A A A A A

Sakani
MATEYU 6:16
“Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.


MATEYU 6:17
Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu,


MATEYU 6:18
kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.


MATEYU 17:21
Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”


MARKO 9:29
Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”


LUKA 2:37
ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:2
Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.”


MACHITIDWE A ATUMWI 14:23
Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira.


Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®