A A A A A

Sakani
LUKA 1:13
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane.


LUKA 5:33
Ndipo iwo anati kwa iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawiri kawiri, ndi kucita mapemphero; cimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.


LUKA 20:47
amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga acita mai pemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.


2 AKORINTO 1:11
amene timyembekezera kuti adzalanditsanso; pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri cifukwa ca ife.


AEFESO 1:16
sindileka kuyamikacifukwa ca inu, ndi kukumbukila inu m'mapemphero anga;


AEFESO 6:18
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


AFILIPI 4:6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.


AKOLOSE 4:12
Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira cifukwa ca inu m'mapemphero ace znasiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'cifuniro conse ca Mulungu.


1 ATESALONIKA 1:2
Tiyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu nonse, ndi kukumbukila inu m'mapemphero athu;


1 ATESALONIKA 3:10
ndi kucurukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa cikhulupiriro canu?


1 TIMOTEO 2:1
Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse;


1 TIMOTEO 5:5
Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


2 TIMOTEO 1:3
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi cikumbu mtima coyera, kuti ndikumbukila iwe kosalekeza m'mapemphero anga,


FILEMONI 1:4
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukila iwe m'mapemphero anga,


FILEMONI 1:22
Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.


YAKOBO 5:15
ndipo pemphero la cikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adacita macimo adzakhululukidwa kwa iye.


YAKOBO 5:16
Cifukwa cace mubvomerezane wina ndi mnzace macimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzace kuti muciritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukuru m'macitidweace.


1 PETRO 3:7
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa cidziwitso, ndi kucitira mkazi ulemu, monga cotengera cocepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa cisomo ca moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.


1 PETRO 4:7
Koma citsiriziro ca zinthu zonse ciri pafupi; cifukwa cace khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


CHIVUMBULUTSO 5:8
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nao azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 8:3
Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala naco cotengera ca zofukiza cagolidi; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wacifumu.


CHIVUMBULUTSO 8:4
Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kuturuka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society