A A A A A

Sakani
MATEYU 12:31
Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa.


MARKO 3:29
koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”


YOHANE 1:29
Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi!


YOHANE 8:7
Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.”


YOHANE 8:34
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:60
Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:23
Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo.”


MACHITIDWE A ATUMWI 13:39
Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose.


AROMA 3:20
Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.


AROMA 5:12
Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa.


AROMA 5:13
Pakuti Malamulo asanaperekedwe, tchimo linali mʼdziko lapansi. Koma pamene palibe Malamulo, tchimo silitengedwa kukhala tchimo.


AROMA 5:16
Ndiponso, mphatso ya Mulungu sifanana ndi zotsatira za kuchimwa kwa munthu mmodzi. Chiweruzo chinatsatira tchimo la munthu mmodzi ndi kubweretsa kutsutsidwa koma mphatso inatsatira zolakwa zambiri ndi kubweretsa kulungamitsidwa.


AROMA 5:18
Choncho monga tchimo limodzi linabweretsa kutsutsika pa anthu onse, chimodzimodzinso ntchito imodzi yolungama inabweretsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuwapatsa moyo.


AROMA 5:21
Choncho monga momwe tchimo linkalamulira anthu ndi kubweretsa imfa pa iwo, chomwecho kunali koyenera kuti chisomo chilamulire pobweretsa chilungamo kwa anthu, ndi kuwafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.


AROMA 6:2
Ayi. Mʼnjira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitirira bwanji kukhalabe mʼmenemo?


AROMA 6:6
Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo


AROMA 6:7
chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.


AROMA 6:10
Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.


AROMA 6:11
Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.


AROMA 6:12
Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa.


AROMA 6:13
Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.


AROMA 6:14
Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.


AROMA 6:16
Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake.


AROMA 6:17
Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira.


AROMA 6:18
Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.


AROMA 6:20
Pomwe munali akapolo atchimo, simunkalabadira za chilungamo.


AROMA 6:22
Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.


AROMA 6:23
Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.


AROMA 7:7
Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, “Usasirire.”


AROMA 7:17
Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga.


AROMA 7:20
Tsopano ngati ine ndimachita zimene sindikuzifuna, si inenso amene ndimazichita, koma ndi tchimo limene lili mʼkati mwanga.


AROMA 8:2
chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.


AROMA 8:3
Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu,


AROMA 14:23
Koma munthu amene akukayika atsutsidwa ngati adya, chifukwa kudya kwake si kwa chikhulupiriro; ndipo chilichonse chosachokera mʼchikhulupiriro ndi tchimo.


1 AKORINTO 8:13
Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse.


1 AKORINTO 15:56
Ululu wa imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo.


2 AKORINTO 5:21
Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.


2 AKORINTO 11:7
Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?


AGALATIYA 6:1
Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.


AHEBRI 3:13
Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.


AHEBRI 9:26
Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe.


AHEBRI 9:28
momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.


AHEBRI 10:6
Simunakondwere nazo nsembe zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.


AHEBRI 10:8
Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe.


AHEBRI 12:1
Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.


YAKOBO 1:15
Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.


1 PETRO 2:22
“Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza.”


1 PETRO 2:24
Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.


1 YOHANE 1:7
Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.


1 YOHANE 1:8
Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi.


1 YOHANE 3:4
Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo.


1 YOHANE 3:5
Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo.


1 YOHANE 5:16
Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi.


1 YOHANE 5:17
Chilichonse chosalungama ndi tchimo ndipo pali tchimo losadzetsa imfa.


YUDA 1:11
Tsoka kwa iwo chifukwa anatsatira njira ya Kaini. Iwo athamangira phindu, nʼchifukwa chake anagwa mʼtchimo la Baalamu. Iwo anawonongedwa chifukwa chowukira monga anachitira Kora.


Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®