MATEYU 5:9 |
Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
|
MATEYU 10:13 |
Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
|
MATEYU 10:34 |
Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.
|
MARKO 5:34 |
Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.
|
MARKO 9:50 |
Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.
|
LUKA 1:79 |
Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.
|
LUKA 2:14 |
Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.
|
LUKA 2:29 |
Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere;
|
LUKA 7:50 |
Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.
|
LUKA 8:48 |
Ndipo Iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.
|
LUKA 10:5 |
Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.
|
LUKA 10:6 |
Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.
|
LUKA 11:21 |
Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;
|
LUKA 12:51 |
Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;
|
LUKA 14:32 |
Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.
|
LUKA 19:38 |
nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere m'Mwamba, ndi ulemerero m'Mwambamwamba.
|
LUKA 19:42 |
nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.
|
LUKA 24:36 |
Ndipo pakulankhula izi iwowa, Iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu.
|
YOHANE 14:27 |
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
|
YOHANE 16:33 |
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
|
YOHANE 20:19 |
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.
|
YOHANE 20:21 |
Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.
|
YOHANE 20:26 |
Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.
|
MACHITIDWE A ATUMWI 9:31 |
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.
|
MACHITIDWE A ATUMWI 10:36 |
Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)
|
MACHITIDWE A ATUMWI 12:20 |
Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.
|
MACHITIDWE A ATUMWI 15:33 |
Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza.
|
MACHITIDWE A ATUMWI 16:36 |
Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.
|
Apostlagärningarna 24:2 |
Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,
|
1 AKORINTO 1:3 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
1 AKORINTO 7:15 |
Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M'milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.
|
1 AKORINTO 14:33 |
pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.
|
1 AKORINTO 16:11 |
chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.
|
2 AKORINTO 1:2 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
2 AKORINTO 13:11 |
Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.
|
AGALATIYA 1:3 |
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,
|
AGALATIYA 5:22 |
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
|
AGALATIYA 6:16 |
Ndipo onse amene atsatsa chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.
|
AEFESO 1:2 |
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
AEFESO 2:14 |
Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,
|
AEFESO 2:15 |
atachotsa udani m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;
|
AEFESO 2:17 |
ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;
|
AEFESO 4:3 |
ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.
|
AEFESO 6:15 |
ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;
|
AEFESO 6:23 |
Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
AFILIPI 1:2 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
AFILIPI 4:7 |
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
|
AFILIPI 4:9 |
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
|
AKOLOSE 1:2 |
kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a m'Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.
|
AKOLOSE 1:20 |
mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'Mwamba.
|
AKOLOSE 3:15 |
Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.
|
1 ATESALONIKA 1:1 |
Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere.
|
1 ATESALONIKA 5:3 |
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
|
1 ATESALONIKA 5:13 |
ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
|
1 ATESALONIKA 5:23 |
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
|
2 ATESALONIKA 1:2 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
2 ATESALONIKA 3:16 |
Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.
|
1 TIMOTEO 1:2 |
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
|
2 TIMOTEO 1:2 |
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.
|
2 TIMOTEO 2:22 |
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
|
TITO 1:4 |
kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
|
FILEMONI 1:3 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
|
AHEBRI 7:2 |
amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;
|
AHEBRI 11:31 |
Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeka pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.
|
AHEBRI 12:11 |
Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.
|
AHEBRI 12:14 |
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
|
AHEBRI 13:20 |
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,
|
YAKOBO 2:16 |
ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?
|
YAKOBO 3:17 |
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
|
YAKOBO 3:18 |
Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.
|
1 PETRO 1:2 |
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.
|
1 PETRO 3:11 |
ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.
|
1 PETRO 5:14 |
Mupatsane moni ndi chipsompsono cha chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.
|
2 PETRO 1:2 |
Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.
|
2 PETRO 3:14 |
Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.
|
2 YOHANE 1:3 |
Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi.
|
3 YOHANE 1:15 |
Mtendere ukhale nawe. Akupereka moni abwenzi. Upereke moni kwa abwenzi ndi kutchula maina ao.
|
YUDA 1:2 |
Chifundo ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni.
|
CHIVUMBULUTSO 1:4 |
Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri m'Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;
|
CHIVUMBULUTSO 6:4 |
Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.
|
Chewa Bible 2014 |
Bible Society of Malawi |