A ATUMWI 2:9
Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya;

LEVITIKO 11:5
Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika ciboda, muiyese yodetsedwa.

MLALIKI 1:1
MAU a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu.

EKSODO 30:34
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi libano loona; miyeso yofanana;

YOBU 9:9
Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe, Ndi Kumpotosimpita,

MACHITIDWE A ATUMWI 6:5
Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi cikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolao, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:

CHIVUMBULUTSO 1:11
ndi kuti, Cimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.

1 MAFUMU 8:13
Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo inu nthawi zosatha.

MARKO 3:23
Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kuturutsa Satana?

YOSWA 24:15
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society