A A A A A


Sakani

MATEYU 2:11
Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure.


MATEYU 14:33
Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”


MATEYU 15:9
Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”


MATEYU 28:9
Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nati, “Moni.” Iwo anabwera kwa Iye, nagwira mapazi ake namulambira.


MATEYU 28:17
Atamuona Iye, anamulambira; koma ena anakayika.


MARKO 7:7
Amandilambira Ine kwachabe; ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.


MARKO 15:19
Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye.


LUKA 4:7
Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.”


LUKA 24:52
Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.


YOHANE 9:38
Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:25
Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira.


Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®