A A A A A

Sakani
MATEYU 9:15
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? koma adzafika masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.


MATEYU 19:10
Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wace uti wotere, sikuli kwabwino kukwatira.


MATEYU 22:2
Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wace phwando la ukwati,


MATEYU 22:3
natumiza akapolo ace kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.


MATEYU 22:4
Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsya: idzani kuukwati.


MATEYU 22:8
Pomwepo inanena kwa akapolo ace, Za ukwati tsopano zapsya, koma oitanidwawo sanayenera.


MATEYU 22:9
Cifukwa cace pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene ali yense mukampeze, itanani kuukwatiku.


MATEYU 22:10
Ndipo akapolo ao anaturukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pacakudya.


MATEYU 22:11
Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosabvala cobvala ca ukwati;


MATEYU 22:12
nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala naco cobvala ca ukwati? Ndipo iye analibe mau.


MATEYU 22:30
Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.


MATEYU 24:38
Pakuti monga m'masiku aja, cisanafike cigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'cingalawa,


MATEYU 25:10
Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo, analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.


MARKO 2:19
Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.


LUKA 5:34
Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?


LUKA 12:36
ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.


LUKA 14:8
Pamene pali ponse waitanidwa iwe ndi munthu ku cakudya ca ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,


LUKA 20:35
koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dzikolijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.


YOHANE 2:1
Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amace wa Yesu anali komweko.


YOHANE 2:2
Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace anaitanidwa ku ukwatiwo.


1 AKORINTO 7:9
Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.


1 AKORINTO 7:28
Koma ungakhale ukwatira, sunacimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanacimwa. Koma otere adzakhala naco cisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.


1 TIMOTEO 4:3
akuletsa ukwati, osivitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti acikhulupiriro ndi ozindikira coonadi azilandire ndi ciyamiko.


1 TIMOTEO 5:11
Koma amasiyeang'ono uwakane; pakuti pamene ayambakumcitira Kristu cipongwe afuna kukwatiwa;


AHEBRI 13:4
Ukwati ucitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi acigololo adzawaweruza Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 19:7
Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.


CHIVUMBULUTSO 19:9
Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society