A A A A A


Sakani

MATEYU 1:18
Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.


MATEYU 1:20
Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.


MATEYU 3:11
“Ine ndikubatizani ndi madzi kusonyeza kutembenuka mtima. Koma pambuyo panga akubwera wina amene ali ndi mphamvu kuposa ine, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani ndi Mzimu Woyera ndi moto.


MATEYU 3:16
Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati nkhunda natera pa Iye.


MATEYU 4:1
Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.


MATEYU 5:3
“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.


MATEYU 9:32
Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula.


MATEYU 9:33
Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.”


MATEYU 10:20
pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.


MATEYU 10:28
Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.


MATEYU 12:18
“Taonani mnyamata wanga amene ndinamusankha, Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye. Pa Iye ndidzayika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.


MATEYU 12:28
Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.


MATEYU 12:31
Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa.


MATEYU 12:32
Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo.


MATEYU 12:43
“Pamene mzimu woyipa utuluka mwa munthu, umadutsa malo wopanda madzi kufunafuna malo opumulira ndipo suwapeza.


MATEYU 22:43
Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,


MATEYU 26:41
Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”


MATEYU 27:50
Ndipo pamene Yesu analiranso mofuwula, anapereka mzimu wake.


MATEYU 28:19
Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,


MARKO 1:8
Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”


MARKO 1:10
Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda.


MARKO 1:12
Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu,


MARKO 1:23
Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti,


MARKO 1:26
Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.


MARKO 2:8
Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi?


MARKO 3:29
koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”


MARKO 3:30
Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”


MARKO 5:2
Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye.


MARKO 5:8
Pakuti Yesu anati kwa iye, “Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!”


MARKO 7:25
Kunena zoona, amayi amene kamwana kawo kakakazi kanali kogwidwa ndi mzimu woyipa, atangomva za Iye, anabwera nagwada pa mapazi ake.


MARKO 9:17
Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula.


MARKO 9:18
Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”


MARKO 9:20
Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.


MARKO 9:25
Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, “Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”


MARKO 9:26
Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.”


MARKO 12:36
Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti, “Ambuye anati kwa Ambuye anga: ‘Khalani pa dzanja langa lamanja kufikira nditayika adani anu pansi pa mapazi anu.’


MARKO 13:11
Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.


MARKO 14:38
Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”


LUKA 1:15
chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa.


LUKA 1:17
Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”


LUKA 1:35
Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu.


LUKA 1:41
Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera.


LUKA 1:47
Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,


LUKA 1:67
Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,


LUKA 1:80
Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.


LUKA 2:25
Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


LUKA 2:26
Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye.


LUKA 2:27
Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo,


LUKA 3:16
Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto.


LUKA 3:22
Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”


LUKA 4:1
Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu,


LUKA 4:14
Yesu anabwerera ku Galileya mu mphamvu ya Mzimu Woyera, ndipo mbiri yake inafalikira ku madera onse a ku midzi.


LUKA 4:18
“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,


LUKA 4:33
Mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu woyipa. Iye analira ndi mawu akulu, akuti


LUKA 8:29
Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.


LUKA 8:55
Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya.


LUKA 9:42
Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake.


LUKA 10:21
Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.


LUKA 11:13
Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”


LUKA 11:24
“Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’


LUKA 12:10
Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.


LUKA 12:12
pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”


LUKA 13:11
ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe.


LUKA 23:46
Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.


YOHANE 1:32
Kenaka Yohane anapereka umboni uwu: “Ine ndinaona Mzimu Woyera ngati nkhunda kuchokera kumwamba nakhala pa Iye.


YOHANE 1:33
Ine sindikanamudziwa Iye, koma kuti amene anandituma ine kudzabatiza ndi madzi anati kwa ine, ‘Munthu amene udzaona Mzimu Woyera akutsika nakhazikika pa Iye ndi amene adzabatize ndi Mzimu Woyera.’


YOHANE 3:5
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:6
Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu.


YOHANE 3:8
Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”


YOHANE 3:34
Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire.


YOHANE 4:23
Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna.


YOHANE 4:24
Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”


YOHANE 6:63
Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.


YOHANE 7:39
Ponena izi Iye amatanthauza Mzimu Woyera, amene adzalandire amene amakhulupirira Iye. Pa nthawiyi nʼkuti Mzimu Woyera asanaperekedwe, pakuti Yesu anali asanalemekezedwe.


YOHANE 11:33
Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu.


YOHANE 13:21
Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”


YOHANE 14:17
Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu.


YOHANE 14:26
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.


YOHANE 15:26
“Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine.


YOHANE 16:13
Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.


YOHANE 16:15
Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”


YOHANE 19:30
Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.


YOHANE 20:22
Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:2
mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:5
Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”


MACHITIDWE A ATUMWI 1:8
Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”


MACHITIDWE A ATUMWI 1:16
Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:4
Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:17
“ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:18
Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi, ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:33
Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:8
Petro wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anawawuza kuti, “Inu olamulira ndi akulu!


MACHITIDWE A ATUMWI 4:25
Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti, “ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu, ndipo akonzekera kuchita zopandapake?


MACHITIDWE A ATUMWI 4:31
Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:3
Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama?


MACHITIDWE A ATUMWI 5:9
Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.”


MACHITIDWE A ATUMWI 5:32
Ife ndife mboni za zimenezi, ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu anapereka kwa iwo akumvera Iye.”


MACHITIDWE A ATUMWI 6:3
Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:5
Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:10
Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:51
“Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera:


MACHITIDWE A ATUMWI 7:55
Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:59
Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.”


MACHITIDWE A ATUMWI 8:15
Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera,


MACHITIDWE A ATUMWI 8:16
chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:17
Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:18
Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati,


MACHITIDWE A ATUMWI 8:19
“Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.”


MACHITIDWE A ATUMWI 8:29
Mzimu anamuwuza Filipo kuti, “Pita pa galeta ilo ndipo ukakhale pafupi nalo.”


MACHITIDWE A ATUMWI 8:39
Pamene iwo anatuluka mʼmadzimo, Mzimu wa Ambuye anamukwatula Filipo, ndipo Ndunayo sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:17
Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.”


MACHITIDWE A ATUMWI 9:31
Pamenepo mpingo wa ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unakhala pamtendere, unalimbikitsidwa; ndi kupatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera, unakula mʼchiwerengero, ndi kukhala moopa Ambuye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:19
Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:38
kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:44
Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:45
Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:47
“Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.”


MACHITIDWE A ATUMWI 11:12
Mzimu anandiwuza kuti ndisakayike, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi awa anapitanso nane ndipo tinalowa mʼnyumba ya munthuyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:15
“Nditangoyamba kuyankhula, Mzimu Woyera anafika pa iwo monga momwe anafikira pa ife poyamba paja.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:16
Kenaka ndinakumbukira zimene Ambuye ananena kuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’


MACHITIDWE A ATUMWI 11:24
Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:28
Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo).


MACHITIDWE A ATUMWI 13:2
Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.”


MACHITIDWE A ATUMWI 13:4
Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:9
Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati,


MACHITIDWE A ATUMWI 13:52
Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:8
Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:28
Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi:


MACHITIDWE A ATUMWI 16:6
Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:7
Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:16
Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:18
Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, “Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:2
Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?” Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.”


MACHITIDWE A ATUMWI 19:6
Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:15
Tsiku lina mzimu woyipa unawayankha kuti, “Yesu ndimamudziwa ndiponso Paulo ndimamudziwa, nanga inu ndinu ndani?”


MACHITIDWE A ATUMWI 19:16
Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:22
“Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.”


MACHITIDWE A ATUMWI 20:23
Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:28
Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:4
Tinafunafuna ophunzira kumeneko, ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku asanu ndi awiri. Iwowa, mwa Mzimu Woyera anakakamiza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:11
Atafika kwa ife, anatenga lamba wa Paulo, nadzimanga naye manja ake ndi mapazi ake ndipo anati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwini lambayu, Ayuda adzamumanga chomwechi ku Yerusalemu, ndipo adzamupereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina.’ ”


MACHITIDWE A ATUMWI 23:9
Panali phokoso lalikulu, ndipo aphunzitsi ena amalamulo amene anali a gulu la Afarisi anayimirira natsutsa kwambiri. Iwo anati, “Ife sitikupeza cholakwa ndi munthu uyu, chifukwa mwina ndi mzimu kapena mngelo amene wayankhula naye.”


MACHITIDWE A ATUMWI 28:25
Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti,


AROMA 1:4
Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu,


AROMA 2:29
Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.


AROMA 5:5
Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.


AROMA 7:6
Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa.


AROMA 8:2
chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.


AROMA 8:4
ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu.


AROMA 8:5
Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu.


AROMA 8:6
Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere.


AROMA 8:9
Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu.


AROMA 8:10
Ndipo ngati Khristu ali mwa inu, thupi lanu ndi lakufa chifukwa cha uchimo, koma mzimu wanu ndi wamoyo chifukwa cha chilungamo.


AROMA 8:11
Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.


AROMA 8:13
Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo.


AROMA 8:14
Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.


AROMA 8:15
Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.”


AROMA 8:16
Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.


AROMA 8:23
Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.


AROMA 8:26
Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa.


AROMA 8:27
Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.


AROMA 9:1
Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni.


AROMA 11:8
monga kwalembedwa kuti, “Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu, maso osatha kupenya; makutu osatha kumva mpaka lero lino.”


AROMA 12:11
Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye.


AROMA 14:17
Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


AROMA 15:13
Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.


AROMA 15:16
kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.


AROMA 15:19
mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu.


AROMA 15:30
Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu.


1 AKORINTO 2:4
Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu,


1 AKORINTO 2:10
koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake. Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe.


1 AKORINTO 2:11
Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo.


1 AKORINTO 2:12
Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere.


1 AKORINTO 2:13
Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu.


1 AKORINTO 2:14
Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu.


1 AKORINTO 3:16
Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?


1 AKORINTO 4:21
Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?


1 AKORINTO 5:3
Ngakhale sindili nanu mʼthupi, ndili nanu mu mzimu. Ndipo ineyo ndapereka kale chiweruzo pa munthu amene amachita zotere, ngati kuti ndili komweko.


1 AKORINTO 5:4
Mukasonkhana mu dzina la Ambuye athu Yesu, ine ndili nanu mu mzimu, ndipo mphamvu ya Ambuye athu Yesu ili pomwepo,


1 AKORINTO 5:5
mumupereke munthuyu kwa Satana, kuti chikhalidwe chake cha uchimo chiwonongedwe ndikuti mzimu wake udzapulumuke pa tsiku la Ambuye.


1 AKORINTO 6:11
Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.


1 AKORINTO 6:17
Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi.


1 AKORINTO 6:19
Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi.


1 AKORINTO 7:40
Mʼmaganizo anga, mkaziyo adzakhala wokondwa koposa ngati atangokhala wosakwatiwa. Ndipo ndikuganiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.


1 AKORINTO 12:1
Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu.


1 AKORINTO 12:3
Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.


1 AKORINTO 12:4
Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo.


1 AKORINTO 12:7
Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.


1 AKORINTO 12:8
Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso.


1 AKORINTO 12:9
Kwa wina, Mzimu yemweyo amapereka chikhulupiriro, kwa wina mphatso zamachiritso, Mzimu yemweyo.


1 AKORINTO 12:11
Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.


1 AKORINTO 12:13
Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi mʼthupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo.


1 AKORINTO 14:2
Pakuti aliyense amene amayankhula malilime sayankhula kwa anthu, koma kwa Mulungu. Zoonadi, palibe amene amamva zimene akunena chifukwa Mzimu ndiye amamuyankhulitsa zachinsinsi.


1 AKORINTO 14:12
Chimodzimodzinso inu. Popeza mumafunitsitsa mphatso za Mzimu, yesetseni kuchita bwino pa mphatso zimene zimamanga mpingo.


1 AKORINTO 14:14
Popeza ngati ndipemphera mʼmalilime, ndi mzimu wanga umene ukupemphera, koma nzeru zanga sizikupindula kanthu.


1 AKORINTO 14:15
Tsono pamenepa nʼkutani? Ndidzapemphera ndi mzimu wanga, komanso ndidzapemphera ndi nzeru zanga. Ndidzayimba ndi mzimu wanga, komanso ndidzayimba ndi nzeru zanga.


1 AKORINTO 14:16
Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena?


1 AKORINTO 14:37
Ngati wina aliyense akuganiza kuti ndi mneneri kapena kuti ali ndi mphatso za Mzimu, ayenera kudziwa kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo la Ambuye.


1 AKORINTO 16:18
Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu womwe. Anthu a mtundu oterewa ngofunika kuwalemekeza.


2 AKORINTO 1:22
nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.


2 AKORINTO 3:3
Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.


2 AKORINTO 3:6
Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.


2 AKORINTO 3:8
kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa?


2 AKORINTO 3:17
Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu.


2 AKORINTO 3:18
Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.


2 AKORINTO 5:5
Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.


2 AKORINTO 6:6
pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi


2 AKORINTO 7:1
Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.


2 AKORINTO 11:4
Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.


2 AKORINTO 12:18
Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?


2 AKORINTO 13:14
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


AGALATIYA 3:2
Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva?


AGALATIYA 3:3
Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi?


AGALATIYA 3:5
Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva?


AGALATIYA 3:14
Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.


AGALATIYA 4:6
Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.”


AGALATIYA 4:29
Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero.


AGALATIYA 5:5
Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza.


AGALATIYA 5:16
Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.


AGALATIYA 5:17
Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna.


AGALATIYA 5:18
Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo.


AGALATIYA 5:22
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,


AGALATIYA 5:25
Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.


AGALATIYA 6:1
Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.


AGALATIYA 6:8
Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.


AGALATIYA 6:18
Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu zikhale ndi mzimu wanu abale. Ameni.


AEFESO 1:13
Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.


AEFESO 1:14
Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.


AEFESO 1:17
Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni.


AEFESO 2:2
mmene inu munkakhalamo pamene munkatsatira njira za dziko lapansi ndi za ulamuliro waufumu wa mlengalenga, mzimu umene ukugwira ntchito tsopano mwa amene samvera.


AEFESO 2:18
Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.


AEFESO 2:22
Ndipo mwa Iye, inunso mukamangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake.


AEFESO 3:5
chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri.


AEFESO 3:16
Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake,


AEFESO 4:3
Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere.


AEFESO 4:4
Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani.


AEFESO 4:30
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.


AEFESO 5:18
Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.


AEFESO 6:17
Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.


AEFESO 6:18
Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.


AFILIPI 1:19
pakuti ndikudziwa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndi thandizo lochokera kwa Mzimu wa Yesu Khristu, zimene zandionekera zidzathandiza kuti ndimasulidwe.


AFILIPI 1:27
Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino


AFILIPI 2:1
Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo,


AFILIPI 2:2
tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso.


AFILIPI 3:3
Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi


AFILIPI 4:23
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.


AKOLOSE 1:8
Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani.


AKOLOSE 2:5
Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.


1 ATESALONIKA 1:5
chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni.


1 ATESALONIKA 1:6
Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.


1 ATESALONIKA 4:8
Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.


1 ATESALONIKA 5:11
Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.


1 ATESALONIKA 5:19
Musazimitse moto wa Mzimu Woyera.


1 ATESALONIKA 5:23
Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 2:13
Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.


1 TIMOTEO 3:16
Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu: Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu anamuchitira umboni, angelo anamuona, analalikidwa pakati pa mitundu yonse, dziko lapansi linamukhulupirira, anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.


1 TIMOTEO 4:1
Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda.


2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.


2 TIMOTEO 1:14
Samalira bwino zokoma zimene anakusungitsa. Uzisamalire mothandizidwa ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.


2 TIMOTEO 4:22
Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale ndi inu nonse.


TITO 3:5
Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera


FILEMONI 1:25
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.


AHEBRI 2:4
Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.


AHEBRI 3:7
Tsono monga Mzimu Woyera akuti, “Lero mukamva mawu ake,


AHEBRI 4:12
Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.


AHEBRI 6:4
Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera.


AHEBRI 9:8
Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo.


AHEBRI 9:14
nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.


AHEBRI 10:15
Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,


AHEBRI 10:29
Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?


YAKOBO 2:26
Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.


YAKOBO 4:5
Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife?


1 PETRO 1:2
Mulungu Atate anakusankhani, atakudziwani kuyambira pachiyambi, ndipo Mzimu Woyera wakuyeretsani kuti mumvere Yesu Khristu ndikutsukidwa ndi magazi ake. Chisomo ndi mtendere zikhale ndi inu mochuluka.


1 PETRO 1:11
kufuna kudziwa nthawi ndi momwe zidzachitikire zinthu zimene Mzimu wa Khristu amene ali mwa iwo ankanenera za kuvutika kwa Khristu, ndi ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake.


1 PETRO 1:12
Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.


1 PETRO 3:4
Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.


1 PETRO 3:18
Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.


1 PETRO 3:19
Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende,


1 PETRO 4:6
Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.


1 PETRO 4:14
Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu.


2 PETRO 1:21
Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.


1 YOHANE 3:24
Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.


1 YOHANE 4:1
Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.


1 YOHANE 4:2
Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu,


1 YOHANE 4:3
koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.


1 YOHANE 4:6
Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.


1 YOHANE 4:13
Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake.


1 YOHANE 5:6
Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi.


1 YOHANE 5:8
Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana.


YUDA 1:19
Anthu amenewa ndi amene akubweretsa mipatuko pakati panu, amatsatira nzeru zachibadwa ndipo alibe Mzimu Woyera.


YUDA 1:20
Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.


CHIVUMBULUTSO 1:10
Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga,


CHIVUMBULUTSO 2:7
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 2:11
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.


CHIVUMBULUTSO 2:17
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’ ”


CHIVUMBULUTSO 2:29
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.


CHIVUMBULUTSO 3:6
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”


CHIVUMBULUTSO 3:13
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’ ”


CHIVUMBULUTSO 3:22
Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”


CHIVUMBULUTSO 4:2
Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo.


CHIVUMBULUTSO 14:13
Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.” “Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”


CHIVUMBULUTSO 17:3
Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.


CHIVUMBULUTSO 19:10
Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”


CHIVUMBULUTSO 21:10
Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 22:17
Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.


Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®