A A A A A


Sakani

MATEYU 3:17
ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


MATEYU 12:18
Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; Pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, Ndipo Iye adzalalikira ciweruzo kwa akunja.


MATEYU 17:5
Akali cilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphi mba iwo: ndipo onani, mau alikunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


MARKO 1:11
ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.


MARKO 9:7
Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munaturuka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.


MARKO 12:6
Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wace wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamcitira ulemu mwana wanga.


LUKA 3:22
ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.


LUKA 7:2
Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.


AROMA 9:25
Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawacha anthu anga; Ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.


AROMA 16:5
ndipo mulankhule Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Mulankhule Epeneto wokondedwa wanga, ndiye cipatso coundukula ca Asiya ca kwa Kristu,


AROMA 16:8
Mulankhule Ampliato wokondedwa wanga mwa Ambuye.


AROMA 16:9
Mulankhule Urbano wanchito mnzathu mwa Kristu, ndi Staku wokondedwa wanga,


AROMA 16:12
Mulankhule Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa nchito mwa Ambuyeo Mulankhule. Persida, wokondedwayo amene anagwiritsa nchito zambiri mwa Ambuye.


1 AKORINTO 4:17
Cifukwa ca ici ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Kristu, monga ndiphunzitsa ponsepom'Mipingo yonse.


AEFESO 1:6
kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


AEFESO 6:21
Koma 2 kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndicita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tukiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;


AKOLOSE 1:7
monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiyemtumiki wokhulupirika wa Kristu cifukwa ca ife;


AKOLOSE 4:7
Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:


AKOLOSE 4:9
pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.


AKOLOSE 4:14
Akulankhulani inu Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.


2 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.


FILEMONI 1:1
PAULO, wandende wa Kristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wanchito mnzathu,


FILEMONI 1:16
osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.


2 PETRO 1:17
Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;


2 PETRO 3:15
Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu cipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa cwa iye, anakulemberani;


3 YOHANE 1:1
MKURUYO kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'coonadi.


3 YOHANE 1:2
Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera,


3 YOHANE 1:5
Wokondedwa, ucita cokhulupirika naco ciri conse, uwacitira abale ndi alendo omwe;


3 YOHANE 1:11
Wokondedwa, usatsanza ciri coipa komatu cimene ciri cokoma. Iye wakucita cokoma acokera kwa Mulungu; ye wakucita coipa sanamuona Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 20:9
Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society