A A A A A


Sakani

LUKA 1:13
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.


LUKA 5:33
Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.


LUKA 20:47
amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:42
Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:4
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:31
nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.


AROMA 1:10
ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga, ngati nkutheka tsopano mwa chifuniro cha Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.


AROMA 10:1
Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.


AROMA 15:30
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;


2 AKORINTO 1:11
pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.


AEFESO 1:16
sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga;


AEFESO 6:18
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


AFILIPI 4:6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.


AKOLOSE 4:12
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m'mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.


1 ATESALONIKA 1:2
Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu;


1 ATESALONIKA 3:10
ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?


1 TIMOTEO 2:1
Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;


1 TIMOTEO 5:5
Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


2 TIMOTEO 1:3
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbu mtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,


FILEMONI 1:4
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga,


FILEMONI 1:22
Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.


AHEBRI 5:7
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


YAKOBO 5:15
ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.


YAKOBO 5:16
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


1 PETRO 3:7
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.


1 PETRO 4:7
Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


CHIVUMBULUTSO 5:8
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 8:3
Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.


CHIVUMBULUTSO 8:4
Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.


Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi