A A A A A


Sakani

MATEYU 1:19
Koma Yosefe, mwamuna wace, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri,


MATEYU 2:16
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'miraga yace yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.


MATEYU 3:8
Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:


MATEYU 3:11
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zace: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


MATEYU 5:8
Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.


MATEYU 5:28
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kucita naye cigololo mumtima mwace.


MATEYU 6:21
pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.


MATEYU 9:2
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pachika: ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, macimo ako akhululukidwa.


MATEYU 9:3
Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu acitira Mulungu mwano.


MATEYU 9:22
Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, cikhulupiriro cako cakuciritsa. Ndipo mkaziyo anacira kuyambira nthawi yomweyo.


MATEYU 9:36
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi cisoni cifukwa ca iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.


MATEYU 10:16
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi; cifukwa cace khalani ocenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


MATEYU 11:21
Tsoka kwa iwe, Korazini! tsoka kwa iwe, Betsaida! cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa inu zikadacitidwa m'Turo ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kale kale m'ziguduli ndi m'phulusa.


MATEYU 11:29
Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.


MATEYU 12:34
Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwace kwa mtima.


MATEYU 12:40
pakuti monga Yona anali m'mimba mwa cinsomba masiku atatu ndi usiku wace, comweco Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wace.


MATEYU 12:41
1 Anthu a ku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa 2 iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwace kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.


MATEYU 13:15
Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa, Ndipo m'makutu ao anamva mogontha, Ndipo maso ao anatsinzina; Kuti asaone konse ndi maso, Asamve ndi makutu, Asazindikire ndi mtima wao, Asatembenuke, Ndipo ndisawaciritse iwo.


MATEYU 13:19
Munthu ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.


MATEYU 14:27
Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.


MATEYU 14:31
Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lace, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?


MATEYU 15:8
Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.


MATEYU 15:18
Koma zakuturuka m'kamwa zicokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu.


MATEYU 15:19
Pakuti mumtima mucokera maganizo oipa, zakupha, zacigololo, zaciwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;


MATEYU 15:32
Ndipo Yesu anaitana ophunzira ace, nati, Mtima wanga ucitira cifundo khamu la anthuwa, pakuti ali cikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira,


MATEYU 18:27
Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi cisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.


MATEYU 19:8
Iye ananena kwa iwo, Cifukwa ca kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kucotsa akazi anu; koma paciyambi sikunakhala comweco.


MATEYU 20:24
Ndipo m'mene khurniwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.


MATEYU 21:15
Koma ansembe akuru ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazicita, ndi ana alinkupfuula kuKacisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,


MATEYU 21:29
Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pace analapa mtima napita.


MATEYU 22:37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.


MATEYU 22:46
Ndipo sanalimbika mtima munthu ali yense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.


MATEYU 24:48
Koma kapolo woipa akanena mumtima mwace, Mbuye wanga wacedwa;


MATEYU 25:24
Ndipo uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza;


MATEYU 26:8
Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Cifukwa ninji kuononga kumeneku?


MATEYU 26:75
Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, 12 Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anaturukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.


MATEYU 27:52
ndi Manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;


MATEYU 28:14
Ndipo ngati ici cidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.


MARKO 1:4
Yohane anadza nabatiza m'cipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku cikhululukiro ca macimo.


MARKO 1:15
nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.


MARKO 2:6
Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao,


MARKO 2:8
Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwace kuti alikuganizira comweco mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?


MARKO 6:20
pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, oakondwa kumva iye.


MARKO 6:50
pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope,


MARKO 7:6
Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, Koma mtima wao ukhala kutari ndi ine.


MARKO 7:19
cifukwa sikalowa mumtima mwace, koma m'mimba mwace, ndipo katurukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.


MARKO 10:41
Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima cifukwa ca Yakobo ndi Yohane.


MARKO 10:49
Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.


MARKO 11:23
Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwace, koma adzakhulupirira kuti cimene acinena cicitidwa, adzakhala naco.


MARKO 12:30
ndipouzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.


MARKO 12:33
ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzace monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.


MARKO 12:34
Ndipo palmona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kwnfunsa Iye kanthu.


MARKO 14:4
Koma anakhalako ena anabvutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa cifukwa ninji?


MARKO 14:33
Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.


MARKO 15:15
Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Baraba, napereka Yesu, atamkwapula, akampacike pamtanda.


MARKO 15:43
anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.


MARKO 16:14
Ndipo citatha ico anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pacakudya; ndipo anawadzudzula cifukwa ca kusabvomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanabvomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.


LUKA 1:6
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa.


LUKA 1:17
Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


LUKA 1:51
Iye anacita zamphamvu ndi mkono wace; 6 Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao,


LUKA 1:66
Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nangamwana uyu adzakhala wotani? Pakuti 13 dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.


LUKA 1:70
15 (Monga iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ace oyera mtima, a kale lomwe),


LUKA 1:78
Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;


LUKA 2:19
Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.


LUKA 2:25
Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lace Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


LUKA 2:51
Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo 7 amace anasunga zinthu izi zonse mumtima mwace.


LUKA 3:3
Ndipo iye anadza ku dziko lonse la m'mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku cikhululukiro ca macimo;


LUKA 3:8
Cifukwa cace balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.


LUKA 5:21
Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, ndani Uyu alankhula zomcitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira macimo, koma Mulungu yekha?


LUKA 5:32
Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ocimwa kuti atembenuke mtima,


LUKA 6:40
9 Wophunzira saposa mphunzitsi wace; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wace.


LUKA 6:45
13 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cokoma ca mtima wace; ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'coipa cace: pakuti m'kamwa mwace mungolankhula mwa kucuruka kwa mtima wace.


LUKA 8:15
Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.


LUKA 10:27
Ndipo iye anayankha nati, 3 Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.


LUKA 12:29
Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.


LUKA 12:34
Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.


LUKA 12:45
Koma 2 kapolo uyo akanena mumtima mwace, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;


LUKA 13:3
Ndinena kwa inu, iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.


LUKA 13:5
Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse ci, modzimodzi.


LUKA 13:14
Ndipo mkuru wa sunagoge anabvutika mtima, cifukwa Yesu anaciritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira nchito, cifukwa cace idzani kudzaciritsldwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.


LUKA 14:18
Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituruke kukauona; ndikupempha undilole ine ndisafika.


LUKA 15:7
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.


LUKA 15:10
Comweco, ndinena kwa inu, kuli cimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu cifukwa ca munthu wocimwa mmodzi amene atembenuka mtima.


LUKA 15:17
Koma m'mene anakumbukila mumtima, anati, Anchito olipidwa ambiri a atate wanga ali naco cakudya cocuruka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?


LUKA 16:3
Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwace, Ndidzacita ciani, cifukwa mbuye wanga andicotsera ukapitao? kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundicititsa manyazi.


LUKA 16:30
Koma anati, lai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wocokera kwa akufa adzasandulika mtima.


LUKA 16:31
Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.


LUKA 18:1
Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima;


LUKA 18:7
Ndipo kodi Mulungu sadzacitira cilungamo osankhidwa ace akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?


LUKA 19:21
pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula cimene simunaciika pansi, mututa cimene simunacifesa.


LUKA 19:22
Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula cimene sindinaciika, ndi wotuta cimene sindinacifesa;


LUKA 20:6
ndiponso, tikanena, Ucokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.


LUKA 20:20
Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ace, kotero kuti akampereke iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.


LUKA 20:40
Pakuti sanalimbanso mtima kumfunsa iye kanthu kena.


LUKA 21:14
Cifukwa cace tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire cimene mudzayankha.


LUKA 22:44
Ndipo 2 pokhala iye m'cipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lace linakhala ngati madontho akuru a mwazi alinkugwa pansi.


LUKA 22:62
Ndipo anaturuka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.


LUKA 24:25
Ndipo iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndiozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


LUKA 24:32
Ndipo anati wina kwa mnzace, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitseguliramalembo?


LUKA 24:38
Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji obvutika? ndipo matsutsano am auka bwanji m'mtima mwanu?


YOHANE 11:19
koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.


YOHANE 12:40
4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, Nangatembenuke, Ndipo ndingawaciritse.


YOHANE 13:2
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adathakuika mu mtima wace wa Yudase mwana wa Simoni Isikariote, kuti akampereke iye,


YOHANE 14:1
Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.


YOHANE 14:27
4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.


YOHANE 16:6
Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu.


YOHANE 16:22
Ndipo inu tsono muli naco cisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzacotsa kwa inu cimwemwe canu.


YOHANE 16:33
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:26
Mwa ici unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; Ndipo thupi langanso lidzakhala m'ciyembekezo.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:37
Koma pamene anamva ici, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzacita ciani, amuna inu, abale?


MACHITIDWE A ATUMWI 2:46
Ndipo tsiku ndi tsiku 7 anali cikhalire ndi mtima umodzi m'Kacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:2
obvutika mtima cifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:13
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:24
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri m'menemo;


MACHITIDWE A ATUMWI 4:29
Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,


MACHITIDWE A ATUMWI 4:31
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 4:32
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka cuma anali naco ndi kace ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:3
Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?


MACHITIDWE A ATUMWI 5:4
Pamene unali nao, sunali wako kodi? ndipo pamene unaugulitsa sunali m'manja mwako kodi? bwanji cinalowa ici mumtima mwako? sunanyenga anthu, komatu Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:12
Ndipo mwa manja aatumwi zizindikilo ndi zozizwa zambiri zinacitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khumbi la Solomo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:13
Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;


MACHITIDWE A ATUMWI 5:33
Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:23
Koma pamene zaka zace zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwace kuzonda abale ace ana a Israyeli,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:32
5 akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:39
amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha acoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Aigupto,


MACHITIDWE A ATUMWI 7:51
22 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:54
Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.


MACHITIDWE A ATUMWI 7:57
Koma anapfuula ndi mau akuru, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;


MACHITIDWE A ATUMWI 8:6
Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:21
Ulibe gawo kapena colandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 8:22
Cifukwa: cace lapa coipa calm ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingiriraca mtima wako.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:13
Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;


MACHITIDWE A ATUMWI 9:27
Koma Bamaba anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:29
nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Aheleniste; koma anayesayesa kumupha iye.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:32
Koma kunali, pakupita Petro ponse ponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhalaku Luda.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:41
Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:18
Ndipo pamene anamva izi, anakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, a Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 11:23
ameneyo, m'mene anafika, naona cisomo ca Mulungu, anakondwa; ndipo anawandandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


MACHITIDWE A ATUMWI 11:29
Ndipo akuphunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya;


MACHITIDWE A ATUMWI 12:20
Koma Herode anaipidwa nao a ku Turo ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zocokera ku dziko la mfumu.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:22
Ndipo m'mene atamcotsa iye, anawautsira Davine akhale mfumu yao; amenenso anamcitira umboni, nati, Ndapeza Davine, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzacita cifuniro canga conse.


MACHITIDWE A ATUMWI 13:46
Ndipo Paulo ndi Bamaba analimbika mtima ponena, nati, 9 Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. 10 Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:3
Cifukwa cace anakhala nthawi yaikuru nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anacitira umboni mau a cisomo cace, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zicitidwe ndi manja ao.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:8
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawacitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;


MACHITIDWE A ATUMWI 15:25
cinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Bamaba ndi Paulo,


MACHITIDWE A ATUMWI 15:39
Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzace; ndipo Bamaba anatenga Marko, nalowa n'ngalawa, nanka ku Kupro.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:14
Ndipo anatimva mkazi wina dzina lace Lidiya, wakugulitsa cibakuwa, wa ku mudzi wa Tiyatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wace Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:18
Ndipo anacita cotero masiku ambiri. Koma Paulo anabvutika mtima ndithu, naceuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Kristu, turuka mwa iye. Ndipo unaturuka nthawi yomweyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:5
Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa acabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nacititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwaturutsira kwa anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:11
Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:16
Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anabvutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.


MACHITIDWE A ATUMWI 17:30
Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima;


MACHITIDWE A ATUMWI 18:12
Tsono pamene Galiyo anali ciwanga ca Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye ku mpando wa ciweruziro,


MACHITIDWE A ATUMWI 18:26
ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Priskila ndi Akula, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:4
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire iye amene adzadza pambuyo pace, ndiye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:8
Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.


MACHITIDWE A ATUMWI 19:9
Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Turano.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:3
Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo a atampangira ciwembu Ayuda, pori iye apite ndi ngalawa ku Suriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Makedoniya.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:16
Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.


MACHITIDWE A ATUMWI 20:21
ndi kucitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi cikhulupiriro colinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.


MACHITIDWE A ATUMWI 21:13
Pamenepo Paulo anayankha, Mucitanji, polira ndi kundiswera mtima? pakuti ndakonzeka Ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:1
Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akuru anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi cikumbu mtima cokoma conse kufikira lero lomwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 23:11
Ndipo usiku wace Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandicitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundicitira umboni ku Roma.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:16
M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale naco nthawi zonse cikumbu mtima cosanditsutsa ca kwa Mulungu ndi kwa anthu.


MACHITIDWE A ATUMWI 25:25
Koma ndinapeza ine kuti sanacita kanthu, koyenera imfa iye; ndipo popeza, iye yekha anati akaturukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:3
makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; cifukwa cace ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:10
Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:11
Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.


MACHITIDWE A ATUMWI 26:20
komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kucita nchito zoyenera kutembenuka mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:22
Koma tsopano ndikucenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:25
Cifukwa cace, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.


MACHITIDWE A ATUMWI 27:36
Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga cakudya iwo omwe.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:15
Kucokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apiyo, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:19
Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kuturukira kwa Kaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.


MACHITIDWE A ATUMWI 28:27
Pakuti mtima wa anthu awa watupatu, Ndipo m'makutu mwao mmolemakumva, Ndipo masoao anawatseka; Kuti angaone ndi maso, Nangamve ndi makutu, Nangazindikire ndi mtima, Nangatembenuke, Ndipo Ine ndingawaciritse.


AROMA 1:7
kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


AROMA 1:13
Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.


AROMA 1:21
cifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamcitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pace m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira,


AROMA 1:28
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;


AROMA 2:5
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa dzuwa la mkwiyo ndi la kubvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;


AROMA 2:9
nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu ali yense wakucita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mhelene;


AROMA 2:15
popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;


AROMA 2:19
nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,


AROMA 2:29
koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwace sikucokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.


AROMA 4:21
nakhazikikanso mumtima kuti, o cimene iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakucicita.


AROMA 5:7
Pakuti ndi cibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.


AROMA 6:17
Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco;


AROMA 7:23
koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m'ziwalo zanga.


AROMA 7:25
Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo.


AROMA 8:27
ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.


AROMA 8:28
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.


AROMA 8:35
Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?


AROMA 8:38
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu,


AROMA 9:1
Ndinena zoona mwa Kristu, sindinama ai, cikumbu mtima canga cicita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,


AROMA 9:2
kuti ndagwidwa ndi cisoni cacikuru ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.


AROMA 9:11
pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo,


AROMA 9:18
Cotero iye acitira cifundo amene iye afuna, ndipo amene iye afuna amuumitsamtima.


AROMA 10:1
Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.


AROMA 10:6
Koma cilungamo ca cikhulupiriro citero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? ndiko, kutsitsako Kristu;


AROMA 10:8
Koma citani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a cikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:


AROMA 10:9
kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:


AROMA 10:10
pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m'kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso


AROMA 10:20
Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifuna; Ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunsa.


AROMA 11:7
Ndipo ciani tsono? ici cimene Israyeli afunafuna sanacipeza; koma osankhidwawo anacipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;


AROMA 11:20
Cabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi cikhulupiriro cako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:


AROMA 11:22
Cifukwa cace onani cifatso ndi kuuma mtima kwace kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwace; koma kwa iwe cifatso cace ca Mulungu, ngati ukhala cikhalire m'eifatsomo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.


AROMA 11:25
Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa cinsinsi ici, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israyeli, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;


AROMA 11:34
Pakuti 5 anadziwitsa ndani mtima wace wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wace ndani?


AROMA 12:2
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.


AROMA 12:8
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, acite ndi kukondwa mtima.


AROMA 12:13
Patsani zosowa oyera mtima; cerezani aulendo.


AROMA 12:16
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.


AROMA 13:5
Cifukwa cace, kuyenera kuti mukhale omvera, si cifukwa ca mkwiyo woo kha, komanso cifukwa ca cikumbu mtima.


AROMA 14:5
Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzace; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu ali yense akhazikike konse mumtima mwace.


AROMA 14:14
Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe cinthu conyansa pa cokha; koma kwa ameneyo aciyesa conyansa, kwa iye cikhala conyansa.


AROMA 15:5
Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;


AROMA 15:14
Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzace.


AROMA 15:15
Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, cifukwa ca cisomo capatsidwa kwa ine ndi Mulungu,


AROMA 15:18
Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,


AROMA 15:25
Koma 1 tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndirikutumikira oyera mtima.


AROMA 15:26
Pakuti 2 kunakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya kucereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.


AROMA 15:31
kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;


AROMA 16:2
kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zili zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.


AROMA 16:15
Mulankhule Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wace, ndi Olumpa, ndi oyeramtima onse ali pamodzi nao.


1 AKORINTO 1:2
kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Kristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


1 AKORINTO 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.


1 AKORINTO 2:2
Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu koma Yesu Kristu, ndi iye wopacikidwa.


1 AKORINTO 2:9
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, Nisizinalowa mu mtima wa munthu, Zimene ziri zonse Mulungi anakonzereratu iwo aku mkonda iye.


1 AKORINTO 2:16
Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize iye? Koma ife tiri nao mtima wa Kristu.


1 AKORINTO 4:5
Cifukwa cace musaweruze kanthu isanadze nthawi yace, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wace wa kwa Mulungu.


1 AKORINTO 5:8
cifukwa cace ticita phwando, si ndi cotupitsa cakale, kapena ndi cotupttsaca dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi coonadi.


1 AKORINTO 6:1
Kodiakhoza winawa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzace, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?


1 AKORINTO 6:2
Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tocepacepa?


1 AKORINTO 7:9
Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.


1 AKORINTO 7:12
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkaziwosakhulupira, ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.


1 AKORINTO 7:13
Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, nabvomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.


1 AKORINTO 7:37
Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwace, wopanda cikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa cifuniro ca iye yekha, natsimikiza ici mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wace wamkazi, adzacita bwino.


1 AKORINTO 8:7
Komatu cidziwitso siciri mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo cikumbu mtima cao, popeza ncofoka, cidetsedwa.


1 AKORINTO 8:10
Pakuti wina akaona iwe amene uli naco cidziwitso, ulikukhala pacakudya m'kacisi wa fano, kodi cikumbu mtima cace, popeza ali wofoka, sieidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?


1 AKORINTO 8:12
Koma pakucimwira abale, ndi kulasa cikumbu mtima cao cofoka, mucimwira kotero Kristu.


1 AKORINTO 10:25
Conse cogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu cifukwa ca cikumbu mtima;


1 AKORINTO 10:27
Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.


1 AKORINTO 10:28
Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, cifukwa ca iyeyo wakuuza, ndi cifukwa ca cikumbu mtima.


1 AKORINTO 10:29
Ndinena cikumbu mtima, si ca iwe mwini, koma ca winayo; 1 pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi cikumbu mtima ca wina?


1 AKORINTO 13:4
Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,


1 AKORINTO 13:5
sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;


1 AKORINTO 14:25
zobisika za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.


1 AKORINTO 14:33
pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.


1 AKORINTO 16:1
Koma za copereka ca kwa oyera mtima, mongandinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero citani inunso.


1 AKORINTO 16:15
Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),


2 AKORINTO 1:1
PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya lonse:


2 AKORINTO 1:12
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa cikumbu mtima cathu, kuti m'ciyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'cisomo ca Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


2 AKORINTO 1:17
Pamenepo, pakufuna cimene, kodi ndinacitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?


2 AKORINTO 2:1
Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi cisoni.


2 AKORINTO 2:4
Pakuti m'cisautso cambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni cisoni, koma kuti mukadziwe cikondi ca kwa inu, cimene ndiri naco koposa.


2 AKORINTO 2:17
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akucita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa coona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.


2 AKORINTO 3:12
Pokhala naco tsono ciyembekezo cotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukuru,


2 AKORINTO 3:15
Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, cophimba cigona pamtima pao.


2 AKORINTO 4:2
koma takaniza zobisfka za manyazi, osayendayenda mocenjerera, kapena kucita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a coonadi tidzibvomeretsa tokha ku cikumbu mtima ca anthu onse pamaso pa Mulungu.


2 AKORINTO 5:6
Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tiri kwathu m'thupi, sitiri kwa Ambuye,


2 AKORINTO 5:8
koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.


2 AKORINTO 5:11
Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtimazanu.


2 AKORINTO 5:12
Sitidzibvomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu cifukwa ca kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.


2 AKORINTO 6:6
m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;


2 AKORINTO 6:11
M'kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.


2 AKORINTO 6:12
Simupsinjika mwa ife, koma mupsiniika mumtima mwanu.


2 AKORINTO 7:4
Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga cifukwa ca inu nkwakukuru; ndidzazidwa naco citonthozo, ndisefukira naco cimwemwe m'cisautso cathu conse.


2 AKORINTO 7:8
Kuti ngakhale ndakumvetsani cisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani cisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.


2 AKORINTO 7:9
Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.


2 AKORINTO 7:10
Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.


2 AKORINTO 7:11
Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.


2 AKORINTO 7:16
Ndikondwera kuti m'zonse ndilimbika mtima za inu.


2 AKORINTO 8:2
kuti m'citsimikizo cacikuru ca cisautso, kucurukitsa kwa cimwemwe cao, ndi kusauka kwaokweni kweni zidacurukira ku colemera ca kuolowa mtima kwao.


2 AKORINTO 8:4
anacita eni ace, natiumirfza ndi kutidandauliraza cisomoco, ndi za ciyanjano ca utumiki wa kwa oyera mtima;


2 AKORINTO 8:16
Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.


2 AKORINTO 9:1
Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;


2 AKORINTO 9:7
Yense acite monga anatsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.


2 AKORINTO 9:12
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma ucurukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;


2 AKORINTO 10:1
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Kristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzicepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


2 AKORINTO 10:2
koma ndipempha kuti pokhala ndiri pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi,


2 AKORINTO 10:12
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwookha, alibe nzeru.


2 AKORINTO 11:2
Pakuti ndicita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Kristu.


2 AKORINTO 11:3
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kucenjerera kwace, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima ziri kwa Kristu.


2 AKORINTO 11:21
Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.


2 AKORINTO 13:11
Cotsalira, abale, kondwerani, Mucitidwe angwiro; mutorithozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa cikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.


2 AKORINTO 13:13
Oyera mtima onse alankhula inu,


AGALATIYA 5:10
Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza citsutso cace.


AGALATIYA 5:20
nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru,


AGALATIYA 5:22
Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,


AEFESO 1:1
PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Kristu Yesu:


AEFESO 1:4
monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,


AEFESO 1:9
Anatizindikiritsa ife cinsinsi ca cifuniro cace, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa iye,


AEFESO 1:11
Mwa iye tinayesedwa colowa cace, popeza tinakonzekeratu monga mwa citsimikizo mtima ca iye wakucita zonse monga mwa uphungu wa cifuniro cace;


AEFESO 1:15
Mwa ici inenso, m'mene ndamva za cikhulupiriro'ca mwa Ambuye Yesu ciri mwa inu, cimenenso mufikitsira oyera mtima onse,


AEFESO 1:18
ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero wacolowa cace mwa oyera mtima,


AEFESO 2:7
kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.


AEFESO 2:19
Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;


AEFESO 3:8
Kwa ine wocepa ndi wocepetsa wa onse, oyera mtima anandipatsa cisomo ici, ndilalikire kwa amitundu cuma cosalondoleka ca Kristu;


AEFESO 3:11
monga mwa citsimikizo mtima ca nthawi za nthawi, cimene anacita mwa Kristu Yesu Ambuye wathu:


AEFESO 3:12
amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa cikhulupiriro ca pa iye.


AEFESO 3:13
Mwa ici ndipempha kuti musade mtima, m'zisautso zanga cifukwa ca inu, ndiwo ulemerero wanu.


AEFESO 3:18
mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,


AEFESO 4:12
kuti akonzere oyera mtima: ku nchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu;


AEFESO 4:17
Pamenepo ndinena ici, ndipo ndicita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'citsiru ca mtima wao,


AEFESO 4:23
koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,


AEFESO 4:31
11 Ciwawo conse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi ciwawa, ndi mwano zicotsedwe kwa inu, ndiponso coipa conse.


AEFESO 4:32
Koma 12 mukhalirane okoma wina ndi mnzace, a mtima wacifundo, akukhululukirana nokha, 13 monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.


AEFESO 5:3
Koma dama ndi cidetso conse, kapena cisiriro, zisachulidwe ndi kuchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;


AEFESO 5:19
ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;


AEFESO 6:5
Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukila kanthu kena, monga kwa Kristu;


AEFESO 6:6
si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima;


AEFESO 6:7
akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai;


AEFESO 6:18
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


AFILIPI 1:1
PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


AFILIPI 1:7
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'codzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'cisomo.


AFILIPI 1:10
kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Kristu;


AFILIPI 1:14
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


AFILIPI 1:15
Enatu alalikiranso Kristu cifukwa ca kaduka ndi ndeu; koma enanso cifukwa ca kukoma mtima;


AFILIPI 1:20
monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.


AFILIPI 2:2
kwaniritsani cimwemwe canga, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala naco cikondi comwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;


AFILIPI 2:3
musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;


AFILIPI 2:5
Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,


AFILIPI 2:13
pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma mtima kwace, ndiye Mulungu,


AFILIPI 2:20
Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, amene adza: samalira za kwa inu ndi mtima woona.


AFILIPI 2:26
popeza anali wolakalaka inu nonse, nabvutika mtima cifukwa mudamva kuti anadwala.


AFILIPI 3:15
Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ici mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzabvumbulutsira inu;


AFILIPI 4:2
Ndidandaulira Euodiya, ndidandaulira Suntuke, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.


AFILIPI 4:8
Cotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi.


AFILIPI 4:10
Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukuru, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pocitapo.


AFILIPI 4:21
Lankhulani woyera mtima ali yense mwa Kristu Yesu. Abalewo akukhala ndiine alankhula inu.


AFILIPI 4:22
Oyera mtima onse alankhula inu, koma makamaka-fwo a banja la Kaisara.


AKOLOSE 1:2
kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Kristu a m'Kolose: Cisomo kwa inu ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu.


AKOLOSE 1:4
popeza tidamva za cikhulupiriro canu ca mwa Kristu Yesu, ndi cikondi muli naco kwa oyera mtima onse;


AKOLOSE 1:11
olimbikitsidwa m'cilimbiko conse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wace, kucitira cipiriro conse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi cimwemwe,


AKOLOSE 1:12
ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao colowa ca oyera mtima m'kuunika;


AKOLOSE 1:26
5 ndiwo cinsinsico cinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anacionetsa tsopano kwa oyera mtima ace,


AKOLOSE 3:8
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:


AKOLOSE 3:12
Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;


AKOLOSE 3:14
koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.


AKOLOSE 3:16
Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.


AKOLOSE 3:19
Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.


AKOLOSE 3:21
Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.


AKOLOSE 3:22
Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;


AKOLOSE 3:23
ciri conse mukacicita, gwirani nchito mocokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;


AKOLOSE 4:11
ndi Yesu, wochedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo anchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine conditonthoza mtima.


1 ATESALONIKA 2:10
Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


1 ATESALONIKA 2:17
Koma ife, abale, angakhale adaticotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi cilakolako cacikuru;


1 ATESALONIKA 3:1
Cifukwa cace, posakhoza kulekereranso, tidabvomereza mtima atisiye tokhaku Atene;


1 ATESALONIKA 3:13
kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda cifukwa m'ciyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ace onse.


1 ATESALONIKA 4:12
kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.


1 ATESALONIKA 5:14
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani ampwayi, limbikitsani amantha mtima? cirikizani ofok a, mukhale oleza mtima pa onse.


2 ATESALONIKA 1:10
pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ace, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m'tsiku lija.


2 ATESALONIKA 2:2
kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;


1 TIMOTEO 1:5
koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;


1 TIMOTEO 1:16
komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.


1 TIMOTEO 1:19
ndi kukhala naco cikhulupiriro ndi cikumbu mtima cokoma, cimene ena adacikankha, cikhulupiriro cao cidatayika;


1 Timothy 2:2
cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.


1 Timothy 3:9
okhala naco cinsinsi ca cikhulupiriro m'cikumbu mtima coona.


1 Timothy 4:2
m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olocedwa m'cikumbu mtima mwao monga ndi citsulo camoto;


1 Timothy 4:12
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala citsanzo kwa iwo okhulupira, m'mau, m'mayendedwe, m'cikondi, m'cikhulupiriro, m'kuyera mtima.


1 Timothy 4:15
Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.


1 Timothy 5:2
akazi akulu ngati amai; akazi ang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.


1 Timothy 5:10
wa mbiri ya nchito zabwino; ngati walera ana, ngati wacereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a nzera mtima, ngati wathapdiza osautsidwa, ngati anatsatadi nchito zonse zabwino.


1 Timothy 5:22
Usafulumira kuika manja pa munthu ali yense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


TITO 1:7
Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;


TITO 1:8
komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;


TITO 1:15
Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi cikumbu mtima cao.


TITO 3:4
Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka,


TITO 3:12
Pamene ndikatuma Artema kwa iwe, kapena Tukiko, cita cangu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yacisanu.


FILEMONI 1:5
pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;


FILEMONI 1:7
Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.


FILEMONI 1:8
Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,


FILEMONI 1:12
amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weni weni wa ine.


FILEMONI 1:14
koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kucita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.


FILEMONI 1:20
Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Kristu.


AHEBRI 3:1
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi. Mkuluwansembe wa cibvomerezo cathu, Yesu;


AHEBRI 3:6
koma Kristu monga mwana, wosunga nyumba yace; ndife nyumba yace, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa ciye-I mbekezoeo, kucigwira kufikira citsiriziro.


AHEBRI 3:8
Musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, Monga muja tsiku la ciyesero m'cipululu,


AHEBRI 3:10
Momwemo ndinakwiya nao mbadwouwu, Ndipo ndinati, Nthawi zonse amasocera mumtima; Koma sanazindikira njira zangaiwowa;


AHEBRI 3:12
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


AHEBRI 3:15
umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ace, Musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.


AHEBRI 3:16
Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adaturuka m'Aigupto ndi Mose?


AHEBRI 4:12
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.


AHEBRI 4:16
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.


AHEBRI 6:1
Mwa ici, polekana nao mau a ciyambidwe ca Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo nchito zakufa, ndi a cikhulupiriro ca pa Mulungu,


AHEBRI 6:4
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,


AHEBRI 6:9
Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu ziri zoposa ndi zophatikana cipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;


AHEBRI 6:10
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


AHEBRI 6:12
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa cikhulupiriro ndi kuleza mtima.


AHEBRI 7:26
Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ocimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


AHEBRI 8:10
Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli, Atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, Ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; Ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, Ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:


AHEBRI 9:9
ndico ciphiphiritso ca ku nthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za cikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.


AHEBRI 9:14
koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


AHEBRI 10:2
Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, cifukwa otumikirawo sakadakhala naco cikumbu mtima ca macimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?


AHEBRI 10:16
ici ndi cipangano ndidzapangana nao, Atapira masiku ajawo, anena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; Ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;


AHEBRI 10:22
tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


AHEBRI 12:15
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera cisomo ca Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungabvute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


AHEBRI 13:5
Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


AHEBRI 13:6
Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; smdidzaopa; Adzandicitira ciani munthu?


AHEBRI 13:9
Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundu mitundu, ndi acilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi cisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo.


AHEBRI 13:18
Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri naco cikumbu mtima cokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.


AHEBRI 13:24
Lankhulani 5 atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akulankhulani iwo a ku Italiya.


YAKOBO 1:19
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu ali yense akhale wochera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.


YAKOBO 1:26
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lace, koma adzinyenga mtima wace, kupembedza kwace kwa munthuyu nkopanda pace.


YAKOBO 3:14
Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi cotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana naco coonadi.


YAKOBO 5:7
Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwace kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira cipatso cofunikatu ca dziko, ndi kuleza mtima naco kufikira cikalandira mvula ya myundo ndi masika,


YAKOBO 5:8
Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwace kwa Ambuye kuyandikira.


YAKOBO 5:10
Tengani, abale, citsanzo ca kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri ameneanalankhulam'dzina la Ambuyeo


1 PETRO 1:13
Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu m'bvumbulutso la Yesu Kristu;


1 PETRO 1:15
komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;


1 PETRO 1:16
popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.


1 PETRO 1:22
Popeza 5 mwayeretsa moyo wanu pakumvera coonadi kuti 6 mukakonde abale ndi cikondi cosanyenga, mukondane kweni kweni kucokera kumtima;


1 PETRO 2:3
ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;


1 PETRO 2:5
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu,


1 PETRO 2:9
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa;


1 PETRO 2:19
Pakuti ici ndi cisomo ngati munthu, cifukwa ca cikumbu mtima pa Mulungu alola zacisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.


1 PETRO 3:4
koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.


1 PETRO 3:5
Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;


1 PETRO 3:16
ndi kukhala naco cikumbu mtima cabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Kristu akacitidwe manyazi.


1 PETRO 3:20
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka cingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;


1 PETRO 3:21
cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu;


1 PETRO 4:1
Popeza Kristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo cimo;


2 PETRO 1:19
Ndipo tiri nao mau a cinenero okhazikika koposa; amene mucita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukaca, nikauka nthanda pa mtima yanu;


2 PETRO 2:7
ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja


2 PETRO 2:14
okhala nao maso odzala ndi cigololo, osakhoza kuleka ucimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;


2 PETRO 3:1
Okondedwa, uyu ndiye kalata waciwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;


2 PETRO 3:9
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.


1 YOHANE 2:28
Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa iye; kuti 10 akaonekere iye tikakhale nako kulimbika mtima, osacita manyazi kwa iye pa kudza kwace.


1 YOHANE 3:19
Umo tidzazindikira kuti tiri ocokera m'coonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pace,


1 YOHANE 3:20
1 m'mene monse mtima wathu utitsutsa; cifukwa Mulungu ali wamkuru woposa mitima yathu, nazindikira zonse.


1 YOHANE 3:21
Okondedwa, 2 mtima wathu ukapanda kuritsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu;


1 YOHANE 4:17
M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.


YUDA 1:3
Okondedwa, pakucira cangu conse cakukulemberani za cipulumutso ca ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu cifukwa ca cikhulupiriro capatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.


YUDA 1:9
Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pakucita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumehulira cifukwa comcitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.


CHIVUMBULUTSO 3:19
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero cita cangu, nutembenuke mtima.


CHIVUMBULUTSO 5:8
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nao azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 8:3
Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala naco cotengera ca zofukiza cagolidi; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wacifumu.


CHIVUMBULUTSO 8:4
Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kuturuka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 11:18
Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akuru; ndi kuononga iwo akuononga dziko.


CHIVUMBULUTSO 13:7
Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.


CHIVUMBULUTSO 13:10
N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 14:10
iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'cikho ca mkwiyo wace; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa j


CHIVUMBULUTSO 14:12
Pano pali cipiriro ca oyera mtima, ca iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi cikhulupiriro ca Yesu.


CHIVUMBULUTSO 16:6
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.


CHIVUMBULUTSO 17:6
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukuru.


CHIVUMBULUTSO 17:9
Pano pali mtima wakukhaia nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;


CHIVUMBULUTSO 17:13
Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa cirombo.


CHIVUMBULUTSO 17:17
Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kucita za m'mtima mwace, ndi kucita ca mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa cirombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.


CHIVUMBULUTSO 18:7
Monga momwe unadzicitira ulemu, nudyerera, momwemo muucitire eouzunza ndi couliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwace, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.


CHIVUMBULUTSO 18:20
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; cifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


CHIVUMBULUTSO 18:24
Ndipo 3 momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.


CHIVUMBULUTSO 19:8
Ndipo anampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.


CHIVUMBULUTSO 20:6
Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.


CHIVUMBULUTSO 20:9
Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.


CHIVUMBULUTSO 22:21
5 Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale ndi oyera mtima onse, Amen.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society