A A A A A

Sakani
MATEYU 6:16
Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


MATEYU 6:18
kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.


MARKO 2:18
Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?


MARKO 2:19
Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.


LUKA 2:37
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zace: makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sanacoka kuKacisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.


MACHITIDWE A ATUMWI 14:23
Ndipo pamene anawaikira akuru mosankha mu Mpingo Mpingo, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, anaikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.


Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society