A A A A A

Sakani
MATEYU 1:23
“Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”


MATEYU 3:9
Ndipo musaganize ndi kunena mwa inu nokha kuti, ‘Tili nawo abambo athu Abrahamu.’ Ndinena kwa inu kuti Mulungu akhoza kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abrahamu.


MATEYU 3:16
Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati nkhunda natera pa Iye.


MATEYU 4:3
Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”


MATEYU 4:4
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”


MATEYU 4:5
Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu.


MATEYU 4:6
Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa: “ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe, ndipo adzakunyamula ndi manja awo kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”


MATEYU 4:7
Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”


MATEYU 4:10
Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”


MATEYU 5:8
Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.


MATEYU 5:9
Ndi odala amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.


MATEYU 5:34
Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu.


MATEYU 6:24
“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.


MATEYU 6:30
Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa!


MATEYU 8:29
Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”


MATEYU 9:3
Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.”


MATEYU 9:8
Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu.


MATEYU 12:4
Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha.


MATEYU 12:5
Kodi simunawerenge mʼmalamulo kuti pa Sabata ansembe mʼNyumba ya Mulungu amaphwanya lamulo la Sabata komabe sawayesa olakwa?


MATEYU 12:6
Ine ndikuwuzani kuti wamkulu kuposa Nyumba ya Mulunguyo ali pano.


MATEYU 12:28
Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.


MATEYU 14:33
Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”


MATEYU 15:3
Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu?


MATEYU 15:4
Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’


MATEYU 15:5
Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’


MATEYU 15:6
iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu.


MATEYU 15:31
Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.


MATEYU 16:16
Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”


MATEYU 16:23
Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”


MATEYU 17:24
Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”


MATEYU 19:4
Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’


MATEYU 19:6
Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.”


MATEYU 19:24
Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”


MATEYU 19:26
Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”


MATEYU 21:12
Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda.


MATEYU 21:14
Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa.


MATEYU 21:23
Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”


MATEYU 21:31
“Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?” Anamuyankha nati, “Woyambayo.” Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.”


MATEYU 21:43
“Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake.


MATEYU 22:16
Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?


MATEYU 22:21
Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.” Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”


MATEYU 22:29
Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.


MATEYU 22:31
Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,


MATEYU 22:32
‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”


MATEYU 22:37
Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.


MATEYU 23:5
“Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo.


MATEYU 23:14
Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera akazi amasiye chuma chawo, kwinaku nʼkumanamizira kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.


MATEYU 23:16
“Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’


MATEYU 23:21
Ndipo iye wolumbira potchula Nyumba ya Mulungu alumbira pa Nyumbayo ndi pa Iye amene amakhala mʼmenemo.


MATEYU 23:22
Ndipo iye wolumbira kutchula kumwamba alumbira kutchula mpando waufumu wa Mulungu ndi pa Iye wokhalapo.


MATEYU 23:35
Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu.


MATEYU 24:1
Yesu anatuluka mʼNyumba ya Mulungu ndipo akuchoka ophunzira ake anadza kwa Iye ndi kumuonetsa mamangidwe a Nyumbayo.


MATEYU 26:55
Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo, “Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire.


MATEYU 26:61
Ndipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ”


MATEYU 26:63
Koma Yesu anakhalabe chete. Mkulu wa ansembe anati kwa Iye, “Ndikulamulira Iwe ndi lumbiro pamaso pa Mulungu wa Moyo: utiwuze ife ngati ndiwe Khristu Mwana wa Mulungu.”


MATEYU 26:65
Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake.


MATEYU 27:5
Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira.


MATEYU 27:6
Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.”


MATEYU 27:40
Ndipo anati, “Iwe amene ungapasule Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanga masiku atatu, dzipulumutse wekha! Tsika pa mtandapo ngati ndiwe Mwana wa Mulungu!”


MATEYU 27:43
Amadalira Mulungu, mulekeni Mulunguyo amupulumutse tsopano ngati akumufuna pakuti anati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’ ”


MATEYU 27:46
Ndipo nthawi ili ngati 3 koloko, Yesu analira mofuwula nati, “Eloi, Eloi, lama sabakitani!” Kutanthauza kuti, “Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, mwandisiyiranji Ine?”


MATEYU 27:51
Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika.


MATEYU 27:54
Mkulu wa asilikali ndi amene ankalondera Yesu ataona chivomerezi ndi zonse zinachitika, anachita mantha, ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu!”


MARKO 1:1
Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu,


MARKO 1:14
Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati,


MARKO 1:15
“Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”


MARKO 1:24
“Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”


MARKO 2:7
“Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?”


MARKO 2:12
Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”


MARKO 2:26
Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.”


MARKO 3:11
Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!”


MARKO 3:35
Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”


MARKO 4:11
Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo:


MARKO 4:26
Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka.


MARKO 4:30
Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera?


MARKO 5:7
Iye anafuwula kwambiri nati, “Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!”


MARKO 7:8
Mwasiya malamulo a Mulungu ndipo mwagwiritsitsa miyambo ya anthu.”


MARKO 7:9
Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo!


MARKO 7:11
Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu),


MARKO 7:13
Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”


MARKO 8:33
Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”


MARKO 9:1
Ndipo anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ena amene ayimirira pano sadzafa asanaone ufumu wa Mulungu ukubwera mwa mphamvu.”


MARKO 9:47
Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena,


MARKO 10:6
Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’


MARKO 10:9
Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”


MARKO 10:14
Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa.


MARKO 10:15
Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.”


MARKO 10:18
Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha.


MARKO 10:23
Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!”


MARKO 10:25
Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.”


MARKO 10:27
Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”


MARKO 11:11
Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.


MARKO 11:15
Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda,


MARKO 11:16
ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu.


MARKO 11:22
Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.


MARKO 11:27
Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.


MARKO 12:14
Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?


MARKO 12:17
Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” Ndipo anazizwa naye.


MARKO 12:24
Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu?


MARKO 12:26
Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’


MARKO 12:27
Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”


MARKO 12:29
Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi!


MARKO 12:30
Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’


MARKO 12:32
Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha.


MARKO 12:34
Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.


MARKO 12:35
Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’


MARKO 12:41
Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri.


MARKO 13:1
Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”


MARKO 13:3
Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti,


MARKO 13:19
chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena.


MARKO 14:25
Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”


MARKO 14:49
Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.”


MARKO 14:58
“Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ”


MARKO 15:29
Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu,


MARKO 15:34
Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?”


MARKO 15:38
Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi.


MARKO 15:39
Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.”


MARKO 15:43
Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu.


MARKO 16:19
Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.


LUKA 1:6
Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse.


LUKA 1:8
Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu,


LUKA 1:16
Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo.


LUKA 1:19
Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu.


LUKA 1:21
Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu.


LUKA 1:26
Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya,


LUKA 1:30
Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu.


LUKA 1:32
Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide,


LUKA 1:35
Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu.


LUKA 1:37
Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”


LUKA 1:47
Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,


LUKA 1:64
Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu.


LUKA 1:68
“Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.


LUKA 1:78
chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,


LUKA 2:13
Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,


LUKA 2:14
“Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba, ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”


LUKA 2:20
Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.


LUKA 2:27
Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo,


LUKA 2:28
Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:


LUKA 2:37
ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera.


LUKA 2:38
Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.


LUKA 2:40
Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.


LUKA 2:46
Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso.


LUKA 2:52
Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.


LUKA 3:2
Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu.


LUKA 3:6
Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”


LUKA 3:8
Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana.


LUKA 3:38
mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.


LUKA 4:3
Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.”


LUKA 4:8
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”


LUKA 4:9
Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano.


LUKA 4:12
Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”


LUKA 4:34
“Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”


LUKA 4:41
Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.


LUKA 4:43
Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.”


LUKA 5:1
Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu.


LUKA 5:21
Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?”


LUKA 5:25
Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu.


LUKA 5:26
Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.”


LUKA 6:4
Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.”


LUKA 6:12
Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.


LUKA 6:20
Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.


LUKA 7:16
Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.”


LUKA 7:28
Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”


LUKA 7:29
Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane.


LUKA 7:30
Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.


LUKA 8:1
Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye,


LUKA 8:10
Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.”


LUKA 8:11
“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu.


LUKA 8:21
Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”


LUKA 8:28
Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!”


LUKA 8:39
“Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.


LUKA 9:2
Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala.


LUKA 9:11
Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.


LUKA 9:20
Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”


LUKA 9:27
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”


LUKA 9:43
Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu. Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake,


LUKA 9:60
Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”


LUKA 9:62
Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”


LUKA 10:9
Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’


LUKA 10:11
‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’


LUKA 10:27
Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”


LUKA 11:20
Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.


LUKA 11:28
Koma Yesu anayankha kuti, “ Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”


LUKA 11:42
“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.


LUKA 11:49
Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’


LUKA 12:6
Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu.


LUKA 12:8
“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu.


LUKA 12:9
Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu.


LUKA 12:20
“Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’


LUKA 12:21
“Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”


LUKA 12:24
Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame.


LUKA 12:28
Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa!


LUKA 13:13
Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.


LUKA 13:18
Kenaka Yesu anafunsa kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani?


LUKA 13:20
Iye anafunsanso kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani?


LUKA 13:28
“Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja.


LUKA 13:29
Anthu adzachokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kummwera, kudzakhala pa phwando mu ufumu wa Mulungu.


LUKA 14:14
Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”


LUKA 14:15
Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”


LUKA 15:10
Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”


LUKA 16:13
“Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”


LUKA 16:15
Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.


LUKA 16:16
“Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo.


LUKA 17:15
Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza.


LUKA 17:18
Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?”


LUKA 17:20
Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso,


LUKA 17:21
kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”


LUKA 18:2
Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu.


LUKA 18:4
“Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu,


LUKA 18:7
Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira?


LUKA 18:10
“Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho.


LUKA 18:11
Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu.


LUKA 18:13
“Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’


LUKA 18:14
“Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”


LUKA 18:16
Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere.


LUKA 18:17
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”


LUKA 18:19
Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha.


LUKA 18:24
Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!


LUKA 18:25
Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”


LUKA 18:27
Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”


LUKA 18:29
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu


LUKA 18:43
Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.


LUKA 19:11
Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo.


LUKA 19:37
Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.


LUKA 19:44
Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”


LUKA 19:45
Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda.


LUKA 19:47
Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe.


LUKA 20:1
Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.


LUKA 20:21
Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi.


LUKA 20:25
Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”


LUKA 20:36
Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.


LUKA 20:37
Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’


LUKA 20:38
Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”


LUKA 21:1
Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu.


LUKA 21:5
Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati,


LUKA 21:31
Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.


LUKA 21:37
Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse.


LUKA 21:38
Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.


LUKA 22:4
Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu.


LUKA 22:16
Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”


LUKA 22:18
Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”


LUKA 22:52
Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga?


LUKA 22:53
Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”


LUKA 22:69
Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”


LUKA 22:70
Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.”


LUKA 23:35
Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”


LUKA 23:40
Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi?


LUKA 23:45
pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati.


LUKA 23:47
Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.”


LUKA 23:51
Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu.


LUKA 24:19
Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?” Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.


LUKA 24:53
Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.


YOHANE 1:1
Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.


YOHANE 1:2
Mawuwa anali ndi Mulungu pachiyambi.


YOHANE 1:6
Kunabwera munthu amene anatumizidwa kuchokera kwa Mulungu; Iyeyo dzina lake linali Yohane.


YOHANE 1:12
Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;


YOHANE 1:13
ana wobadwa osati monga mwachilengedwe, kapena chisankho cha munthu, kapena chifuniro cha mwamuna koma wobadwa mwa Mulungu.


YOHANE 1:18
Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.


YOHANE 1:29
Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi!


YOHANE 1:34
Ine ndaona ndipo ndikuchitira umboni kuti uyu ndi Mwana wa Mulungu.”


YOHANE 1:36
Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”


YOHANE 1:49
Kenaka Natanieli ananena kuti, “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli.”


YOHANE 1:51
Ndipo Iye anapitirira kuti, “Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”


YOHANE 2:14
Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo.


YOHANE 2:19
Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”


YOHANE 2:21
Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.


YOHANE 3:2
Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.”


YOHANE 3:3
Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”


YOHANE 3:5
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:16
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.


YOHANE 3:17
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi.


YOHANE 3:18
Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.


YOHANE 3:21
Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”


YOHANE 3:33
Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona.


YOHANE 3:34
Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire.


YOHANE 3:36
Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”


YOHANE 4:10
Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”


YOHANE 4:24
Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”


YOHANE 5:14
Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.”


YOHANE 5:18
Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.


YOHANE 5:25
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.


YOHANE 5:30
Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.


YOHANE 5:42
koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu.


YOHANE 5:44
Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?


YOHANE 6:27
Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”


YOHANE 6:28
Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”


YOHANE 6:29
Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”


YOHANE 6:33
Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”


YOHANE 6:45
Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine.


YOHANE 6:46
Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate.


YOHANE 6:69
Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.”


YOHANE 7:14
Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa.


YOHANE 7:17
Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha.


YOHANE 7:28
Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa,


YOHANE 7:32
Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.


YOHANE 7:45
Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”


YOHANE 8:2
Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa.


YOHANE 8:20
Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.


YOHANE 8:40
Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi.


YOHANE 8:41
Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.” Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”


YOHANE 8:42
Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha.


YOHANE 8:47
Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”


YOHANE 8:54
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine.


YOHANE 8:59
Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.


YOHANE 9:3
Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu.


YOHANE 9:16
Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.” Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.


YOHANE 9:24
Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”


YOHANE 9:29
Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”


YOHANE 9:31
Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake.


YOHANE 9:33
Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”


YOHANE 10:22
Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira,


YOHANE 10:33
Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”


YOHANE 10:35
Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,


YOHANE 10:36
nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’


YOHANE 11:4
Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.”


YOHANE 11:22
Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.”


YOHANE 11:27
Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”


YOHANE 11:40
Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”


YOHANE 11:52
ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi.


YOHANE 11:56
Iwo anapitiriza kumufunafuna Yesu, ndipo pamene ankayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi ukuganiza chiyani? Kodi Iye sabwera konse kuphwando?”


YOHANE 12:43
pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.


YOHANE 13:3
Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo;


YOHANE 13:31
Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso.


YOHANE 13:32
Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.


YOHANE 14:1
“Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso.


YOHANE 16:2
Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu.


YOHANE 16:30
Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”


YOHANE 17:3
Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma.


YOHANE 18:20
Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri.


YOHANE 19:7
Ayuda anayimirira nati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo molingana ndi lamulolo, Iyeyu ayenera kuphedwa chifukwa akudzitcha kuti ndi Mwana wa Mulungu.”


YOHANE 20:17
Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”


YOHANE 20:28
Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”


YOHANE 20:31
Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.


YOHANE 21:19
Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”


MACHITIDWE A ATUMWI 1:3
Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:5
Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:11
Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 2:17
“ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:22
“Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:23
Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:24
Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:30
Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:32
Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:33
Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:36
“Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”


MACHITIDWE A ATUMWI 2:39
Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”


MACHITIDWE A ATUMWI 2:46
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:47
Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:1
Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:8
Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:9
Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 3:13
Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:15
Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:18
Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:19
Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,


MACHITIDWE A ATUMWI 3:21
Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:22
Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:25
Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’


MACHITIDWE A ATUMWI 3:26
Pamene Mulungu anaukitsa mtumiki wake, anamutuma Iye poyamba kwa inu kuti akudalitseni pobweza aliyense wa inu ku zoyipa zake.”


MACHITIDWE A ATUMWI 4:1
Pamene Petro ndi Yohane amayankhula ndi anthu, kunabwera ansembe, mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndiponso Asaduki.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:10
tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:19
Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:21
Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:24
Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:31
Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:4
Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 5:20
Mngeloyo anati, “Pitani, ku mabwalo a Nyumba ya Mulungu ndipo mukawuze anthu uthenga onse wamoyo watsopanowu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 5:21
Kutacha mmawa, atumwi analowa mʼbwalo la mʼNyumba ya Mulungu, monga anawuzidwa ndipo anayamba kuphunzitsa anthu. Mkulu wa ansembe pamodzi ndi omuthandiza ake amene anali naye anafika, anayitanitsa msonkhano wa Bwalo Lalikulu, ndilo bwalo la akulu onse a Israeli. Anatuma alonda kuti akatenge atumwi aja kundende.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:24
Mkulu wa alonda a Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe atamva zimenezi anathedwa nzeru, osadziwa kuti zimenezi zidzatha bwanji.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:25
Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 5:29
Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!


MACHITIDWE A ATUMWI 5:30
Mulungu wa makolo athu anamuukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pa mtengo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:31
Mulungu anamukweza Iye ku dzanja lake lamanja kukhala Mfumu ndi Mpulumutsi kuti Iye apatse Aisraeli mtima wolapa ndi chikhululukiro cha machimo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:32
Ife ndife mboni za zimenezi, ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu anapereka kwa iwo akumvera Iye.”


MACHITIDWE A ATUMWI 5:39
Koma ngati ndi zochokera kwa Mulungu inu simudzatha kuwaletsa anthu awa: inu mwina muzapezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 5:42
Ndipo tsiku ndi tsiku, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira mʼNyumba ya Mulungu komanso nyumba ndi nyumba, Uthenga Wabwino wa kuti Yesu ndi Khristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:2
Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:7
Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:8
Stefano, munthu wodzazidwa ndi chisomo cha Mulungu ndi mphamvu anachita zodabwitsa ndiponso zizindikiro zazikulu pakati pa anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:11
Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 7:2
Stefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:3
Mulungu anati, ‘Tuluka mʼdziko lako, siya abale ako, ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.’


MACHITIDWE A ATUMWI 7:4
“Ndipo iye anatulukadi mʼdziko la Akaldeya ndi kukakhala ku Harani. Atamwalira abambo ake, Mulungu anamuchotsa kumeneko ndi kumubweretsa mʼdziko lino limene inu mukukhalamo tsopano.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:5
Mulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:6
Mulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’


MACHITIDWE A ATUMWI 7:7
Mulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’


MACHITIDWE A ATUMWI 7:8
Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:9
“Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye


MACHITIDWE A ATUMWI 7:10
ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:17
“Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:25
Mose anaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu anamuyika kuti awapulumutse koma iwo sanazindikire.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:32
‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.’ Mose ananjenjemera chifukwa cha mantha ndipo sanalimbe mtima kuyangʼananso.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:35
“Uyu ndi Mose yemwe uja amene Aisraeli anamukana ndi kunena kuti, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza?’ Iyeyo anatumidwa ndi Mulungu mwini kuti akakhale wowalamulira ndiponso mpulumutsi, mothandizidwa ndi mngelo amene anamuonekera pa chitsamba.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:37
“Uyu ndi Mose uja amene anati kwa Aisraeli, ‘Mulungu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine.’


MACHITIDWE A ATUMWI 7:42
Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti, “ ‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’


MACHITIDWE A ATUMWI 7:43
Ayi, inu mwanyamula tenti ya Moloki ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwapembedza. Chifukwa chake, Ine ndidzakutumizani kutali, kupitirira dziko la Babuloni.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:44
“Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:45
Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:46
amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:55
Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:56
Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 8:2
Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:10
ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 8:12
Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:14
Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:20
Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama!


MACHITIDWE A ATUMWI 8:21
Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:27
Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 8:37
Filipo anati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa.” Ndunayo inayankha kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 9:20
Posakhalitsa anayamba kulalikira mʼsunagoge kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:2
Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:3
Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”


MACHITIDWE A ATUMWI 10:4
Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?” Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:7
Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:15
Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”


MACHITIDWE A ATUMWI 10:22
Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.”


MACHITIDWE A ATUMWI 10:28
Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:31
Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:33
Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”


MACHITIDWE A ATUMWI 10:34
Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:36
Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:38
kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:40
koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:41
Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:42
Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:46
Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati,


MACHITIDWE A ATUMWI 11:1
Atumwi ndi abale a ku Yudeya konse anamva kuti anthu a mitundu ina analandiranso Mawu a Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:9
“Mawu ochokera kumwamba ananenanso kachiwiri kuti, ‘Chimene Mulungu wachiyeretsa usanene kuti ndi chodetsedwa.’


MACHITIDWE A ATUMWI 11:17
Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?”


MACHITIDWE A ATUMWI 11:18
Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”


MACHITIDWE A ATUMWI 11:23
Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye.


MACHITIDWE A ATUMWI 12:5
Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 12:22
Anthuwo anafuwula nati, “Amenewa ndi mawu a mulungu osati a munthu ayi.”


MACHITIDWE A ATUMWI 12:23
Nthawi yomweyo mngelo wa Mulungu anamukantha chifukwa sanapereke ulemu kwa Mulungu ndipo anadyedwa ndi mphutsi nafa.


MACHITIDWE A ATUMWI 12:24
Koma Mawu a Mulungu anapitirirabe kufalikirafalikira.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:5
Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:7
Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:16
Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani!


MACHITIDWE A ATUMWI 13:17
Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:19
Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:20
Izi zonse zinatenga zaka 450. “Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:22
Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’


MACHITIDWE A ATUMWI 13:23
“Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:26
“Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:30
Koma Mulungu anamuukitsa,


MACHITIDWE A ATUMWI 13:32
“Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:34
Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa: “ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’


MACHITIDWE A ATUMWI 13:36
“Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:37
Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:43
Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:46
Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:50
Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:15
“Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:22
Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 14:26
Ku Ataliyako, anakwera sitima ya pamadzi kubwerera ku Antiokeya kumene anayitanidwa mwachisomo cha Mulungu kuti agwire ntchito imene tsopano anali atayitsiriza.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:27
Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:4
Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:7
Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:8
Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:10
Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza?


MACHITIDWE A ATUMWI 15:12
Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:14
Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:19
“Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:6
Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:10
Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:14
Mmodzi wa amayi amene amamvetserawo ndi Lidiya amene amagulitsa nsalu zofiira, wochokera ku mzinda wa Tiyatira, ndipo amapembedza Mulungu. Ambuye anatsekula mtima wake kuti amve mawu a Paulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:17
Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, “Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso.”


MACHITIDWE A ATUMWI 16:25
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:34
Woyangʼanira ndendeyo anapita nawo ku nyumba yake, nakawapatsa chakudya, ndipo banja lonse linadzazidwa ndi chimwemwe chifukwa anakhulupirira Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:2
Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu,


MACHITIDWE A ATUMWI 17:4
Ena mwa Ayuda anakopeka mtima ndipo anatsatira Paulo ndi Sila, monganso linachitira gulu lalikulu la Agriki woopa Mulungu, pamodzi ndi amayi odziwika ambiri.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:13
Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulalikira Mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko, ndi kuwutsa mitima ya anthu nayambitsa chisokonezo.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:17
Tsono anakambirana ndi Ayuda ndi Agriki amene amaopa Mulungu mʼsunagoge, komanso anthu amene amapezeka pa msika tsiku ndi tsiku ndi ena amene amakumana nawo.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:23
Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:24
“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:27
Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:29
“Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:30
Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:7
Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:11
Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:13
Iwo anati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu.”


MACHITIDWE A ATUMWI 18:21
Koma pamene amachoka anawalonjeza kuti, “Ndidzabweranso Mulungu akalola.” Ndipo anakwera sitima ya pamadzi kuchoka ku Efeso.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:26
Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:8
Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:11
Mulungu anachita zodabwitsa zapadera kudzera mwa Paulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:27
Choopsa ndi chakuti sikungowonongeka kwa ntchito yathu yokha ayi, komanso kuti nyumba ya mulungu wamkulu wamkazi Atemi idzanyozedwa ndipo mulungu wamkazi weniweniyo amene amapembedzedwa ku Asiya konse ndi dziko lapansi, ukulu wake udzawonongekanso.”


MACHITIDWE A ATUMWI 19:35
Mlembi wa mzindawo anakhazikitsa bata gulu la anthuwo ndipo anati, “Anthu a ku Efeso, kodi ndani pa dziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayangʼanira nyumba ya mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba?


MACHITIDWE A ATUMWI 19:37
Inu mwabweretsa anthu awa pano, ngakhale kuti iwo sanabe mʼnyumba zathu zamapemphero kapena kunenera chipongwe mulungu wathu wamkazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:21
Ine ndinawuza Ayuda komanso Agriki kuti ayenera kutembenukira kwa Mulungu polapa ndikuti akhulupirire Ambuye athu Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:24
Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:25
“Tsopano ndikudziwa kuti inu nonse amene ndinakuyenderani ndi kumakulalikirani ufumu wa Mulungu simudzaonanso nkhope yanga.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:27
Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:28
Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:32
“Tsopano ine ndikukuperekani kwa Mulungu ndiponso kwa mawu a chisomo chake, amene ali ndi mphamvu zokulitsa inu ndi kukupatsani chuma pakati pa onse amene anayeretsedwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:19
Paulo anawalonjera ndi kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:20
Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:23
tsono iwe chita zimene ife tikuwuze. Tili nawo amuna anayi pano amene anachita lumbiro kwa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:26
Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:27
Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo,


MACHITIDWE A ATUMWI 21:29
Iwo ananena izi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mu mzindamo ndipo iwo ankaganiza kuti Paulo anamulowetsa mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 22:3
“Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero.


MACHITIDWE A ATUMWI 22:12
“Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu.


MACHITIDWE A ATUMWI 22:14
“Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake.


MACHITIDWE A ATUMWI 22:17
“Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:1
Paulo anayangʼanitsitsa anthu a Bwalo Lalikulu nati, “Abale anga, ndakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu mpaka lero lino.”


MACHITIDWE A ATUMWI 23:3
Pamenepo Paulo anamuwuza kuti, “Mulungu adzakukantha, iwe munthu wachiphamaso! Wakhala pamenepo kuti undiweruze ine monga mwalamulo, koma iweyo ukuphwanya lamulolo polamulira kuti andimenye!”


MACHITIDWE A ATUMWI 23:4
Anthu amene anayimirira pafupi ndi Paulo anati, “Bwanji ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?”


MACHITIDWE A ATUMWI 24:6
Anayesera ngakhale kudetsa Nyumba ya Mulungu wathu. Ndiye ife tinamugwira.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:12
Amene akundiyimba mlanduwa sanandipeze mʼNyumba ya Mulungu ndi kutsutsana ndi wina aliyense kapena kuyambitsa chisokonezo mʼsunagoge kapena pena paliponse mu mzindamo.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:14
Komatu ine ndikuvomera kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu, monga wotsatira wa Njirayo, imene iwo akuyitchula mpatuko. Ine ndimakhulupirira chilichonse chimene chimagwirizana ndi malamulo ndiponso zimene zinalembedwa ndi Aneneri.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:15
Ine ndili nacho chiyembekezo chomwecho chimene iwo ali nacho mwa Mulungu, kuti kudzakhala kuuka kwa akufa kwa olungama ndiponso kwa ochimwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:16
Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:18
Pamene ndinkachita zimenezi, iwo anandipeza mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wodziyeretsa. Panalibe gulu la anthu kapena kuti ndimachita za chisokonezo chilichonse.


MACHITIDWE A ATUMWI 25:8
Kenaka Paulo ananena mawu ake odziteteza kuti, “Ine sindinalakwirepo lamulo la Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu kapenanso Kaisara.”


MACHITIDWE A ATUMWI 26:6
Ndipo tsopano ndikuyimbidwa mlandu lero chifukwa cha chiyembekezo changa pa zimene Mulungu analonjeza makolo athu.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:7
Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:8
Nʼchifukwa chiyani ena a inu mukuganiza kuti nʼkosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?


MACHITIDWE A ATUMWI 26:11
Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:18
kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:20
Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko, a ku Yerusalemu, a ku Yudeya konse ndi kwa anthu a mitundu inanso, ndinalalikira kuti akuyenera kulapa ndi kutembenukira kwa Mulungu ndikuti aonetse kulapa kwawo mwa ntchito zawo.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:21
Ichi nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:22
Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero lino. Ine ndayima pano kuti ndichitire umboni kwa anthu onse otchuka ndi anthu wamba. Ine sindikunena zina zowonjezera koma zimene Aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:29
Paulo anayankha kuti, “Ngakhale kanthawi kochepa kapena nthawi yayitali, ine ndikupempha kwa Mulungu kuti osati inu nokha koma aliyense amene akundimva lero lino akhale monga ine, kupatulapo maunyolo okhawa.”


MACHITIDWE A ATUMWI 27:23
Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine,


MACHITIDWE A ATUMWI 27:24
ndipo iyeyu anati, ‘Usachite mantha, Paulo. Ukuyenera kukayima pamaso pa Kaisara; ndipo Mulungu mwa kukoma mtima kwake wakupatsa miyoyo ya anthu onse amene ukuyenda nawo.’


MACHITIDWE A ATUMWI 27:25
Tsono limbani mtima, anthu inu, pakuti ine ndili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti zichitika monga momwe wandiwuzira.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:35
Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:6
Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:15
Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:23
Iwo anakonza tsiku lina loti akumane ndi Paulo, ndipo anabwera anthu ambiri ku nyumba kumene amakhala. Kuyambira mmawa mpaka madzulo, Paulo anawafotokozera ndi kuwawuza za ufumu wa Mulungu ndipo anayesa kuwakopa kuti akhulupirire Yesu kuchokera mʼMalamulo a Mose ndiponso mʼmabuku a Aneneri.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:28
“Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.”


MACHITIDWE A ATUMWI 28:31
Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.


AROMA 1:1
Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu


AROMA 1:4
Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu,


AROMA 1:7
Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima. Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.


AROMA 1:8
Poyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akukamba za chikhulupiriro chanu.


AROMA 1:9
Mulungu amene ndimamutumikira ndi mtima wanga onse polalikira Uthenga Wabwino wa Mwana wake, ndi mboni yanga kuti ndimakupemphererani nthawi zonse.


AROMA 1:10
Mʼmapemphero anga, nthawi zonse, ndimapemphera kuti ngati nʼkotheka mwachifuniro cha Mulungu, njira inditsekukire kuti ndibwere kwanuko.


AROMA 1:16
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene.


AROMA 1:17
Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”


AROMA 1:18
Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa.


AROMA 1:19
Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo.


AROMA 1:20
Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.


AROMA 1:21
Ngakhale iwo anadziwa Mulungu, sanamulemekeze ngati Mulungu kapena kumuthokoza, koma maganizo awo anasanduka wopanda pake ndipo mʼmitima yawo yopusa munadzaza mdima.


AROMA 1:23
Iwo anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu wosafa ndi mafano opangidwa ndi manja wooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame, ndi nyama kapena zokwawa.


AROMA 1:24
Nʼchifukwa chake Mulungu anawasiya kuti azingochita zilakolako zochititsa manyazi zauchimo zomwe mitima yawo inkafuna. Zotsatira zake anachita za chiwerewere wina ndi mnzake kunyazitsa matupi awo.


AROMA 1:25
Iwo anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza ndipo anapembedza ndi kutumikira zinthu zolengedwa mʼmalo mwa Mlengi amene ali woyenera kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni.


AROMA 1:26
Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo.


AROMA 1:28
Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo.


AROMA 1:30
osinjirira, odana ndi Mulungu, achipongwe, odzitama ndi odzitukumula. Iwo amapeza njira zochitira zoyipa. Samvera makolo awo,


AROMA 1:32
Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.


AROMA 2:2
Tsopano ife tikudziwa kuti chiweruzo cha Mulungu, chotsutsa amene amachita zinthu zotere, nʼchokhazikika pa choonadi.


AROMA 2:3
Kodi ukuganiza kuti udzathawa chiweruzo cha Mulungu iwe munthu wamba, pamene uweruza ena, iwe ndi kumachitanso zomwezo?


AROMA 2:4
Kodi kapena ukupeputsa kukoma mtima kwa Mulungu, kuleza mtima kwake ndi kupirira kwake? Kodi sukuzindikira kuti kukoma mtima kwakeko, nʼkofuna kuti iweyo ulape machimo ako?


AROMA 2:5
Koma pakuti ndiwe wosamvera ndi wa mtima wosafuna kulapa, ukudzisungira chilango pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu, pamene chiweruzo cholungama cha Mulungu chidzaonetsedwa.


AROMA 2:6
Mulungu adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake.


AROMA 2:8
Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa.


AROMA 2:11
Pajatu Mulungu alibe tsankho.


AROMA 2:13
Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama.


AROMA 2:16
Izi zidzachitika pa tsiku limene Mulungu adzaweruza zinsinsi za anthu kudzera mwa Yesu Khristu, monga momwe Uthenga wanga Wabwino unenera.


AROMA 2:17
Koma iweyo, amene umadzitcha kuti ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira ubale wako ndi Mulungu,


AROMA 2:23
Kodi iwe amene umadzitama ndi Malamulo, umamuchititsa manyazi Mulungu posamvera Malamulowo?


AROMA 2:24
Monga kwalembedwa, “Dzina la Mulungu likuchitidwa chipongwe pakati pa a mitundu ina chifukwa cha inu.”


AROMA 2:29
Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.


AROMA 3:2
Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge.


AROMA 3:3
Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu?


AROMA 3:4
Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti, “Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi kupambana pamene muweruza.”


AROMA 3:5
Koma ngati kuyipa mtima kwathu kuonetsa poyera kuti Mulungu ndi wolungama, ife tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wosalungama pamene aonetsa mkwiyo wake pa ife? (Ine ndikuyankhula monga mmene anthu ena amayankhulira).


AROMA 3:6
Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ngati zikanakhala zotero, kodi Mulungu akanaweruza bwanji dziko lapansi?


AROMA 3:7
Wina atanena kuti, “Ngati kunama kwanga kukuonetsa koposa kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemerero wake, nanga nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa kuti ndine wochimwa?”


AROMA 3:11
Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira, palibe amene amafunafuna Mulungu.


AROMA 3:18
“Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.”


AROMA 3:19
Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu.


AROMA 3:21
Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni.


AROMA 3:22
Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina,


AROMA 3:23
pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu


AROMA 3:25
Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale.


AROMA 3:29
Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso,


AROMA 3:30
popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho.


AROMA 4:2
Kunena zoona, Abrahamu akanalungamitsidwa ndi ntchito zake, akanakhala nako kanthu kodzitamandira, koma osati pamaso pa Mulungu.


AROMA 4:3
Kodi Malemba akuti chiyani? “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.”


AROMA 4:5
Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo.


AROMA 4:6
Davide ponena zomwezi pamene anayankhula za kudala kwa munthu amene Mulungu amulungamitsa osati chifukwa cha ntchito zake akuti,


AROMA 4:17
Monga kwalembedwa kuti, “Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri.” Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.


AROMA 4:20
Komabe iye sanagwedezeke chifukwa chosakhulupirira pa zokhudzana ndi lonjezo la Mulungu. Iye analimbikitsidwa mʼchikhulupiriro chake ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.


AROMA 4:21
Anatsimikiza mu mtima mwake kuti Mulungu anali ndi mphamvu yochita chomwe analonjeza.


AROMA 4:24
komanso chifukwa ife amene Mulungu adzatiyesa olungama, ife amene tikhulupirira mwa Iye amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu Ambuye athu.


AROMA 5:1
Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.


AROMA 5:2
Iyeyo ndiye amene anatsekulira njira mwachikhulupiriro yolowera mʼchisomo mʼmene takhazikikamo. Ndipo tikukondwerera chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.


AROMA 5:5
Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.


AROMA 5:8
Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.


AROMA 5:9
Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu.


AROMA 5:10
Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye?


AROMA 5:11
Sikuti izi zili chomwechi chabe, koma timakondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Kudzera mwa Iye, ife tsopano tayanjanitsidwa ndi Mulungu.


AROMA 5:15
Koma sitingafananitse mphatso yaulereyo ndi kuchimwa kwa anthu. Pakuti ngati anthu ambiri anafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga chisomo cha Mulungu ndi mphatso zomwe zinabwera ndi chisomo cha munthu mmodzi, Yesu Khristu, ndi kusefukira kwa ambiri!


AROMA 5:16
Ndiponso, mphatso ya Mulungu sifanana ndi zotsatira za kuchimwa kwa munthu mmodzi. Chiweruzo chinatsatira tchimo la munthu mmodzi ndi kubweretsa kutsutsidwa koma mphatso inatsatira zolakwa zambiri ndi kubweretsa kulungamitsidwa.


AROMA 5:20
Malamulo a Mulungu anaperekedwa ndi cholinga chakuti anthu onse azindikire kuchuluka kwa machimo awo. Koma pamene machimo anachuluka, chisomo chinachuluka koposa.


AROMA 6:10
Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.


AROMA 6:11
Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.


AROMA 6:13
Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.


AROMA 6:17
Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira.


AROMA 6:22
Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.


AROMA 6:23
Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.


AROMA 7:4
Chimodzimodzi inunso, abale anga, munafa ku Malamulo kudzera mʼthupi la Khristu, kuti mukwatiwe ndi wina, ndi Iye amene anauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu chipatso.


AROMA 7:6
Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa.


AROMA 7:22
Mtima wanga umakondwera ndi lamulo la Mulungu.


AROMA 7:25
Atamandike Mulungu, amene amandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu! Kotero tsono, ineyo ndi mtima wanga ndimatumikira lamulo la Mulungu, koma ndi thupi langa ndimatumikira lamulo la uchimo.


AROMA 8:3
Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu,


AROMA 8:7
Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero.


AROMA 8:8
Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.


AROMA 8:9
Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu.


AROMA 8:11
Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.


AROMA 8:14
Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.


AROMA 8:16
Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.


AROMA 8:17
Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.


AROMA 8:19
Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu.


AROMA 8:21
chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.


AROMA 8:27
Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.


AROMA 8:28
Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.


AROMA 8:29
Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri.


AROMA 8:31
Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?


AROMA 8:33
Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa.


AROMA 8:34
Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.


AROMA 8:39
ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.


AROMA 9:4
anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake.


AROMA 9:5
Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.


AROMA 9:6
Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli.


AROMA 9:8
Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu.


AROMA 9:9
Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”


AROMA 9:11
Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire,


AROMA 9:14
Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe!


AROMA 9:15
Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti, “Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo, ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”


AROMA 9:16
Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu.


AROMA 9:17
Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.”


AROMA 9:18
Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.


AROMA 9:19
Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?”


AROMA 9:20
Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ”


AROMA 9:22
Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko.


AROMA 9:25
Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”


AROMA 9:26
ndipo, “Pamalo omwewo pamene ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”


AROMA 10:1
Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.


AROMA 10:2
Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.


AROMA 10:3
Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu.


AROMA 10:4
Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.


AROMA 10:9
kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.


AROMA 11:1
Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini.


AROMA 11:2
Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati,


AROMA 11:4
Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.”


AROMA 11:8
monga kwalembedwa kuti, “Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu, maso osatha kupenya; makutu osatha kumva mpaka lero lino.”


AROMA 11:15
Pakuti ngati kukanidwa kwawo kunayanjanitsa anthu a dziko lapansi ndi Mulungu, nanga kudzatani, Iye akadzawalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka.


Rómaiakhoz 11:21
Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachibadwidwe, Iye sadzakulekererani inunso.


Rómaiakhoz 11:22
Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso.


Rómaiakhoz 11:23
Ngati iwo asiya kukhala osakhulupirira, adzalumikizidwanso pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso.


Rómaiakhoz 11:24
Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi?


Rómaiakhoz 11:28
Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja.


Rómaiakhoz 11:29
Pakuti Mulungu akayitana munthu ndi kumupatsa mphatso sangasinthenso.


Rómaiakhoz 11:30
Monga mmene inu munalili, osamvera Mulungu pa nthawi ina, tsopano mwalandira chifundo chifukwa cha kusamvera kwawo.


Rómaiakhoz 11:31
Chonchonso iwo akhala osamvera tsopano kuti iwonso alandire chifundo chifukwa cha chifundo cha Mulungu kwa inu.


Rómaiakhoz 11:32
Pakuti Mulungu anasandutsa anthu onse a mʼndende ya kusamvera kuti Iye akaonetse chifundo kwa onse.


Rómaiakhoz 11:33
Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri! Ndani angazindikire maweruzidwe ake, ndipo njira zake angazitulukire ndani?


Rómaiakhoz 11:35
“Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezere iye?”


Rómaiakhoz 12:1
Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.


Rómaiakhoz 12:2
Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.


Rómaiakhoz 12:3
Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.


Rómaiakhoz 12:13
Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.


Rómaiakhoz 12:19
Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye.


Rómaiakhoz 13:1
Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu.


Rómaiakhoz 13:2
Kotero kuti, iwo amene awukira ulamuliro atsutsana ndi chimene Mulungu anakhazikitsa. Ndipo amene atero adzibweretsera okha chilango.


Rómaiakhoz 13:4
Pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokuchitirani zabwino. Koma ngati muchita zoyipa muchite mantha, pakuti iye ali ndi mphamvu zolangira. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wobweretsa mkwiyo ndi kulanga onse ochita zoyipa.


Rómaiakhoz 13:6
Ichi nʼchifukwa chakenso inu mumapereka msonkho. Pakuti olamulira ndi atumiki a Mulungu amene amapereka nthawi yawo yonse kulamulira.


Rómaiakhoz 14:3
Munthu amene amadya chilichonse sayenera kunyoza amene satero, ndipo munthu amene samadya chilichonse asaweruze munthu amene amatero, pakuti Mulungu anamulandira.


Rómaiakhoz 14:6
Iye amene amaganiza kuti tsiku limodzi ndi lopambana, amatero kwa Ambuye. Iye amene amadya nyama, amadya mwa Ambuye pakuti amayamika Mulungu. Ndipo iye amene sadya, amatero kwa Ambuye ndi kuyamika Mulungu.


Rómaiakhoz 14:10
Tsono nʼchifukwa chiyani iwe ukuweruza mʼbale wako? Kapena nʼchifukwa chiyani ukumunyoza mʼbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Mulungu.


Rómaiakhoz 14:11
Kwalembedwa, akutero Ambuye, “Pamene Ine ndili ndi moyo, aliyense adzandigwadira ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.”


Rómaiakhoz 14:12
Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.


Rómaiakhoz 14:17
Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Rómaiakhoz 14:18
Nʼchifukwa chake aliyense amene atumikira Khristu mʼnjira iyi akondweretsa Mulungu ndi kuvomerezedwa ndi anthu.


Rómaiakhoz 14:20
Musawononge ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Chakudya chonse ndi choyera, koma munthu amalakwa ngati adya chilichonse chimene chimakhumudwitsa wina.


Rómaiakhoz 14:22
Tsono zimene ukukhulupirira pa zinthu izi zikhale pakati pa iwe ndi Mulungu. Wodala munthu amene sadzitsutsa yekha pa zimene amazivomereza.


Rómaiakhoz 15:5
Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni maganizo amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu,


Rómaiakhoz 15:6
kotero kuti ndi mtima umodzi ndi movomerezana mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.


Rómaiakhoz 15:7
Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke.


Rómaiakhoz 15:8
Chifukwa kunena zoona, Khristu wasanduka mtumiki wa Ayuda, kuonetsa kuti Mulungu ndi wokhulupirika pa malonjezo amene anachita kwa makolo awo


Rómaiakhoz 15:9
kuti a mitundu ina atamande Mulungu chifukwa cha chifundo chake. Monga kwalembedwa kuti, “Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa a mitundu; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”


Rómaiakhoz 15:13
Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.


Rómaiakhoz 15:15
Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine


Rómaiakhoz 15:16
kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.


Rómaiakhoz 15:17
Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga.


Rómaiakhoz 15:18
Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita


Rómaiakhoz 15:30
Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu.


Rómaiakhoz 15:32
Kuti mwachifuniro cha Mulungu ndibwere kwa inu ndi chimwemwe kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu.


Rómaiakhoz 15:33
Mulungu wamtendere akhale ndi inu nonse. Ameni.


Rómaiakhoz 16:20
Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu. Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.


Rómaiakhoz 16:26
koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye,


Rómaiakhoz 16:27
kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.


2 AKORINTO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo, Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse.


2 AKORINTO 1:2
Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 AKORINTO 1:3
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse.


2 AKORINTO 1:4
Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.


2 AKORINTO 1:9
Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa.


2 AKORINTO 1:10
Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe.


2 AKORINTO 1:12
Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu.


2 AKORINTO 1:18
Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.”


2 AKORINTO 1:19
Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.”


2 AKORINTO 1:20
Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu.


2 AKORINTO 1:21
Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife,


2 AKORINTO 1:23
Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni.


2 AKORINTO 2:14
Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.


2 AKORINTO 2:15
Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka.


2 AKORINTO 2:17
Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.


2 AKORINTO 3:3
Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.


2 AKORINTO 3:4
Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu.


2 AKORINTO 3:5
Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu.


2 AKORINTO 4:1
Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima.


2 AKORINTO 4:2
Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake.


2 AKORINTO 4:4
Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu.


2 AKORINTO 4:6
Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.


2 AKORINTO 4:7
Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.


2 AKORINTO 4:15
Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.


2 AKORINTO 5:1
Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu.


2 AKORINTO 5:5
Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.


2 AKORINTO 5:11
Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu.


2 AKORINTO 5:13
Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike.


2 AKORINTO 5:18
Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso.


2 AKORINTO 5:19
Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso.


2 AKORINTO 5:20
Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.


2 AKORINTO 5:21
Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.


2 AKORINTO 6:1
Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe.


2 AKORINTO 6:4
Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa.


2 AKORINTO 6:7
ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo.


2 AKORINTO 6:8
Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza.


2 AKORINTO 6:16
Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti, “Ndidzakhala mwa iwo ndipo ndidzayendayenda pakati pawo, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo adzakhala anthu anga.”


2 AKORINTO 7:1
Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.


2 AKORINTO 7:6
Koma Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza mtima ndi kufika kwa Tito,


2 Korintusi 7:9
Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse.


2 Korintusi 7:10
Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa.


2 Korintusi 7:11
Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa.


2 Korintusi 7:12
Choncho ngakhale ndinakulemberani kalata ija, sindinayilembe ndi chifukwa cha amene analakwayo kapena wolakwiridwa, koma ndinayilemba kuti inuyo muone kudzipereka kwanu kwa ife pamaso a Mulungu.


2 Korintusi 8:1
Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya.


2 Korintusi 8:5
Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu.


2 Korintusi 8:16
Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu.


2 Korintusi 9:1
Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu.


2 Korintusi 9:7
Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.


2 Korintusi 9:8
Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino.


2 Korintusi 9:10
Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu.


2 Korintusi 9:11
Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.


2 Korintusi 9:12
Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu.


2 Korintusi 9:13
Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense.


2 Korintusi 9:15
Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!


2 Korintusi 10:4
Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga.


2 Korintusi 10:5
Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.


2 Korintusi 10:13
Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu.


2 Korintusi 11:2
Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro.


2 Korintusi 11:7
Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?


2 Korintusi 11:11
Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!


2 Korintusi 11:31
Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama.


2 Korintusi 12:2
Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu.


2 Korintusi 12:3
Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu.


2 Korintusi 12:19
Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani.


2 Korintusi 12:21
Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.


2 Korintusi 13:4
Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.


2 Korintusi 13:7
Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera.


2 Korintusi 13:11
Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.


2 Korintusi 13:13
Anthu onse a Mulungu akupereka moni.


2 Korintusi 13:14
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


AEFESO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu. Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:


AEFESO 1:2
Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.


AEFESO 1:3
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.


AEFESO 1:4
Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,


AEFESO 1:7
Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu


AEFESO 1:14
Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.


AEFESO 1:16
ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga.


AEFESO 1:17
Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni.


AEFESO 1:20
imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba.


AEFESO 1:22
Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo,


AEFESO 2:4
Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo,


AEFESO 2:6
Ndipo Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Khristu ndi kutikhazika pamodzi ndi Iye mmwamba mwa Khristu Yesu,


AEFESO 2:8
Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu,


AEFESO 2:10
Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.


AEFESO 2:12
Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi.


AEFESO 2:16
ndi kuyanjanitsa onse awiriwa mʼthupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo.


AEFESO 2:19
Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu.


AEFESO 2:22
Ndipo mwa Iye, inunso mukamangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake.


AEFESO 3:2
Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu,


AEFESO 3:5
chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri.


AEFESO 3:7
Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu.


AEFESO 3:8
Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu.


AEFESO 3:9
Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse.


AEFESO 3:10
Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu.


AEFESO 3:11
Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu.


AEFESO 3:12
Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima.


AEFESO 3:19
Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.


AEFESO 4:6
Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse.


AEFESO 4:13
Izi zidzatifikitsa tonse ku umodzi wachikhulupiriro, kumudziwa Mwana wa Mulungu, kukhwima msinkhu ndi kufika pa muyeso wangwiro weniweni wopezeka mwa Khristu.


AEFESO 4:18
Maganizo awo ndi odetsedwa, ndi osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo chifukwa cha kuwuma mtima kwawo.


AEFESO 4:24
ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.


AEFESO 4:30
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.


AEFESO 4:32
Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.


AEFESO 5:1
Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu.


AEFESO 5:2
Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.


AEFESO 5:3
Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.


AEFESO 5:5
Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.


AEFESO 5:6
Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.


AEFESO 5:19
Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu.


AEFESO 5:20
Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.


AEFESO 6:6
Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu.


AEFESO 6:11
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.


AEFESO 6:13
Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.


AEFESO 6:17
Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.


AEFESO 6:23
Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse.


AFILIPI 1:2
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale kwa inu.


AFILIPI 1:3
Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu.


AFILIPI 1:7
Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu.


AFILIPI 1:8
Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu.


AFILIPI 1:11
Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.


AFILIPI 1:14
Moti chifukwa cha maunyolo angawa, abale ambiri alimbikitsidwa kuyankhula Mawu a Mulungu molimbika ndi mopanda mantha.


AFILIPI 1:28
osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu.


AFILIPI 2:6
Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.


AFILIPI 2:9
Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse


AFILIPI 2:11
ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.


AFILIPI 2:13
pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.


AFILIPI 2:15
kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba


AFILIPI 2:27
Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke.


AFILIPI 3:3
Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi


AFILIPI 3:9
ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.


AFILIPI 3:14
Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 3:15
Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani.


AFILIPI 3:19
Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi.


AFILIPI 4:6
Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.


AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 4:9
Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.


AFILIPI 4:18
Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu.


AFILIPI 4:19
Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 4:20
Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.


1 ATESALONIKA 1:1
Paulo, Silivano ndi Timoteyo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. Chisomo ndi mtendere kwa inu.


1 ATESALONIKA 1:2
Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu.


1 ATESALONIKA 1:3
Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.


1 ATESALONIKA 1:4
Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani,


1 ATESALONIKA 1:8
Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu,


1 ATESALONIKA 1:9
pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona.


1 ATESALONIKA 1:10
Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.


1 ATESALONIKA 2:2
Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe.


1 ATESALONIKA 2:4
Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu.


1 ATESALONIKA 2:5
Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu.


1 ATESALONIKA 2:8
moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu.


1 ATESALONIKA 2:9
Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.


1 ATESALONIKA 2:10
Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira.


1 ATESALONIKA 2:12
kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.


1 ATESALONIKA 2:13
Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.


1 ATESALONIKA 2:14
Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda,


1 ATESALONIKA 2:15
amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse


1 ATESALONIKA 2:16
ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano.


1 ATESALONIKA 3:2
Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu,


1 ATESALONIKA 3:9
Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu?


1 ATESALONIKA 3:11
Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko.


1 ATESALONIKA 3:13
Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.


1 ATESALONIKA 4:1
Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale.


1 ATESALONIKA 4:3
Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama;


1 ATESALONIKA 4:5
osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu.


1 ATESALONIKA 4:7
Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.


1 ATESALONIKA 4:8
Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.


1 ATESALONIKA 4:9
Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake.


1 ATESALONIKA 4:10
Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.


1 ATESALONIKA 4:14
Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.


1 ATESALONIKA 4:16
Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba.


1 ATESALONIKA 5:9
Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.


1 ATESALONIKA 5:18
Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.


1 ATESALONIKA 5:23
Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 1:1
Paulo, Silivano ndi Timoteyo. Kulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 1:2
Chisomo ndi mtendere kwa inu kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 1:3
Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe.


2 ATESALONIKA 1:4
Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo.


2 ATESALONIKA 1:5
Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira.


2 ATESALONIKA 1:6
Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo


2 ATESALONIKA 1:8
Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.


2 ATESALONIKA 1:11
Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro.


2 ATESALONIKA 1:12
Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 2:4
Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.


2 ATESALONIKA 2:11
Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza.


2 ATESALONIKA 2:13
Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.


2 ATESALONIKA 2:16
Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino,


2 ATESALONIKA 3:5
Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.


1 TIMOTEO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu.


1 TIMOTEO 1:2
Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro. Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe.


1 TIMOTEO 1:4
kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro.


1 TIMOTEO 1:9
Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena.


1 TIMOTEO 1:11
Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.


1 TIMOTEO 1:16
Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha.


1 TIMOTEO 1:17
Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.


1 TIMOTEO 1:20
Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu.


1 TIMOTEO 2:2
Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.


1 TIMOTEO 2:3
Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,


1 TIMOTEO 2:5
Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.


1 TIMOTEO 2:8
Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.


1 TIMOTEO 2:10
Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.


1 TIMOTEO 3:5
(Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?)


1 TIMOTEO 3:15
Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi.


1 TIMOTEO 4:3
Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika.


1 TIMOTEO 4:4
Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika,


1 TIMOTEO 4:5
pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.


1 TIMOTEO 4:7
Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu.


1 TIMOTEO 4:8
Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.


1 TIMOTEO 4:10
Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira.


1 TIMOTEO 4:13
Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.


1 TIMOTEO 5:4
Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.


1 TIMOTEO 5:5
Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza.


1 TIMOTEO 5:10
Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.


1 TIMOTEO 5:18
Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.”


1 TIMOTEO 5:21
Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.


1 TIMOTEO 6:1
Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu.


1 TIMOTEO 6:3
Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu,


1 TIMOTEO 6:5
ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma.


1 TIMOTEO 6:6
Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu.


1 TIMOTEO 6:11
Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.


1 TIMOTEO 6:13
Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni.


1 TIMOTEO 6:15
Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye.


1 TIMOTEO 6:16
Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.


1 TIMOTEO 6:17
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa.


1 TIMOTEO 6:20
Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru.


2 TIMOTEO 1:1
Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu. Anandituma kuti ndilalike za lonjezo la moyo umene uli mwa Khristu Yesu.


2 TIMOTEO 1:2
Kwa Timoteyo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye athu Yesu Khristu.


2 TIMOTEO 1:3
Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.


2 TIMOTEO 1:6
Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja.


2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.


2 TIMOTEO 1:8
Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu.


2 TIMOTEO 1:10
Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe.


2 TIMOTEO 1:16
Mulungu achitire chifundo banja lonse la Onesiforo chifukwa ankandisangalatsa kawirikawiri ndipo sankachita nane manyazi ngakhale ndinali womangidwa ndi maunyolo.


2 TIMOTEO 2:9
umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo.


2 TIMOTEO 2:14
Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo.


2 TIMOTEO 2:15
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.


2 TIMOTEO 2:16
Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera.


2 TIMOTEO 2:19
Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”


2 TIMOTEO 2:25
Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi.


2 TIMOTEO 3:4
opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu.


2 TIMOTEO 3:12
Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,


2 TIMOTEO 3:16
Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo


2 TIMOTEO 3:17
kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.


2 TIMOTEO 4:1
Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti:


2 TIMOTEO 4:16
Podziteteza koyamba pa mlandu wanga, panalibe ndi mmodzi yemwe amene anandithandiza, koma aliyense anandithawa. Mulungu awakhululukire.


FILEMONI 1:3
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.


FILEMONI 1:4
Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga.


FILEMONI 1:22
Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.


YAKOBO 1:1
Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana. Landirani moni.


YAKOBO 1:5
Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.


YAKOBO 1:12
Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.


YAKOBO 1:13
Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense.


YAKOBO 1:20
Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu.


YAKOBO 1:27
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.


YAKOBO 2:5
Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?


YAKOBO 2:19
Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.


YAKOBO 2:23
Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.


YAKOBO 3:9
Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu.


YAKOBO 4:2
Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.


YAKOBO 4:4
Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu.


YAKOBO 4:5
Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife?


YAKOBO 4:6
Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”


YAKOBO 4:7
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.


YAKOBO 4:8
Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.


2 PETRO 1:1
Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.


2 PETRO 1:2
Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.


2 PETRO 1:3
Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake.


2 PETRO 1:4
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.


2 PETRO 1:6
Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu.


2 PETRO 1:7
Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.


2 PETRO 1:17
Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.”


2 PETRO 1:21
Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.


2 PETRO 2:4
Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe.


2 PETRO 2:5
Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo.


2 PETRO 2:6
Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu.


2 PETRO 2:17
Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani.


2 PETRO 2:21
Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa.


2 PETRO 3:5
Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi.


2 PETRO 3:7
Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.


2 PETRO 3:11
Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu


2 PETRO 3:12
pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha.


2 PETRO 3:13
Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.


2 PETRO 3:15
Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa.


1 YOHANE 1:5
Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.


1 YOHANE 1:10
Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife.


1 YOHANE 2:4
Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi.


1 YOHANE 2:5
Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye.


1 YOHANE 2:6
Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.


1 YOHANE 2:14
Ana okondedwa, ndikukulemberani chifukwa mumawadziwa Atate. Abambo, ndikukulemberani chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani chifukwa ndinu amphamvu. Mawu a Mulungu amakhala mwa inu ndipo mumamugonjetsa woyipayo.


1 YOHANE 2:17
Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.


1 YOHANE 2:29
Popeza mukudziwa kuti Khristu ndi wolungama, choncho mukudziwanso kuti aliyense amene amachita chilungamo ndi mwana wa Mulungu.


1 YOHANE 3:1
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.


1 YOHANE 3:2
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.


1 YOHANE 3:8
Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi.


1 YOHANE 3:9
Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.


1 YOHANE 3:10
Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.


1 YOHANE 3:17
Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?


1 YOHANE 3:19
Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu,


1 YOHANE 3:20
nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.


1 YOHANE 3:21
Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu.


1 YOHANE 4:1
Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.


1 YOHANE 4:2
Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu,


1 YOHANE 4:3
koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.


1 YOHANE 4:4
Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.


1 YOHANE 4:6
Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.


1 YOHANE 4:7
Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu.


1 YOHANE 4:8
Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.


1 YOHANE 4:9
Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo.


1 YOHANE 4:10
Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.


1 YOHANE 4:11
Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.


1 YOHANE 4:12
Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.


1 YOHANE 4:15
Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu.


1 YOHANE 4:16
Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.


1 YOHANE 4:19
Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.


1 YOHANE 4:20
Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone.


1 YOHANE 4:21
Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.


1 YOHANE 5:1
Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake.


1 YOHANE 5:2
Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake.


1 YOHANE 5:3
Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa,


1 YOHANE 5:4
chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi.


1 YOHANE 5:5
Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.


1 YOHANE 5:9
Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake.


1 YOHANE 5:10
Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake.


1 YOHANE 5:11
Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake.


1 YOHANE 5:12
Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.


1 YOHANE 5:13
Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha.


1 YOHANE 5:14
Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera.


1 YOHANE 5:16
Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi.


1 YOHANE 5:18
Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze.


1 YOHANE 5:19
Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo.


1 YOHANE 5:20
Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.


2 YOHANE 1:1
Ndine mkulu wampingo, kulembera: Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi.


2 YOHANE 1:3
Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.


2 YOHANE 1:9
Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana.


2 YOHANE 1:13
Ana a mlongo wanu wosankhidwa ndi Mulungu akupereka moni.


YUDA 1:1
Ndine Yuda, mtumiki wa Yesu Khristu, komanso mʼbale wake wa Yakobo. Kwa inu amene Mulungu Atate anakuyitanani, amene amakukondani ndikukusungani mwa Yesu Khristu.


YUDA 1:3
Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima.


YUDA 1:4
Pakuti anthu ena amene za chilango chawo zinalembedwa kale, alowa mobisika pakati panu. Amenewa ndi anthu osapembedza Mulungu, amene amapotoza chisomo cha Mulungu wathu kuchisandutsa ufulu ochitira zonyansa ndiponso amakana Yesu Khristu amene Iye ndiye Mbuye ndi Mfumu yathu.


YUDA 1:6
Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo.


YUDA 1:8
Nʼchimodzimodzinso zimene akuchita anthu amenewa potsata maloto awo, amadetsa matupi awo, amakana ulamuliro wa Mulungu ndiponso amachitira chipongwe angelo akumwamba.


YUDA 1:13
Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya.


YUDA 1:15
kuti adzaweruze aliyense, ndi kudzagamula kuti onse osapembedza ndi olakwa, chifukwa cha ntchito zawo zosalungama zimene anachita mʼmoyo wawo osaopa Mulungu. Adzawatsutsa chifukwa cha mawu onse achipongwe amene osapembedzawa ananyoza nawo Ambuye.”


YUDA 1:21
Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.


YUDA 1:25
kwa Mulungu yekhayo, Mpulumutsi wathu, kwa Iye kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, kuyambira isanayambe nthawi, tsopano mpaka muyaya. Ameni.


Dutch Bible 2007
Copyright © 1979, 1988, 2007 by Biblica, Inc.®