1 TIMOTEO 5:8 |
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yace ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lace, wakana cikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira. |
|
2 AKORINTO ९:८ |
Ndipo Mulungu akhoza kucurukitsira cisomo conse kwa inu; kuti inu, pokhala naco cikwaniro conse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukacurukire ku nchito yonse yabwino; |
|
DEUTERONOMO 29:12 |
kuti mulowe cipangano ca Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lace, limene Yehova Mulungu wanu acita ndi inu lero lino; |
|
AEFESO ३:२० |
Ndipo kwa iye amene angathe kucita koposa-posatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kucita mwa ife, |
|
EKSODO ३४:६ |
Ndipo Yehova anapita pamaso pace, napfuula, Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wacoonadi; |
|
YAKOBO १:१७ |
Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko, kapena mthunzi wa citembenukiro. |
|
YOHANE 10:10 |
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka. |
|
LUKA ६:३८ |
6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu. |
|
LUKA 6:45 |
13 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cokoma ca mtima wace; ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'coipa cace: pakuti m'kamwa mwace mungolankhula mwa kucuruka kwa mtima wace. |
|
MATEYU ६:३३ |
Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. |
|
AFILIPI 4:19 |
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m'ulemerero mwa Kristu Yesu. |
|
MIYAMBO 3:5-10 |
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;[6] Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.[7] Usadziyese wekha wanzeru; Opa Yehova, nupatuke pazoipa;[8] Mitsempha yako idzalandirapo moyo, Ndi mafupa ako uwisi.[9] Lemekeza Yehova ndi cuma cako, Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;[10] Motero nkhokwe zako zidzangoti the, Mbiya zako zidzasefuka vinyo. |
|
MASALIMO 23:5 |
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga: Mwandidzoza mutu wanga mafuta; cikho canga cisefuka. |
|
MASALIMO 36:8 |
Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu: Ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu. |
|
MASALIMO 37:11 |
Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; Nadzakondwera nao mtendere wocuruka. |
|
MASALIMO 65:11 |
Mubveka cakaci ndi ukoma wanu; Ndipo mabande anu akukha zakuca. |
|
MASALIMO 72:16 |
M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzocuruka pamwamba pa mapiri; Zipatso zace zidzati waa, ngati za ku Lebano: Ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi. |
|
AROMA 15:13 |
Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. |
|
MASALIMO 66:8-12 |
[8] Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu, Ndipo mumveketse liu la cilemekezo cace:[9] Iye amene asunga moyo wathu tingafe, Osalola phazi lathu literereke.[10] Pakati munatiyesera, Mulungu: Munatiyenga monga ayenga siliya.[11] Munapita nafe kuukonde; Munatisenza cothodwetsa pamsana pathu.[12] Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; Tinapyola moto ndi madzi; Koma munatifikitsa potitsitsimutsa. |
|
Chewa Bible (BL) 1992 |
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society |