A A A A A

Sakani
MATEYU 17:21
Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”


MATEYU 21:13
Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”


MATEYU 21:22
Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”


MATEYU 23:14
Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera akazi amasiye chuma chawo, kwinaku nʼkumanamizira kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.


MARKO 11:17
Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”


MARKO 11:24
Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.


MARKO 12:40
Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”


LUKA 1:13
Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane.


LUKA 19:46
Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”


LUKA 20:47
Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”


AROMA 1:10
Mʼmapemphero anga, nthawi zonse, ndimapemphera kuti ngati nʼkotheka mwachifuniro cha Mulungu, njira inditsekukire kuti ndibwere kwanuko.


AROMA 10:1
Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.


AROMA 12:12
Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.


1 AKORINTO 7:5
Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa.


1 AKORINTO 14:16
Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena?


2 AKORINTO 1:11
Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri.


2 AKORINTO 13:9
Ife timasangalala kuti pamene tafowoka, inu muli amphamvu; ndipo pemphero lathu ndi lakuti mukhale angwiro.


AEFESO 1:16
ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga.


AEFESO 6:18
Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.


AFILIPI 1:4
Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe


AFILIPI 1:9
Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo,


AFILIPI 1:19
pakuti ndikudziwa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndi thandizo lochokera kwa Mzimu wa Yesu Khristu, zimene zandionekera zidzathandiza kuti ndimasulidwe.


AFILIPI 4:6
Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.


1 ATESALONIKA 1:2
Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu.


1 TIMOTEO 2:1
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.


1 TIMOTEO 4:5
pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.


2 TIMOTEO 1:3
Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.


FILEMONI 1:4
Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga.


FILEMONI 1:22
Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.


AHEBRI 5:7
Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka.


YAKOBO 5:15
Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.


YAKOBO 5:16
Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.


1 PETRO 3:7
Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.


1 PETRO 3:12
Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo. Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”


CHIVUMBULUTSO 5:8
Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 8:3
Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu.


CHIVUMBULUTSO 8:4
Fungo la lubani pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima zinakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo.


Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®