A A A A A

Sakani
MATEYU 12:5
Kapena simunawerenga kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m'Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo?


MARKO 3:29
koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;


YOHANE 1:29
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


YOHANE 8:7
Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.


YOHANE 8:21
Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


YOHANE 8:34
Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa chimolo.


YOHANE 8:46
Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?


YOHANE 9:41
Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.


YOHANE 15:22
Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao.


YOHANE 15:24
Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.


YOHANE 19:11
Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:60
Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.


1 AKORINTO 6:18
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.


AHEBRI 12:1
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,


AHEBRI 12:4
Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo tchimo;


YAKOBO 4:17
Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.


1 PETRO 2:22
amene sanachita tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


1 PETRO 4:1
Popeza Khristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo tchimo;


1 YOHANE 3:4
Yense wakuchita tchimo achitanso kusaweruzika; ndipo tchimo ndilo kusaweruzika.


1 YOHANE 3:5
Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.


1 YOHANE 3:8
iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.


1 YOHANE 3:9
Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.


1 YOHANE 5:16
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


1 YOHANE 5:17
Chosalungama chilichonse chili uchimo; ndipo pali tchimo losati la kuimfa.


Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi