A A A A A

Sakani
MATEYU 2:22
Koma pakumva iye kuti Arikelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wace Herode, anacita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anacenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa ku dziko la Galileya,


MATEYU 8:26
Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikuru.


MATEYU 14:26
Koma m'mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, ndi mzukwa! Ndipo anapfuula ndi mantha.


MATEYU 28:8
Ndipo iwo anacoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukuru, nathamanga kukauza ophunzira ace.


MARKO 4:40
Ndipo ananena nao, Mucitiranji mantha? kufikira tsopano mulibe cikhulupiriro kodi?


MARKO 4:41
Ndipo iwo anacita mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?


MARKO 5:33
Koma mkaziyo anacita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa cimene anamcitira iye, nadza, namgwadira, namuuza coona conse.


MARKO 9:6
Pakuti sanadziwa cimene adzayankha; cifukwa anacita mantha ndithu.


MARKO 10:32
Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anacita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,


MARKO 13:36
kuti angabwere balamantha nakakupezani muli m'tulo.


MARKO 16:8
Ndipo anaturuka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukuru kudawagwira; ndipo sanauza kanthu kwa munthu ali yense; pakuti anacitamantha.


LUKA 1:12
Ndipo Zakariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.


LUKA 1:65
Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko: lonse la mapiri a Yudeya,


LUKA 1:74
Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu, 17 Tidzamtumikira iye, opanda mantha,


LUKA 2:9
Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru.


LUKA 5:26
Ndipo cizizwo cinagwira anthu onse, ndipo analemekeza Mulungu nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.


LUKA 7:16
Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace.


LUKA 8:25
Ndipo iye anati kwa iwo, Cikhulupiriro canu ciri kuti? Ndipo m'kucita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera iye?


LUKA 8:37
Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa Ioyandikira anamfunsa iye acoke kwa iwo; cifukwa anagwidwa ndi mantha akuru. Ndipo iye analowa m'ngalawa, nabwerera.


LUKA 21:26
anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;


LUKA 24:5
ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?


LUKA 24:37
Koma anaopsedwandi kucita mantha, 1 nayesa alikuona mzimu.


YOHANE 6:19
Ndipo parnene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anacita mantha.


YOHANE 14:27
4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.


MACHITIDWE A ATUMWI 2:43
Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo 5 zozizwa ndi zizindikilo zambiri zinacitika ndi atumwi.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:5
Koma Hananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akuru anagwera onse akumvawo.


MACHITIDWE A ATUMWI 5:11
Ndipo anadza mantha akuru pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumvaizi.


MACHITIDWE A ATUMWI 16:29
Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthunrlra ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Sila,


MACHITIDWE A ATUMWI 19:17
Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Yesu Iinakuzika.


MACHITIDWE A ATUMWI 24:25
Ndipo m'mene anamfotokozera za cilungamo, ndi cidziletso, ndi ciweruziro cirinkudza, Felike anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.


AROMA 8:15
Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,


1 AKORINTO 2:3
Ndipo ine ndinakhala nanu mofoka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri.


1 AKORINTO 16:10
Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira nchito ya Ambuye, monganso ine;


2 AKORINTO 7:5
Pakutinso pakudza ife m'Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.


2 AKORINTO 7:11
Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.


2 AKORINTO 7:15
Ndipo cikondi ceni ceni care cicurukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.


AFILIPI 1:14
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


AFILIPI 2:12
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani nchito yace ya cipulumutso canu ndi mantha, ndi kunthunthumira;


1 ATESALONIKA 5:14
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani ampwayi, limbikitsani amantha mtima? cirikizani ofok a, mukhale oleza mtima pa onse.


1 TIMOTEO 5:20
Iwo akucimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo acite mantha.


2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.


Hebreerbrevet 11:7
Ndi cikhulupiriro Nowa, pocenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pocita mantha, anamanga cingalawa ca kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yace; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa cilungamo ciri monga mwa cikhulupiriro.


Hebreerbrevet 12:28
Mwa ici polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale naco cisomo, cimene tikatumikire naco Mulungu momkondweretsa, ndi kumcitira ulemu ndi mantha.


1 PETRO 1:17
Ndipo mukamuitana ngati Alate, iye amene aweruza monga mwa nchito ya yense, wopanda tsankhu, khalani ndi mantha nthawi ya cilendo canu;


1 PETRO 3:15
koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kucita codzikanira pa yense wakukufunsani cifukwa ca ciyembekezo ciri mwa inu, komatu ndi cifatsondi mantha;


1 YOHANE 4:18
Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.


YUDA 1:12
Iwo ndiwo okhala mawanga pa mapwando anu a cikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawid, yozuka mizu;


YUDA 1:23
koma ena 6 muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwacitire cifundo ndi mantha, 7 nimudane naonso maraya ocitidwa mawanga ndi thupi


CHIVUMBULUTSO 11:11
Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lace mzimu wamoyo wocokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala ciriri; ndipomantha akuru anawagwera iwo akuwapenya.


CHIVUMBULUTSO 11:13
Ndipo panthawipo panali cibvomezi cacikuru, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi Iidagwa; ndipo anaphedwa m'cibvomezico anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.


CHIVUMBULUTSO 21:8
Koma amantha, ndi osakhulupira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi acigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, colandira cao cidzakhala m'nyanja yotentha ndi mota ndi sulfure; ndiyo imfa yaciwiri.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society