A A A A A

Sakani
MATEYU 1:18
Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.


MATEYU 1:20
Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.


MATEYU 3:11
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zace: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


MATEYU 3:16
Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


MATEYU 4:1
Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kumka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.


MATEYU 5:3
Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.


MATEYU 10:20
pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.


MATEYU 12:18
Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; Pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, Ndipo Iye adzalalikira ciweruzo kwa akunja.


MATEYU 12:28
Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.


MATEYU 12:31
Cifukwa cace ndinena kwa inu, Macimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma camwano ca pa Mzimu Woyera sicidzakhululukidwa.


MATEYU 12:32
Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudzayo.


MATEYU 12:43
Koma mzimu wonyansa, utaturuka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.


MATEYU 22:43
Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amchula Iye bwanji Ambuye, nanena,


MATEYU 26:41
Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka.


MATEYU 27:50
Ndipo Yesu, 9 pamene anapfuula ndi mau akuru, anapereka mzimu wace.


MATEYU 28:19
Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


MARKO 1:8
Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.


MARKO 1:10
Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:


MARKO 1:12
Ndipo pomwepo Mzimu anamkangamiza kunka kucipululu.


MARKO 1:23
Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anapfuula iye


MARKO 1:26
Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kupfuula ndi mau akuru, unaturuka mwa iye.


MARKO 3:29
koma ali yense adzacitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anaparamuladi cimo losatha;


MARKO 3:30
pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.


MARKO 5:2
Ndipo pameneadaturuka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu woturuka kumanda wa mzimu wonyansa,


MARKO 5:8
Pakuti ananena kwa iye, Turuka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.


MARKO 7:25
Koma pomwepo mkazi, kabuthu kace kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ace.


MARKO 8:12
Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wace, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna cizindikilo bwanji? indetu ndinena kwa inu, ngati cizindikilo cidzapatsidwa kwa mbadwo uno!


MARKO 9:17
Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula;


MARKO 9:20
Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsya; ndipo anagwa pansi nabvimbvinika ndi kucita thobvu.


MARKO 9:25
Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lirikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, turuka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.


MARKO 12:36
Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala ku dzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.


MARKO 13:11
Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musada nkhawa usanayambe mrandu ndi cimene mudzalankhula; koma ci mene cidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, mucilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.


MARKO 14:38
Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.


MARKO 15:37
Ndipo Yesr anaturutsa mau okweza, napereka mzimu wace.


MARKO 15:39
Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.


LUKA 1:15
Pakuti iye adzakhala wamkuru pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena, kacasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.


LUKA 1:17
Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


LUKA 1:35
Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.


LUKA 1:41
Ndipo panali pamene Elisabeti anamva kulankhula kwace kwa Mariya, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwace; ndipo Elisabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;


LUKA 1:47
Ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.


LUKA 1:67
Ndipo atate wace Zakariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,


LUKA 1:80
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wace, ndipo 23 iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.


LUKA 2:25
Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lace Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


LUKA 2:26
Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu wace wa Ambuye.


LUKA 2:27
Ndipo iye analowa kuKacisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amace analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamcitira iye mwambo wa cilamulo,


LUKA 3:16
Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zace; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


LUKA 3:22
ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.


LUKA 4:1
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.


LUKA 4:14
Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yace ya iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.


LUKA 4:18
Mzimu wa Ambuye uli paine, Cifukwa cace iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, Ndi akhungu kuti apenyenso, Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,


LUKA 8:29
Pakuti iye adalamula mzimu wonyansa uturuke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi ciwandaco kumapululu.


LUKA 8:55
Ndipo mzimu wace unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya.


LUKA 9:39
ndipo onani, umamgwira iye mzimu, napfuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumcititsa thobvu pakamwa, nucoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye.


LUKA 9:42
Ndipo akadadza iye, ciwandaco cinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa, Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, naciritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wace.


LUKA 10:21
Nthawi yomweyo iye anakondwera ndi Mzimu Wovera, nati, Ndikubvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.


LUKA 11:13
Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha iye?


LUKA 11:24
Pamene pali ponse mzimu wonyansa ukaturuka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinaturukako;


LUKA 12:10
Ndipo amene ali yense adzanenera Mwana wa munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.


LUKA 12:12
pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.


LUKA 13:11
Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.


Луки 23:46
Ndipo pamene Yesu anapfuula ndi mau akuru, anati, 1 Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wace.


Луки 24:37
Koma anaopsedwandi kucita mantha, 1 nayesa alikuona mzimu.


Луки 24:39
Penyani manja anga ndi mapazianga, kuti Ine ndine mwini: 2 ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe, mnofu ndi mafupa, monga muona ndirinazo Ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:2
kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;


MACHITIDWE A ATUMWI 1:5
pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:8
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.


MACHITIDWE A ATUMWI 1:16
Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davine za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:4
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:17
Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse, Ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, Ndi akulu anu adzalota maloto;


MACHITIDWE A ATUMWI 2:18
Ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa Ndidzathira ca Mzimu wanga; ndipo adzanenera.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:33
Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja Lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ici, cimene inu mupenya nimumva.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:8
Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,


MACHITIDWE A ATUMWI 4:25
amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davine mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera cifukwaciani? Nalingirira zopanda pace anthu?


MACHITIDWE A ATUMWI 4:31
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:3
Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?


MACHITIDWE A ATUMWI 5:9
Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kuturuka nawe.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:32
Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:3
Cifukwa cace, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yahwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge nchito iyi.


MACHITIDWE A ATUMWI 6:5
Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi cikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolao, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


MACHITIDWE A ATUMWI 6:10
Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:51
22 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:55
Koma iye, 25 pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:59
Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, 29 Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:15
amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:


MACHITIDWE A ATUMWI 8:17
Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:18
Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,


MACHITIDWE A ATUMWI 8:19
nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene ali yense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:29
Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:39
Ndipo pamene anakwera kururuka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yace wokondwera.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:17
Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:31
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:19
Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu ananena naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:38
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nacita zabwino, naciritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:44
Petro ali cilankhulire, 5 Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:45
Ndipo 6 anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, cifukwa pa 7 amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:47
Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera 8 ngatinso ife?


MACHITIDWE A ATUMWI 11:12
Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;


MACHITIDWE A ATUMWI 11:15
Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:16
Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:24
cifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi cikhulupiriro: ndipo khamu lalikuru lidaonjezeka kwa Ambuye.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:28
Ndipo anyanamuka mmodzi wa iwo, dzina lace Agabo, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudiyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:2
Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:4
Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya; ndipo pocokerapo anapita m'ngalawa ku Kupro.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:9
Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye,


MACHITIDWE A ATUMWI 13:52
Ndipo 14 akuphunzira anadzazidwa ndi cimwemwe ndi Mzimu Woyera.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:8
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawacitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;


MACHITIDWE A ATUMWI 15:28
Pakuti cinakomer a Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu cothodwetsa cacikuru cina coposa izi zoyenerazi;


MACHITIDWE A ATUMWI 16:6
Ndipo anapita pa dziko la Frugiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Musiya,


MACHITIDWE A ATUMWI 16:7
anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;


MACHITIDWE A ATUMWI 16:16
Ndipo panali, pamene tinalinkunka kukapemphera, anakomana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ace zambiri pakubwebweta pace.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:18
Ndipo anacita cotero masiku ambiri. Koma Paulo anabvutika mtima ndithu, naceuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Kristu, turuka mwa iye. Ndipo unaturuka nthawi yomweyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 18:25
Iyeyo aoaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wacangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


MACHITIDWE A ATUMWI 19:2
ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira? Ndipo anati, lai, sitinamva konsekuti Mzimu Woyera waperekedwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:6
Ndipo pamene Paulo anaika manja ace pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:15
Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?


MACHITIDWE A ATUMWI 19:16
Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amarisece ndi olasidwa.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:21
Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wace, atapita pa Makedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:22
Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidza'ndigwera ine kumeneko;


MACHITIDWE A ATUMWI 20:23
koma kuti Mzimu Woyera andicitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:28
Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:4
Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masikuasanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:11
Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:8
Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi abvomereza ponse pawiri.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:9
Ndipo cidauka cipolowe cacikuru; ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza coipa ciri conse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo: walankhula naye?


MACHITIDWE A ATUMWI 28:25
Koma popeza sanabvomerezana, anacoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,


Римлян 1:4
amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa ciyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu;


Римлян 1:9
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wace, kuti kosalekeza ndikumbukila inu, ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga,


Римлян 2:29
koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwace sikucokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.


Римлян 5:5
ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.


Римлян 7:6
Koma tsopano tinamasulidwa kucilamulo, popeza tinafa kwa ici cimene tinagwidwa naco kale; cotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'cilembo cakale ai.


Римлян 8:2
Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.


Римлян 8:4
kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.


Римлян 8:5
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:


Римлян 8:6
pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.


Римлян 8:9
Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.


Римлян 8:10
Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.


Римлян 8:11
Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.


Римлян 8:13
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.


Римлян 8:14
Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,


Римлян 8:15
Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,


Римлян 8:16
Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;


Римлян 8:23
Ndipo si cotero cokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo ciomboledwe ca thupi lathu.


Римлян 8:26
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene tizipempha monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;


Римлян 8:27
ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.


Римлян 9:1
Ndinena zoona mwa Kristu, sindinama ai, cikumbu mtima canga cicita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,


Римлян 11:8
monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.


Римлян 12:11
musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani Ambuye;


Римлян 14:17
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala cakudya ndi cakumwa, koma cilungamo, ndi mtendere, ndi cimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Римлян 15:13
Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.


Римлян 15:16
kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.


Римлян 15:19
mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu;


Римлян 15:30
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;


2 AKORINTO 1:22
amenenso anatisindikiza cizindikilo, natipatsa cikole ca Mzimu mu mitima yathu.


2 AKORINTO 2:13
ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Makedoniya.


2 AKORINTO 3:3
popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosatim'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.


2 AKORINTO 3:6
amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la cilembo, koma la mzimu; pakuti cilembo cipha, koma mzimu ucititsa moyo.


2 AKORINTO 3:8
koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala m'ulemerero?


2 AKORINTO 3:17
Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.


2 AKORINTO 3:18
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'cithunzihunzi comweci kucokera kuulenerero kumka kuulemerero, monga ngati kucokera kwa Ambuye Mzimu.


2 AKORINTO 4:13
Koma pokhala nao mzimu womwewo wa cikhulupiriro, monga mwa colembedwaco, ndinakhulupira, cifukwa cace ndinalankhula; ifenso tikhulupira, cifukwa cace tilankhula;


2 AKORINTO 5:5
Ndipo wotikonzera ife ici cimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife cikhole ca Mzimu,


2 AKORINTO 6:6
m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;


2 AKORINTO 7:1
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsirfza ciyero m'kuopa Mulungu.


2 AKORINTO 7:13
Cifukwa ca icitatonthozedwa; ndipo m'citonthozo cathu tinakondwera koposa ndithu pa cimwemwe ca Tito, kuti mzimu wace unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.


2 AKORINTO 11:4
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena uthenga wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana nave bwino lomwe.


2 AKORINTO 12:18
Kodi Tito anakucenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?


2 AKORINTO 13:14
Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mulungu, ndi ciyanjano ca Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


AGALATIYA 3:2
ici cokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?


AGALATIYA 3:3
Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?


AGALATIYA 3:5
Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nacita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?


AGALATIYA 3:14
kutidalitso la Abrahamu mwa Yesu Kristu, licitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa cikhulupiriro.


AGALATIYA 4:6
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wace alowe m'mitima yathu, wopfuula Abba, Atate.


AGALATIYA 4:29
Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano,


AGALATIYA 5:5
Pakuti ife mwa Mzimu, kucokera m'cikhulupiriro, tilindira ciyembekezo ca cilungamo,


AGALATIYA 5:16
Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.


AGALATIYA 5:17
Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.


AGALATIYA 5:18
Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.


AGALATIYA 5:22
Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,


AGALATIYA 5:25
1 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.


AGALATIYA 6:1
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa cifatso; ndikudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.


AGALATIYA 6:8
Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m'thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.


AGALATIYA 6:18
Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.


AEFESO 1:3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;


AEFESO 1:13
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,


AEFESO 1:17
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire iye;


AEFESO 2:2
zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakucita tsopano mwa ana a kusamvera;


AEFESO 2:18
kuti mwa iye ife tonse awiri tiri nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.


AEFESO 2:22
3 cimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale cokhalamo Mulungu mwa Mzimu.


AEFESO 3:5
cimene sanacizindikiritsa ana a anthu m'mibadwo yina, monga anacibvumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ace oyera mwa Mzimu,


AEFESO 3:16
kuti monga mwa cuma ca ulemerero wace akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wace, m'kati mwanu,


AEFESO 4:3
ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa cimangiriro ca mtendere.


AEFESO 4:4
Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi ca maitanidwe anu;


AEFESO 4:23
koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,


AEFESO 4:30
Ndipo 10 musamvetse cisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe.


AEFESO 5:18
Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu,


AEFESO 6:17
Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;


AEFESO 6:18
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


AFILIPI 1:19
Pakuti ndidziwa kuti ici cidzandicitira ine cipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Kristu;


AFILIPI 1:27
Cokhaci, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Kristu: kuti, ndingakhale nditi ndirinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndiri kwina, ndikamva za kwa inu, kuti mucirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi cikhulupiriro ca Uthenga Wabwino;


AFILIPI 2:1
Ngati tsono muli citonthozo mwa Kristu, ngati cikhazikitso ca cikondi, ngati ciyanjano ca Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,


AFILIPI 3:3
pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi;


AFILIPI 4:23
Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu.


AKOLOSE 1:8
amenenso anatifotokozera cikondi canu mwa Mzimu.


AKOLOSE 1:9
Mwa ici ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi cizindikiritso ca cifuniro cace mu nzeru zonse ndi cidziwitso ca mzimu,


AKOLOSE 2:5
Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.


1 ATESALONIKA 1:5
kuti Vthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kucuruka kwakukuru; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu cifukwa ca inu.


1 ATESALONIKA 1:6
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'cisautso cambiri, ndi cimwemwe ca Mzimu Woyera;


1 ATESALONIKA 4:8
Cifukwa cace iye wotaya ici, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wace Woyera kwa inu.


1 ATESALONIKA 5:19
Musazime Mzimuyo;


1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.


2 ATESALONIKA 2:2
kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;


2 ATESALONIKA 2:8
Ndipo pamenepo adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pace, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwace;


2 ATESALONIKA 2:13
Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi;


1 TIMOTEO 3:16
Ndipo pobvomerezeka, cinsinsi ca kucitira Mulungu ulemu ncacikuru: iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.


1 TIMOTEO 4:1
Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya cikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosoceretsa ndi maphunziro a ziwanda,


2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.


2 TIMOTEO 1:14
Cosungitsa cokomaca udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.


2 TIMOTEO 4:22
2 Ambuye akhale ndi mzimu wako. Cisomo cikhale nanu.


TITO 3:5
zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,


FILEMONI 1:25
Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen.


AHEBRI 2:4
pocita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikilo, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundu mitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa cifuniro cace.


AHEBRI 3:7
Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ace,


AHEBRI 4:12
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.


AHEBRI 6:4
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,


AHEBRI 9:8
Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo ku malo opatulika siinaonetsedwe, pokhala cihema coyamba ciri ciriri;


AHEBRI 9:14
koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


AHEBRI 10:15
Koma Mzimu Woyeranso aticitira umboni; pakuti adatha kunena,


AHEBRI 10:29
ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa cipangano umene anayeretsedwa nao cinthu wamba, z nacitira cipongwe Mzimu wa cisomo;


YAKOBO 2:26
Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso cikhulupiriro copanda nchito ciri cakufa.


YAKOBO 4:5
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena cabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kucita nsanje?


1 PETRO 1:2
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.


1 PETRO 1:11
ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera, pakucitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero, worsarana nao.


1 PETRO 1:12
Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kucokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


1 PETRO 3:4
koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.


1 PETRO 3:18
Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu;


1 PETRO 4:6
Pakuti cifukwa ca ici walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m'thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.


1 PETRO 4:14
Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.


2 PETRO 1:21
pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


3 YOHANE 1:2
Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera,


YUDA 1:19
Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe acibadwidwe, osakhala naye Mzimu.


YUDA 1:20
Koma inu, okondedwa, 3 podzimangirira nokha pa cikhulupiriro canu coyeretsetsa, ndi 4 kupemphera mu Mzimu Woyera,


CHIVUMBULUTSO 1:10
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akuru, ngati a lipenga,


CHIVUMBULUTSO 2:7
Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo, K wa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 2:11
Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzacitidwa coipa ndi imfa yaciwiri.


CHIVUMBULUTSO 2:17
Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.


CHIVUMBULUTSO 2:29
Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.


CHIVUMBULUTSO 3:6
Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.


CHIVUMBULUTSO 3:13
Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.


CHIVUMBULUTSO 3:22
Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.


CHIVUMBULUTSO 4:2
Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wacifumu m'Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;


CHIVUMBULUTSO 11:11
Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lace mzimu wamoyo wocokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala ciriri; ndipomantha akuru anawagwera iwo akuwapenya.


CHIVUMBULUTSO 14:13
Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti nchito zao zitsatana nao pamodzi.


CHIVUMBULUTSO 17:3
Ndipo ananditenga kumka nane kucipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pacirombo cofiiritsa, codzala ndi maina a mwano, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.


CHIVUMBULUTSO 19:10
Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.


CHIVUMBULUTSO 21:10
Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka ku phiri lalikuru ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika m'Mwamba kucokera kwa Mulungu,


CHIVUMBULUTSO 22:17
Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani, Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society