A A A A A

Sakani
MATEYU 2:2
nati, Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? cifukwa tinaona nyenyezi yace kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.


MATEYU 2:8
Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.


MATEYU 4:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.


MATEYU 15:9
Koma andilambira Ine kwacabe, Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.


MATEYU 28:17
Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.


MARKO 7:7
Koma andilambira Ine kwacabe, Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.


MARKO 15:19
Ndipo anampanda Iye pamutu pace ndi bango, namthira malobvu, nampindira maondo, namlambira.


LUKA 24:52
Ndipo 14 anamlambira iye, nabwera ku Yerusalemu ndi cimwemwe cacikuru;


YOHANE 4:20
Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.


YOHANE 4:21
Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.


YOHANE 4:22
Inu mulambira cimene simucidziwa; ife tilambira cimene ticidziwa; pakuti cipulumutso cicokera kwa Ayuda.


YOHANE 4:23
Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'coonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace.


YOHANE 4:24
Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'coonadi.


YOHANE 12:20
Koma panali Ahelene ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira paphwando,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:43
15 Ndipo munatenga cihema ca Moloki, Ndi nyenyezi ya mulungu Refani, Zithunzizo mudazipanga kuzilambira; Ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwace mwa Babulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:25
Ndipo panali pakulowa Petro, Komeliyo anakomana naye, nagwa pa mapazi ace, namlambira.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:11
popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha cikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;


AHEBRI 9:1
Ndipo cingakhale cipangano coyambaci cinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi.


AHEBRI 9:6
Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'cihema coyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;


AHEBRI 9:9
ndico ciphiphiritso ca ku nthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za cikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.


CHIVUMBULUTSO 4:10
akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa iye wakukhala pa mpando wacifumu, namlambira iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao ku mpando wacifumu, ndi kunena,


CHIVUMBULUTSO 5:14
Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuruwo anagwa pansi nalambira.


CHIVUMBULUTSO 11:1
Ndipoanandipatsa ine bango ngati ndodo, ndikuti, Tanyamuka, nuyese Kacisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.


CHIVUMBULUTSO 11:16
Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yacifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,


CHIVUMBULUTSO 13:4
ndipo analambira cinjoka, cifukwa cinacipatsa ulamuliro ciromboco; ndipo analambira cirombo ndi kunena, Manana ndi cirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo naco?


CHIVUMBULUTSO 13:8
Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,


CHIVUMBULUTSO 13:15
Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.


CHIVUMBULUTSO 14:9
Ndipo anawatsata mngelo wina, wacitatu, nanena ndi mau akuru, Ngati wina alambira ciromboco, ndi fane lace, nalandira lembapamphumi pace, kapena pa dzanja lace,


CHIVUMBULUTSO 14:11
ndipo utsi wa kuzunza kwao tukwera ku nthawiza nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku: iwo akulambira ciromboco ndi fano lace, ndi iye ali yense akalandira lemba la dzina lace.


CHIVUMBULUTSO 15:4
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


CHIVUMBULUTSO 16:2
Ndipo anacoka woyamba, natsanulira mbale yace kudziko; ndipo kunakhala cironda coipa ndi cosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la cirombo nalambira fano lace.


CHIVUMBULUTSO 19:4
Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wacifumu, nizinena, Amen; Aleluya.


CHIVUMBULUTSO 19:10
Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.


CHIVUMBULUTSO 19:20
Ndipo 5 cinagwidwa ciromboco, ndi pamodzi naco mneneri wonyenga amene adacita zizindikilo pamaso pace, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la cirombo, ndi iwo akulambira fano lace; 6 iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulfure:


CHIVUMBULUTSO 20:4
Ndipo ndinaona mipando yacifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa ciweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi cifukwa ca umboni wa Yesu, ndi cifukwa ca mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira cirombo, kapena fano lace, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nacita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka cikwi.


CHIVUMBULUTSO 21:8
Koma amantha, ndi osakhulupira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi acigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, colandira cao cidzakhala m'nyanja yotentha ndi mota ndi sulfure; ndiyo imfa yaciwiri.


CHIVUMBULUTSO 22:8
Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.


CHIVUMBULUTSO 22:9
Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usacite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society