A A A A A


Sakani

MATEYU 9:15
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.


MATEYU 19:10
Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.


MATEYU 22:2
Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati,


MATEYU 22:3
natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa kuukwati umene; ndipo iwo sanafune kudza.


MATEYU 22:4
Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati.


MATEYU 22:8
Pomwepo inanena kwa akapolo ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma oitanidwawo sanayenera.


MATEYU 22:9
Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeze, itanani kuukwatiku.


MATEYU 22:10
Ndipo akapolo ao anatulukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pachakudya.


MATEYU 22:11
Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala cha ukwati;


MATEYU 22:12
nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau.


MATEYU 22:30
Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.


MATEYU 24:38
Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa,


MATEYU 25:10
Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.


MARKO 2:19
Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.


LUKA 5:34
Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?


LUKA 12:36
ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.


LUKA 14:8
Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,


LUKA 20:35
koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.


YOHANE 2:1
Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko.


YOHANE 2:2
Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo.


1 AKORINTO 7:9
Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.


1 AKORINTO 7:28
Koma ungakhale ukwatira, sunachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.


1 TIMOTEO 4:3
a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.


1 TIMOTEO 5:11
Koma amasiye ang'ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa;


AHEBRI 13:4
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 19:7
Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.


CHIVUMBULUTSO 19:9
Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.


Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi