A A A A A

Sakani
MATEYU 4:10
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.


MATEYU 12:26
ndipo ngati Satana amaturutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wace?


MATEYU 16:23
Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe condikhumudwitsa Ine; cifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.


MATEYU 27:62
Ndipo m'mawa mwace, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe akuru ndi Afarisi anasonkhanira kwa Pilato,


MARKO 1:13
Ndipo anakhala m'cipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo anamtumikira.


MARKO 3:23
Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kuturutsa Satana?


MARKO 3:26
Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika.


MARKO 4:15
Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nacotsa mau ofesedwa mwa iwo.


MARKO 8:33
Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ace, namdzudzula Petro, nanena, Coka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.


LUKA 9:49
Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa satsatana nafe.


LUKA 10:18
Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wocokera kumwamba.


LUKA 11:18
Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.


LUKA 13:16
Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yace imeneyi tsiku la Sabata?


LUKA 22:3
Ndipo Satana analowa m'Yudase wonenedwa Isikariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo,


LUKA 22:31
Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;


YOHANE 13:27
Ndipopambuyo pace pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Cimene ucita, cita msanga,


MACHITIDWE A ATUMWI 1:21
Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife,


MACHITIDWE A ATUMWI 5:3
Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?


MACHITIDWE A ATUMWI 26:18
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine.


AROMA 16:20
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.


1 AKORINTO 5:5
kumpereka iye wocita cotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


1 AKORINTO 7:5
Musakanizana, koma ndi kubvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, cifukwa ca kusadziletsa kwanu.


1 AKORINTO 14:27
Ngati wina alankhula lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.


2 AKORINTO 2:11
kuti asaticenierere Satana; pakuti sitikhala osadziwa macenjerero ace.


2 AKORINTO 11:14
Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.


2 AKORINTO 12:7
Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, cifukwa ca ukulu woposa wa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelowa Satana kutianditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.


1 ATESALONIKA 2:18
cifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa.


2 ATESALONIKA 2:9
ndiye amene kudza kwace kuli monga mwa macitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikilo ndi zozizwa zonama;


1 TIMOTEO 1:20
a iwo ali Humenayo ndi Alesandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.


1 TIMOTEO 5:15
pakuti adayamba enakupatuka ndi kutsata Satana.


YUDA 1:7
Monga; Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kursara zilakolako zacilendo, iikidwa citsanzo, pakucitidwa cilango ca mota wosatha.


CHIVUMBULUTSO 2:9
Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.


CHIVUMBULUTSO 2:13
Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wacifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza cikhulupiriro canga, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


CHIVUMBULUTSO 2:24
Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiyatira, onse amene alibe ciphunzitso ici, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.


CHIVUMBULUTSO 3:9
Taona, ndikupatsa ena oturuka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


CHIVUMBULUTSO 6:8
Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.


CHIVUMBULUTSO 12:9
Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.


CHIVUMBULUTSO 14:13
Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti nchito zao zitsatana nao pamodzi.


CHIVUMBULUTSO 20:2
Ndipo anagwira cinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka cikwi,


CHIVUMBULUTSO 20:7
Ndipo pamene zidzatha zaka cikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yace;


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society