A A A A A

Sakani
MATEYU 1:1
Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


MATEYU 1:16
ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye.


MATEYU 1:18
Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.


MATEYU 1:21
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.


MATEYU 1:25
ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.


MATEYU 2:1
Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


MATEYU 3:13
Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.


MATEYU 3:15
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


MATEYU 3:16
Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


MATEYU 4:1
Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.


MATEYU 4:7
Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


MATEYU 4:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


MATEYU 4:12
Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;


MATEYU 4:17
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.


MATEYU 4:18
Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


MATEYU 4:23
Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


MATEYU 7:28
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:


MATEYU 8:3
Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.


MATEYU 8:4
Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.


MATEYU 8:7
Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye.


MATEYU 8:10
Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeza chikhulupiriro chotere.


MATEYU 8:13
Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.


MATEYU 8:14
Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.


MATEYU 8:18
Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina.


MATEYU 8:20
Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


MATEYU 8:22
Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.


MATEYU 8:34
Ndipo onani, mudzi wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m'malire ao.


MATEYU 9:2
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.


MATEYU 9:4
Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m'mitima yanu?


MATEYU 9:9
Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.


MATEYU 9:10
Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.


MATEYU 9:12
Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala.


MATEYU 9:15
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.


MATEYU 9:19
Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe.


MATEYU 9:22
Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


MATEYU 9:23
Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,


MATEYU 9:27
Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.


MATEYU 9:28
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.


MATEYU 9:30
Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense.


MATEYU 9:35
Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.


MATEYU 10:5
Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:


MATEYU 11:1
Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'midzi mwao.


MATEYU 11:4
Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:


MATEYU 11:7
Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya nji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?


MATEYU 11:25
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


MATEYU 12:1
Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.


MATEYU 12:15
Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse,


MATEYU 12:25
Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;


MATEYU 13:1
Tsiku lomwelo Yesu anatuluka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja.


MATEYU 13:34
Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo;


MATEYU 13:53
Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko.


MATEYU 13:57
Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.


MATEYU 14:1
Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu,


MATEYU 14:12
Ndipo ophunzira ake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.


MATEYU 14:13
Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi.


MATEYU 14:16
Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye.


MATEYU 14:27
Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.


MATEYU 14:29
Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


MATEYU 14:31
Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?


MATEYU 15:1
Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ochokera ku Yerusalemu, nati,


MATEYU 15:21
Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni.


MATEYU 15:28
Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.


MATEYU 15:29
Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.


MATEYU 15:32
Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.


MATEYU 15:34
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono.


MATEYU 16:6
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.


MATEYU 16:8
Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana chifukwa ninji wina ndi mnzake, kuti simunatenga mikate?


MATEYU 16:13
Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa Munthu ndiye yani?


MATEYU 16:17
Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.


MATEYU 16:21
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


MATEYU 16:24
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


MATEYU 17:1
Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha pa phiri lalitali;


MATEYU 17:4
Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.


MATEYU 17:7
Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa.


MATEYU 17:8
Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha.


MATEYU 17:9
Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.


MATEYU 17:17
Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.


MATEYU 17:18
Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


MATEYU 17:19
Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuchitulutsa?


MATEYU 17:22
Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;


MATEYU 17:25
Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?


MATEYU 17:26
Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu.


MATEYU 18:1
Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?


MATEYU 18:2
Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,


MATEYU 18:22
Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.


MATEYU 19:1
Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordani.


MATEYU 19:14
Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.


MATEYU 19:18
Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,


MATEYU 19:21
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.


MATEYU 19:23
Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba.


MATEYU 19:26
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


MATEYU 19:28
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


MATEYU 20:17
Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,


MATEYU 20:22
Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.


MATEYU 20:25
Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo.


MATEYU 20:30
Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'mphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide.


MATEYU 20:32
Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?


MATEYU 20:34
Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.


MATEYU 21:1
Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,


MATEYU 21:6
Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza;


MATEYU 21:11
Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


MATEYU 21:12
Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


MATEYU 21:16
nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


MATEYU 21:21
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


MATEYU 21:24
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:


MATEYU 21:27
Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.


MATEYU 21:31
Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.


MATEYU 21:42
Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


MATEYU 22:1
Ndipo Yesu anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati,


MATEYU 22:18
Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?


MATEYU 22:29
Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.


MATEYU 22:37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.


MATEYU 22:41
Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,


MATEYU 23:1
Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ake,


MATEYU 24:1
Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipo ophunzira ake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo.


MATEYU 24:4
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.


MATEYU 26:1
Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ake,


MATEYU 26:4
nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi chinyengo, namuphe.


MATEYU 26:6
Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,


MATEYU 26:10
Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino.


MATEYU 26:17
Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye?


MATEYU 26:19
Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska.


MATEYU 26:26
Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa.


MATEYU 26:31
Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


MATEYU 26:34
Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.


MATEYU 26:36
Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.


MATEYU 26:49
Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.


MATEYU 26:50
Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.


MATEYU 26:51
Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.


MATEYU 26:52
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.


MATEYU 26:55
Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.


MATEYU 26:57
Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe.


MATEYU 26:59
Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


MATEYU 26:63
Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


MATEYU 26:64
Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


MATEYU 26:69
Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.


MATEYU 26:71
Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.


MATEYU 26:75
Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.


MATEYU 27:1
Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


MATEYU 27:11
Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.


MATEYU 27:17
Chifukwa chake pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Barabasi kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu?


MATEYU 27:20
Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu.


MATEYU 27:22
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.


MATEYU 27:26
Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.


MATEYU 27:27
Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.


MATEYU 27:37
Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.


MATEYU 27:46
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau akulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


MATEYU 27:50
Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau akulu, anapereka mzimu wake.


MATEYU 27:54
Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


MATEYU 27:55
Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patali, omwe anatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye;


MATEYU 27:57
Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimatea, dzina lake Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu;


MATEYU 27:58
yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe.


MATEYU 28:5
Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa.


MATEYU 28:9
Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira.


MATEYU 28:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.


MATEYU 28:16
Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira.


MATEYU 28:18
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.


MARKO 1:1
Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.


MARKO 1:9
Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordani.


MARKO 1:14
Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,


MARKO 1:17
Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.


MARKO 1:24
Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.


MARKO 1:25
Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye.


MARKO 1:41
Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.


MARKO 1:45
Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


MARKO 2:5
Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.


MARKO 2:8
Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?


MARKO 2:15
Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.


MARKO 2:17
Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.


MARKO 2:19
Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.


MARKO 3:7
Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,


MARKO 5:6
Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye;


MARKO 5:7
ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.


MARKO 5:15
Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.


MARKO 5:20
Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.


MARKO 5:21
Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.


MARKO 5:27
m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake.


MARKO 5:30
Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga?


MARKO 5:36
Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.


MARKO 6:4
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m'nyumba yake.


MARKO 6:30
Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.


MARKO 8:17
Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma?


MARKO 8:27
Ndipo anatuluka Yesu, ndi ophunzira ake, nalowa kumidzi ya ku Kesareya-Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ake, nanena nao, Kodi anthu ananena kuti Ine ndine yani?


MARKO 9:2
Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:


MARKO 9:4
Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.


MARKO 9:5
Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.


MARKO 9:8
Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.


MARKO 9:23
Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.


MARKO 9:25
Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.


MARKO 9:27
Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira.


MARKO 9:39
Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.


MARKO 10:5
Koma Yesu anati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili.


MARKO 10:14
Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


MARKO 10:18
Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.


MARKO 10:21
Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.


MARKO 10:23
Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!


MARKO 10:24
Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!


MARKO 10:27
Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


MARKO 10:29
Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo,


MARKO 10:32
Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anachita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,


MARKO 10:38
Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?


MARKO 10:39
Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;


MARKO 10:42
Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu ao amachita ulamuliro pa iwo.


MARKO 10:47
Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kufuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo.


MARKO 10:49
Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.


MARKO 10:50
Ndipo iye anataya chofunda chake, nazunzuka, nadza kwa Yesu.


MARKO 10:51
Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.


MARKO 10:52
Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.


MARKO 11:6
Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye.


MARKO 11:7
Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, naika zovala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.


MARKO 11:22
Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu.


MARKO 11:29
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi.


MARKO 11:33
Ndipo iwo anamyankha Yesu, ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi.


MARKO 12:17
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.


MARKO 12:24
Yesu ananena nao, Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu?


MARKO 12:29
Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israele; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;


MARKO 12:34
Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu.


MARKO 12:35
Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa m'Kachisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide?


MARKO 13:2
Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.


MARKO 13:5
Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusocheretseni.


MARKO 14:6
Koma Yesu anati, Mlekeni, mumvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino.


MARKO 14:18
Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.


MARKO 14:27
Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.


MARKO 14:30
Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.


MARKO 14:48
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira Ine monga wachifwamba?


MARKO 14:53
Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe aakulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi.


MARKO 14:55
Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeze.


MARKO 14:60
Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira mboni?


MARKO 14:62
Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa Munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.


MARKO 14:67
ndipo anaona Petro alikuotha moto, namyang'ana iye, nanena, Iwenso unali naye Mnazarene, Yesu.


MARKO 14:72
Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.


MARKO 15:1
Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


MARKO 15:5
Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.


MARKO 15:15
Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.


MARKO 15:34
Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?


MARKO 15:37
Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake.


MARKO 15:43
anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu.


MARKO 16:6
Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m'mene anaikamo Iye!


MARKO 16:19
Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.


LUKA 1:31
Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.


LUKA 2:21
Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.


LUKA 2:27
Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo,


LUKA 2:43
ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe;


LUKA 2:52
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.


LUKA 3:21
Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,


LUKA 3:23
Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli,


LUKA 4:1
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu


LUKA 4:4
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.


LUKA 4:8
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.


LUKA 4:12
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


LUKA 4:14
Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.


LUKA 4:34
Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.


LUKA 4:35
Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosamphweteka konse.


LUKA 4:38
Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.


LUKA 5:8
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.


LUKA 5:10
ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.


LUKA 5:12
Ndipo panali, pamene Iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.


LUKA 5:19
Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.


LUKA 5:22
Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu?


LUKA 5:31
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo.


LUKA 5:34
Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?


LUKA 6:3
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi;


LUKA 6:9
Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?


LUKA 6:11
Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.


LUKA 7:1
Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao.


LUKA 7:3
Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake.


LUKA 7:4
Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;


LUKA 7:6
Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi panyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa;


LUKA 7:9
Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.


LUKA 7:37
Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,


LUKA 7:40
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.


LUKA 8:28
Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau akulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.


LUKA 8:30
Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.


LUKA 8:35
Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.


LUKA 8:39
Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumudzi wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.


LUKA 8:40
Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.


LUKA 8:41
Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake;


LUKA 8:45
Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.


LUKA 8:46
Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine.


LUKA 8:50
Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupirira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.


LUKA 9:33
Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.


LUKA 9:36
Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.


LUKA 9:41
Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.


LUKA 9:42
Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.


LUKA 9:47
Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo,


LUKA 9:50
Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.


LUKA 9:51
Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,


LUKA 9:58
Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu.


LUKA 9:62
Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.


LUKA 10:29
Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


LUKA 10:30
Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.


LUKA 10:37
Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo.


LUKA 13:12
Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.


LUKA 13:14
Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.


LUKA 14:3
Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai?


LUKA 17:13
ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo.


LUKA 17:17
Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwe khumi? Koma ali kuti asanu ndi anai aja?


LUKA 18:16
Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.


LUKA 18:19
Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.


LUKA 18:22
Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.


LUKA 18:24
Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu!


LUKA 18:37
Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


LUKA 18:38
Ndipo anafuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.


LUKA 18:40
Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye,


LUKA 18:42
Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.


LUKA 19:3
Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sanathe, chifukwa cha khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu.


LUKA 19:5
Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.


LUKA 19:9
Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.


LUKA 19:35
Ndipo anadza naye kwa Yesu; ndipo anayalika zovala zao pa mwana wa buluyo, nakwezapo Yesu.


LUKA 20:8
Ndipo Yesu anati kwa iwo Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu izi.


LUKA 20:34
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:


LUKA 21:1
Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.


LUKA 22:47
Pamene Iye anali chilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona Iye.


LUKA 22:48
Koma Yesu anati kwa iye, Yudasi, ulikupereka Mwana wa Munthu ndi chimpsompsono kodi?


LUKA 22:51
Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lake, namchiritsa.


LUKA 22:52
Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?


LUKA 22:63
Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza Iye, nampanda.


LUKA 23:8
Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa anamva za Iye; nayembekeza kuona chizindikiro china chochitidwa ndi Iye.


LUKA 23:20
Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;


LUKA 23:25
Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.


LUKA 23:26
Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.


LUKA 23:28
Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.


LUKA 23:34
Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.


LUKA 23:42
Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu.


LUKA 23:46
Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau akulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.


LUKA 23:52
yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wake wa Yesu.


LUKA 24:3
Ndipo m'mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu.


LUKA 24:15
Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.


LUKA 24:19
Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;


YOHANE 1:17
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


YOHANE 1:29
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


YOHANE 1:36
ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!


YOHANE 1:37
Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.


YOHANE 1:38
Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?


YOHANE 1:42
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).


YOHANE 1:43
M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.


YOHANE 1:45
Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.


YOHANE 1:47
Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!


YOHANE 1:48
Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.


YOHANE 1:50
Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi.


YOHANE 2:1
Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko.


YOHANE 2:2
Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo.


YOHANE 2:3
Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo.


YOHANE 2:4
Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike.


YOHANE 2:7
Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, ndendende.


YOHANE 2:11
Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


YOHANE 2:13
Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


YOHANE 2:19
Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.


YOHANE 2:22
Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.


YOHANE 2:24
Koma Yesu sanakhulupirire iwo kuti akhale nao, chifukwa Iye anadziwa anthu onse,


YOHANE 3:2
Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


YOHANE 3:3
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:5
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:10
Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israele, ndipo sudziwa izi?


YOHANE 3:22
Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.


YOHANE 4:1
Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane


YOHANE 4:2
(angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake),


YOHANE 4:6
ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.


YOHANE 4:7
Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka m'Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.


YOHANE 4:10
Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


YOHANE 4:13
Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu;


YOHANE 4:16
Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.


YOHANE 4:17
Mkazi anayankha nati kwa Iye, Ndilibe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndilibe;


YOHANE 4:21
Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.


YOHANE 4:26
Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.


YOHANE 4:34
Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


YOHANE 4:44
Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.


YOHANE 4:46
Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala m'Kapernao.


YOHANE 4:47
Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wachokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa Iye, nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti anali pafupi imfa.


YOHANE 4:48
Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.


YOHANE 4:50
Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo. Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka.


YOHANE 4:53
Chifukwa chake atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupirira iye yekha ndi a pa banja lake onse.


YOHANE 4:54
Ichi ndi chizindikiro chachiwiri Yesu anachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa m'Galileya.


YOHANE 5:1
Zitapita izi panali chikondwerero cha Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


YOHANE 5:6
Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikulu pamenepo, ananena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi?


YOHANE 5:8
Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende.


YOHANE 5:13
Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.


YOHANE 5:14
Zitapita izi Yesu anampeza m'Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.


YOHANE 5:15
Munthuyo anachoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa.


YOHANE 5:16
Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata.


YOHANE 5:17
Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.


YOHANE 5:19
Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.


YOHANE 6:1
Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.


YOHANE 6:3
Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi ophunzira ake.


YOHANE 6:5
Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?


YOHANE 6:10
Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.


YOHANE 6:11
Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.


YOHANE 6:15
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.


YOHANE 6:17
ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.


YOHANE 6:19
Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.


YOHANE 6:22
M'mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m'ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha;


YOHANE 6:23
koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika;


YOHANE 6:24
chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.


YOHANE 6:26
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.


YOHANE 6:29
Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.


YOHANE 6:32
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.


YOHANE 6:35
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.


YOHANE 6:42
Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?


YOHANE 6:43
Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze wina ndi mnzake.


YOHANE 6:53
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.


YOHANE 6:61
Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?


YOHANE 6:64
Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.


YOHANE 6:67
Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka?


YOHANE 6:70
Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?


YOHANE 7:1
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda m'Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.


YOHANE 7:6
Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.


YOHANE 7:14
Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa m'Kachisi, naphunzitsa.


YOHANE 7:16
Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.


YOHANE 7:21
Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse.


YOHANE 7:28
Pamenepo Yesu anafuula m'Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.


YOHANE 7:33
Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.


YOHANE 7:37
Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.


YOHANE 7:39
Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


YOHANE 8:1
Koma Yesu anamuka kuphiri la Azitona.


YOHANE 8:6
Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.


YOHANE 8:9
Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.


YOHANE 8:10
Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?


YOHANE 8:11
Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.


YOHANE 8:12
Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


YOHANE 8:14
Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.


YOHANE 8:19
Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.


YOHANE 8:25
Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.


YOHANE 8:28
Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.


YOHANE 8:31
Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu;


YOHANE 8:34
Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa chimolo.


YOHANE 8:39
Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.


YOHANE 8:42
Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.


YOHANE 8:49
Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.


YOHANE 8:54
Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;


YOHANE 8:58
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.


YOHANE 8:59
Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka m'Kachisi.


YOHANE 9:3
Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.


YOHANE 9:11
Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya.


YOHANE 9:14
Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ake.


YOHANE 9:35
Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Munthu?


YOHANE 9:37
Yesu anati kwa iye, Wamuona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo.


YOHANE 9:39
Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.


YOHANE 9:41
Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.


YOHANE 10:6
Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.


YOHANE 10:7
Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.


YOHANE 10:23
Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kachisi m'khonde la Solomoni.


YOHANE 10:25
Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira. Ntchitozi ndidzichita Ine m'dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni.


YOHANE 10:32
Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?


YOHANE 10:34
Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu?


YOHANE 11:4
Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


YOHANE 11:5
Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro.


YOHANE 11:9
Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi.


YOHANE 11:13
Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.


YOHANE 11:14
Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.


YOHANE 11:17
Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai.


YOHANE 11:20
Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi Iye; koma Maria anakhalabe m'nyumba.


YOHANE 11:21
Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.


YOHANE 11:23
Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka.


YOHANE 11:25
Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


YOHANE 11:30
(Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye.)


YOHANE 11:32
Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.


YOHANE 11:33
Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,


YOHANE 11:35
Yesu analira.


YOHANE 11:38
Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.


YOHANE 11:39
Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.


YOHANE 11:40
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?


YOHANE 11:41
Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.


YOHANE 11:44
Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.


YOHANE 11:46
Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazichita.


YOHANE 11:51
Koma ichi sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo;


YOHANE 11:54
Chifukwa chake Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.


YOHANE 11:56
Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzake poimirira iwo m'Kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuchikondwerero kodi?


YOHANE 12:1
Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.


YOHANE 12:3
Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.


YOHANE 12:7
Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga.


YOHANE 12:9
Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.


YOHANE 12:11
pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.


YOHANE 12:12
M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,


YOHANE 12:14
Koma Yesu, m'mene adapeza kabulu anakhala pamenepo; monga mulembedwa:


YOHANE 12:16
Izi sanazidziwa ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.


YOHANE 12:21
Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.


YOHANE 12:22
Filipo anadza nanena kwa Andrea; nadza Andrea ndi Filipo, nanena ndi Yesu.


YOHANE 12:23
Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.


YOHANE 12:30
Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika chifukwa cha Ine, koma cha inu.


YOHANE 12:35
Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


YOHANE 12:36
Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira.


YOHANE 12:44
Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine.


YOHANE 13:1
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


YOHANE 13:3
Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


YOHANE 13:7
Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake.


YOHANE 13:8
Petro ananena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga kunthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine.


YOHANE 13:10
Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.


YOHANE 13:21
Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.


YOHANE 13:23
Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.


YOHANE 13:25
Iyeyu potsamira pomwepo, pa chifukwa cha Yesu, anena ndi Iye, Ambuye, ndiye yani?


YOHANE 13:26
Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.


YOHANE 13:27
Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.


YOHANE 13:29
Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.


YOHANE 13:31
Tsono m'mene adatuluka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa Munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa Iye;


YOHANE 13:36
Simoni Petro anena ndi Iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, udzanditsata bwino lomwe.


YOHANE 13:38
Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.


YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


YOHANE 14:9
Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?


YOHANE 14:23
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


YOHANE 16:19
Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?


YOHANE 16:31
Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano?


YOHANE 17:1
Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;


YOHANE 17:3
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


YOHANE 18:1
M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake.


YOHANE 18:2
Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akamkako kawirikawiri ndi ophunzira ake.


YOHANE 18:4
Pamenepo Yesu, podziwa zonse zilinkudza pa Iye, anatuluka, nati kwa iwo, Mufuna yani?


YOHANE 18:5
Anayankha Iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudasi yemwe, wompereka Iye, anaima nao pamodzi.


YOHANE 18:7
Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? Koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.


YOHANE 18:8
Yesu anayankha, Nati, Ndine; chifukwa chake ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;


YOHANE 18:11
Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?


YOHANE 18:12
Ndipo khamulo ndi kapitao wamkulu, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga Iye,


YOHANE 18:15
Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;


YOHANE 18:19
Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za ophunzira ake, ndi chiphunzitso chake.


YOHANE 18:20
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.


YOHANE 18:22
Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?


YOHANE 18:23
Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula choipa, chita umboni wa choipacho, koma ngati bwino, undipandiranji?


YOHANE 18:28
Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowa ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


YOHANE 18:32
kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.


YOHANE 18:33
Chifukwa chake Pilato analowanso m'Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?


YOHANE 18:34
Yesu anayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?


YOHANE 18:36
Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.


YOHANE 18:37
Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.


YOHANE 19:1
Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.


YOHANE 19:5
Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!


YOHANE 19:9
Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankha kanthu.


YOHANE 19:11
Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


YOHANE 19:13
Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma m'Chihebri, Gabata.


YOHANE 19:16
Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Pamenepo anatenga Yesu;


YOHANE 19:18
kumene anampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, chakuno ndi chauko, koma Yesu pakati.


YOHANE 19:19
Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.


YOHANE 19:20
Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Chihebri, ndi m'Chilatini, ndi m'Chigriki.


YOHANE 19:23
Pamenepo asilikali, m'mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko.


YOHANE 19:25
Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.


YOHANE 19:26
Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu!


YOHANE 19:28
Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


YOHANE 19:30
Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


YOHANE 19:33
koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona Iye, kuti wafa kale, sanathyola miyendo yake;


YOHANE 19:38
Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake.


YOHANE 19:40
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.


YOHANE 19:42
Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.


YOHANE 20:2
Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye.


YOHANE 20:12
ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.


YOHANE 20:14
M'mene adanena izi, anacheuka m'mbuyo, naona Yesu ali chilili, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu.


YOHANE 20:15
Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa.


YOHANE 20:16
Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye m'Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.


YOHANE 20:17
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


YOHANE 20:19
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.


YOHANE 20:21
Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.


YOHANE 20:24
Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza.


YOHANE 20:26
Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.


YOHANE 20:29
Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaona.


YOHANE 20:30
Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwa m'buku ili;


YOHANE 20:31
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.


YOHANE 21:1
Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.


YOHANE 21:4
Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu.


YOHANE 21:5
Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha Iye, Iai.


YOHANE 21:7
Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja.


YOHANE 21:10
Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano.


YOHANE 21:12
Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa ophunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye.


YOHANE 21:13
Yesu anadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba.


YOHANE 21:14
Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudzionetsera Yesu kwa ophunzira ake, m'mene atauka kwa akufa.


YOHANE 21:15
Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga.


YOHANE 21:17
Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.


YOHANE 21:20
Petro, m'mene anacheuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?


YOHANE 21:21
Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu?


YOHANE 21:22
Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Unditsate Ine iwe.


YOHANE 21:23
Chifukwa chake mau awa anatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe?


YOHANE 21:25
Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phee, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:1
Taonani Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,


MACHITIDWE A ATUMWI 1:11
amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:14
Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:16
Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:21
Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa natuluka mwa ife,


MACHITIDWE A ATUMWI 2:22
Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:32
Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:36
Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:6
Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:13
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:20
ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:2
ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:10
zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:13
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:18
Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:27
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:30
m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:33
Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:30
Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpachika pamtengo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:40
Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:42
Ndipo masiku onse, m'Kachisi ndi m'nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:14
pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:55
Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:59
Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:12
Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:16
pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:35
Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:5
Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


MACHITIDWE A ATUMWI 9:17
Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:20
Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:27
Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:34
Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:36
Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)


MACHITIDWE A ATUMWI 10:38
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:48
Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:17
Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?


MACHITIDWE A ATUMWI 11:20
Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:6
Ndipo m'mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:23
Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:33
kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:11
Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:26
anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:7
pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;


MACHITIDWE A ATUMWI 16:18
Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:31
Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:3
natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:7
amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:18
Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:5
Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:25
Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


MACHITIDWE A ATUMWI 18:28
pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:4
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:5
Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:13
Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:15
Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?


MACHITIDWE A ATUMWI 19:17
Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:21
ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:24
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:35
M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:13
Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 22:8
Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:24
Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 25:19
koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:9
Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:15
Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:23
Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:31
ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.


AROMA 1:1
Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


AROMA 1:4
amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;


AROMA 1:6
mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Khristu;


AROMA 1:7
kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


AROMA 1:8
Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka pa dziko lonse lapansi.


AROMA 2:16
tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.


AROMA 3:22
ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;


AROMA 3:24
ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu;


AROMA 3:26
kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.


AROMA 4:24
koma chifukwa cha ifenso, kwa ife amene chidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira Iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu,


AROMA 5:1
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;


AROMA 5:11
Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.


AROMA 5:15
Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Khristu, zinachulukira anthu ambiri.


AROMA 5:17
Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu.


AROMA 5:21
kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.


AROMA 6:3
Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake?


AROMA 6:11
Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.


AROMA 6:23
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


AROMA 7:25
Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.


AROMA 8:1
Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.


AROMA 8:2
Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.


AROMA 8:11
Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.


AROMA 8:34
ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.


AROMA 8:39
ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


AROMA 10:9
kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:


AROMA 13:14
Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.


AROMA 14:14
Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.


AROMA 15:5
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;


AROMA 15:6
kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.


AROMA 15:16
kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


AROMA 15:17
Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha m'Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.


AROMA 15:30
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;


AROMA 16:3
Mupereke moni kwa Prisika ndi Akwila, antchito anzanga mwa Khristu Yesu,


AROMA 16:20
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.


AROMA 16:25
Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,


AROMA 16:27
kwa Mulungu wanzeru yekhayo, mwa Yesu Khristu, kwa yemweyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.


1 AKORINTO 1:1
Paulo, woitanidwa akhale mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo,


1 AKORINTO 1:2
kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


1 AKORINTO 1:3
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


1 AKORINTO 1:4
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chinapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;


1 AKORINTO 1:7
kotero kuti sichikusowani inu chaufulu chilichonse; pakulindira inu vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Khristu;


1 AKORINTO 1:8
amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m'tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.


1 AKORINTO 1:9
Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.


1 AKORINTO 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.


1 AKORINTO 1:30
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


1 AKORINTO 2:2
Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.


1 AKORINTO 3:11
Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu.


1 AKORINTO 4:15
Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.


1 AKORINTO 5:4
m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,


1 AKORINTO 5:5
kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


1 AKORINTO 6:11
Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


1 AKORINTO 8:6
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.


1 AKORINTO 9:1
Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?


1 AKORINTO 11:23
Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;


1 AKORINTO 12:3
Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


1 AKORINTO 15:31
Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu.


1 AKORINTO 15:57
koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


1 AKORINTO 16:23
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi inu.


1 AKORINTO 16:24
Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Amen.


2 AKORINTO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya monse:


2 AKORINTO 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 AKORINTO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,


2 AKORINTO 1:14
monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.


2 AKORINTO 1:19
Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.


2 AKORINTO 4:5
Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.


2 AKORINTO 4:6
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


2 AKORINTO 4:10
nthawi zonse tilikusenzasenza m'thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu.


2 AKORINTO 4:11
Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa.


2 AKORINTO 4:14
podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.


2 AKORINTO 8:9
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.


2 AKORINTO 11:4
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana naye bwino lomwe.


2 AKORINTO 11:31
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.


2 AKORINTO 13:5
Dziyeseni nokha, ngati muli m'chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa.


2 AKORINTO 13:14
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


AGALATIYA 1:1
Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),


AGALATIYA 1:3
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,


AGALATIYA 1:12
Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa vumbulutso la Yesu Khristu.


AGALATIYA 2:4
ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.


AGALATIYA 2:16
koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.


AGALATIYA 3:1
Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pa maso panu, wopachikidwa?


AGALATIYA 3:14
Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.


AGALATIYA 3:22
Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.


AGALATIYA 3:26
Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


AGALATIYA 3:28
Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


AGALATIYA 4:14
ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputsa, kapena sichinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini.


AGALATIYA 5:6
Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.


AGALATIYA 5:24
Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.


AGALATIYA 6:14
Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.


AGALATIYA 6:17
Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.


AGALATIYA 6:18
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.


AEFESO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:


AEFESO 1:2
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


AEFESO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


AEFESO 1:5
Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,


AEFESO 1:15
Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse,


AEFESO 1:17
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;


AEFESO 2:6
ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu;


AEFESO 2:7
kuti akaonetsere m'nthawi zilinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.


AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


AEFESO 2:13
Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.


AEFESO 2:20
omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;


AEFESO 3:1
Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


AEFESO 3:6
kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,


AEFESO 3:11
monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:


AEFESO 3:21
kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.


AEFESO 4:21
ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu;


AEFESO 5:20
ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;


AEFESO 6:7
akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai;


AEFESO 6:23
Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.


AEFESO 6:24
Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka.


AFILIPI 1:1
Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


AFILIPI 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


AFILIPI 1:6
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;


AFILIPI 1:8
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 1:11
odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.


AFILIPI 1:19
Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;


AFILIPI 1:26
kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke m'Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.


AFILIPI 2:5
Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu,


AFILIPI 2:10
kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,


AFILIPI 2:11
ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.


AFILIPI 2:19
Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.


AFILIPI 2:21
Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Khristu.


AFILIPI 3:3
pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


AFILIPI 3:8
Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,


AFILIPI 3:12
Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.


AFILIPI 3:14
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 3:20
Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;


AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 4:19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 4:21
Lankhulani woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine alankhula inu.


AFILIPI 4:23
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu.


AKOLOSE 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,


AKOLOSE 1:3
Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi kupempherera inu nthawi zonse,


AKOLOSE 1:4
popeza tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu, ndi chikondi muli nacho kwa oyera mtima onse;


AKOLOSE 2:6
Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye,


AKOLOSE 3:17
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


AKOLOSE 4:11
ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.


AKOLOSE 4:12
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m'mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.


1 ATESALONIKA 1:1
Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere.


1 ATESALONIKA 1:3
ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;


1 ATESALONIKA 1:10
ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife kumkwiyo ulinkudza.


1 ATESALONIKA 2:14
Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;


1 ATESALONIKA 2:15
amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;


1 ATESALONIKA 2:19
Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake?


1 ATESALONIKA 3:11
Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu;


1 ATESALONIKA 3:13
kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.


1 ATESALONIKA 4:1
Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.


1 ATESALONIKA 4:2
Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.


1 ATESALONIKA 4:14
Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.


1 ATESALONIKA 5:9
Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,


1 ATESALONIKA 5:18
M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.


1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


1 ATESALONIKA 5:28
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale nanu.


2 ATESALONIKA 1:1
Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu:


2 ATESALONIKA 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 1:7
ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,


2 ATESALONIKA 1:8
m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;


2 ATESALONIKA 1:12
kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 Tessalonicesi 2:1
Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye;


2 Tessalonicesi 2:8
Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;


2 Tessalonicesi 2:14
kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.


2 Tessalonicesi 2:16
Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,


2 Tessalonicesi 3:6
Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.


2 Tessalonicesi 3:12
Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.


2 Tessalonicesi 3:18
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.


2 TIMOTEO 1:1
Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Khristu Yesu,


2 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.


2 TIMOTEO 1:9
amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,


2 TIMOTEO 1:10
koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,


2 TIMOTEO 1:13
Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


2 TIMOTEO 2:1
Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha m'Khristu Yesu.


2 TIMOTEO 2:3
Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.


2 TIMOTEO 2:8
Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;


2 TIMOTEO 2:10
Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.


2 TIMOTEO 3:12
Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.


2 TIMOTEO 3:15
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


2 TIMOTEO 4:1
Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake;


TITO 1:1
Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,


TITO 1:4
kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.


TITO 2:13
akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;


TITO 3:6
amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu;


FILEMONI 1:1
Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu,


FILEMONI 1:3
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


FILEMONI 1:5
pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;


FILEMONI 1:9
koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;


FILEMONI 1:23
Epafra wandende mnzanga mwa Khristu Yesu akukupatsa moni;


FILEMONI 1:25
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen.


AHEBRI 2:9
Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.


AHEBRI 3:1
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;


AHEBRI 4:14
Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


AHEBRI 6:20
m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


AHEBRI 7:22
Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.


AHEBRI 10:10
Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.


AHEBRI 10:19
Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,


AHEBRI 12:2
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


AHEBRI 12:24
ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


AHEBRI 13:8
Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.


AHEBRI 13:12
Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.


AHEBRI 13:20
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


AHEBRI 13:21
akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.


YAKOBO 1:1
Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


YAKOBO 2:1
Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.


1 PETRO 1:1
Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya,


1 PETRO 1:2
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


1 PETRO 1:3
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


1 PETRO 1:7
kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;


1 PETRO 1:13
Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;


1 PETRO 2:5
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


1 PETRO 3:21
chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


1 PETRO 4:11
akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.


2 PETRO 1:1
Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:


2 PETRO 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.


2 PETRO 1:8
Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.


2 PETRO 1:11
pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.


2 PETRO 1:14
podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.


2 PETRO 1:16
Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.


2 PETRO 2:20
Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.


2 PETRO 3:18
Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


1 YOHANE 1:3
chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu;


1 YOHANE 1:7
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.


1 YOHANE 2:1
Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;


1 YOHANE 2:22
Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.


1 YOHANE 3:23
Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira.


1 YOHANE 4:2
M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu;


1 YOHANE 4:3
ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,


1 YOHANE 4:15
Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.


1 YOHANE 5:1
Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


1 YOHANE 5:5
Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?


1 YOHANE 5:6
Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.


1 YOHANE 5:20
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


2 YOHANE 1:3
Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi.


2 YOHANE 1:7
Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


YUDA 1:1
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:


YUDA 1:4
Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.


YUDA 1:17
Koma inu, abale, mukumbukire mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu;


YUDA 1:21
mudzisunge nokha m'chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha.


YUDA 1:25
kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.


CHIVUMBULUTSO 1:1
Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


CHIVUMBULUTSO 1:2
amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona.


CHIVUMBULUTSO 1:5
ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


CHIVUMBULUTSO 1:9
Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.


CHIVUMBULUTSO 12:17
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, nichinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.


CHIVUMBULUTSO 14:12
Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.


CHIVUMBULUTSO 17:6
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.


CHIVUMBULUTSO 19:10
Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.


CHIVUMBULUTSO 20:4
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chilombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.


CHIVUMBULUTSO 22:16
Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi m'Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.


CHIVUMBULUTSO 22:20
Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.


CHIVUMBULUTSO 22:21
Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi oyera mtima onse. Amen.


Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi