A A A A A


Sakani

MATEYU 1:23
Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.


MATEYU 2:22
Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya,


MATEYU 3:9
ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.


MATEYU 3:16
Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


MATEYU 4:3
Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.


MATEYU 4:4
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.


MATEYU 4:6
nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.


MATEYU 4:7
Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


MATEYU 4:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


MATEYU 5:8
Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.


MATEYU 5:9
Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.


MATEYU 5:34
koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu;


MATEYU 6:24
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.


MATEYU 6:30
Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?


MATEYU 8:29
Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?


MATEYU 9:3
Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano.


MATEYU 9:8
Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.


MATEYU 12:4
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


MATEYU 12:28
Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.


MATEYU 14:33
Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.


MATEYU 15:3
Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?


MATEYU 15:4
Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.


MATEYU 15:5
Koma inu munena, Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu;


MATEYU 15:6
iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.


MATEYU 15:31
kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.


MATEYU 15:36
natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.


MATEYU 16:16
Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.


MATEYU 16:23
Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


MATEYU 19:6
Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.


MATEYU 19:26
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


MATEYU 21:12
Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


MATEYU 21:43
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.


MATEYU 22:16
Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.


MATEYU 22:21
Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


MATEYU 22:29
Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.


MATEYU 22:31
Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,


MATEYU 22:32
Ine ndili Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.


MATEYU 22:37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.


MATEYU 23:22
Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.


MATEYU 26:61
nati, Uyu ananena kuti, Ndikhoza kupasula Kachisi wa Mulunguyu, ndi kummanganso masiku atatu.


MATEYU 26:63
Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


MATEYU 26:65
Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;


MATEYU 27:6
Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.


MATEYU 27:40
nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.


MATEYU 27:43
Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.


MATEYU 27:46
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau akulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


MATEYU 27:54
Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


MARKO 1:1
Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.


MARKO 1:14
Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,


MARKO 1:15
nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani Uthenga Wabwino.


MARKO 1:24
Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.


MARKO 2:7
Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?


MARKO 2:12
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.


MARKO 2:26
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?


MARKO 3:11
Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.


MARKO 3:35
Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.


MARKO 4:11
Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo;


MARKO 4:26
Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;


MARKO 4:30
Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?


MARKO 5:7
ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.


MARKO 7:8
Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.


MARKO 7:9
Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu.


MARKO 7:13
muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.


MARKO 8:33
Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.


MARKO 9:1
Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.


MARKO 9:47
Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'Gehena;


MARKO 10:9
Chifukwa chake chimene Mulungu anachimanga pamodzi, asachilekanitse munthu.


MARKO 10:14
Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


MARKO 10:15
Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


MARKO 10:18
Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.


MARKO 10:23
Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!


MARKO 10:24
Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!


MARKO 10:25
Nkwa pafupi kuti ngamira ipyole diso la singano kuposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.


MARKO 10:27
Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


MARKO 11:22
Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu.


MARKO 12:14
Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


MARKO 12:17
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.


MARKO 12:24
Yesu ananena nao, Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu?


MARKO 12:26
simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?


MARKO 12:27
Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu.


MARKO 12:29
Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israele; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;


MARKO 12:30
ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.


MARKO 12:34
Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu.


MARKO 13:19
Pakuti masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso, nthawi zonse.


MARKO 14:25
Ndipo ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.


MARKO 15:34
Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?


MARKO 15:39
Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.


MARKO 15:43
anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu.


MARKO 16:19
Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.


LUKA 1:6
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


LUKA 1:8
Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu,


LUKA 1:16
Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.


LUKA 1:19
Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.


LUKA 1:26
Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumudzi wa ku Galileya dzina lake Nazarete,


LUKA 1:30
Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu.


LUKA 1:32
Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:


LUKA 1:35
Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


LUKA 1:37
Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.


LUKA 1:47
ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,


LUKA 1:64
Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.


LUKA 1:67
Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,


LUKA 1:68
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


LUKA 1:78
chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.


LUKA 2:13
Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,


LUKA 2:14
Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


LUKA 2:20
Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.


LUKA 2:28
pomwepo iye anamlandira Iye m'manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati,


LUKA 2:37
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.


LUKA 2:38
Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.


LUKA 2:40
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.


LUKA 2:52
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.


LUKA 3:2
pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu.


LUKA 3:6
ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.


LUKA 3:8
Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.


LUKA 3:38
mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.


LUKA 4:3
Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.


LUKA 4:8
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.


LUKA 4:9
Ndipo anamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;


LUKA 4:12
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


LUKA 4:34
Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.


LUKA 4:41
Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.


LUKA 4:43
Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumidzi yinanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.


LUKA 5:1
Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


LUKA 5:21
Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?


LUKA 5:25
Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu.


LUKA 5:26
Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.


LUKA 6:4
kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?


LUKA 6:12
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.


LUKA 6:20
Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.


LUKA 7:16
Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.


LUKA 7:28
Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.


LUKA 7:29
Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.


LUKA 7:30
Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.


LUKA 8:1
Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,


LUKA 8:10
Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.


LUKA 8:11
Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu.


LUKA 8:21
Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita.


LUKA 8:28
Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau akulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.


LUKA 8:39
Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumudzi wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.


LUKA 9:2
Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.


LUKA 9:11
Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.


LUKA 9:20
Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu.


LUKA 9:27
Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.


LUKA 9:43
Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,


LUKA 9:60
Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.


LUKA 9:62
Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.


LUKA 10:9
ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako,


LUKA 10:11
Lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.


LUKA 10:27
Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.


LUKA 11:20
Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.


LUKA 11:28
Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.


LUKA 11:42
Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.


LUKA 11:49
Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;


LUKA 12:6
Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;


LUKA 12:8
Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa Munthu adzamvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu;


LUKA 12:9
Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.


LUKA 12:20
Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?


LUKA 12:21
Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.


LUKA 12:24
Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!


LUKA 12:28
Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wa kuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?


LUKA 13:13
Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.


LUKA 13:18
Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani?


LUKA 13:20
Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani?


LUKA 13:28
Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.


LUKA 13:29
Ndipo anthu adzachokera kum'mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu.


LUKA 14:15
Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.


LUKA 15:10
Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.


LUKA 16:13
Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.


LUKA 16:15
Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.


LUKA 16:16
Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kulowamo.


LUKA 17:15
Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau akulu;


LUKA 17:18
Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?


LUKA 17:20
Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;


LUKA 17:21
ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.


LUKA 18:2
nanena, M'mudzi mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu.


LUKA 18:4
Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu;


LUKA 18:7
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?


LUKA 18:11
Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


LUKA 18:13
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


LUKA 18:16
Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.


LUKA 18:17
Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.


LUKA 18:19
Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.


LUKA 18:24
Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu!


LUKA 18:25
Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.


LUKA 18:27
Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.


LUKA 18:29
Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum'bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu,


LUKA 18:43
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.


LUKA 19:11
Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.


LUKA 19:37
Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;


LUKA 20:21
Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;


LUKA 20:25
Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


LUKA 20:36
Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.


LUKA 20:37
Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.


LUKA 20:38
Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.


LUKA 21:31
Inde chotero inunso, pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.


LUKA 22:16
pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.


LUKA 22:18
pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.


LUKA 22:69
Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthu adzakhala pa dzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.


LUKA 22:70
Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo Iye anati kwa iwo, Munena kuti ndine.


LUKA 23:35
Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.


LUKA 23:40
Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku?


LUKA 23:47
Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.


LUKA 23:51
(amene sanavomereze kuweruza kwao ndi ntchito yao) wa ku Arimatea, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu,


LUKA 24:19
Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;


LUKA 24:53
ndipo anakhala chikhalire m'Kachisi, nalikuyamika Mulungu. Amen.


YOHANE 1:1
Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.


YOHANE 1:2
Awa anali pachiyambi kwa Mulungu.


YOHANE 1:6
Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane.


YOHANE 1:12
Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;


YOHANE 1:13
amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.


YOHANE 1:18
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.


YOHANE 1:29
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


YOHANE 1:34
Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.


YOHANE 1:36
ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!


YOHANE 1:49
Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


YOHANE 1:51
Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.


YOHANE 3:2
Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


YOHANE 3:3
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:5
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.


YOHANE 3:17
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.


YOHANE 3:18
Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.


YOHANE 3:21
Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.


YOHANE 3:33
Iye amene analandira umboni wake anaikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona.


YOHANE 3:34
Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.


YOHANE 3:36
Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.


YOHANE 4:10
Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


YOHANE 4:24
Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.


YOHANE 5:18
Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.


YOHANE 5:25
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


YOHANE 5:42
Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.


YOHANE 5:44
Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?


YOHANE 6:27
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


YOHANE 6:28
Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?


YOHANE 6:29
Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.


YOHANE 6:33
Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.


YOHANE 6:45
Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.


YOHANE 6:46
Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.


YOHANE 6:69
Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.


YOHANE 7:17
Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.


YOHANE 8:20
Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa m'Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.


YOHANE 8:40
Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite.


YOHANE 8:41
Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwa ife m'chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.


YOHANE 8:42
Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.


YOHANE 8:47
Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.


YOHANE 8:54
Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;


YOHANE 9:3
Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.


YOHANE 9:16
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.


YOHANE 9:24
Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.


YOHANE 9:29
Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo.


YOHANE 9:31
Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.


YOHANE 9:33
Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.


YOHANE 10:33
Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.


YOHANE 10:35
Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),


YOHANE 10:36
kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?


YOHANE 11:4
Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


YOHANE 11:22
Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu.


YOHANE 11:27
Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.


YOHANE 11:40
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?


YOHANE 11:52
ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo.


YOHANE 12:43
pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.


YOHANE 13:3
Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


YOHANE 13:31
Tsono m'mene adatuluka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa Munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa Iye;


YOHANE 13:32
ndipo Mulungu adzamlemekeza Iye mwa Iye yekha, adzamlemekeza Iye tsopano apa.


YOHANE 14:1
Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.


YOHANE 16:2
Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


YOHANE 16:30
Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti munatuluka kwa Mulungu.


YOHANE 17:3
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


YOHANE 19:7
Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.


YOHANE 20:17
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


YOHANE 20:28
Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.


YOHANE 20:31
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.


YOHANE 21:19
Koma ichi ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:3
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:11
ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:17
Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:22
Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:23
ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:24
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:30
Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:32
Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:33
Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:36
Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:39
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:47
nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:8
Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:9
Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu;


MACHITIDWE A ATUMWI 3:13
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:15
ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:18
Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:21
amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:22
Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu zilizonse akalankhule nanu.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:25
Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:26
Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:10
zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:19
Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:21
Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:24
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:31
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:4
Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m'manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:29
Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:30
Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpachika pamtengo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:31
Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:32
Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:39
koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:2
Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:7
Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:11
Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:2
Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harani;


MACHITIDWE A ATUMWI 7:4
Pamenepo anatuluka m'dziko la Akaldeya namanga m'Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;


MACHITIDWE A ATUMWI 7:6
Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:7
Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:9
Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:17
Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka m'Ejipito,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:20
Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wake:


MACHITIDWE A ATUMWI 7:25
Ndipo anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sanazindikira.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:32
akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isaki, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:35
Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:37
Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:42
Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?


MACHITIDWE A ATUMWI 7:43
Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:45
Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;


MACHITIDWE A ATUMWI 7:46
amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:55
Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:56
nati, Taonani, ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:10
ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:12
Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:14
Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;


MACHITIDWE A ATUMWI 8:20
Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:21
Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:20
Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:2
ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:3
Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:4
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:15
Ndipo mau anamdzeranso nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:22
Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:28
ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;


MACHITIDWE A ATUMWI 10:31
nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:33
Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:34
Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho;


MACHITIDWE A ATUMWI 10:38
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:40
Ameneyo, Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti aonetsedwe,


MACHITIDWE A ATUMWI 10:41
si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:42
Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:46
Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,


MACHITIDWE A ATUMWI 11:1
Koma atumwi ndi abale akukhala m'Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:9
Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m'mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:17
Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?


MACHITIDWE A ATUMWI 11:18
Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:23
ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


MACHITIDWE A ATUMWI 12:5
Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.


MACHITIDWE A ATUMWI 12:22
Ndipo anthu osonkhanidwawo anafuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai.


MACHITIDWE A ATUMWI 12:23
Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.


MACHITIDWE A ATUMWI 12:24
Koma mau a Mulungu anakula, nachulukitsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:5
Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:7
ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:16
Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:17
Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:21
Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:23
Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:26
Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:30
Koma Mulungu anamuukitsa Iye kwa akufa;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:33
kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:36
Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:37
koma Iye amene Mulungu anamuukitsa sanaona chivundi.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:43
Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m'chisomo cha Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:44
Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:46
Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:48
Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:15
nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:


MACHITIDWE A ATUMWI 14:22
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:26
komweko anachoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adaimalizayo.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:27
Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:4
Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:7
Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:8
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;


MACHITIDWE A ATUMWI 15:10
Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?


MACHITIDWE A ATUMWI 15:12
Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:14
Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:19
Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 16:10
Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:14
Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumudzi wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:17
Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:25
Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;


MACHITIDWE A ATUMWI 16:34
Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:13
Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereanso, anadza komwekonso, nautsa, navuta makamu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:23
Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:24
Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja;


MACHITIDWE A ATUMWI 17:27
kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife;


MACHITIDWE A ATUMWI 17:29
Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:30
Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;


MACHITIDWE A ATUMWI 18:7
Ndipo anachoka kumeneko, nalowa m'nyumba ya munthu, dzina lake Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yake inayandikizana ndi sunagoge.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:11
Ndipo anakhala komwe chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mau a Mulungu mwa iwo.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:13
kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana chilamulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:21
koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:26
ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:8
Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:11
Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo;


MACHITIDWE A ATUMWI 19:27
ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:37
Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za m'Kachisi, kapena ochitira mulungu wathu mwano.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:21
ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:24
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:27
Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:28
Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:32
Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:19
Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:20
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;


MACHITIDWE A ATUMWI 22:3
Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;


MACHITIDWE A ATUMWI 22:14
Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:1
Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbu mtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:3
Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?


MACHITIDWE A ATUMWI 23:4
Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?


MACHITIDWE A ATUMWI 24:14
Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;


MACHITIDWE A ATUMWI 24:15
ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:16
M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:6
Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu analichita kwa makolo athu;


MACHITIDWE A ATUMWI 26:7
kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:8
Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa?


MACHITIDWE A ATUMWI 26:18
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:20
komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:22
Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika;


MACHITIDWE A ATUMWI 26:29
Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:23
Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,


MACHITIDWE A ATUMWI 27:24
nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:25
Chifukwa chake, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:35
Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:6
Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:15
Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:23
Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Teot 28:28
Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


Teot 28:31
ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.


1 AKORINTO 1:1
Paulo, woitanidwa akhale mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo,


1 AKORINTO 1:2
kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


1 AKORINTO 1:3
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


1 AKORINTO 1:4
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chinapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;


1 AKORINTO 1:9
Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.


1 AKORINTO 1:14
Ndiyamika Mulungu kuti sindinabatiza mmodzi yense wa inu, koma Krispo ndi Gayo;


1 AKORINTO 1:18
Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.


1 AKORINTO 1:20
Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?


1 AKORINTO 1:21
Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.


1 AKORINTO 1:24
koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.


1 AKORINTO 1:25
Chifukwa kuti chipusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.


1 AKORINTO 1:27
koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;


1 AKORINTO 1:28
ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko;


1 AKORINTO 1:29
kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.


1 AKORINTO 1:30
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


1 AKORINTO 2:1
Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu.


1 AKORINTO 2:5
kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.


1 AKORINTO 2:7
koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,


1 AKORINTO 2:9
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, nisizinalowa mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.


1 AKORINTO 2:10
Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.


1 AKORINTO 2:11
Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.


1 AKORINTO 2:12
Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.


1 AKORINTO 2:14
Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.


1 AKORINTO 3:6
Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.


1 AKORINTO 3:7
Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.


1 AKORINTO 3:9
Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.


1 AKORINTO 3:10
Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.


1 AKORINTO 3:16
Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?


1 AKORINTO 3:17
Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.


1 AKORINTO 3:19
Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;


1 AKORINTO 3:23
koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.


1 AKORINTO 4:1
Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.


1 AKORINTO 4:5
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


1 AKORINTO 4:9
Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.


1 AKORINTO 4:20
Pakuti ufumu wa Mulungu suli m'mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani?


1 AKORINTO 5:13
koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.


1 AKORINTO 6:9
Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,


1 AKORINTO 6:10
kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


1 AKORINTO 6:11
Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


1 AKORINTO 6:13
Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;


1 AKORINTO 6:14
koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.


1 AKORINTO 6:19
Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.


1 AKORINTO 6:20
Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.


1 AKORINTO 7:7
Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.


1 AKORINTO 7:15
Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M'milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.


1 AKORINTO 7:17
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse.


1 AKORINTO 7:19
Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.


1 AKORINTO 7:24
Yense, m'mene anaitanidwamo, abale, akhale momwemo ndi Mulungu.


1 AKORINTO 7:40
Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.


1 AKORINTO 8:3
Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.


1 AKORINTO 8:4
Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.


1 AKORINTO 8:6
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.


1 AKORINTO 8:8
Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako.


1 AKORINTO 9:9
Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe?


1 AKORINTO 9:21
kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.


1 AKORINTO 10:5
Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'chipululu.


1 AKORINTO 10:13
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


1 AKORINTO 10:20
Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.


1 AKORINTO 10:31
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


1 AKORINTO 10:32
Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu;


1 AKORINTO 11:3
Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.


1 AKORINTO 11:7
Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.


1 AKORINTO 11:12
Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu.


1 AKORINTO 11:13
Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?


1 AKORINTO 11:16
Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Mpingo wa Mulungu.


1 AKORINTO 11:22
Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.


1 AKORINTO 12:3
Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


1 AKORINTO 12:6
Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.


1 AKORINTO 12:18
Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna.


1 AKORINTO 12:24
Koma zokoma zathu zilibe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho;


1 AKORINTO 12:28
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.


1 AKORINTO 14:2
Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.


1 AKORINTO 14:18
Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;


1 AKORINTO 14:25
zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.


1 AKORINTO 14:28
Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.


1 AKORINTO 14:33
pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.


1 AKORINTO 14:36
Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha?


1 AKORINTO 15:9
Pakuti ine ndili wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu.


1 AKORINTO 15:10
Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhala chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


1 AKORINTO 15:15
Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.


1 AKORINTO 15:24
Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.


1 AKORINTO 15:28
Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.


1 AKORINTO 15:34
Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.


1 AKORINTO 15:38
koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lakelake.


1 AKORINTO 15:50
Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.


1 AKORINTO 15:57
koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


2 AKORINTO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya monse:


2 AKORINTO 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 AKORINTO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,


2 AKORINTO 1:4
wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.


2 AKORINTO 1:9
koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;


2 AKORINTO 1:12
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


2 AKORINTO 1:18
Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhala eya ndi iai.


2 AKORINTO 1:19
Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.


2 AKORINTO 1:20
Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.


2 AKORINTO 1:21
Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;


2 AKORINTO 1:23
Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.


2 AKORINTO 2:14
Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.


2 AKORINTO 2:15
Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa;


2 AKORINTO 2:17
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.


2 AKORINTO 3:3
popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.


2 AKORINTO 3:4
Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu:


2 AKORINTO 3:5
si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;


2 AKORINTO 3:16
Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, chophimbacho chichotsedwa.


2 AKORINTO 4:2
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


2 AKORINTO 4:4
mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


2 AKORINTO 4:6
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


2 AKORINTO 4:7
Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


2 AKORINTO 4:15
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.


2 AKORINTO 5:1
Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba.


2 AKORINTO 5:5
Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.


2 AKORINTO 5:11
Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.


2 AKORINTO 5:13
Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.


2 AKORINTO 5:18
Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;


2 AKORINTO 5:19
ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.


2 AKORINTO 5:20
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.


2 AKORINTO 5:21
Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


2 AKORINTO 6:1
Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,


2 AKORINTO 6:4
koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,


2 AKORINTO 6:7
m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,


2 AKORINTO 6:16
Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.


2 AKORINTO 7:1
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.


2 AKORINTO 7:6
Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;


2 AKORINTO 7:9
Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kalikonse.


2 AKORINTO 7:10
Pakuti chisoni cha kwa Mulungu titembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


2 AKORINTO 7:11
Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.


2 AKORINTO 7:12
Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.


2 AKORINTO 8:1
Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwa Mipingo ya ku Masedoniya,


2 AKORINTO 8:5
ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.


2 AKORINTO 8:16
Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.


2 AKORINTO 9:7
Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.


2 AKORINTO 9:8
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;


2 AKORINTO 9:11
polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.


2 AKORINTO 9:12
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;


2 AKORINTO 9:13
popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;


2 AKORINTO 9:14
ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.


2 AKORINTO 9:15
Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.


2 AKORINTO 10:4
(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);


2 AKORINTO 10:5
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;


2 AKORINTO 10:13
Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.


2 AKORINTO 11:2
Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.


2 AKORINTO 11:7
Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?


2 AKORINTO 11:11
Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.


2 AKORINTO 11:31
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.


2 AKORINTO 12:2
Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.


2 AKORINTO 12:3
Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu),


2 AKORINTO 12:19
Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu.


2 AKORINTO 12:21
kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.


2 AKORINTO 13:4
pakuti anapachikidwa m'ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.


2 AKORINTO 13:7
Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.


2 AKORINTO 13:11
Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.


2 AKORINTO 13:14
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


AGALATIYA 1:1
Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),


AGALATIYA 1:3
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,


AGALATIYA 1:4
amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;


AGALATIYA 1:10
Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.


AGALATIYA 1:13
Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,


AGALATIYA 1:15
Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,


AGALATIYA 1:20
Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.


AGALATIYA 1:24
ndipo analemekeza Mulungu mwa ine.


AGALATIYA 2:6
Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezera ine kanthu;


AGALATIYA 2:19
Pakuti ine mwa lamulo ndafa kulamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.


AGALATIYA 2:20
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.


AGALATIYA 2:21
Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe.


AGALATIYA 3:6
Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye chilungamo,


AGALATIYA 3:8
Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.


AGALATIYA 3:11
Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro;


AGALATIYA 3:17
Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.


AGALATIYA 3:18
Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.


AGALATIYA 3:20
Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.


AGALATIYA 3:21
Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.


AGALATIYA 3:26
Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


AGALATIYA 4:4
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,


AGALATIYA 4:6
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!


AGALATIYA 4:7
Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.


AGALATIYA 4:8
Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;


AGALATIYA 4:9
koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?


AGALATIYA 4:14
ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputsa, kapena sichinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini.


AGALATIYA 5:21
njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


AGALATIYA 6:7
Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.


AGALATIYA 6:16
Ndipo onse amene atsatsa chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.


AEFESO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:


AEFESO 1:2
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


AEFESO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


AEFESO 1:17
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;


AEFESO 2:4
koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,


AEFESO 2:8
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;


AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


AEFESO 2:12
kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.


AEFESO 2:16
ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;


AEFESO 2:19
Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;


AEFESO 2:22
chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.


AEFESO 3:2
ngatitu munamva za udindo wa chisomo cha Mulungu chimene anandipatsa ine cha kwa inu;


AEFESO 3:7
umene anandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene anandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake.


AEFESO 3:9
ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;


AEFESO 3:10
kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,


AEFESO 3:19
ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.


AEFESO 4:6
Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.


AEFESO 4:13
kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.


AEFESO 4:18
odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao;


AEFESO 4:24
nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.


AEFESO 4:30
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.


AEFESO 4:32
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.


AEFESO 5:1
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;


AEFESO 5:2
ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


AEFESO 5:5
Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa m'ufumu wa Khristu ndi Mulungu.


AEFESO 5:6
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.


AEFESO 5:20
ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;


AEFESO 6:6
si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;


AEFESO 6:11
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.


AEFESO 6:13
Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.


AEFESO 6:17
Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;


AEFESO 6:23
Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.


AFILIPI 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


AFILIPI 1:3
Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;


AFILIPI 1:8
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 1:11
odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.


AFILIPI 1:14
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


AFILIPI 1:28
osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;


AFILIPI 2:6
ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu,


AFILIPI 2:9
Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,


AFILIPI 2:11
ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.


AFILIPI 2:13
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.


AFILIPI 2:15
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


AFILIPI 2:27
Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.


AFILIPI 3:3
pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


AFILIPI 3:9
ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;


AFILIPI 3:14
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 3:15
Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu;


AFILIPI 3:19
chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


AFILIPI 4:6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.


AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 4:9
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.


AFILIPI 4:18
Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fundo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


AFILIPI 4:19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.


AFILIPI 4:20
Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen.


AKOLOSE 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,


AKOLOSE 1:2
kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a m'Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.


AKOLOSE 1:3
Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi kupempherera inu nthawi zonse,


AKOLOSE 1:6
umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu, kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira chisomo cha Mulungu m'choonadi;


AKOLOSE 1:10
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;


AKOLOSE 1:15
amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse;


AKOLOSE 1:25
amene ndinakhala mtumiki wake, monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakuchitira inu, wakukwaniritsa mau a Mulungu,


AKOLOSE 1:27
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;


AKOLOSE 2:2
kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'chikondi, kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu, ndiye Khristu,


AKOLOSE 2:9
pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,


AKOLOSE 2:12
popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.


AKOLOSE 2:19
kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.


AKOLOSE 3:1
Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.


AKOLOSE 3:3
Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.


AKOLOSE 3:6
chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;


AKOLOSE 3:12
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;


AKOLOSE 3:16
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


AKOLOSE 3:17
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


AKOLOSE 4:3
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,


AKOLOSE 4:11
ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.


AKOLOSE 4:12
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m'mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.


1 ATESALONIKA 1:1
Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere.


1 ATESALONIKA 1:2
Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu;


1 ATESALONIKA 1:3
ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;


1 ATESALONIKA 1:4
podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, chisankhidwe chanu,


1 ATESALONIKA 1:8
Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.


1 ATESALONIKA 1:9
Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,


1 ATESALONIKA 2:2
koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


1 ATESALONIKA 2:4
komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.


1 ATESALONIKA 2:5
Pakuti sitinayenda nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;


1 ATESALONIKA 2:8
kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.


1 ATESALONIKA 2:9
Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.


1 ATESALONIKA 2:10
Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


1 ATESALONIKA 2:12
ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.


1 ATESALONIKA 2:13
Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.


1 ATESALONIKA 2:14
Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;


1 ATESALONIKA 2:15
amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;


1 ATESALONIKA 3:2
ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m'Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;


1 ATESALONIKA 3:9
Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;


1 ATESALONIKA 3:11
Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu;


1 ATESALONIKA 3:13
kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.


1 ATESALONIKA 4:1
Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.


1 ATESALONIKA 4:3
Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;


1 ATESALONIKA 4:5
kosati m'chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;


1 ATESALONIKA 4:7
Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso.


1 ATESALONIKA 4:8
Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


1 ATESALONIKA 4:9
Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake;


1 ATESALONIKA 4:14
Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.


1 ATESALONIKA 4:16
Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;


1 ATESALONIKA 5:9
Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,


1 ATESALONIKA 5:18
M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.


1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 1:1
Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu:


2 ATESALONIKA 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 1:3
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;


2 ATESALONIKA 1:4
kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;


2 ATESALONIKA 1:5
ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;


2 ATESALONIKA 1:6
popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso,


2 ATESALONIKA 1:8
m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;


2 ATESALONIKA 1:11
Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse chomkomera chonse, ndi ntchito ya chikhulupiriro mumphamvu;


2 ATESALONIKA 1:12
kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


2 ATESALONIKA 2:4
amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.


2 ATESALONIKA 2:11
Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;


2 ATESALONIKA 2:13
Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;


2 ATESALONIKA 2:16
Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,


2 ATESALONIKA 3:5
Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu.


1 TIMOTEO 1:1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu:


1 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


1 TIMOTEO 1:4
kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;


1 TIMOTEO 1:11
monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.


1 TIMOTEO 1:17
Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.


1 TIMOTEO 2:2
chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.


1 TIMOTEO 2:3
Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;


1 TIMOTEO 2:5
Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu,


1 TIMOTEO 2:10
komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.


1 TIMOTEO 3:5
Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?


1 TIMOTEO 3:15
kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.


1 TIMOTEO 3:16
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.


1 TIMOTEO 4:3
a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.


1 TIMOTEO 4:4
Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;


1 TIMOTEO 4:5
pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.


1 TIMOTEO 4:10
Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.


1 TIMOTEO 5:4
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.


1 TIMOTEO 5:5
Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


1 TIMOTEO 5:21
Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.


1 TIMOTEO 6:1
Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.


1 TIMOTEO 6:11
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.


1 TIMOTEO 6:13
Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato;


1 TIMOTEO 6:17
Lamulira iwo achuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


2 TIMOTEO 1:1
Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Khristu Yesu,


2 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.


2 TIMOTEO 1:3
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbu mtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,


2 TIMOTEO 1:6
Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.


2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.


2 TIMOTEO 1:8
Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;


2 TIMOTEO 2:9
m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.


2 TIMOTEO 2:15
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.


2 TIMOTEO 2:19
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


2 TIMOTEO 2:25
wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,


2 TIMOTEO 3:4
achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;


2 TIMOTEO 3:16
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:


2 TIMOTEO 3:17
kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.


2 TIMOTEO 4:1
Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake;


TITO 1:1
Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,


TITO 1:2
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;


TITO 1:3
koma pa nyengo za Iye yekha anaonetsa mau ake muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu:


TITO 1:4
kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.


TITO 1:7
Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;


TITO 1:16
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.


TITO 2:5
akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.


TITO 2:10
osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.


TITO 2:11
Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse,


TITO 2:13
akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;


TITO 3:4
Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka,


TITO 3:8
Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;


FILEMONI 1:3
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


FILEMONI 1:4
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga,


AHEBRI 1:1
Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


AHEBRI 1:6
Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.


AHEBRI 1:8
Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.


AHEBRI 1:9
Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.


AHEBRI 2:4
pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


AHEBRI 2:9
Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.


AHEBRI 2:13
Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.


AHEBRI 2:17
Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.


AHEBRI 3:4
Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.


AHEBRI 3:12
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


AHEBRI 4:4
Pakuti wanena pena za tsiku lachisanu ndi chiwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse.


AHEBRI 4:9
Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.


AHEBRI 4:10
Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.


AHEBRI 4:12
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.


AHEBRI 4:14
Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


AHEBRI 5:1
Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:


AHEBRI 5:4
Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.


AHEBRI 5:7
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


AHEBRI 5:10
wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


AHEBRI 5:12
Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.


AHEBRI 6:1
Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,


AHEBRI 6:3
Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.


AHEBRI 6:5
nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza,


AHEBRI 6:6
koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.


AHEBRI 6:7
Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:


AHEBRI 6:10
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


AHEBRI 6:13
Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,


AHEBRI 6:17
Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;


AHEBRI 6:18
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


AHEBRI 7:1
Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,


AHEBRI 7:3
wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.


AHEBRI 7:19
(pakuti chilamulo sichinachitira kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu.


AHEBRI 7:25
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.


AHEBRI 8:10
Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:


AHEBRI 9:14
koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


AHEBRI 9:20
nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulani.


AHEBRI 9:24
Pakuti Khristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;


AHEBRI 10:7
pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.


AHEBRI 10:12
koma Iye, m'mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire;


AHEBRI 10:21
ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;


AHEBRI 10:29
ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


AHEBRI 10:31
Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.


AHEBRI 10:36
Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.


AHEBRI 11:3
Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zoonekazo.


AHEBRI 11:4
Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.


AHEBRI 11:5
Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;


AHEBRI 11:6
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.


AHEBRI 11:7
Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.


AHEBRI 11:10
pakuti analindirira mudzi wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.


AHEBRI 11:16
Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.


AHEBRI 11:19
poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.


AHEBRI 11:25
nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;


AHEBRI 11:40
popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife.


AHEBRI 12:2
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


AHEBRI 12:7
Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?


AHEBRI 12:15
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


AHEBRI 12:22
Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,


AHEBRI 12:23
ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,


AHEBRI 12:28
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.


AHEBRI 12:29
Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.


AHEBRI 13:4
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


AHEBRI 13:7
Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.


AHEBRI 13:15
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.


AHEBRI 13:16
Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.


AHEBRI 13:20
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


YAKOBO 1:1
Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


YAKOBO 1:5
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.


YAKOBO 1:13
Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:


YAKOBO 1:20
Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.


YAKOBO 1:26
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


YAKOBO 1:27
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.


YAKOBO 2:5
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


YAKOBO 2:19
Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.


YAKOBO 2:23
ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.


YAKOBO 3:9
Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;


YAKOBO 4:4
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


YAKOBO 4:6
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.


YAKOBO 4:7
Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.


YAKOBO 4:8
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


YAKOBO 4:15
Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.


1 PETRO 1:2
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


1 PETRO 1:3
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


1 PETRO 1:5
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.


1 PETRO 1:21
chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


1 PETRO 1:23
inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.


1 PETRO 1:25
koma Mau a Mulungu akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.


1 PETRO 2:4
amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,


1 PETRO 2:5
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


1 PETRO 2:10
inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.


1 PETRO 2:12
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


1 PETRO 2:15
Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;


1 PETRO 2:16
monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.


1 PETRO 2:17
Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.


1 PETRO 2:19
Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.


1 PETRO 2:20
Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.


1 PETRO 3:4
koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.


1 PETRO 3:5
Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;


1 PETRO 3:17
Pakuti, kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu.


1 PETRO 3:18
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


1 PETRO 3:20
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;


1 PETRO 3:21
chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


1 PETRO 3:22
amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


1 PETRO 4:2
kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.


1 PETRO 4:6
Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m'thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.


1 PETRO 4:10
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;


1 PETRO 4:11
akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.


1 PETRO 4:14
Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.


1 PETRO 4:16
koma akamva zowawa ngati mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili.


1 PETRO 4:17
Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?


1 PETRO 4:19
Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.


1 PETRO 5:2
Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


1 PETRO 5:5
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


1 PETRO 5:6
Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;


1 PETRO 5:10
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.


1 PETRO 5:12
Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.


2 PETRO 1:1
Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:


2 PETRO 1:2
Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.


2 PETRO 1:3
Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha;


2 PETRO 1:4
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili pa dziko lapansi m'chilakolako.


2 PETRO 1:17
Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;


2 PETRO 1:21
pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


2 PETRO 2:4
Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;


2 PETRO 3:5
Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;


2 PETRO 3:12
akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.


1 YOHANE 1:5
Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.


1 YOHANE 2:5
koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;


1 YOHANE 2:14
Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.


1 YOHANE 2:17
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.


1 YOHANE 3:1
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.


1 YOHANE 3:2
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


1 YOHANE 3:8
iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.


1 YOHANE 3:9
Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.


1 YOHANE 3:10
M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.


1 YOHANE 3:17
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?


1 YOHANE 3:20
m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.


1 YOHANE 3:21
Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu;


1 YOHANE 4:1
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.


1 YOHANE 4:2
M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu;


1 YOHANE 4:3
ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,


1 YOHANE 4:4
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;


1 YOHANE 4:6
Ife ndife ochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa choonadi, ndi mzimu wa chisokeretso.


1 YOHANE 4:7
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.


1 YOHANE 4:8
Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.


1 YOHANE 4:9
Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.


1 YOHANE 4:10
Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.


1 YOHANE 4:11
Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.


1 YOHANE 4:12
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;


1 YOHANE 4:15
Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.


1 YOHANE 4:16
Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.


1 YOHANE 4:20
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.


1 YOHANE 4:21
Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.


1 YOHANE 5:1
Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


1 YOHANE 5:2
Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake.


1 YOHANE 5:3
Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.


1 YOHANE 5:4
Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.


1 YOHANE 5:5
Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?


1 YOHANE 5:9
Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake.


1 YOHANE 5:10
Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.


1 YOHANE 5:11
Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.


1 YOHANE 5:12
Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.


1 YOHANE 5:13
Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.


1 YOHANE 5:16
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


1 YOHANE 5:18
Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


1 YOHANE 5:19
Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.


1 YOHANE 5:20
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


2 YOHANE 1:3
Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi.


2 YOHANE 1:9
Yense wakupitirira, wosakhala m'chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m'chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana.


3 YOHANE 1:6
amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:


3 YOHANE 1:11
Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuona Mulungu.


YUDA 1:1
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:


YUDA 1:4
Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.


YUDA 1:21
mudzisunge nokha m'chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha.


YUDA 1:25
kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.


CHIVUMBULUTSO 1:1
Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


CHIVUMBULUTSO 1:2
amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona.


CHIVUMBULUTSO 1:6
natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.


CHIVUMBULUTSO 1:8
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


CHIVUMBULUTSO 1:9
Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.


CHIVUMBULUTSO 2:7
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 2:18
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:


CHIVUMBULUTSO 3:1
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


CHIVUMBULUTSO 3:2
Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga.


CHIVUMBULUTSO 3:12
Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa m'Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m'Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.


CHIVUMBULUTSO 3:14
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:


CHIVUMBULUTSO 4:5
Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


CHIVUMBULUTSO 4:8
Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.


CHIVUMBULUTSO 4:11
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.


CHIVUMBULUTSO 5:6
Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.


CHIVUMBULUTSO 5:9
Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


CHIVUMBULUTSO 5:10
ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.


CHIVUMBULUTSO 6:9
Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao:


CHIVUMBULUTSO 7:2
Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau akulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,


CHIVUMBULUTSO 7:3
nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.


CHIVUMBULUTSO 7:10
ndipo afuula ndi mau akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.


CHIVUMBULUTSO 7:11
Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu,


CHIVUMBULUTSO 7:12
ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.


CHIVUMBULUTSO 7:15
Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku m'Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,


CHIVUMBULUTSO 7:17
chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.


CHIVUMBULUTSO 8:2
Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.


CHIVUMBULUTSO 8:4
Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 9:4
Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena chabiriwiri chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pao ndiwo.


CHIVUMBULUTSO 9:13
Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu,


CHIVUMBULUTSO 10:7
komatu m'masiku a mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri m'mene iye adzayamba kuomba lipenga, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri.


CHIVUMBULUTSO 11:1
Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.


CHIVUMBULUTSO 11:11
Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chilili; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya.


CHIVUMBULUTSO 11:13
Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.


CHIVUMBULUTSO 11:16
Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,


CHIVUMBULUTSO 11:17
nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.


CHIVUMBULUTSO 11:19
Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali m'Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, m'Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala akulu.


CHIVUMBULUTSO 12:5
Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake.


CHIVUMBULUTSO 12:6
Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.


CHIVUMBULUTSO 12:10
Ndipo ndinamva mau akulu m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.


CHIVUMBULUTSO 12:17
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, nichinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.


CHIVUMBULUTSO 13:6
Ndipo chinatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala m'Mwamba.


CHIVUMBULUTSO 14:4
Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.


CHIVUMBULUTSO 14:7
ndi kunena ndi mau akulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.


CHIVUMBULUTSO 14:10
iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulufure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa;


CHIVUMBULUTSO 14:12
Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.


CHIVUMBULUTSO 14:19
Ndipo mngelo anaponya chisenga chake kudziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 15:1
Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 15:2
Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anachilaka chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 15:3
Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


CHIVUMBULUTSO 15:7
Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.


CHIVUMBULUTSO 15:8
Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.


CHIVUMBULUTSO 16:1
Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 16:7
Ndipo ndinamva wa pa guwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.


CHIVUMBULUTSO 16:9
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amchitire ulemu.


CHIVUMBULUTSO 16:11
nachitira mwano Mulungu wa m'Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalapa ntchito zao.


CHIVUMBULUTSO 16:14
pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.


CHIVUMBULUTSO 16:19
Ndipo chimudzi chachikulucho chidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo wamkali wa mkwiyo wake.


CHIVUMBULUTSO 16:21
Ndipo anatsika kumwamba matalala akulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.


CHIVUMBULUTSO 17:17
Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 18:5
pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.


CHIVUMBULUTSO 18:8
Chifukwa chake miliri yake idzadza m'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.


CHIVUMBULUTSO 18:20
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


CHIVUMBULUTSO 19:1
Zitatha izi ndinamva ngati mau akulu a khamu lalikulu m'Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;


CHIVUMBULUTSO 19:4
Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, nizinena, Amen; Aleluya.


CHIVUMBULUTSO 19:5
Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, ang'ono ndi akulu.


CHIVUMBULUTSO 19:6
Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


CHIVUMBULUTSO 19:9
Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 19:10
Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.


CHIVUMBULUTSO 19:13
Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 19:15
Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.


CHIVUMBULUTSO 19:17
Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anafuula ndi mau akulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu,


CHIVUMBULUTSO 20:4
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chilombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.


CHIVUMBULUTSO 20:6
Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.


CHIVUMBULUTSO 21:2
Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.


CHIVUMBULUTSO 21:3
Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


CHIVUMBULUTSO 21:7
Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.


CHIVUMBULUTSO 21:10
Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika m'Mwamba kuchokera kwa Mulungu,


CHIVUMBULUTSO 21:11
ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;


CHIVUMBULUTSO 21:22
Ndipo sindinaona Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.


CHIVUMBULUTSO 21:23
Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.


CHIVUMBULUTSO 22:1
Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.


CHIVUMBULUTSO 22:3
Ndipo sipadzakhalanso temberero lililonse; ndipo mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ake adzamtumikira Iye,


CHIVUMBULUTSO 22:5
Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.


CHIVUMBULUTSO 22:6
Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga.


CHIVUMBULUTSO 22:9
Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 22:18
Ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mau a chinenero cha buku ili, Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu:


CHIVUMBULUTSO 22:19
ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.


Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi