A A A A A

Zowonjezera: [Mowa]


1 PETRO 4:3
Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kucita cifuno ca amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

1 TIMOTEO 5:23
Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu ucite naye vinyo pang'ono, cifukwa ca mimba yako ndi zofoka zako zobwera kawiri kawiri.

MLALIKI 9:7
Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wabvomerezeratu zocita zako.

AEFESO 5:18
Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

MIYAMBO 20:1
Vinyo acita ciphwete, cakumwa caukali cisokosa; Wosocera nazo alibe nzeru.

MIYAMBO 23:31
Usayang'ane pavinyo alikufiira. Alikung'azimira m'cikho. Namweka mosalala.

AROMA 13:13
Tiyendeyeode koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'cigololo ndi conyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.

MIYAMBO 31:4-5
[4] Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo; Akalonga sayenera kunena, Cakumwa caukali ciri kuti?[5] Kuti angamwe, naiwale malamulo, Naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

MASALIMO 104:14-15
[14] Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, Ndi zitsamba acite nazo munthu; Naturutse cakudya cocokera m'nthaka;[15] Ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, Ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yace, Ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

1 AKORINTO 10:23-24
[23] Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.[24] Munthu asafune zace za iye yekha, kama za mnzace.

YESAYA 62:8-9
[8] Yehova analumbira pa dzanja lace lamanja, ndi mkono wace wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale cakudya ca adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira nchito;[9] koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamchera adzamumwa m'mabwalo a kacisi wanga.

AGALATIYA 5:19-21
[19] Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano,[20] nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru,[21] kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

1 AKORINTO 9:19-23
[19] Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ocuruka.[20] Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;[21] kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo twa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.[22] Kwa ofoka ndinakhala ngati wofoka, kuti ndipindule ofoka, Ndakhala zonse kwa anthu onse, 1 kuti pali ponse ndikapulumutse ena.[23] Koma ndicita zonse zifukwa ca Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

AROMA 14:15-21
[15] Koma ngati iwe wacititsa mbale wako cisoni ndi cakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi cikondano. Usamuononga ndi cakudya cako, iye amene Kristu adamfera.[16] Cifukwa cace musalole cabwino canu acisinjirire,[17] Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala cakudya ndi cakumwa, koma cilungamo, ndi mtendere, ndi cimwemwe mwa Mzimu Woyera.[18] Pakuti iye amene atumikira Kristu mu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu.[19] Cifukwa cace tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzace.[20] Usapasule nchito ya Mulungu cifukwa ca cakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.[21] Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusacita cinthu ciri conse cakukhumudwitsa mbale wako.

YOHANE 2:3-11
[3] Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo,[4] Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.[5] Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri conse akanena kwa inu, citani.[6] Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.[7] Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde.[8] Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwamkulu wa phwando. Ndipo anapita nao.[9] Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwa kumene anacokera (koma atumiki amene adatiinga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,[10] nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.[11] Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira iye.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society