A A A A A

Zowonjezera: [Kudya munthu wina]


YEREMIYA 19:9
Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao amuna ndi akazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wace, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.

EZEKIELE 5:10
Cifukwa cace atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzacita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse.

LEVITIKO 26:29
Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.

2 MAFUMU 6:28-29
[28] Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa.[29] Ndipo tinaphika mwana wanga ndi kumudya, ndi mawa wace ndinanena naye, Tenga mwana wako, timudye; koma wambisa mwana wace.

MALIRO 4:10
Manja a akazi acisoni anaphika anaanao; Anali cakudya cao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

MALIRO 2:20
Onani Yehova, nimupenye, mwacitira ayani ici? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawaseweza? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?

DEUTERONOMO 28:53-57
[53] Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.[54] Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu diso lace lidzaipira mbale wace, ndi mkazi wa pa mtima wace, ndi ana ace otsalira;[55] osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ace alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse.[56] Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lace popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lace lidzamuipira mwamuna wa pamtima pace, ndi mwana wace wamwamuna ndi wamkazi;[57] ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.

GENESIS 1:26-27
[26] Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[27] Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

2 AKORINTO 5:8
koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.

LUKA 16:19-26
[19] Ndipo panali munthu mwini cuma amabvala cibakuwa ndi nsaru yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;[20] ndipo wopemphapempha wina, dzina lace Lazaro, adaikidwa pakhomo pace wodzala ndi zironda,[21] ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini cumayo; komatu agarunso anadza nanyambita zirondazace.[22] Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka ku cifuwa ca Abrahamu; ndipo mwini cumayo adafanso, naikidwa m'manda.[23] Ndipo m'Hade anakweza maso ace, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'cifuwa mwace.[24] Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundicitire cifundo, mutome Lazaro, kuti abviike nsonga ya cala cace m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.[25] Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukila kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.[26] Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikuru, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kucokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kucokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.

CHIVUMBULUTSO 20:11-15
[11] Ndipo ndinaona, mpando wacifumu waukuru woyera, ndi iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace, ndipo sanapezedwamalo ao.[12] Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao.[13] Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace,[14] Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto.[15] Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

DEUTERONOMO 28:53
Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.

1 AKORINTO 14:34-35
[34] Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula, Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena,[35] Koma ngati afuna kuphunzirakanthu afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.

LUKA 1:37
Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

YOHANE 1:1
PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

DEUTERONOMO 28:57
ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.

1 TIMOTEO 2:11-15
[11] Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse.[12] Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.[13] Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;[14] ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;[15] koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'cikhulupiriro ndi cikondi ndi ciyeretso pamodzi ndi cidziletso.

1 TIMOTEO 5:3-16
[3] Citira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.[4] Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kucitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ici ncolandirika pamaso pa Mulungu.[5] Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.[6] Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo,[7] Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda ciremao[8] Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yace ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lace, wakana cikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.[9] Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,[10] wa mbiri ya nchito zabwino; ngati walera ana, ngati wacereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a nzera mtima, ngati wathapdiza osautsidwa, ngati anatsatadi nchito zonse zabwino.[11] Koma amasiyeang'ono uwakane; pakuti pamene ayambakumcitira Kristu cipongwe afuna kukwatiwa;[12] pokhala naco citsutso, popeza adataya cikhulupiriro cao coyamba.[13] Ndipo aphunziraponso kucita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pace, nacita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.[14] Cifukwa cace nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa cifukwa kwa mdaniyo cakulalatira;[15] pakuti adayamba enakupatuka ndi kutsata Satana.[16] Ngati mkazi wina wokhulupira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.

1 AKORINTO 11:2-16
[2] Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukila ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.[3] Koma ndifunakuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu,[4] Mwamuna yense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wace.[5] Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.[6] Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,[7] Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.[8] Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;[9] pakutinso mwamuna sanalengedwa cifukwa ca mkazi;[10] koma mkazi cifukwa ca mwamuna; cifukwa ca ici mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pace, cifukwa ca angelo.[11] Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.[12] Pakuti monga mkazi aliwa kwa mwamuna, comweconso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mu, lungu.[13] Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosapfunda mutu?[14] Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi cimnyozetsa iye?[15] Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lace lapatsidwa kwa iye ngati cophimba.[16] Koma akaoneka wina ngati wotetana, tiribe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society