A A A A A

Sakani
MATEYU 5:9
Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.


MATEYU 10:13
Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.


MATEYU 10:34
2 Musalingalire kuti nelidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sinelinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.


MARKO 5:34
Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, cikhulupiriro, cako cakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wocira cibvutiko cako.


MARKO 9:50
Mcere uli wabwino; koma ngati mcere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi ciani? Khalani nao mcere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzace.


LUKA 1:79
22 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; Kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.


LUKA 2:14
Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


LUKA 2:29
Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, Lolani ine, kapolo wanu, ndicoke mumtendere;


LUKA 7:50
Ndipo Iyeanati kwa mkaziyo, Cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.


LUKA 8:48
Ndipo iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.


LUKA 10:5
Ndipo m'nyumba iri yonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.


LUKA 10:6
Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.


LUKA 11:21
Pamene pali ponse mwini mphamvu alonda pabwalo pace zinthu zace ziri mumtendere;


LUKA 12:51
Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapani? Ndinena wa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;


LUKA 14:32
Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.


LUKA 19:38
nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere m'Mwamba, ndi ulemerero m'Mwambamwamba.


LUKA 19:42
nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! koma tsopano zibisika pamaso pako.


LUKA 24:36
Ndipo pakulankhula izi iwowa, iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu.


YOHANE 14:27
4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.


YOHANE 16:33
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.


YOHANE 20:19
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali citsekere, kumene anakhala akuphunzira, cifukwa ca kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.


YOHANE 20:21
Cifukwa cace Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.


YOHANE 20:26
Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu akuphunzira ace analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao: Yesu anadza, makomo ali citsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.


MACHITIDWE A ATUMWI 9:31
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.


MACHITIDWE A ATUMWI 10:36
Mau amene anatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Kristu (ndiye Ambuye wa onse)


MACHITIDWE A ATUMWI 12:20
Koma Herode anaipidwa nao a ku Turo ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zocokera ku dziko la mfumu.


MACHITIDWE A ATUMWI 15:33
Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza. [


MACHITIDWE A ATUMWI 16:36
Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu turukani, mukani mumtendere.


Acts 24:2
Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena. Popeza tiri nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,


1 AKORINTO 1:3
Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


1 AKORINTO 7:15
Koma ngati wosakhulupirayo acoka, acoke. M'mirandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo, Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.


1 AKORINTO 14:33
pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.


1 AKORINTO 16:11
cifukwa cace munthu asampeputse, Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze: kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale,


2 AKORINTO 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


2 AKORINTO 13:11
Cotsalira, abale, kondwerani, Mucitidwe angwiro; mutorithozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa cikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.


AGALATIYA 1:3
Cisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu,


AGALATIYA 5:22
Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,


AGALATIYA 6:16
Ndipo onse amene atsatsa cilangizo ici, mtendere ndi cifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu.


AEFESO 1:2
Cisomo kwa inu, ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.


AEFESO 2:14
Pakuti iye ndiye mtendere wathu, amene anacita kutionse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,


AEFESO 2:15
atacotsa udani m'thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kucitapo mtendere;


AEFESO 2:17
ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;


AEFESO 4:3
ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa cimangiriro ca mtendere.


AEFESO 6:15
ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;


AEFESO 6:23
3 Mtendere ukhale kwa abale, ndi cikondi, pamodzi ndi cikhulupiriro, zocokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Kristu.


AFILIPI 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.


AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.


AFILIPI 4:9
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo citani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.


AKOLOSE 1:2
kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Kristu a m'Kolose: Cisomo kwa inu ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu.


AKOLOSE 1:20
mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.


AKOLOSE 3:15
Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.


1 ATESALONIKA 1:1
PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu: Cisomo kwa inu ndi mtendere.


1 ATESALONIKA 5:3
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


1 ATESALONIKA 5:13
ndipo muwacitire ulemu woposatu mwa cikondi, cifukwa ca nchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.


1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.


2 ATESALONIKA 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu.


2 ATESALONIKA 3:16
Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.


1 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'cikhulupiriro: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Kristu Yesu Ambuye wathu.


2 TIMOTEO 1:2
kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.


2 TIMOTEO 2:22
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate cilungamo, cikhulupiriro, cikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.


TITO 1:4
kwa Tito, mwana wanga weni weni monga mwa cikhulupiriro ca ife tonse: Cisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Mpulumutsi wathu.


FILEMONI 1:3
Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.


AHEBRI 7:2
amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya cilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere;


AHEBRI 11:31
Ndi cikhulupiriro 4 Rahabi wadama uja sanaonongeka pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.


AHEBRI 12:11
Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.


AHEBRI 12:14
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:


AHEBRI 13:20
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye woturuka mwa akufa 1 Mbusa wamkuru wa nkhosa 2 ndi mwazi wa cipangano cosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


YAKOBO 2:16
ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, muitapfunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwace nciani?


YAKOBO 3:17
Koma nzeru yocokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala cifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.


YAKOBO 3:18
Ndipo cipatso ca cilungamo cifesedwa mumtendere kwa iwo akucita mtendere.


1 PETRO 1:2
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.


1 PETRO 3:11
j Ndipo apatuke pacoipa, nacite cabwino; Afunefune mtendere ndi kuulondola.


1 PETRO 5:14
Lankhulanani ndi cipsompsono ca cikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Kristu.


2 PETRO 1:2
Cisomo kwa inu ndi mtendere zicurukitsidwe m'cidziwitso ca Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.


2 PETRO 3:14
Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.


2 YOHANE 1:3
Cisomo, cifundo, mtendere zikhale ndi ife zocokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Kristu Mwana wa Atate, m'coonadi ndi m'cikondi.


3 YOHANE 1:14
koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana, Mtendere ukhale nawe. Akulankhula abwenzi, Lankhula abwenzi ndi kuchula maina ao.


YUDA 1:2
Cifundo ndi mtendere ndi cikondi zikucurukireni.


CHIVUMBULUTSO 6:4
Ndipo anaturuka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakucotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikuru.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society