A A A A A


Sakani

LUKA 1:69
Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife mu nyumba ya mtumiki wake Davide.


LUKA 1:71
chipulumutso kuchoka kwa adani athu ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,


LUKA 1:77
kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,


LUKA 2:30
Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,


LUKA 2:38
Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.


LUKA 3:6
Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”


LUKA 19:9
Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu.


LUKA 21:28
Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”


YOHANE 4:22
Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:47
Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:12
Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”


MACHITIDWE A ATUMWI 13:26
“Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:47
Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”


MACHITIDWE A ATUMWI 16:17
Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, “Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso.”


MACHITIDWE A ATUMWI 28:28
“Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.”


AROMA 11:11
Ine ndikufunsanso kuti, kodi iwo anapunthwa ndi kugwa kotheratu? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo, chipulumutso chinafika kwa a mitundu ina kuti Aisraeli achite nsanje.


AROMA 13:11
Ndipo chitani ichi pozindikira nthawi ino. Nthawi yafika yoti inu mudzuke kutulo, chifukwa chipulumutso chathu chili pafupi tsopano kuposa pamene tinayamba kukhulupirira.


1 AKORINTO 1:30
Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.


2 AKORINTO 6:2
Pakuti akunena kuti, “Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera, ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza. Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”


2 AKORINTO 7:10
Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa.


AGALATIYA 5:11
Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa.


AEFESO 1:13
Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.


AEFESO 6:17
Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.


AFILIPI 2:12
Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera,


1 ATESALONIKA 5:8
Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa.


1 ATESALONIKA 5:9
Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.


AHEBRI 1:14
Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?


AHEBRI 2:3
Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira.


AHEBRI 2:10
Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo.


AHEBRI 5:9
Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.


AHEBRI 6:9
Okondedwa anga, ngakhale tikuyankhula zimenezi, ife tikudziwa kuti muli nazo zinthu zabwino zomwe zimabwera pamodzi ndi chipulumutso.


AHEBRI 9:12
Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha.


AHEBRI 9:28
momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.


1 PETRO 1:5
Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza.


1 PETRO 1:9
Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu.


1 PETRO 1:10
Kunena za chipulumutso chimenechi, aneneri amene ananeneratu za chisomo chimene chimabwera kwa inu, anafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi,


1 PETRO 2:2
Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,


2 PETRO 3:15
Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa.


YUDA 1:3
Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 7:10
Ndipo ankafuwula mokweza kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu, wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa.”


CHIVUMBULUTSO 12:10
Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti, “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera. Pakuti woneneza abale athu uja, amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku, wagwetsedwa pansi.


CHIVUMBULUTSO 19:1
Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti, “Haleluya! Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,


Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®