A A A A A


Sakani

MATEYU 1:1
BUKU la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


MATEYU 1:16
ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wace wa Mariya, amene Yesu, wochedwa Kristu, anabadwa mwa iye.


MATEYU 1:18
Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.


MATEYU 1:21
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao.


MATEYU 1:25
ndipo sanamdziwa iye kufikira atabala rriwana wace; namucha dzina lace Yesu.


MATEYU 2:1
Ndipo pa kubadwa kwace kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


MATEYU 3:13
Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.


MATEYU 3:15
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.


MATEYU 3:16
Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


MATEYU 4:1
Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kumka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.


MATEYU 4:7
Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


MATEYU 4:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.


MATEYU 4:12
Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;


MATEYU 4:17
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.


MATEYU 4:18
Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya, mbale wace, analikuponya psasa m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


MATEYU 4:23
Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, naciritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


MATEYU 7:28
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi ciphunzitso cace:


MATEYU 8:3
Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lace, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lace linacoka.


MATEYU 8:4
Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwaiwo.


MATEYU 8:7
Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamciritsa iye.


MATEYU 8:10
Ndipo pakumva ici, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israyeli, sindinapeza cikhulupiriro cotere.


MATEYU 8:13
Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anaciritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.


MATEYU 8:14
Ndipo pofika Yesu ku nyumba ya Petro, anaona mpongozi wace ali gone, alikudwala malungo.


MATEYU 8:18
Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke ku tsidya lina,


MATEYU 8:20
Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wace.


MATEYU 8:22
Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.


MATEYU 8:34
Ndipo onani, mudzi wonse unaturukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti acoke m'malire ao.


MATEYU 9:2
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pachika: ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, macimo ako akhululukidwa.


MATEYU 9:4
Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Cifukwa canji mulinkuganizira zoipam'mitimayanu?


MATEYU 9:9
Ndipo Yesu popita, kucokera kumeneko, anaona munthu, dzina lace Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.


MATEYU 9:10
Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pacakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ocimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace.


MATEYU 9:12
Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala.


MATEYU 9:15
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? koma adzafika masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.


MATEYU 9:19
Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ace omwe.


MATEYU 9:22
Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, cikhulupiriro cako cakuciritsa. Ndipo mkaziyo anacira kuyambira nthawi yomweyo.


MATEYU 9:23
Ndipo Yesu polowa m'nyumba yace ya mkuruyo, ndi poona oyimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,


MATEYU 9:27
Ndipo popita Yesu kucokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, opfuula ndi kuti, Muticitire ife cifundo, mwana wa Davide.


MATEYU 9:28
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kucita ici? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.


MATEYU 9:30
Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa Iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu ali yense.


MATEYU 9:35
Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, naciritsa nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.


MATEYU 10:5
Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite ku njira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:


MATEYU 11:1
Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ace khumi Ndi awiri, Iye anacokera kumeneko kukaphunzitsa Ndi kulalikira m'midzi mwao.


MATEYU 11:4
Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:


MATEYU 11:7
Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena Ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munaturuka kunka kucipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka nd: mphepo kodi?


MATEYU 11:25
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndibvomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


MATEYU 12:1
Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ace anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.


MATEYU 12:15
Koma Yesu m'mene anadziwa, anacokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawaciritsa iwo onse,


MATEYU 12:25
Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uti wonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uti wonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;


MATEYU 13:1
Tsiku lomwelo Yesu anaturuka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja.


MATEYU 13:34
Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo;


MATEYU 13:53
Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anacokera kumeneko.


MATEYU 13:57
Ndipo iwo anakhumudwa cifukwa ca Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, 6 Mneneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwace.


MATEYU 14:1
Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu,


MATEYU 14:12
Ndipo ophunzira ace anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.


MATEYU 14:13
Ndipo Yesu pakumva, anacokera kumeneko m'ngalawa, kunka ku malo acipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kucokera m'midzi.


MATEYU 14:16
Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe cifukwa ca kumukira, apatseni ndinu adye.


MATEYU 14:27
Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.


MATEYU 14:29
Ndipo Iye anati, Idza, Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


MATEYU 14:31
Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lace, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?


MATEYU 15:1
Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ocokera ku Yerusalemu, nati,


MATEYU 15:21
Ndipo Yesu anaturukapo napatukira ku mbali za Turo ndi Sidoni.


MATEYU 15:28
Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, cikhulupiriro cako ndi cacikuru; cikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wace anacira nthawi yomweyo.


MATEYU 15:29
Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.


MATEYU 15:32
Ndipo Yesu anaitana ophunzira ace, nati, Mtima wanga ucitira cifundo khamu la anthuwa, pakuti ali cikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira,


MATEYU 15:34
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono.


MATEYU 16:6
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi ndi Asaduki.


MATEYU 16:8
Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana cifukwa ninji wina ndi mnzace, kuti simunatenga mikate?


MATEYU 16:13
Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kaisareya wa Filipi, anafunsa ophunzira ace, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani?


MATEYU 16:17
Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bar-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ici, koma Atate wanga wa Kumwamba.


MATEYU 16:21
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ace, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akuru, ndi ansembe akuru, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lacitatu kuuka kwa akufa.


MATEYU 16:24
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine.


MATEYU 17:1
Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wace, napita nao pa okha pa phiri lalitari;


MATEYU 17:4
Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pane misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.


MATEYU 17:7
Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa,


MATEYU 17:8
Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaona munthu, koma Yesu yekha.


MATEYU 17:9
Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalangiza iwo kuti, Musakauze munthu coonekaco, kufikira Mwana wa munthu adadzauka kwa akufa.


MATEYU 17:17
Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? ndidzalekerera inu nthawi yanji? mudze naye kwa Ine kuno.


MATEYU 17:18
Ndipo. Yesu anamdzudzula; ndipo ciwanda cinaturuka mwa iye; ndipo mnyamatayo anacira kuyambira nthawi yomweyo.


MATEYU 17:19
Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuciturutsa?


MATEYU 17:22
Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;


MATEYU 17:25
Iye anabvomera, Apereka, Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?


MATEYU 17:26
Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Cifukwa cace anawo ali aufulu.


MATEYU 18:1
Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?


MATEYU 18:2
Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,


MATEYU 18:22
Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi ananu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.


MATEYU 19:1
Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anacokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano.


MATEYU 19:14
Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: cifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.


MATEYU 19:18
Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usacite cigololo, Usabe, Usacite umboni wonama,


MATEYU 19:21
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhaia ndi cuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.


MATEYU 19:23
Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ace, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini cuma adzalowa mobvutika mu Ufumu wa Kumwamba.


MATEYU 19:26
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, ici sicitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


MATEYU 19:28
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa cimpando ca ulemerero wace, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.


MATEYU 20:17
Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khurni ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,


MATEYU 20:22
Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa cimene mupempha, Kodi mukhoza kumwera cikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.


MATEYU 20:25
Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akuru ao amacita ufumu pa iwo.


MATEYU 20:30
Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'rnphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anapfuula nati, Muticitire ife cifundo, Inu Mwana wa Davide.


MATEYU 20:32
Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikucitireni ciani?


MATEYU 20:34
Ndipo Yesu anagwidwa ndi cifundo, nakhudza maso ao; ndipo pornwepo anapenyanso, namtsata Iye.


MATEYU 21:1
Ndipo parnene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, ku phiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,


MATEYU 21:6
Ndipo ophunzirawo anamuka, nacita monga Yesu anawauza;


MATEYU 21:11
Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


MATEYU 21:12
Ndipo Yesu analowa ku Kacisi wa Mulungu naturutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


MATEYU 21:16
nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi cimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


MATEYU 21:21
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala naco cikhulupiriro, osakayika-kayika, mudzacita si ici ca pa mkuyu cokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nvania, cidzacitidwa.


MATEYU 21:24
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati muneliuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi:


MATEYU 21:27
Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, lnenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi.


MATEYU 21:31
Ndani wa awiriwo anacita cifuniro ca atate wace? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi aciwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.


MATEYU 21:42
Yesu ananena kwa iwo, 1 Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba Womwewu unakhala mutu wa pangondya: ici cinacokera kwa Ambuye, Ndipo ciri cozizwitsa m'maso mwathu?


MATEYU 22:18
Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?


MATEYU 22:29
Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa a osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.


MATEYU 22:37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.


MATEYU 22:41
Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,


MATEYU 23:1
Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ace,


MATEYU 24:1
Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo.


MATEYU 24:4
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.


MATEYU 26:1
Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ace,


MATEYU 26:4
nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi cinyengo, namuphe.


MATEYU 26:6
Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,


MATEYU 26:10
Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? popeza andicitira Ine nchito yabwino.


MATEYU 26:17
Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda cotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye?


MATEYU 26:19
Ndipo ophunzira anacita monga Yesu anawauza, nakonza Paskha.


MATEYU 26:26
Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ici ndi thupi langa.


MATEYU 26:31
Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa cifukwa ca Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, Ndipo zidzabalalika Nkhosa za gulu.


MATEYU 26:34
Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.


MATEYU 26:36
Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo ochedwa Getsemane, nanena kwa ophunzira ace, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.


MATEYU 26:49
Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.


MATEYU 26:50
Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji: iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.


MATEYU 26:51
Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lace, nasolola Iupanga lace, nakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, nadula khutu lace.


MATEYU 26:52
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza Iupanga lako m'cimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi Iupanga,


MATEYU 26:55
Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munaturukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wacifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kacisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.


MATEYU 26:57
Ndipo iwo akugwira Yesu anaaka naye kwa Kayafa, mkuru wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akuru omwe.


MATEYU 26:59
Ndipo ansembe akuru ndi akuru mirandu onse mafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


MATEYU 26:63
Koma 4 Yesu anangokhala cete. Ndipo mkuru wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.


MATEYU 26:64
Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, 5 Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


MATEYU 26:69
Ndipo 10 Petro adakhala pabwato: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.


MATEYU 26:71
Ndipo pamene iye anaturuka kunka kucipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.


MATEYU 26:75
Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, 12 Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anaturukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.


MATEYU 27:1
Ndipo pakudza mamawa, ansembe akuru ndi akuru a anthu onse anakhala upo wakumcitira Yesu, kuti amuphe;


MATEYU 27:11
Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.


MATEYU 27:17
Cifukwa cace pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wochedwa Kristu?


MATEYU 27:20
Koma ansembe akuru anapangira anthu kuti apemphe Baraba, koma kuti aononge Yesu.


MATEYU 27:22
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzacita ciani ndi Yesu, wochedwa Kristu?


MATEYU 27:26
Pomwepo iye anamasulira iwo Baraba, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampacike pamtanda.


MATEYU 27:27
Pomwepo asilikari a kazembe anamuka naye Yesu ku bwalo la mirandu, nasonkhanitsa kwa iye khamu lao lonse.


MATEYU 27:37
Ndipo anaika pamwamba pamutu pace liwongo lace lolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.


MATEYU 27:46
Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu 7 anapfuula ndi mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


MATEYU 27:50
Ndipo Yesu, 9 pamene anapfuula ndi mau akuru, anapereka mzimu wace.


MATEYU 27:54
Ndipo pamene mkuru wa asilikari, ndi iwo anali naye 11 akudikira Yesu, anaona cibvomezi, ndi zinthu zimene zinacitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyo ndiye Mwana wa Mulungu.


MATEYU 27:55
Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patari, 12 Omwe anatsata Yesu kucokera ku Galileya, namatumikira Iye;


MATEYU 27:57
Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wacuma wa ku Arimateya, dzina lace Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu;


MATEYU 27:58
yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe.


MATEYU 28:5
Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapacikidwa.


MATEYU 28:9
Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ace, namgwadira.


MATEYU 28:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.


MATEYU 28:16
Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangifa.


MATEYU 28:18
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.


MARKO 1:1
CIYAMBI cace ca Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu.


MARKO 1:9
Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kucokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordano.


MARKO 1:14
Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu,


MARKO 1:17
Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.


MARKO 1:24
kuti, Tiri ndi ciani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.


MARKO 1:25
Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli cete, nuturuke mwa iye.


MARKO 1:41
Ndipo Yesu anagwidwa cifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.


MARKO 1:45
Koma 2 iye anaturuka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowansopoyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a ku malo onse.


MARKO 2:5
Ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, macimo ako akhululukidwa.


MARKO 2:8
Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwace kuti alikuganizira comweco mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?


MARKO 2:15
Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwace, ndipo amisonkho ndi ocimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.


MARKO 2:17
Ndipo pamene Yesu anamva ici, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa.


MARKO 2:19
Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.


MARKO 3:7
Ndipo Yesu anacokako pamodzi ndi ophunzira ace nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikuru la a ku Galileya, ndi aku Yudeya,


MARKO 5:6
Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye;


MARKO 5:7
ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Ndiri ndi ciani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.


MARKO 5:15
Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wobvala ndi wa nzeru zace zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.


MARKO 5:20
Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikuru Yesu adamcitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.


MARKO 5:21
Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikuru linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.


MARKO 5:27
m'mene iye anamva mbiri yace ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwace, nakhudza cobvala cace.


MARKO 5:30
Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idaturuka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zobvala zanga?


MARKO 5:36
Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkuru wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.


MARKO 6:4
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.


MARKO 6:30
Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza ziri zonse adazicita, ndi zonse adaziphunzitsa,


MARKO 8:17
Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana cifukwa mulibe mkate? kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? kodi muli nayo mitima yanu youma?


MARKO 8:27
Ndipo anaturuka Yesu, ndi ophunzira ace, nalowa ku midzi ya ku Kaisareya wa Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ace, nanena nao, Kodi anthu anena kuti Ine ndine yani?


MARKO 9:2
Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:


MARKO 9:4
Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.


MARKO 9:5
Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.


MARKO 9:8
Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.


MARKO 9:23
Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.


MARKO 9:25
Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lirikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, turuka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.


MARKO 9:27
Koma Yesu anamgwira dzanja lace, namnyamutsa; ndipo anaimirira.


MARKO 9:39
Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzacita camphamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.


MARKO 10:5
Koma Yesu anati kwa iwo, Cifukwa ca kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili.


MARKO 10:14
Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


MARKO 10:18
Ndipo Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.


MARKO 10:21
Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Cinthu cimodzi cikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo cuma udzakhala naco m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.


MARKO 10:23
Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ace, Okhala naco cuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kubvuta nanga!


MARKO 10:24
Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ace. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkobvuta ndithu kwa iwo akutama cuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!


MARKO 10:27
Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


MARKO 10:29
Yesu anati, Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca Ine, ndi cifukwa ca Uthenga Wabwinowo,


MARKO 10:32
Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anacita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,


MARKO 10:38
Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa cimene mucipempha, Mukhoza kodi kumwera cikho cimene ndimwera Ine? kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?


MARKO 10:39
Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Cikho cimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;


MARKO 10:42
Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amacita ufumu pa iwo; ndipo akuru ao amacita ulamuliro pa iwo.


MARKO 10:47
Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kupfuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundicitire ine cifundo.


MARKO 10:49
Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.


MARKO 10:50
Ndipo iye anataya copfunda cace, nazunzuka, nadza kwa Yesu.


MARKO 10:51
Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikucitire ciani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.


MARKO 10:52
Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.


MARKO 11:6
Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye.


MARKO 11:7
Ndipo anabwera naye mwana wa buru kwa Yesu, naika zobvala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.


MARKO 11:22
Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu,


MARKO 11:29
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.


MARKO 11:33
Ndipo iwo anamyankha Yesu, nanena, Sitidziwa. Ndipo Yesu ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.


MARKO 12:17
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zace za Kaisara kwa Kaisara, ndi zace za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.


MARKO 12:24
Yesu ananena nao, Simusocera nanga mwa ici, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yace ya Mulungu?


MARKO 12:29
Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;


MARKO 12:34
Ndipo palmona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kwnfunsa Iye kanthu.


MARKO 12:35
Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa m'Kacisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Kristu ndiye mwana wa Davide?


MARKO 13:2
Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikuru? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzace, umene sudzagwetsedwa.


MARKO 13:5
Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusoceretseni.


MARKO 14:6
Koma Yesu anati, Mlekeni, mumbvutiranji? wandicitira Ine nchito yabwino.


MARKO 14:18
Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.


MARKO 14:27
Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.


MARKO 14:30
Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.


MARKO 14:48
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira ine monga wacifwamba?


MARKO 14:53
Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe akuru onse ndi akuru a anthu, ndi alembi,


MARKO 14:55
Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.


MARKO 14:60
Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?


MARKO 14:62
Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.


MARKO 14:67
ndipo anaona Petro alikuotha noto, namyang'ana iye, nanena, wenso unali naye Mnazarene, Yesu.


MARKO 14:72
Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi.


MARKO 15:1
Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ndi alembi, ndi akuru a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


MARKO 15:5
Koma Yesu sanayankhanso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.


MARKO 15:15
Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Baraba, napereka Yesu, atamkwapula, akampacike pamtanda.


MARKO 15:34
Ndipo pa ora lacisanu ndi cinai Yesu anapfuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


MARKO 15:43
anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.


MARKO 16:6
Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapacikidwa: anauka; sali pano; taonani, mbuto m'men e anaikamo Iye!


MARKO 16:19
Pamenepo Ambuye Yesu, ata-tha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.


LUKA 1:31
Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamucha dzina lace Yesu.


LUKA 2:21
Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula iye, anamucha dzina lace Yesu, limene anachula mngeloyo asanalandiridwe iye m'mimba.


LUKA 2:27
Ndipo iye analowa kuKacisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amace analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamcitira iye mwambo wa cilamulo,


LUKA 2:43
ndipo pakumariza masiku ace, pakubwera iw, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amace sanadziwa;


LUKA 2:52
Ndipo Yesu 8 anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'cisomo ca pa Mulungu ndi ca pa anthu.


LUKA 3:21
Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo,


LUKA 3:23
Ndipo Yesuyo, pamene anayamba nchito yace, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,


LUKA 4:1
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.


LUKA 4:4
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.


LUKA 4:8
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, Ndipo iye yekha yekha uzimtumikira,


LUKA 4:12
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako,


LUKA 4:14
Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yace ya iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.


LUKA 4:34
Ha! tiri ndi ciani ndi Inu, Yesu wa ku N azarete? kodi munadza kutiononga ife? ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wace wa Mulungu.


LUKA 4:35
Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nuturuke mwa iye. Ndipo ciwandaco m'mene cinamgwetsa iye pakati, cinaturuka mwa iye cosampweteka konse.


LUKA 4:38
Ndipo iye ananyamuka kucokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wace wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.


LUKA 5:8
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa.


LUKA 5:10
ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.


LUKA 5:12
Ndipo panali, pamene iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipopameneanaona Yesu, anagwa nkhope yace pansi, nampempha iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.


LUKA 5:19
Ndipo posapeza polowa naye, cifukwa ca unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wace, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.


LUKA 5:22
Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu?


LUKA 5:31
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo.


LUKA 5:34
Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?


LUKA 6:3
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale cimene anacita Davine, pamene paja anamva Njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi,


LUKA 6:9
Ndipo Iyeananyamuka, naimirira. Ndipo Yesuanati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kucita zabwino, kapena kucita zoipa? kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?


LUKA 6:11
Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzace kuti amcitire Yesu ciani.


LUKA 7:1
Pamene Yesu adamariza mau ace onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao.


LUKA 7:3
Ndipo pamene iye ana-I mva za Yesu, anatuma kwa iye akuru a Ayuda, namfunsa iye kuti adze kupulumutsa kapolo wace.


LUKA 7:4
Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumcitire ici;


LUKA 7:6
Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika iye tsono pafupi panyumba yace, kenturiyo anatuma kwa iye abwenzi ace, kunena naye, Ambuye, musadzibvute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa;


LUKA 7:9
Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israyeli, cikhulupiriro cacikuru cotere.


LUKA 7:37
Ndipo onani, mkazi wocimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pacakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino,


LUKA 7:40
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anabvomera, Mphunzitsi, nenani.


LUKA 8:28
Ndipo pakuona Yesu, iye anapfuula, nagwa pansi pamaso pace, nati ndi mau akuru, Ndiri naco ciani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikupemphani Inu musandizunze.


LUKA 8:30
Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, cifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.


LUKA 8:35
Ndipo iwo anaturuka kukaona cimene cinacitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinaturuka mwa iye, alikukhala pansi ku mapazi ace a Yesu wobvala ndi wa nzeru zace; ndipo iwo anaopa.


LUKA 8:39
Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuruzo anakucitira iwe Mulungu. Ndipo iye anacoka, nalalikira ku mudzi wonse zazikuruzo Yesu anamcitira iye,


LUKA 8:40
Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira iye; pakuti onse analikumlindira iye.


LUKA 8:41
Ndipo onani, panadza munthu dzina lace Yairo, ndipo iye ndiye mkuru wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ace a Yesu, nampempha iye adze kunyumba kwace;


LUKA 8:45
Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.


LUKA 8:46
Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti a ndazindikira Ine kuti mphamvu yaturuka mwa Ine.


LUKA 8:50
Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.


LUKA 9:33
Ndipo panali polekana iwo aja ndi iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tiri pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye cimene alikunena.


LUKA 9:36
Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala cete, ndipo sanauza munthu ali yense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.


LUKA 9:41
Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? idza naye kuno mwana wako.


LUKA 9:42
Ndipo akadadza iye, ciwandaco cinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa, Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, naciritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wace.


LUKA 9:47
Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pace, nati kwa iwo,


LUKA 9:50
Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.


LUKA 9:51
Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe iye kumwamba, Yesu anatsimika kuloza nkhope yace kunka ku Yerusalemu,


LUKA 9:58
Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe ziri nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu.


LUKA 9:62
Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira cikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.


LUKA 10:29
Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


LUKA 10:30
Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a acifwamba amene anambvula zobvala, namkwapula, nacoka atamsiya wofuna kufa.


LUKA 10:37
Ndipo anati, iye wakumcitira cifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita, nucite iwe momwemo.


LUKA 13:12
Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.


LUKA 13:14
Ndipo mkuru wa sunagoge anabvutika mtima, cifukwa Yesu anaciritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira nchito, cifukwa cace idzani kudzaciritsldwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.


LUKA 14:3
Ndipo Yesu anayankha nati kwa acilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuciritsa, kapena iai?


LUKA 17:13
ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, muticitire cifundo.


LUKA 17:17
Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwa khumi? koma ali kuti asanu ndi anai aja?


LUKA 18:16
Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uti wa otere.


LUKA 18:19
Koma Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.


LUKA 18:22
Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa cinthu cimodzi: gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala naco cuma ceni ceni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.


LUKA 18:24
Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! nkubvutika nanga kwa anthu eni cuma kulowa Ufumu wa Mulungu!


LUKA 18:37
Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


LUKA 18:38
Ndipo anapfuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.


LUKA 18:40
Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa iye: ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye,


LUKA 18:42
Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.


LUKA 19:3
Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sana the, cifukwa ca khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu.


LUKA 19:5
Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.


LUKA 19:9
Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero cipulumutso cagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.


LUKA 19:35
Ndipo anadzanave kwa Yesu; ndipo anayalika zobvala zao pa mwana wa buruyo, nakwezapo Yesu.


LUKA 20:8
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu izi.


LUKA 20:34
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:


LUKA 21:1
Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni cuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.


LUKA 22:47
Pamene iye anali cilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wochedwa Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona iye.


LUKA 22:48
Koma Yesu anati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi cimpsompsono kodi?


LUKA 22:51
Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lace, namciritsa.


LUKA 22:52
Ndipo 5 Yesu anati kwa ansembe akulu ndi akapitao a Kacisi, ndi akuru, amene anadza kumgwira iye, Munaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wacifwamba?


LUKA 22:63
Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza iye, nampanda.


LUKA 23:8
Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya iye, cifukwa anamva za iye; nayembekeza kuona cizindikilo cina cocitidwa ndi iye.


LUKA 23:20
Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;


LUKA 23:25
Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa cifuniro cao.


LUKA 23:26
Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pace pa Yesu,


LUKA 23:28
Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.


LUKA 23:34
Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa cimene acita. Ndipo anagawana zobvala zace, poyesa maere.


LUKA 23:42
Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukileni m'mene mulowa Ufumuwanu.


LUKA 23:46
Ndipo pamene Yesu anapfuula ndi mau akuru, anati, 1 Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wace.


LUKA 23:52
yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wace wa Yesu.


LUKA 24:3
Ndipo m'mene analowa sanapeza mtembo wa Ambuye Yesu.


LUKA 24:15
Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.


LUKA 24:19
Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa iye, lzi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'nchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;


YOHANE 1:17
Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu.


YOHANE 1:29
M'mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, 4 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu 5 amene acotsa cimo lace la dziko lapasi!


YOHANE 1:36
ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, 10 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!


YOHANE 1:37
Ndipo akuphunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.


YOHANE 1:38
Koma Yesu anaceuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna ciani? Ndipo anati kwa iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?


YOHANE 1:42
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; 11 udzachedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).


YOHANE 1:43
M'mawa mwace anafuna kuturuka kunka ku Galileya, napeza Filipo, Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.


YOHANE 1:45
Filipo anapeza Natanayeli, nanena naye, iye 12 amene Mose analembera za iye m'cilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.


YOHANE 1:47
Yesu anaona Natanayeli alinkudza kwa iye, nanena za iye, Onani, M-israyeli ndithu, mwa iye mulibe cinyengo!


YOHANE 1:48
Natanayeli ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.


YOHANE 1:50
Yesu anayankha nati kwa iye, Cifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? udzaona zoposa izi.


YOHANE 2:1
Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amace wa Yesu anali komweko.


YOHANE 2:2
Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace anaitanidwa ku ukwatiwo.


YOHANE 2:3
Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo,


YOHANE 2:4
Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.


YOHANE 2:7
Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde.


YOHANE 2:11
Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira iye.


YOHANE 2:13
Ndipo Paskha wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


YOHANE 2:19
Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani kacisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.


YOHANE 2:22
Cifukwa cace atauka kwa akufa, akuphunzira ace anakumbukira kuti ananena ici; ndipo anakhulupirira colemba, ndi mau amene Yesu ananena.


YOHANE 2:24
Koma Yesu sanakhulupirira iwo kuti akhale nao, cifukwa iye anadziwa anthu onse,


YOHANE 3:2
Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye,


YOHANE 3:3
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:5
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.


YOHANE 3:10
Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi?


YOHANE 3:22
Zitapita in anadza Yesu ndi akuphunzira ace ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.


YOHANE 4:1
Cifukwa cace pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane


YOHANE 4:2
(angakhale Yesu sanabatiza yekha koma ophunzira ace),


YOHANE 4:6
ndipo pamenepo panali citsime ca Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wace, motero anakhala pacitsime,


YOHANE 4:7
Kunali ngati ora lacisanu ndi cimodzi. Kunadza mkazi woturuka m'Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.


YOHANE 4:10
Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


YOHANE 4:13
Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso Iudzu;


YOHANE 4:16
Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.


YOHANE 4:17
Mkazi anayankha nati kwa iye, Ndiribe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;


YOHANE 4:21
Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.


YOHANE 4:26
Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.


YOHANE 4:34
Yesu ananena nao, Cakudya canga ndico kuti ndicite cifuniro ca iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza nchito yace.


YOHANE 4:44
Pakuti Yesu mwini anacita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.


YOHANE 4:46
Cifukwa cace Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunalimkulu wina wa mfumu, mwana wace anadwala m'Kapernao.


YOHANE 4:47
Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wacokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa iye, nampempha kuti atsike kukaciritsa mwana wace; pakuti anali pafupi imfa.


YOHANE 4:48
Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikilo ndi zozizwa, simudzakhulupira.


YOHANE 4:50
Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo, Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka.


YOHANE 4:53
Cifukwa cace atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupira iye yekha ndi a pa banja lace onse.


YOHANE 4:54
Ici ndi cizindikilo caciwiri Yesu anacita, ataeokera ku Yudeya, ndi kulowa m'Galileya.


YOHANE 5:1
Zitapita izi panali phwando la Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


YOHANE 5:6
Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikuru pamenepo, ananena naye, Ufuna kuciritsidwa kodi?


YOHANE 5:8
Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende,


YOHANE 5:13
Koma wociritsidwayo sanadziwa ngati ndani; pakuti Yesu anacoka kacetecete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.


YOHANE 5:14
Zitapita izi Yesu anampeza m'Kacisi, nati kwa iye, Taona, waeiritsidwa; usacimwenso, kuti cingakugwere ecipa coposa.


YOHANE 5:15
Munthuyo anacoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adameiritsa.


YOHANE 5:16
Ndipo cifukwa ca ici Ayuda analondalonda Yesu, popeza anacita izo dzuwa la Sabata.


YOHANE 5:17
Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira nchito kufikira tsopano, lnenso ndigwira nchito.


YOHANE 5:19
Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha, koma cimene aona Atate acicita, ndico. Pakuti zimene iye azicita, zomwezo Mwananso azicita momwemo.


YOHANE 6:1
Zitapita izi anacoka Yesu kunka ku tsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiya,


YOHANE 6:3
Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.


YOHANE 6:5
Pamenepo Yesu, pokweza maso ace, ndi kuona kuti khamu lalikuru lirinkudza kwa iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?


YOHANE 6:10
N ati Yesu, Akhalitseni anthu pansi, Ndipo panali udzu wambiri pamalopo, Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu.


YOHANE 6:11
Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.


YOHANE 6:15
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira iye, kuti amlonge ufumu, anacokanso kunka kuphiri pa yekha.


YOHANE 6:17
ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.


YOHANE 6:19
Ndipo parnene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anacita mantha.


YOHANE 6:22
M'mawa mwace khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa yina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowa pamodzi ndi akuphunzira ace m'ngalawamo, koma akuphunzira ace adacoka pa okha;


YOHANE 6:23
koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;


YOHANE 6:24
cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.


YOHANE 6:26
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si cifukwa munaona zizindikilo, koma cifukwa munadya mkate, nimunakhuta.


YOHANE 6:29
Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.


YOHANE 6:32
Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.


YOHANE 6:35
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.


YOHANE 6:42
Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wace ndi amai wace tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?


YOHANE 6:43
Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze winandi mnzace.


YOHANE 6:53
Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinenandi inu, 10 Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wace, mulibe moyo mwa inu nokha.


YOHANE 6:61
Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti akuphunzira ace alikung'ung'udza cifukwa ca ici, anati kwa iwo, ici mukhumudwa naco?


YOHANE 6:64
Koma 17 pali ena mwa inu amene sakhuluplra, Pakuti. Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupira, ndi amene adzampereka.


YOHANE 6:67
Cifukwa cace Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kucoka?


YOHANE 6:70
Yesu anayankha iwo, 21 Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu 22 mmodzi ali mdierekezi?


YOHANE 7:1
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafuna kuyendayenda m'Yudeya, cifukwa Ayuda anafuna kumupha iye.


YOHANE 7:6
Cifukwa cace Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.


YOHANE 7:14
Koma pamene padafika pakati pa phwando, Yesu anakwera nalowa m'Kacisi, naphunzitsa,


YOHANE 7:16
Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine.


YOHANE 7:21
Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinacita nchito imodzi, ndipo muzizwa monse,


YOHANE 7:28
Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.


YOHANE 7:33
Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma Ine.


YOHANE 7:37
Koma tsiku lomariza, lalikurulo la phwando, Yesu anaimirira napfuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva Ludzu, adze kwa Ine, namwe.


YOHANE 7:39
Koma 1 ici anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, cifukwa Yesu sanalemekezedwa panthawi pomwepo.


YOHANE 8:1
Koma Yesu anamuka ku phiri la Azitona.


YOHANE 8:6
Koma ici ananena kuti amuyese iye, kuti akhale naco comneneza iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi cala cace.


YOHANE 8:9
Koma iwo, m'mene adamva, anaturukamo amodzi amodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.


YOHANE 8:10
Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?


YOHANE 8:11
Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usacimwenso.


YOHANE 8:12
Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


YOHANE 8:14
Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndicita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; cifukwa ndidziwa kumene ndinacokera ndi kumene ndimukako; koma e inu, simudziwa kumene ndicokera, ndi kumene ndimukako.


YOHANE 8:19
Cifukwa cace ananena ndi iye, Ali kuti Atate, wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukada-dziwanso Atate wanga.


YOHANE 8:25
Pamenepo ananena kwa iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Cimene comwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira paciyambi.


YOHANE 8:28
Cifukwa cace Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindicita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.


YOHANE 8:31
Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu;


YOHANE 8:34
Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.


YOHANE 8:39
Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, 2 Ngati muli ana a Abrahamu, mukadacita nchito za Abrahamu.


YOHANE 8:42
Yesu anati kwa iwo, 4 Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinaturuka, ndi kucokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.


YOHANE 8:49
Yesu anayankha, Ndiribe ciwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.


YOHANE 8:54
Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli cabe; 11 Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu;


YOHANE 8:58
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo 14 Ine ndiripo.


YOHANE 8:59
Pamenepo 15 anatola miyala kuti amponye iye; koma Yesu anabisala, naturuka m'Kacisi.


YOHANE 9:3
Yesu anayankha, Sanacimwa ameneyo, kapena atate wace ndi amace; koma kuti nchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.


YOHANE 9:11
Iyeyu anayankha, Munthuyo wochedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; cifukwa cace ndinacoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya,


YOHANE 9:14
Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ace.


YOHANE 9:35
Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Mulungu?


YOHANE 9:37
Yesu anati kwa iye, Wamuona iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo.


YOHANE 9:39
Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona,


YOHANE 9:41
Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo cimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: cimo lanu likhala.


YOHANE 10:6
Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.


YOHANE 10:7
Cifukwa cace Yesuananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.


YOHANE 10:23
Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kacisi m'khumbi la Solomo,


YOHANE 10:25
Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira, Nchitozi ndizicita Ine m'dzina la Atate wanga, zimenezi zindicitira umboni.


YOHANE 10:32
Yesu anayankha iwo, ndakuonetsani inu nchito zabwino zambiri za kwa Atate; cifukwa ca nchito yiti ya izo mundiponya miyala?


YOHANE 10:34
Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'cilamulo canu, Ndinati Ine, Muli milungu?


YOHANE 11:4
Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


YOHANE 11:5
Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wace, ndi Lazaro.


YOHANE 11:9
Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, cifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi,


YOHANE 11:13
Koma Yesu adanena za imfa yace; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.


YOHANE 11:14
Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.


YOHANE 11:17
Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai.


YOHANE 11:20
Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba.


YOHANE 11:21
Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.


YOHANE 11:23
Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka.


YOHANE 11:25
Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


YOHANE 11:30
(Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye)


YOHANE 11:32
Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.


YOHANE 11:33
Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini,


YOHANE 11:35
Yesu analira.


YOHANE 11:38
Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.


YOHANE 11:39
Yesu ananena, Cotsani mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.


YOHANE 11:40
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu?


YOHANE 11:41
Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.


YOHANE 11:44
Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.


YOHANE 11:46
Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazicita.


YOHANE 11:51
Koma ici sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe caka comweco ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo;


YOHANE 11:54
Cifukwa cace Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anacokapo kunka ku dziko loyandikira cipululu, kumudzi dzina lace Efraimu; nakhala komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.


YOHANE 11:56
Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzace poimirira iwo m'Kacisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuphwando kodi?


YOHANE 12:1
Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paskha, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.


YOHANE 12:3
Pamenepo Mariya m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a nardo a mtengo wace wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wace wa mafutawo.


YOHANE 12:7
Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anacisungira ici tsiku la kuikidwa kwanga.


YOHANE 12:9
Pamenepo khamu lalikuru la Ayuda Iinadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si cifukwa: ca Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.


YOHANE 12:11
pakuti ambiri a Ayuda anacoka cifukwa ca iye, nakhulupirira Yesu.


YOHANE 12:12
M'mawa mwace khamu lalikuru la anthu amene adadza kuphwando, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,


YOHANE 12:14
Koma Yesu, m'mene adapeza kaburu anakhala pamenepo; monga mulembedwa:


YOHANE 12:16
Izisanazidziwa aku phunzira ace poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukila kuti izi zinalembedwa za iye, ndi kuti adamcitira iye izi.


YOHANE 12:21
Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.


YOHANE 12:22
Filipo anadza nanena kwa Andreya; nadza Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu.


YOHANE 12:23
Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.


YOHANE 12:30
Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika cifukwa ca Ine, koma ca inu.


YOHANE 12:35
Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,


YOHANE 12:36
2 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nacoka nawabisalira.


YOHANE 12:44
Koma Yesu anapfuula nati, 8 iye wokhulupirira ine, sakhulupirira Ine, koma iye wondituma Ine.


YOHANE 13:1
Koma pasanafike phwando la Paskha, Yesu, podziwa kuti nthawi yace idadza yakucoka kuturuka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ace a iye yekha a m'dziko lapansi, anawakomia kufikira cimariziro.


YOHANE 13:3
Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa iye zonse m'manja mwace, ndi kuti anacokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


YOHANE 13:7
Yesu anayankha nati kwa iye, Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwace.


YOHANE 13:8
Petro ananena ndi iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.


YOHANE 13:10
Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.


YOHANE 13:21
Yesu m'mene adanenaizi, anabvutika mumzimu, nacita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.


YOHANE 13:23
Koma mmodzi wa akuphunzira ace, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa cifuwa ca Yesu.


YOHANE 13:25
Iyeyu potsamira pomwepo, pa cifuwa ca Yesu, anena ndi iye. Ambuye, ndiye yani?


YOHANE 13:26
Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa, Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudase mwana wa Simoni Isikariote.


YOHANE 13:27
Ndipopambuyo pace pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Cimene ucita, cita msanga,


YOHANE 13:29
Pakuti popeza Yudase anali nalo thumba, enaanalikuyesakuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa paphwando; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.


YOHANE 13:31
Tsono m'mene adaturuka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa iye;


YOHANE 13:36
Simoni Petro anena ndi iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, 2 udzanditsata bwino lomwe.


YOHANE 13:38
Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya cifukwa ca Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.


YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


YOHANE 14:9
Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?


YOHANE 14:23
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


YOHANE 16:19
Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzace za ici, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?


YOHANE 16:31
Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano?


YOHANE 17:1
Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ace Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeoi Inu;


YOHANE 17:3
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.


YOHANE 18:1
M'mene Yesu adanena izi, anaturuka ndi akuphunzira ace, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kunali munda, umene analowamo iye ndi akuphunzira ace.


YOHANE 18:2
Koma Yudasenso amene akampereka iye, anadziwa malowa; cifukwa Yesu akamkako kawiri kawiri ndi akuphunzira ace.


YOHANE 18:4
Pamenepo Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani?


YOHANE 18:5
Anayankha iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudase yemwe, wompereka iye, anaima nao pamodzi.


YOHANE 18:7
Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.


YOHANE 18:8
Yesu anayankha, Ndati, Ndine; cifukwa cace ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;


YOHANE 18:11
Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa Iupanga m'cimakecace; cikho cimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ici kodi?


YOHANE 18:12
Ndipo khamulo ndi kapitao wamkuru, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga iye,


YOHANE 18:15
Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;


YOHANE 18:19
Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za akuphunzira ace, ndi ciphunzitso cace.


YOHANE 18:20
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kacisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.


YOHANE 18:22
Koma m'mene iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe comweco?


YOHANE 18:23
Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula coipa, cita umboni wa coipaco, koma ngati bwino, undipandiranji?


YOHANE 18:28
Pamenepo anamtenga Yesu kucokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowa ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paskha.


YOHANE 18:32
kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene, akuti adzafa nayo.


YOHANE 18:33
Cifukwa cace Pilato analowanso m'Pretorio, naitana Yesu, nati kwa iye, Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda kodi?


YOHANE 18:34
Yesu anayankha, Kodi munena ici mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?


YOHANE 18:36
Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wocokera konkuno.


YOHANE 18:37
Pamenepo Pilato anati kwa iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ici Ine, ndipo ndinadzera ici kudza ku dziko lapansi, kuti ndikacite umboni ndi coonadi. Yense wakukhala mwa coonadi amva mau anga.


YOHANE 19:1
Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.


YOHANE 19:5
Pamenepo Yesu anaturuka kunja, atabvala korona waminga; ndi maraya acibakuwa, Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!


YOHANE 19:9
Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Mucoka kuti? koma Yesu sanamyankha kanthu.


YOHANE 19:11
Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kucokera Kumwamba; cifukwa ca ici iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo cimo loposa.


YOHANE 19:13
Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anaturuka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lace; Bwalo lamiyala, koma m'Cihebri, Gabata,


YOHANE 19:16
Ndipo pamenepo anampereka iye kwa iwo kutiampacike, Pamenepo anatenga Yesu;


YOHANE 19:18
kumene anampacika Iye; ndipo pamodzi ndi iye awiri ena, cakuno ndi cauko, koma Yesu pakati.


YOHANE 19:19
Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.


YOHANE 19:20
Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; cifukwa malo amene Yesu anapaeikidwapo anali pafupipa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Cihebri, ndi m'Ciroma, ndi m'Cihelene.


YOHANE 19:23
Pamenepo asilikari, m'mene adapacika Yesu, anatenga zobvala zace, nadula panai, natenga wina cina, wina cina, ndiponso maraya; koma maraya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pace, analibe msoko.


YOHANE 19:25
Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amace, ndi mbale wa amace, Mariya, mkazi wa Kleopa, ndi Mariya wa Magadala.


YOHANE 19:26
Pamenepo Yesu pakuona amace, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amace, Mkazi, taonani, mwana wanu!


YOHANE 19:28
Citapita ici Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepokuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


YOHANE 19:30
Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


YOHANE 19:33
koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona iye, kuti wafa kale, sanatyola miyendo yace;


YOHANE 19:38
6 Citatha ici. Y osefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, cifukwa ca kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akacotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Cifukwa cace anadza, nacotsa mtembo wace.


YOHANE 19:40
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsaru zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.


YOHANE 19:42
8 Pomwepo ndipo anaika Yesu, cifukwa ca tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.


YOHANE 20:2
Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anacotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika iye.


YOHANE 20:12
ndipo anaona angelo awiri atabvala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.


YOHANE 20:14
M'mene adanena izi, anaceuka m'mbuy'o, naona Yesu ali ciriri, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu.


YOHANE 20:15
Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi iye, Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamcotsa.


YOHANE 20:16
Yesu ananena naye, Mariya. Iyeyu m'mene anaceuka, ananena ndi iye m'Cihebri, Raboni; cimene cinenedwa, Mphunzitsi.


YOHANE 20:17
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.


YOHANE 20:19
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali citsekere, kumene anakhala akuphunzira, cifukwa ca kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.


YOHANE 20:21
Cifukwa cace Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.


YOHANE 20:24
Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wochedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza.


YOHANE 20:26
Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu akuphunzira ace analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao: Yesu anadza, makomo ali citsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.


YOHANE 20:29
Yesu ananena kwa iye, Cifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.


YOHANE 20:30
Ndipo zizindikilo zina zambiri Yesu anazicita pamaso pa akuphunzira ace, zimene sizinalembedwa m'buku ili;


YOHANE 20:31
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupira mukhale nao moyo m'dzina lace.


YOHANE 21:1
Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa akuphunzira ace ku nyanja ya Tiberiya. Koma anadzionetsera cotere.


YOHANE 21:4
Koma pakuyamba kuca, Yesu anaimirira pam bali pa nyanja, komatu akuphunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu.


YOHANE 21:5
Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha iye, lai.


YOHANE 21:7
Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadzibveka maraya a pathupi, pakuti anali wamarisece, nadziponya yekha m'nyanja.


YOHANE 21:10
Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano,


YOHANE 21:12
Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa akuphunzira anatha kumfunsa iye, Ndinu yani? podziwa kuti ndiye Ambuye.


YOHANE 21:13
Yesu anadza natenga mkate napatsa Iwo, momwemonso nsomba.


YOHANE 21:14
Imeneyo ndi nthawi yacitatu yakudzionetsera Yesu kwa akuphunzira ace, m'mene atauka kwa akufa.


YOHANE 21:15
Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa ana a nkhosa anga.


YOHANE 21:17
Ananena: naye kacitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva cisoni kuti anati kwa iye kacitatu, Kodi undikonda Ine? ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.


YOHANE 21:20
Petro, m'mene anaceuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pacifuwa pace pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?


YOHANE 21:21
Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu?


YOHANE 21:22
Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli ciani ndi iwe? unditsate Ine iwe.


YOHANE 21:23
Cifukwa cace mau awa anaturuka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli ciani ndi iwe?


YOHANE 21:25
Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:1
TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzicita ndi kuziphunzitsa,


MACHITIDWE A ATUMWI 1:11
amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:14
Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Mariya, amace wa Yesu, ndi abale ace omwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:16
Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davine za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:21
Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife,


MACHITIDWE A ATUMWI 2:22
Amuna inu Aisrayeli, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wocokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndizimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:32
Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ici tiri mboni ife tonse.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:36
Pamenepo lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampacika.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:6
Koma Petro anati, Siliva ndi golidi ndiribe; koma cimene ndiri naco, ici ndikupatsa, M'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda,


MACHITIDWE A ATUMWI 3:13
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wace Yesu; amene, inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


MACHITIDWE A ATUMWI 3:20
ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Kristu Yesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:2
obvutika mtima cifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:10
zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israyeli, kuti m'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, amene inu munampacika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:13
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:18
Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:27
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontiyo Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumcitira coipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:30
m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:33
Ndipo atumwi anacita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali cisomo cacikuru pa iwo onse.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:30
Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpacika pamtengo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:40
Ndipo anabvomerezana ndi iye; ndipo m'meheadaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kuchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:42
Ndipo masiku onse, m'Kacisi ndi m'nyumba, 2 sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:14
pakuu tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:55
Koma iye, 25 pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:59
Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, 29 Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:12
Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwinowa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:16
pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwam'dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:35
Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pace, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:5
Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


MACHITIDWE A ATUMWI 9:17
Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:20
Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:27
Koma Bamaba anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:34
Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Kristu akuciritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:36
Mau amene anatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Kristu (ndiye Ambuye wa onse)


MACHITIDWE A ATUMWI 10:38
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nacita zabwino, naciritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:48
Ndipo analamulira iwo 9 abatizidwe m'dzina la Yesu Kristu, Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:17
Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Kristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?


MACHITIDWE A ATUMWI 11:20
Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kupro, ndi Kurene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:6
Ndipo m'mene anapitirira cisumbu conse kufikira Pafo, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lace Baryesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:23
Wocokera mu mbeu yace Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israyeli Mpulumutsi, Yesu;


MACHITIDWE A ATUMWI 13:33
kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salmo laciwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:11
Koma tikhulupira tidzapulumuka mwa cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, monga iwo omwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:26
anthu amene anapereka moyo wao cifukwa ca dzina la Yesu Kristu Ambuye wathu.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:7
anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;


MACHITIDWE A ATUMWI 16:18
Ndipo anacita cotero masiku ambiri. Koma Paulo anabvutika mtima ndithu, naceuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Kristu, turuka mwa iye. Ndipo unaturuka nthawi yomweyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:31
Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:3
natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:7
amene Yasoni walandira; ndipo onsewo acita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:18
Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, ici ciani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zacilendo, cifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:5
Koma pamene Sila ndi Timoteo anadza potsika ku Makedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nacitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Kristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:25
Iyeyo aoaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wacangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


MACHITIDWE A ATUMWI 18:28
pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Kristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:4
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire iye amene adzadza pambuyo pace, ndiye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:5
Pamene anamva ici, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:13
Koma Ayuda enanso oyendayenda, oturutsa ziwanda, anadziyesa kuchula pa iwo amene anali ndi mizimu yoipa dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:15
Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?


MACHITIDWE A ATUMWI 19:17
Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Yesu Iinakuzika.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:21
ndi kucitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi cikhulupiriro colinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:24
Komatu sindiuyesa kanthu moyo, wanga, kuti uli wa mtengo wace kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kucitira umboni Uthenga Wabwino wa cisomo ca Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:35
M'zinthu zonse ndinakupatsani citsanzo, cakuti pogwiritsa nchito, koteromuyenerakuthandiza ofoka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:13
Pamenepo Paulo anayankha, Mucitanji, polira ndi kundiswera mtima? pakuti ndakonzeka Ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 22:8
Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa Ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:24
Koma atapita masiku ena, anadza Felike ndi Drusila mkazi wace, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za cikhulupiriro ca Kristu Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 25:19
koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a cipembedzero ca iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:9
Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:15
Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:23
Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza ku nyumba yace anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndikucitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zocokera m'cilamulo ca Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:31
ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.


AROMA 1:1
PAULO, kapolowa Yesu Kristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


AROMA 1:4
amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa ciyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu;


AROMA 1:6
mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Kristu;


AROMA 1:7
kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


AROMA 1:8
Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu cifukwa ca inu nonse, cifukwa kuti mbiri ya cikhulupiriro canu idamveka pa dziko lonse lapansi.


AROMA 2:16
tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Kristu zinsinsi za anthu, monga mwa uthenga wanga wabwino.


AROMA 3:22
ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana;


AROMA 3:24
ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;


AROMA 3:26
kuti aonetse cilungamo cace m'nyengo yatsopano; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu,


AROMA 4:24
koma cifukwa ca ifenso, kwa ife amene cidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu,


AROMA 5:1
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu;


AROMA 5:11
Ndipo si cotero cokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene talandira naye tsopano ciyanjanitso.


AROMA 5:15
Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa cifukwa ca kulakwa kwammodziyo, makamaka ndithu cisomo ca Mulungu, ndi mphatso yaulere zakucokera ndi munthu mmodziyo Yesu Kristu, zinacurukira anthu ambiri.


AROMA 5:17
Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu.


AROMA 5:21
kuti, mongaucimo unacita ufumu muimfa, comweconso cisomo cikacite ufumu mwa cilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.


AROMA 6:3
Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?


AROMA 6:11
Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.


AROMA 6:23
Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.


AROMA 7:25
Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo.


AROMA 8:1
Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.


AROMA 8:2
Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.


AROMA 8:11
Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.


AROMA 8:34
9 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, 10 amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, 11 amenenso atipempherera ife.


AROMA 8:39
ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.


AROMA 10:9
kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:


AROMA 13:14
Koma bvalani inu Ambuye Yesu-Kristu, ndipo musaganizire za thupi kucita zofuna zace.


AROMA 14:14
Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe cinthu conyansa pa cokha; koma kwa ameneyo aciyesa conyansa, kwa iye cikhala conyansa.


AROMA 15:5
Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;


AROMA 15:6
kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.


AROMA 15:16
kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


AROMA 15:17
Cifukwa cace ndiri naco codzitamandira ca m'Kristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.


AROMA 15:30
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;


AROMA 16:3
Mulankhule Priska ndi Akula, anchito anzanga m'Kristu Yesu,


AROMA 16:20
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.


AROMA 16:25
Ndipo kwa iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa uthenga wanga wabwino, ndi kulalildra kwa Yesu Kristu, monga mwa bvumbulutso la cinsinsi cimene cinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,


AROMA 16:27
kwa Mulungu wanzeru Yekha Yekha, mwa Yesu Kristu, kwa Yemweyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.


1 AKORINTO 1:1
PAULO, woitanidwa akhale mtumwi wa Yesu Kristu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Sositene mbaleyo,


1 AKORINTO 1:2
kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Kristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


1 AKORINTO 1:3
Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


1 AKORINTO 1:4
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, cifukwa ca cisomo ca Mulungu cinapatsidwa kwa inu mwa Kristu Yesu;


1 AKORINTO 1:7
kotero kuti sicikusowani inu caufuru ciri conse; pakulindira inu bvumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu;


1 AKORINTO 1:8
amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira cimariziro, kuti mukhale opanda cifukwa m'tsiku la Ambuye: wathu Yesu Kristu.


1 AKORINTO 1:9
Mulungu ali, wokhulupirika amene munaitanidwa mwa iye, ku ciyanjano ca Mwana wace Yesu Kristu, Ambuye wathu.


1 AKORINTO 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.


1 AKORINTO 1:30
Koma kwa iye muli inu mwa Kristu Yesu, 7 amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi cilungamo ndi ciyeretso ndi ciombolo;


1 AKORINTO 2:2
Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu koma Yesu Kristu, ndi iye wopacikidwa.


1 AKORINTO 3:11
Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.


1 AKORINTO 4:15
Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala Inu mwa Uthenga Wabwino.


1 AKORINTO 5:4
m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,


1 AKORINTO 5:5
kumpereka iye wocita cotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


1 AKORINTO 6:11
Ndipo ena ainu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


1 AKORINTO 8:6
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zicokera kwa iye, ndi ire kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.


1 AKORINTO 9:1
Kodi sindine mfulu? Kodi slndine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu nchito yanga mwa Ambuye?


1 AKORINTO 11:23
Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, cimenenso ndinapereka kwainu, kuti Ambuye Yesu usikuuja anaperekedwa, anatenga mkate;


1 AKORINTO 12:3
Cifukwa cace ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yew ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


1 AKORINTO 15:31
2 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndiri nako mwa Kristu Yesu, Ambuye wathu.


1 AKORINTO 15:57
koma 23 ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife cigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.


1 AKORINTO 16:23
Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu cikhale ndi inu.


1 AKORINTO 16:24
Cikondi canga cikhale ndi inu nonse mwa Kristu Yesu. Amen.


2 AKORINTO 1:1
PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya lonse:


2 AKORINTO 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


2 AKORINTO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,


2 AKORINTO 1:14
monganso munatibvomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.


2 AKORINTO 1:19
Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silvano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa iye.


2 AKORINTO 4:5
Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Kristu Yesu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, cifukwa ca Kristu.


2 AKORINTO 4:6
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kuturuka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa ciwalitsiro ca cidziwitso ca ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.


2 AKORINTO 4:10
nthawi zonse tirikusenzasenza m'thupi kufa kwace kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu.


2 AKORINTO 4:11
Pakuti ife amene tiri ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, cifukwa ca Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa.


2 AKORINTO 4:14
podziwa kuti iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.


2 AKORINTO 8:9
Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera.


2 AKORINTO 11:4
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena uthenga wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana nave bwino lomwe.


2 AKORINTO 11:31
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, iye amene alemekezeka ku nthawi yonse, adziwa kuti sindinama.


2 AKORINTO 13:5
Dziyeseni nokha, ngati muli m'cikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Kristu ali mwa inu? mukapanda kukhala osatsimikizidwa.


2 AKORINTO 13:14
Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mulungu, ndi ciyanjano ca Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


AGALATIYA 1:1
PAULO, mtumwi (wosacokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa iye kwa akufa),


AGALATIYA 1:3
Cisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu,


AGALATIYA 1:12
Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa bvumbulutso la Yesu Kristu.


AGALATIYA 2:4
ndico cifukwa ca abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nao mwa Kristu Yesu, kuti akaticititse iukapolo.


AGALATIYA 2:16
koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa: nchito ya lamulo, koma mwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu, ifedi tinakhulupirira kwa Yesu Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndicikhulupiriro ca Kristu, ndipo si ndi nchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi nchito za lamulo.


AGALATIYA 3:14
kutidalitso la Abrahamu mwa Yesu Kristu, licitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa cikhulupiriro.


AGALATIYA 3:22
Komatu lembo Iinatsekereza zonse pansi pa ucimo, kuti lonjezano la kwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.


AGALATIYA 3:26
3 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa cikhulupiriro ca mwa Yesu Kristu.


AGALATIYA 3:28
5 Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; 6 pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.


AGALATIYA 4:14
ndipo cija ca m'thupi langa cakukuyesani inu simunacipeputsa, kapena sicinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Kristu Yesu mwini.


AGALATIYA 5:6
Pakuti mwa Kristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu cikhulupiriro cakucititsa mwa cikondi.


AGALATIYA 5:24
Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace.


AGALATIYA 6:14
Koma kudzitamandira ine konse konse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene mwa iye dziko lapansi lapacikidwira ine, ndi ine ndapacikidwira dziko lapansi.


AGALATIYA 6:17
Kuyambira tsopano palibe munthu andibvute, pakuti ndiri nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.


AGALATIYA 6:18
Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.


AEFESO 1:1
PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Kristu Yesu:


AEFESO 1:2
Cisomo kwa inu, ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


AEFESO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;


AEFESO 1:5
Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana, a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace,


AEFESO 1:15
Mwa ici inenso, m'mene ndamva za cikhulupiriro'ca mwa Ambuye Yesu ciri mwa inu, cimenenso mufikitsira oyera mtima onse,


AEFESO 1:17
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire iye;


AEFESO 2:6
ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Kristu Yesu;


AEFESO 2:7
kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.


AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


AEFESO 2:13
Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Kristu.


AEFESO 2:20
omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa pangondya;


AEFESO 3:1
Cifukwa ca ici ine Paulo, ndine wandende wa Kristu Yesu cifukwa ca inu amitundu,


AEFESO 3:6
kuti amitundu ali olowanyumbapamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi oland ira nafe pamodzi palonjezano mwa Kristu Yesu, mwa Uthenga Wabino,


AEFESO 3:11
monga mwa citsimikizo mtima ca nthawi za nthawi, cimene anacita mwa Kristu Yesu Ambuye wathu:


AEFESO 3:21
kwa iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Kristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.


AEFESO 4:21
ngatitu mudamva iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa iye, monga coonadi ciri mwa Yesu;


AEFESO 5:20
ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;


AEFESO 6:7
akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai;


AEFESO 6:23
3 Mtendere ukhale kwa abale, ndi cikondi, pamodzi ndi cikhulupiriro, zocokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Kristu.


AEFESO 6:24
Akhale naco cisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Kristu m'eosaonongeka.


AFILIPI 1:1
PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


AFILIPI 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.


AFILIPI 1:6
pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;


AFILIPI 1:8
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Kristu Yesu.


AFILIPI 1:11
odzala nacocipatso ca cilungamo cimene ciri mwa Yesu Kristu, kucitira Mulungu ulemerero ndi ciyamiko.


AFILIPI 1:19
Pakuti ndidziwa kuti ici cidzandicitira ine cipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Kristu;


AFILIPI 1:26
kuti kudzitamandira kwanu kucuruke m'Kristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.


AFILIPI 2:5
Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,


AFILIPI 2:10
kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,


AFILIPI 2:11
ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.


AFILIPI 2:19
Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.


AFILIPI 2:21
Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Kristu.


AFILIPI 3:3
pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi;


AFILIPI 3:8
Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale citayiko cifukwa ca mapambanidwe a cizindikiritso ca Kristu Yesu Ambuye wanga, cifukwa ca Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu,


AFILIPI 3:12
Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikacigwire ici cimene anandigwirira Yesu Kristu.


AFILIPI 3:14
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.


AFILIPI 3:20
Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; z kucokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu;


AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.


AFILIPI 4:19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m'ulemerero mwa Kristu Yesu.


AFILIPI 4:21
Lankhulani woyera mtima ali yense mwa Kristu Yesu. Abalewo akukhala ndiine alankhula inu.


AFILIPI 4:23
Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu.


AKOLOSE 1:1
PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,


AKOLOSE 1:3
Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu ndi kupempherera Inu nthawi zonse,


AKOLOSE 1:4
popeza tidamva za cikhulupiriro canu ca mwa Kristu Yesu, ndi cikondi muli naco kwa oyera mtima onse;


AKOLOSE 2:6
Cifukwa cace monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa iye,


AKOLOSE 3:17
Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.


AKOLOSE 4:11
ndi Yesu, wochedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo anchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine conditonthoza mtima.


AKOLOSE 4:12
Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira cifukwa ca inu m'mapemphero ace znasiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'cifuniro conse ca Mulungu.


1 ATESALONIKA 1:1
PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu: Cisomo kwa inu ndi mtendere.


1 ATESALONIKA 1:3
ndi kukumbukila kosalekeza nchito yanu ya cikhulupiriro, ndi cikondi cocitacita, ndi cipiriro ca ciyembekezo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;


1 ATESALONIKA 1:10
ndi kulindirira Mwana wace acokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulinkudza.


1 ATESALONIKA 2:14
Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda;


1 ATESALONIKA 2:15
amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;


1 ATESALONIKA 2:19
Pakuti ciyembekezo cathu, kapena cimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nciani? si ndinu nanga pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwace?


1 ATESALONIKA 3:11
Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu;


1 ATESALONIKA 3:13
kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda cifukwa m'ciyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ace onse.


1 ATESALONIKA 4:1
Cotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, eurukani koposa momwemo.


1 ATESALONIKA 4:2
Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.


1 ATESALONIKA 4:14
Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.


1 ATESALONIKA 5:9
Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire cipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu,


1 ATESALONIKA 5:18
M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.


1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.


1 ATESALONIKA 5:28
Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale nanu.


2 ATESALONIKA 1:1
PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu:


2 ATESALONIKA 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu.


2 ATESALONIKA 1:7
ndi kwa inu akumva cisautso mpumulo pamodzi ndi ire, pa bvumbulutso la Ambuye Yesu wocokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yace,


2 ATESALONIKA 1:8
m'lawi lamoto, ndi kubwezera cilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;


2 ATESALONIKA 1:12
kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa iye, monga mwa cisomo ca Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.


2 ATESALONIKA 2:1
Ndipo tikupemphani, abale, cifukwa ca kudza kwace kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye;


2 ATESALONIKA 2:8
Ndipo pamenepo adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pace, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwace;


2 ATESALONIKA 2:14
kumene aoaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Kristu.


2 ATESALONIKA 2:16
Ndipo Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa elsangalatso cosatha ndi ciyembekezo cokoma mwa cisomo,


2 ATESALONIKA 3:6
Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti mubwebvuke kwa mbale yense wakuyenda dwacedwace, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.


2 ATESALONIKA 3:18
Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.


1 TIMOTEO 1:1
PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu monga mwa cilamuliro ca Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi ca Kristu Yesu, ciyembekezo cathu:


1 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'cikhulupiriro: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Kristu Yesu Ambuye wathu.


1 TIMOTEO 1:12
Ndimyamika iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Kristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,


1 TIMOTEO 1:14
koma cisomo ca Ambuye wathu cidacurukatu pamodzi ndi cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.


1 TIMOTEO 1:15
Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; wa iwowa ine ndine woposa;


1 TIMOTEO 1:16
komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.


1 TIMOTEO 2:5
Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu,


1 TIMOTEO 3:13
Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukuru m'cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.


1 TIMOTEO 4:6
Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Kristu Yesu, woleredwa m'mauwo a cikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;


1 TIMOTEO 5:21
Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Kristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosacita kanthu monga mwa tsankhu.


1 TIMOTEO 6:3
Ngati munthu aphunzitsa zina, wosabvomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi ciphunzitsoco ciri monga mwa cipembedzo:


1 TIMOTEO 6:13
Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Kristu Yesu, amene anacitira umboni cibvomerezo cabwino kwa Pontiyo Pilato;


1 TIMOTEO 6:14
kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda cirema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu;


2 TIMOTEO 1:1
PAULO a mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Kristu Yesu,


2 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.


2 TIMOTEO 1:9
amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa nchito zathu, komatu monga mwa citsimikizo mtima ca iye yekha, ndi cisomo, copatsika kwa ife mwa Kristu Yesu zisanayambe nthawi zoyamba,


2 TIMOTEO 1:10
koma caonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Kristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi cosabvunda mwa Uthenga Wabwino,


2 TIMOTEO 1:13
Gwira citsanzo ca mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.


2 TIMOTEO 2:1
Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'cisomo ca m'Kristu Yesu.


2 TIMOTEO 2:3
Umve zowawa pamodzi nane monga msilikari wabwino wa Kristu Yesu.


2 TIMOTEO 2:8
Kumbukila Yesu Kristu, wouka kwa akufa, wocokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;


2 TIMOTEO 2:10
Mwa ici ndipirira zonse, cifukwa ca osankhika, kuti iwonso akapeze cipulumutsoeo ca mwa Kristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.


2 TIMOTEO 3:12
Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.


2 TIMOTEO 3:15
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira cipulumutso, mwa cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.


2 TIMOTEO 4:1
Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Kristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ace ndi ufumu wace;


TITO 1:1
PAULO, kapolo wa Mulungu ndi mtumwi wa Yesu Kristu monga mwa cikhulupiriro ca osa nkhika a Mulungu, ndi cizindikiritso ca coonadi ciri monga mwa cipembedzo,


TITO 1:4
kwa Tito, mwana wanga weni weni monga mwa cikhulupiriro ca ife tonse: Cisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Mpulumutsi wathu.


TITO 2:13
akulindira ciyembekezo eodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkuru ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu;


TITO 3:6
amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu;


FILEMONI 1:1
PAULO, wandende wa Kristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wanchito mnzathu,


FILEMONI 1:3
Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.


FILEMONI 1:5
pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;


FILEMONI 1:9
koma makamaka ndidandaulira mwa cikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Kristu Yesu;


FILEMONI 1:23
Epafra wandende mnzanga mwa Kristu Yesu akulankhula iwe;


FILEMONI 1:25
Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen.


AHEBRI 2:9
Koma timpenya iye amene adamcepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, cifukwa ca zowawa za imfa, wobvala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi cisomo ca Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu ali yense.


AHEBRI 3:1
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi. Mkuluwansembe wa cibvomerezo cathu, Yesu;


AHEBRI 4:14
Popeza tsono tiri naye Mkuluwansembe wamkuru, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse cibvomerezo cathu.


AHEBRI 6:20
m'mene Yesu mtsogoleri analowamo cifukwa ca ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.


AHEBRI 7:22
Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.


AHEBRI 10:10
Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.


AHEBRI 10:19
Ndipo pokhala naco, abale, cilimbikitso cakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,


AHEBRI 12:2
Yesu, ameneyo, cifukwa ca cimwemwe coikidwaco pamaso pace, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu,


AHEBRI 12:24
ndi kwa Yesu Nkhoswe ya cipangano catsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula cokoma coposa mwazi wa Abeli.


AHEBRI 13:8
Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse.


AHEBRI 13:12
Mwa ici Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa iye yekha, adamva cowawa kunja kwa cipata.


AHEBRI 13:20
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye woturuka mwa akufa 1 Mbusa wamkuru wa nkhosa 2 ndi mwazi wa cipangano cosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


AHEBRI 13:21
3 akuyeseni inu opanda cirema m'cinthu ciri conse cabwino, kuti mucite cifuniro cacej ndi kucita mwa ife comkondweretsa pamaso pace, mwa Yesu Kristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.


YAKOBO 1:1
YAKOBO, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'cibalaliko: ndikulankhulani.


YAKOBO 2:1
Abate anga, musakhale naco cikhulupiriro ca Ambuye wathu Yesu Kristu, Ambuye wa ulemerero, ndi kusamala maonekedwe.


1 PETRO 1:1
PETRO, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala: alendo a cibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,


1 PETRO 1:2
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.


1 PETRO 1:3
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa cifundo cace cacikuru, anatibalanso ku ciyembekezo ca moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu;


1 PETRO 1:7
kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;


1 PETRO 1:13
Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu m'bvumbulutso la Yesu Kristu;


1 PETRO 2:5
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu,


1 PETRO 3:21
cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu;


1 PETRO 4:11
akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, acite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.


2 PETRO 1:1
SIMONI Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Kristu kwa iwo amene adalandira cikhulupiriro ca mtengo wace womwewo ndi ife, m'cilungamo ca Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu:


2 PETRO 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere zicurukitsidwe m'cidziwitso ca Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.


2 PETRO 1:8
Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikacuruka, zidzacita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa cizindikiritso ca Ambuye wathu Yesu Kristu.


2 PETRO 1:11
pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.


2 PETRO 1:14
podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Kristu anandilangiza.


2 PETRO 1:16
Pakuti sitinatsata miyambi yacabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m'maso ukulu wace.


2 PETRO 2:20
Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa cizindikiritsoca, Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zorsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo,


2 PETRO 3:18
Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi Yesu vistu; kwa iye kukhale uleme'ero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


1 YOHANE 1:3
cimene tidaciona, ndipo tidacimva, tikulatikirani inunso, kuti inunso mukayaniane pamodzi ndi ife; ndipo ciyanjano cathu cirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wace Yesu Kristu;


1 YOHANE 1:7
koma ngati tiyenda m'kuunika, mongalye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzace, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo wonse.


1 YOHANE 2:1
Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musacimwe. Ndipo akacimwa wina, Nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama;


1 YOHANE 2:22
4 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Kristu? iye ndiye wokana Kristu, amene akana Atate ndi Mwana.


1 YOHANE 3:23
Ndipo 4 Lamulo lace ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wace Yesu Kristu, ndi 5 kukondana wina ndi mnzace, monga anatilamulira.


1 YOHANE 4:2
M'menemo muzindikira Mzimu Wl Mulungu: mzimu uli wonse umen ubvomereza kuti Yesu Kristu ana dza m'thupi, ucokera mwa. Mulungu


1 YOHANE 4:3
ndipo mzimu uli wonse umen subvomereza Yesu sucokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzirm wa wokana Kristu umene mudamvi kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,


1 YOHANE 4:15
Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.


1 YOHANE 5:1
Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu wabadwa kucokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wocokera mwa iye.


1 YOHANE 5:5
Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu


1 YOHANE 5:6
iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi; ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi.


1 YOHANE 5:20
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife cidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tiri mwa Woonayo, mwa Mwana wace Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


2 YOHANE 1:3
Cisomo, cifundo, mtendere zikhale ndi ife zocokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Kristu Mwana wa Atate, m'coonadi ndi m'cikondi.


2 YOHANE 1:7
Pakuti onyenga ambiri adaturuka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene sabvomereza kuti Yesu Kristu anadza m'thupi, Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.


YUDA 1:1
YUDA, kapolo wa Yesu Kristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Kristu:


YUDA 1:4
Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira citsutso ici, anthu osapembedza, akusandutsa cisomo ca Mulungu wathu cikhale cilak olako conyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.


YUDA 1:17
Koma inu, abale, mukumbukile mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Kristu;


YUDA 1:21
mudzisunge nokha m'cikondi ca Mulungu, ndi 5 kulindira cifundo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.


YUDA 1:25
10 kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.


CHIVUMBULUTSO 1:1
CIBVUMBULUTSO ca Yesu Kristu, cimene Mulungu anambvumbulutsira acionetsere akapolo ace, ndico ca izi ziyenera kucitika posacedwa: ndipo potuma mwa mngelo wace anazindikiritsa izi kwa kapolo wace Yohane;


CHIVUMBULUTSO 1:2
amene anacita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Kristu, zonse zimene adaziona.


CHIVUMBULUTSO 1:5
ndi kwa Yesu Kristu, mboli yokhulupirikayo, wobadwa woyanba wa akufa, ndi mkulu wa mafunu a dziko lapansi, Kwa iye ameieatikonda ife, natimasula ku macimo athu ndi mwazi wace;


CHIVUMBULUTSO 1:9
Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'cisautso ndi ufumu ndi cipiriro zokhala m'Yesu, ndinakhala pa cisumbu cochedwa Patmo, cifukwa ca mao a Mulungu ndi umboni wa Yesu.


CHIVUMBULUTSO 12:17
Ndipo cinjoka cinakwiya ndi mkazi, nicinacoka kunka kucita nkhondondi otsala ambeu yace, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.


CHIVUMBULUTSO 14:12
Pano pali cipiriro ca oyera mtima, ca iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi cikhulupiriro ca Yesu.


CHIVUMBULUTSO 17:6
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukuru.


CHIVUMBULUTSO 19:10
Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.


CHIVUMBULUTSO 20:4
Ndipo ndinaona mipando yacifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa ciweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi cifukwa ca umboni wa Yesu, ndi cifukwa ca mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira cirombo, kapena fano lace, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nacita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka cikwi.


CHIVUMBULUTSO 22:16
Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukucitirani umboni za izi m'Mipingo. Ine ndine muzo ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.


CHIVUMBULUTSO 22:20
Iye wakucitira umboni izi, anena, 4 Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.


CHIVUMBULUTSO 22:21
5 Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale ndi oyera mtima onse, Amen.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society